Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 January tsamba 8-9
  • January 29–February 4

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January 29–February 4
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 January tsamba 8-9

JANUARY 29–FEBRUARY 4

YOBU 40-42

Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Zimene Tikuphunzira Kuchokera pa Zimene Zinachitikira Yobu

(10 min.)

Muzikumbukira kuti mumadziwa zinthu zochepa kwambiri poyerekezera ndi Yehova (Yob 42:1-3; w10 10/15 3-4 ¶4-6)

Muzikhala ofunitsitsa kulandira malangizo ochokera kwa Yehova ndi gulu lake (Yob 42:5, 6; w17.06 25 ¶12)

Yehova amadalitsa anthu omwe amakhalabe okhulupirika ngakhale akukumana ndi mavuto (Yob 42:10-12; Yak 5:11; w22.06 25 ¶17-18)

Yobu ndi mkazi wake ali cha kuphiri ndipo akuyang’anizana mwachikondi. Yobu akuloza ziweto zawo komanso nyumba yawo.

Yehova anadalitsa Yobu chifukwa choti anakhalabe wokhulupirika

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Yob 42:7—Kodi zimene anzake atatu a Yobu ankalankhula, zikusonyeza kuti kwenikweni ankatsutsa ndani, nanga kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji kuti tizipirira pamene tikunyozedwa? (it-2 808)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Yob 42:1-17 (th phunziro 11)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Lalikirani kwa munthu amene si Mkhristu. (lmd phunziro 5 mfundo 3)

5. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 13 mfundo 6-7 komanso Zimene Ena Amanena (lmd phunziro 11 mfundo 4)

6. Nkhani

(4 min.) lmd zakumapeto A mfundo 2—Mutu: Dziko Lapansili Silidzawonongedwa. (th phunziro 13)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 108

7. Muzithandiza Ena Kuona Kuti Yehova Amawakonda

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Tinapeza Chikondi Chachikhristu M’banja la Yehova.” Mimi ndi mayi ake abweretsa maluwa komanso khadi kwa mlongo amene ali m’chipatala.

Timasangalala kwambiri kulambira Mulungu yemwe ndi chikondi. (1Yo 4:8, 16) Chikondi cha Yehova chimatithandiza kuti tikhale anzake komanso timuyandikire. Monga nkhosa za Yehova, tonse timamva kuti iye amatikonda.

Timachita zonse zimene tingathe kuti tizitsanzira chikondi cha Yehova pochita zinthu ndi anthu a m’banja lathu, Akhristu anzathu komanso anthu ena. (Yob 6:14; 1Yo 4:11) Tikamasonyeza ena chikondi, timawathandiza kuti adziwe Yehova n’kumuyandikira. Koma tikamalephera kuwasonyeza chikondi, zingawavute kukhulupirira kuti Yehova amawakonda.

Onerani VIDIYO yakuti Tinapeza Chikondi Chachikhristu M’banja la Yehova. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi nkhani ya Lei Lei ndi Mimi yakuphunzitsani chiyani pa kufunika kosonyeza ena chikondi?

Kodi tingatani kuti tithandize Akhristu anzathu kuti azimva kuti Yehova amawakonda?

  • Tiziwaona kuti ndi nkhosa zamtengo wapatali za Yehova.—Sl 100:3

  • Tizilankhula nawo mowalimbikitsa.—Aef 4:29

  • Tizichita nawo zinthu mosonyeza kuti tikuwamvetsa bwino.—Mt 7:11, 12

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 5 ¶1-8, bokosi patsamba 39

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 126 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena