Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JANUARY 1-7
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 32-33
Muzilimbikitsa Amene Akulimbana ndi Nkhawa
it-1 710
Elihu
Elihu analibe tsankho, sanatchule aliyense ndi dzina la udindo pongofuna kumusangalatsa. Iye ankazindikira kuti mofanana ndi Yobu nayenso anapangidwa ndi dothi ndipo Wamphamvuyonseyo ndi Mlengi wake. Elihu analibe maganizo oopseza Yobu, koma analankhula naye monga mnzake ndipo ankamutchula dzina, zimene Elifazi, Bilidadi ndi Zofali sanazichite n’komwe.—Yob 32:21, 22; 33:1, 6.
Kodi Mumaona Anthu Ofooka Mmene Yehova Amawaonera?
8 Tikhoza kumvetsa bwino abale athu tikamakumbukira zimene iwo akupirira. Ena mwa iwo akudwala, ena ali pabanja ndi munthu wosakhulupirira ndipo ena akuvutika kwambiri ndi nkhawa. Mwina tsiku lina ifenso tidzakumana ndi mavuto omwewo. Aisiraeli ali ku Iguputo anali osauka ndiponso ofooka. Ndiyeno asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, anakumbutsidwa kuti ‘asamaumire mtima’ abale awo ovutika. Yehova ankafuna kuti iwo asamanyoze anthu osauka koma aziwathandiza.—Deut. 15:7, 11; Lev. 25:35-38.
9 Tiyenera kulimbikitsa anthu amene akukumana ndi mavuto osati kuwaweruza kapena kuwakayikira. (Yobu 33:6, 7; Mat. 7:1) Tiyerekezere kuti munthu wachita ngozi pamsewu n’kufika naye kuchipatala. Kodi madokotala amayamba kufufuza ngati wachititsa ngozi ndi iyeyo? Ayi, koma amayamba mwamsanga kumuthandiza. N’chimodzimodzinso ndi Mkhristu mnzathu amene wafooka chifukwa chokumana ndi mavuto. Tiyenera kuyamba mwamsanga kumulimbikitsa.—Werengani 1 Atesalonika 5:14.
10 Kuganizira kwambiri zimene abale athu akukumana nazo kungatithandize kuona zofooka zawo m’njira yoyenera. Mwachitsanzo, taganizirani za alongo amene akhala akutsutsidwa ndi amuna awo kwa zaka zambiri. Iwo akhoza kuoneka ofooka komabe amasonyeza chikhulupiriro cholimba komanso kupirira. Kodi mumamva bwanji mukamaona mlongo amene akulera yekha ana akubwera ku misonkhano limodzi ndi anawo? Kodi mumamuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro chake ndiponso khama lake? Nanga mumamva bwanji mukaona achinyamata amene akukhala okhulupirika ngakhale kuti amakumana ndi mayesero kusukulu? Kukhala odzichepetsa kungatithandize kuzindikira kuti anthu amene amaoneka ngati ofooka angakhale “olemera m’chikhulupiriro” mofanana ndi anthu amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendera.—Yak. 2:5.
Kodi Mumadziwa Nthawi Yoyenera Kulankhula?
17 Munthu wina amene anapita kukaona Yobu anali Elihu, yemwe anali pachibale ndi Abulahamu. Iye ankamvetsera pamene Yobu ndi anthu atatuwo ankalankhula. N’zosachita kufunsa kuti ankamvetsera bwinobwino zonse zimene zinkanenedwa. Tikutero chifukwa chakuti anapereka malangizo mokoma mtima omwe anathandiza Yobu kuti asinthe maganizo ake olakwika. (Yobu 33:1, 6, 17) Chofunika kwambiri kwa Elihu chinali kulemekeza Yehova osati kudzitama kapena kutamanda anthu ena. (Yobu 32:21, 22; 37:23, 24) Zimene Elihu anachita zikusonyeza kuti pali nthawi yoyenera kukhala chete n’kumangomvetsera. (Yak. 1:19) Tikuphunziranso kuti tikamapereka malangizo kwa munthu, cholinga chathu chizikhala choti ulemerero upite kwa Yehova osati kwa ifeyo.
18 Timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya kulankhula tikamatsatira malangizo a m’Baibulo n’kumadziwa nthawi yoyenera kulankhula ndi kukhala chete. Mfumu Solomo anauziridwa kulemba kuti: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Tikamamvetsera zimene anzathu akulankhula komanso kuganiza kaye tisanalankhule, mawu athu adzakhala ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva. Mawuwo amakhala abwino komanso othandiza kwambiri. Ndipo kaya timalankhula pang’ono kapena kwambiri, mawu athu adzakhala olimbikitsa ndipo Yehova adzasangalala nafe. (Miy. 23:15; Aef. 4:29) Tikatero tidzasonyeza kuti timayamikira kwambiri mphatso imene Mulungu anatipatsa.
Mfundo Zothandiza
Pitirizani Kuyandikira Yehova
10 M’pomveka kuganiziranso za maonekedwe athu. Koma si bwino kumangoganizira zimene tingachite kuti tifufute zizindikiro zonse za ukalamba. Zizindikiro zoterezo zikhoza kusonyeza kuti ndife anzeru, olemekezeka komanso kuti munthu wamkati ndi wokongola. Pajatu Baibulo limati: “Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.” (Miy. 16:31) Umu ndi mmene Yehova amationera ndipo ifenso tizidziona choncho. (Werengani 1 Petulo 3:3, 4.) Chotero kodi ndi bwino kuchititsa maopaleshoni oopsa kapena kuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala oopsa n’cholinga choti tizingooneka okongola? “Chimwemwe chimene Yehova amapereka” n’chimene chimakongoletsa munthu ngakhale wokalamba kapena wodwala chifukwa chakuti chimachokera mumtima. (Neh. 8:10) M’dziko latsopano ndi mmene tidzakhala ndi thanzi langwiro ndiponso kuoneka okongola ngati kamwana. (Yobu 33:25; Yes. 33:24) Podikira nthawi imeneyo, tiyeni tizichita zinthu mwanzeru ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Kuchita zimenezi kungatithandize kuyandikirabe Yehova ndiponso kukhala ndi moyo wabwino ngakhale panopa.—1 Tim. 4:8.
JANUARY 8-14
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 34-35
Moyo Ukamaoneka Kuti Ndi Wokondera
Kodi Mulungu Ali Ndi Makhalidwe Otani?
Nthawi zonse Yehova amachita zinthu zabwino. “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo.” (Yobu 34:10) Nthawi zonse chigamulo chake chimakhala choyenera, ngati mmene wamasalimo ananenera kuti: “Mudzaweruza anthu molungama.” (Salimo 67:4) Popeza “Yehova amaona mmene mtima ulili,” sangapusitsidwe ndi chinyengo. Iye amadziwa zoona ndipo amapereka chigamulo choyenera. (1 Samueli 16:7) Komanso Mulungu amadziwa chinthu chilichonse chopanda chilungamo komanso chachinyengo chomwe chikuchitika padzikoli ndipo analonjeza kuti posachedwapa “oipa adzachotsedwa padziko lapansi.”—Miyambo 2:22.
Kodi Ufumu wa Mulungu Ukadzabwera Udzachotsa Zinthu Ziti?
5 Kodi Yehova adzachita chiyani? Panopa Yehova wapereka mwayi kwa anthu oipa kuti asinthe. (Yes. 55:7) Sikuti iye waweruza kale munthu aliyense woipa kuti adzaphedwa. Koma dzikoli ndi limene waliweruza kuti lidzawonongedwa. Ndiye kodi anthu amene akukana kusintha zidzawathera bwanji pa nthawi ya chisautso chachikulu? Yehova analonjeza kuti adzawononga dziko loipali. (Werengani Salimo 37:10.) Mwina anthu ena oipa amaganiza kuti iwowo sadzawonongedwa. N’kutheka kuti ali ndi maganizo amenewa chifukwa choti akhala akuchita zoipa koma salangidwa chifukwa amabisala. Mwinanso n’chifukwa choti sakumana ndi zotsatira za zochita zawozo. (Yobu 21:7, 9) Koma paja Baibulo limati: “Maso ake [a Yehova] amayang’anitsitsa njira za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse. Kulibe mdima wandiweyani woti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.” (Yobu 34:21, 22) Choncho palibe amene adzabisale moti Yehova n’kulephera kumuona. Komanso popeza maso ake amaona paliponse, palibe chimene munthu angachite moti n’kumupusitsa. Choncho Aramagedo ikadzatha, tidzayang’ana paliponse pamene pankakhala anthu oipa, koma sadzapezekapo chifukwa adzakhala atawonongedwa.—Sal. 37:12-15.
Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?
19 Kodi vuto limeneli liliponso masiku ano? Inde. Anthu ambiri amakana uthenga umene timalalikira chifukwa choti sitilowerera zandale. Iwo amafuna kuti tizivota pa nthawi ya zisankho. Komabe, ife timadziwa kuti ngati titasankha munthu kuti azitilamulira, timakhala kuti tikukana Yehova. (1 Sam. 8:4-7) Anthu enanso amaona kuti timayenera kumanga masukulu, zipatala komanso kuchita ntchito zina zachifundo. Iwo amakana uthenga wathu chifukwa choti timaika maganizo athu onse pa ntchito yolalikira, osati kuthetsa mavuto a m’dzikoli.
20 Kodi tingatani kuti tisakhumudwe n’kusiya kutsatira Yesu? (Werengani Mateyu 7:21-23.) Chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu chiyenera kukhala ntchito imene Yesu anatiuza kuti tizigwira. (Mat. 28:19, 20) Sitiyenera kusokonezedwa ndi nkhani zandale komanso kuyesa kuthetsa mavuto a m’dzikoli. N’zoona kuti timakonda anthu komanso timakhudzidwa ndi mavuto amene amakumana nawo, koma timadziwa kuti njira yabwino kwambiri yowathandizira ndi kuwaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu komanso kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova.
Mfundo Zothandiza
Kudzipereka Kwathu Kumachititsa Kuti Yehova Atamandidwe
3 Elihu ankamvetsera zimene Yobu ankakambirana ndi amuna atatu aja. Kenako iye anafunsa Yobu kuti: “Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani [Mulungu]? Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?” (Yobu 35:7) Kodi pamenepa Elihu ankatanthauza kuti zimene timachita potumikira Mulungu n’zopanda ntchito? Ayi. Tikutero chifukwa Yehova sanamudzudzule ngati mmene anachitira ndi amuna atatu aja. Elihu ankatanthauza kuti Yehova ali ndi chilichonse ndipo samadalira zimene timachita pomulambira. Ifeyo sitingamuthandize kuti akhale wolemera kapena wamphamvu kuposa mmene alili. Iye ndi amene amatipatsa luso, mphamvu komanso zinthu zilizonse zabwino zimene tili nazo ndipo amaona mmene timazigwiritsira ntchito.
JANUARY 15-21
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 36-37
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhulupirira Lonjezo la Mulungu Loti Adzatipatsa Moyo Wosatha?
Kodi Mulungu Ndi Wosamvetsetseka?
MULUNGU ALIBE CHIYAMBI KOMANSO MAPETO: Baibulo limanena kuti Mulungu wakhala alipo “kuyambira kalekale” ndipo adzakhalapo “mpaka kalekale.” (Salimo 90:2) Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto. Anthufe sitingathe kumvetsa zimenezi chifukwa “zaka zake n’zosawerengeka.”—Yobu 36:26.
Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Mulungu amatilonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha ngati titamudziwa n’kumachita zimene amafuna. (Yohane 17:3) Kodi zikanakhala zomveka kuti Mulungu alonjeze anthu moyo wosatha zikanakhala kuti Mulunguyo sadzakhalapo mpaka kalekale? Ndi “Mfumu yamuyaya” yokha yomwe ingalonjeze zimenezi.—1 Timoteyo 1:17.
Kodi Timayamikira Zinthu Zimene Mulungu Anatipatsa?
6 Dzikoli linatalikirana ndi dzuwa pamtunda wabwino moti madzi satentha kwambiri n’kukhala nthunzi kapena kuzizira kwambiri mpaka kuundana. Koma ngati likanayandikira pang’ono, madzi onse akanauma ndipo padzikoli pakanakhala potentha kwambiri komanso popanda zamoyo. Ndipo ngati likanatalikiranso pang’ono, madzi onse akanaundana ndipo dziko lonseli likanakhala ayezi yekhayekha. Choncho Yehova anaika dziko ndi dzuwa pamtunda wabwino zimene zimachititsa kuti padzikoli pakhale madzi omwe amathandiza zamoyo. Dzuwa likawala, madzi apadzikoli amakwera m’mwamba ngati nthunzi ndipo imakakhala mitambo. Chaka chilichonse, madzi amene amakwera m’mwambawa akhoza kudzaza madamu 500,000. Damu lililonse kukula kwake kilomita imodzi m’litali, m’lifupi komanso kuya kwake. Madziwa amakhala m’mlengalenga kwa masiku pafupifupi 10 asanagwe ngati mvula kapena sinowo. Zikatero madziwo amabwereranso m’nyanja kapena m’mitsinje ndipo zimenezi zimachitika mobwerezabwereza. Izi zimasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wanzeru komanso wamphamvu.—Yobu 36:27, 28; Mlal. 1:7.
Pitirizani Kulimbitsa Chiyembekezo Chanu
16 Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo ndipo sitimakayikira kuti zidzachitika. Chiyembekezo chili ngati nangula wathu ndipo chimatithandiza kukhala odekha kuti tizipirira mayesero, kuzunzidwa komanso sitiopa kufa. Chilinso ngati chisoti ndipo chimateteza maganizo athu kuti tizipewa kuchita zoipa n’kumayesetsa kuchita zabwino. Chiyembekezo chathu cha m’Baibulo chimatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo chimasonyeza kuti iye amatikonda kwambiri. Zinthu zimatiyendera bwino kwambiri tikapitiriza kukhala ndi chiyembekezo cholimba.
Mfundo Zothandiza
it-1 492
Kulankhulana
M’mayiko akale omwe anatchulidwa m’Baibulo, anthu ankagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana potumizirana mauthenga. Nthawi zambiri anthu ankangouzana pakamwa nkhani zochitika m’mayiko awo kapena m’mayiko ena. (2Sa 3:17, 19; Yob 37:20) Anthu a pa ulendo omwe nthawi zambiri ankayenda pa ngamila kapena nyama zina, akaima kuti adye, amwe madzi kapena kuchita zinthu zina m’mizinda kapena malo ena amene ankadutsa, ankafotokoza nkhani za kumene akuchokera. M’dziko la Palesitina munkadutsa anthu ambiri amene ankapita kapena kuchokera ku mayiko akutali monga ku Asia, Africa, ndi ku Europe. Choncho anthu am’dzikoli sankavutika kumva nkhani zikuluzikulu zochitika m’mayiko ena. Nthawi zambiri pamsika ndi pamene anthu ankakambirana nkhani zochitika m’dziko lawo kapena m’mayiko ena.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwfq 57 ¶5-15
Kodi a Mboni za Yehova Zinawathera Bwanji pa Nthawi Imene Anthu Ambirimbiri Anaphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi ku Germany?
A Mboni za Yehova ankazunzidwa chifukwa choti ankatsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. Akuluakulu a chipani cha Nazi akawauza kuti asiye kutsatira zimene Baibulo limanena, a Mboniwo ankakana. Iwo ankasankha “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Machitidwe 5:29) Taonani mfundo ziwiri zomwe zinkachititsa a Mboniwa kukana zomwe ankauzidwa ndi akuluakulu a boma.
1. Kusalowerera ndale. Masiku ano a Mboni za Yehova m’mayiko onse salowerera nawo ndale. Zimenezi ndi zomwenso a Mboni m’nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ankachita. (Yohane 18:36) Iwo ankakana kuchita zinthu zotsatirazi.
● Kulowa usilikali kapena kuchita chilichonse pothandiza nawo pa nkhondo.—Yesaya 2:4; Mateyu 26:52.
● Kuvota kapena kulowa nawo m’mabungwe a chipani cha Nazi.—Yohane 17:16.
● Kuchitira sailuti mbendera kapena kunena kuti, “Hitler Ndiye Mpulumutsi Wathu.”—Mateyu 23:10; 1 Akorinto 10:14.
2. Kutsatira zomwe amakhulupirira. Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ankaletsedwa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira, iwo ankapitirizabe kuchita zotsatirazi.
● Kusonkhana komanso kuchita zinthu zokhudza kulambira.—Aheberi 10:24, 25.
● Kulalikira komanso kugawira mabuku othandiza pophunzira Baibulo.—Mateyu 28:19, 2
● Kuchita zinthu mokoma mtima kwa anzawo kuphatikizaponso anthu achiyuda.—Maliko 12:31.
● Kusonyezabe chikhulupiriro chawo pokana kusainira makalata osonyeza kuti asiya chipembedzo chawo.—Maliko 12:30.
Pulofesa Robert Gerwarth ananena kuti a Mboni za Yehova ndi “gulu lokhalo lomwe linkazunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira kuchipembedzo chawo, mu ulamuliro wachitatu ku Germany.” Akaidi ena ankachita chidwi kwambiri ndi a Mboni za Yehova chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholimba. Mkaidi wina wa ku Austria ananena kuti: “A Mboni sapita nawo kunkhondo. Amalolera kuphedwa m’malo moti iwowo aphe munthu.”
JANUARY 22-28
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 38-39
Kodi Mumapeza Nthawi Yoona Chilengedwe?
Kodi Mudzayembekezera Yehova Moleza Mtima?
7 Pofotokoza mmene Yehova analengera dziko lapansili, Baibulo limanena kuti iye “anaika miyezo yake,” anazika “maziko ake” komanso anaika “mwala wake wapakona.” (Yobu 38:5, 6) Iye ankapeza nthawi yoonanso mmene zinthu zimene analenga zinkaonekera. (Gen. 1:10, 12) Tangoganizani mmene angelo ankamvera akaona chinthu chatsopano chilichonse chimene Yehova walenga. Iwo ayenera kuti ankasangalala kwambiri. Tikutero chifukwa pa nthawi ina, “anayamba kufuula ndi chisangalalo.” (Yobu 38:7) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Panatenga zaka zambiri kuti Yehova amalize ntchito yake yolenga zinthu, koma ataona zinthu zonse zimene analenga, iye ananena kuti “zinali zabwino kwambiri.”—Gen. 1:31.
Kuukitsidwa Kwa Akufa Kumasonyeza Kuti Yehova Ndi Mulungu Wachikondi, Wanzeru Komanso Woleza Mtima
2 Choyamba, Yehova analenga Mwana wake, Yesu. Ndiyeno limodzi ndi Mwana wakeyo, analenga “zinthu zina zonse” kuphatikizapo angelo. (Akol. 1:16) Yesu ankasangalala kugwira ntchito ndi Atate wake. (Miy. 8:30) Angelo nawonso anasangalala. Iwo analipo ndipo anaona pamene Yehova ndi mmisiri wake Yesu, ankalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi angelowo anasonyeza bwanji kuti anasangalala? Iwo “anayamba kufuula ndi chisangalalo” pamene dziko lapansi linalengedwa ndipo n’zosakayikitsa kuti anapitirizabe kusangalala ndi zinthu zonse zimene Yehova analenga, kuphatikizapo anthu. (Yobu 38:7; Miy. 8:31) Zimene Yehova analengazi zimasonyeza kuti iye ndi wachikondi komanso wanzeru.—Sal. 104:24; Aroma 1:20.
Muziphunzira Zambiri Zokhudza Yehova Poona Chilengedwe Chake
8 Yehova ndi woyenera kuti tizimudalira. Iye anathandiza Yobu kuti azimukhulupirira kwambiri. (Yobu 32:2; 40:6-8) Pamene ankakambirana ndi Yobu, Mulungu anatchula zinthu zambiri zimene zili m’chilengedwe chake monga nyenyezi, mitambo komanso mphezi. Anatchulanso za nyama monga ng’ombe yamphongo yam’tchire komanso hatchi. (Yobu 38:32-35; 39:9, 19, 20) Zinthu zonsezi zinapereka umboni wosonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zodabwitsa, wachikondi komanso ndi wanzeru kwambiri. Chifukwa chokambirana zinthu zimenezi ndi Yehova, Yobu anayamba kumukhulupirira kwambiri kuposa kale. (Yobu 42:1-6) Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira zinthu zam’chilengedwe timakumbutsidwa kuti Yehova ndi wanzeru kwambiri komanso ali ndi mphamvu kuposa ifeyo. Iye angathenso kuthetsa mayesero amene timakumana nawo ndipo ndi zimene adzachite. Mfundo imeneyi ingatithandize kuti tizimukhulupirira kwambiri.
Mfundo Zothandiza
it-2 222
Wopereka Malamulo
Yehova monga Wopereka Malamulo. Yehova yekha ndi amene ali woyenera kupereka malamulo m’chilengedwe chonse. Ena mwa malamulo amene Yehova anakhazikitsa ndi malamulo a m’chilengedwe amene amalamulira zinthu zopanda moyo (Yob 38:4-38; Sl 104:5-19) komanso zinthu zamoyo. (Yob 39:1-30) Anthu, omwe nawonso ndi zolengedwa za Yehova, amatsatira malamulo a m’chilengedwe. Iwo amatsatiranso malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino chifukwa choti analengedwa kuti azikhala ndi nzeru komanso makhalidwewa ndipo amatha kuganiza komanso kukhala anthu auzimu. (Aro 12:1; 1Ak 2:14-16) Kuwonjezera pamenepo, malamulo a Yehova amalamuliranso zolengedwa zauzimu zomwe ndi angelo.—Sl 103:20; 2Pe 2:4, 11.
Malamulo a Yehova a m’chilengedwe sangaphwanyike. (Yer 33:20, 21) Malinga ndi zimene anthu akudziwa zokhudza chilengedwechi, malamulowa ndi okhazikika komanso odalirika kwambiri moti asayansi akhoza kuwerengetsera molondola mmene mwezi, mapulaneti ndi zinthu zina zakuthambo zikuyendera. Cholengedwa chilichonse chimene chimachita zosemphana ndi malamulo a m’chilengedwe nthawi yomweyo chimakumana ndi zotsatirapo zake. Mofananamo, malamulo a Yehova a makhalidwe abwino sangasinthidwe kapena kuphwanyidwa ndipo aliyense amene angayese kuchita zimenezi amakumana ndithu ndi zotsatirapo zake. Malamulo amenewa ndi ofanana ndi malamulo ake a m’chilengedwe koma amangosiyana kuti malamulo a makhalidwe abwinowa chilango chake sichimakhala cha nthawi yomweyo. “Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Aga 6:7; 1Ti 5:24.
JANUARY 29–FEBRUARY 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 40-42
Zimene Tikuphunzira Kuchokera pa Zimene Zinachitikira Yobu
“Ndani Akudziwa Maganizo a Yehova?”
4 Tikamasinkhasinkha zochita za Yehova tiyenera kupewa chizolowezi chomuweruza poyerekezera ndi mfundo zimene anthu amayendera. Chizolowezi chimenechi chatchulidwa m’mawu a Yehova opezeka pa Masalimo 50:21. Lembali limati: “Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.” Izi n’zofanana ndi zimene katswiri wina wa Baibulo ananena zaka 175 zapitazo. Iye anati: “Anthu amakonda kuweruza Mulungu malinga ndi mmene iwo amaonera zinthu ndipo amaganiza kuti iye ndi womangika ndi malamulo amene anthuwo amaona kuti ndi oyenera kuwatsatira.”
5 Tiyenera kusamala kwambiri kuti tisamaganize zoti Yehova ayenera kumachita zinthu mogwirizana ndi mfundo kapena zofuna zathu. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Tikamaphunzira nkhani zina za m’Baibulo, tingamaganize kuti Yehova sanachite bwino pa nkhaniyo. Tingakhale ndi maganizo amenewa chifukwa chakuti sitidziwa zambiri ndiponso ndife opanda ungwiro. Aisiraeli anali ndi maganizo olakwikawa ndipo ankaona kuti Yehova sakuyendetsa bwino zinthu pakati pawo. Taonani zimene Yehova anawauza: “Anthu inu mudzanena kuti: ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.’ Tamverani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njira zanga ndiye zopanda chilungamo? Kodi njira za anthu inu sindizo zopanda chilungamo?”—Ezek. 18:25.
6 Chinthu chofunika kwambiri kuti tisakhale ndi maganizo oweruza Yehova malinga ndi mfundo zimene timayendera, ndi kuzindikira kuti ife sitidziwa zambiri ndipo nthawi zina timakhala ndi maganizo olakwika kwambiri. Izi n’zimene Yobu anafunika kudziwa. Pa nthawi imene ankavutika, Yobu anathedwa nzeru n’kuyamba kumangodziganizira yekha. Iye sankaonanso zinthu zikuluzikulu zofunika, koma Yehova anamuthandiza kuti aziona zinthu moyenera. Iye anamufunsa mafunso oposa 70 amene sanathe kuwayankha. Pochita zimenezi, Yehova anathandiza Yobu kuzindikira kuti sankadziwa zinthu zambiri. Zitatero Yobu anadzichepetsa n’kusintha mmene ankaonera zinthu.—Werengani Yobu 42:1-6.
Musamaiwale Nkhani Yofunika Kwambiri
12 Popeza Yobu anali atavutika kwambiri, kodi zimene Yehova ananenazo zinali zankhanza komanso zopanda chifundo? Ayi, ndipo nayenso Yobu sanaganize choncho. Ngakhale kuti anali atakumana ndi mavutowo, Yobu anayamikira zimene Yehova anamuuza. Iye anafika ponena kuti: “Ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” Izi zikusonyeza kuti malangizo olimbikitsa koma osapita m’mbali a Mulungu anamuthandiza. (Yobu 42:1-6) Yobu anali atalandiranso malangizo ochokera kwa Elihu yemwe anali wamng’ono kwa iye. (Yobu 32:5-10) Yobu atalandira malangizo a Mulungu n’kusintha maganizo ake, Mulunguyo analankhula kwa anthu ena mawu osonyeza kuti akusangalala ndi Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake.—Yobu 42:7, 8.
“Yembekezera Yehova”
17 Yobu ndi mmodzi chabe wa atumiki a Yehova omwe anakhalabe olimba pokumana ndi mayesero. M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anafotokozamo za enanso ambiri omwe anawatchula kuti “mtambo wa mboni waukulu.” (Aheb. 12:1) Onsewa anakumana ndi mayesero akuluakulu, koma anakhalabe okhulupirika kwa Yehova. (Aheb. 11:36-40) Ndiye kodi kupirira komanso khama lawo zinapita pachabe? Ayi ndithu. Ngakhale kuti munthawi yawo sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova, anapitirizabe kumuyembekezera. Ndipo popeza ankakhulupirira kuti Yehova akusangalala nawo, sankakayikira kuti adzaona malonjezowo akukwaniritsidwa. (Aheb. 11:4, 5) Chitsanzo chawo chingatithandize kukhala otsimikiza kwambiri kuti tiziyembekezera Yehova.
18 Panopa tikukhala m’dziko limene likuipiraipirabe. (2 Tim. 3:13) Satana sanasiye kuyesa anthu a Mulungu. Kaya tikumana ndi mavuto otani m’tsogolomu, tiyeni titsimikize mtima kuti tizichita khama potumikira Yehova, n’kumakhulupirira kuti “chiyembekezo chathu chili mwa Mulungu wamoyo.” (1 Tim. 4:10) Tizikumbukira kuti zimene Mulungu anachitira Yobu pambuyo pake zimasonyeza “kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Ifenso tiyeni tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova ndipo tisamakayikire kuti adzapereka mphoto kwa “anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”—Werengani Aheberi 11:6.
Mfundo Zothandiza
it-2 808
Kunyoza
Yobu anali munthu wolungama ndipo anakhalabe wokhulupirika ngakhale pamene ankanyozedwa kwambiri. Koma anayamba kukhala ndi maganizo osayenera ndipo analakwitsa zinthu, zomwe zinachititsa kuti adzudzulidwe. Elihu ananena za Yobu kuti: “Kodi pali munthu wina wofanana ndi Yobu, amene amamwa mawu onyoza ngati madzi?” (Yob 34:7) Yobu ankadziikira kumbuyo kwambiri ndipo pamenepa anasonyeza kuti ndi wolungama kuposa Mulungu. (Yob 35:2; 36:24) Pamene ankanyozedwa ndi “anzake” atatu aja Yobu ankaona kuti akunyoza iyeyo osati Mulungu. Pamenepa Yobu anali ngati munthu amene akunyozedwa ndipo akusangalala ndi kunyozedwako ngati mmene munthu amasangalalira akamamwa madzi. Kenako Mulungu anafotokozera Yobu kuti anthu onyozawo ankanena zabodza zokhudza Mulungu. (Yob 42:7) Yehova anauza mneneri Samueli zofanana ndi zimenezi pamene Aisiraeli ankafuna mfumu. Iye ananena kuti: “Sanakane iwe koma akana ine kuti ndikhale mfumu yawo.” (1Sa 8:7) Ndipo Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mt 24:9) Kukumbukira mfundo zimenezi kungathandize Mkhristu kukhala ndi maganizo oyenera pamene akupirira ndipo zimenezi zingachititse kuti adzalandire madalitso.—Lu 6:22, 23.
FEBRUARY 5-11
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 1-4
Khalani ku Mbali ya Ufumu wa Mulungu
“Ndidzagwedeza Mitundu Yonse ya Anthu”
8 Kodi anthu amatani akamva uthenga wa Ufumu? Ambiri amakana kumvetsera. (Werengani Salimo 2:1-3.) Mitundu ya anthu imakwiya ikamva uthengawu. Iwo amakana Wolamulira amene Yehova wamusankha. Saona uthenga wabwino wa Ufumu umene timalalikirawu ngati “uthenga wabwino.” Ndipotu maboma ena afika poletsa ntchito yathu yolalikira. Ngakhale kuti ambiri mwa olamulira adzikoli amanena kuti amatumikira Mulungu, safuna kutula pansi udindo wawo. Mofanana ndi zimene anachita olamulira mu nthawi ya Yesu, olamulira masiku ano amatsutsa Wodzozedwa wa Yehova polimbana ndi otsatira ake okhulupirika.—Mac. 4:25-28.
Musakhale Mbali ya Dzikoli
11 Kukonda chuma. Ngati timakonda kwambiri chuma tikhoza kugonja titayesedwa pa nkhani zokhudza ndale. Mlongo wina ku Malawi, dzina lake Ruth, anaona abale ndi alongo ena akugonja m’ma 1970. Iye anati: “Anthuwa sankafuna kusiya moyo wawofuwofu. Ena anapita nafe kumsasa koma kenako anavomera kukhala mamembala achipani n’kubwerera kwawo. Ankaona kuti sangathe kukhala moyo wovutika wakumsasako.” Koma atumiki a Mulungu ambiri anakhalabe okhulupirika ndipo analolera kusiya zinthu zawo zonse n’kukhala pa mavuto azachuma.—Aheb. 10:34.
Mfundo Zothandiza
it-1 425
Mankhusu
Mankhusu ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati balere kapena tirigu popuntha. Nthawi zambiri Baibulo limatchula mankhusu mophiphiritsira ndipo likamatchula zimenezi limakhala likunena zimene anthu kale ankakonda kuchita akamapuntha mbewu. Pambuyo pokolola, makoko osadyedwawa ankakhala opanda ntchito, ndipo ankaimira zinthu zopanda pake, zosafunika komanso zoyenera kuti zichotsedwe pa zinthu zabwino n’kuzitaya.
Choyamba, ankapuntha mbewu ndipo mankhusu ankachoka ku mbewuzo. Kenako ankazipeta ndipo mankhusu ankauluzika ndi mphepo ngati fumbi. Zimenezi zikufotokoza bwino mmene Yehova amachotsera anthu ampatuko pakati pa anthu ake komanso mmene amawonongera anthu oipa ndi mitundu yotsutsa. (Yob 21:18; Sl 1:4; 35:5; Yes 17:13; 29:5; 41:15; Ho 13:3) Ufumu wa Mulungu udzaphwanya adani ake ndipo adzauluzika mosavuta ngati mankhusu.—Da 2:35.
Nthawi zambiri mankhusu ankawaunjika pamodzi n’kuwawotcha kuti asauluzike n’kubwereranso kumene kuli mbewu. Mofananamo, Yohane M’batizi ananeneratu za kuwonongedwa kwa anthu onse omwe ali m’chipembedzo chabodza pomwe Yesu Khristu adzatutira tirigu pamodzi “koma mankhusu adzawawotcha ndi moto umene sungazimitsidwe.”—Mt 3:7-12; Lu 3:17.
FEBRUARY 12-18
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 5-7
Muzikhalabe Okhulupirika Posatengera Zimene Ena Achita
Malemba Angatithandize Kuti Tizipirira
7 Kodi mnzanu kapena wachibale wanu anakukhumudwitsani chifukwa cholephera kukhala wokhulupirika kwa inu? Ngati ndi choncho mungapindule mukamawerenga nkhani ya Mfumu Davide ndi mwana wake Abisalomu, yemwe anakhala wosakhulupirika kwa bambo ake ndipo ankafuna kulanda ufumu wawo.—2 Sam. 15:5-14, 31; 18:6-14.
8 (1) Kupemphera. Muzimuuza Yehova mmene mukumvera chifukwa cha zoipa zimene ena akuchitirani. (Sal. 6:6-9) Muzitchula zinthu zenizeni zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipo kenako muzimupempha kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene zingakutsogolereni polimbana ndi vuto limene mwakumana nalo.
Musamakayikire Kuti Zimene Mumakhulupirira Ndi Zoona
3 Chikhulupiriro chathu sichiyenera kungodalira chikondi chomwe timaona pakati pa anthu a Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Tayerekezerani kuti wokhulupirira mnzanu, mkulu kapena mpainiya wachita tchimo lalikulu. Mwinanso m’bale kapena mlongo wina wakukhumudwitsani. Kapenanso wina wayamba mpatuko ndipo akunena kuti zimene timakhulupirira si zoona. Ngati zimenezi zitachitika, kodi mungakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? Pamenepa mfundo ndi yakuti: Ngati mumakhulupirira Yehova chifukwa cha zochita za anthu ena osati chifukwa choti muli naye pa ubwenzi wolimba, chikhulupiriro chanu sichingakhale cholimba. N’zoona kuti mmene mumaonera Yehova komanso anthu ake zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Koma n’zofunikanso kwambiri kumaphunzira Baibulo mwakhama, kumvetsa zimene mukuphunzirazo komanso kufufuza mfundo zina. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzitsimikizira kuti zomwe mukuphunzira zokhudza Yehova ndi zoona.—Aroma 12:2.
4 Yesu ananena kuti anthu ena amalandira choonadi “mwachimwemwe” koma akakumana ndi mavuto, chikhulupiriro chawo chimafooka. (Werengani Mateyu 13:3-6, 20, 21.) N’kutheka kuti anthuwa sadziwa kuti anthu amene amatsatira Yesu amakumana ndi mavuto. (Mat. 16:24) Mwinanso amaganiza kuti chifukwa choti ndi Akhristu ndiye kuti Mulungu aziwathetsera mavuto awo. Koma m’dzikoli n’zosatheka kumakhala osakumana ndi mavuto chifukwa zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu n’kuchititsa kuti tisamasangalale.—Sal. 6:6; Mlal. 9:11.
Mfundo Zothandiza
it-1 995
Manda
Pa Aroma 3:13 mtumwi Paulo anagwira mawu a pa Salimo 5:9, poyerekezera mmero wa anthu oipa komanso anthu achinyengo ndi “manda otseguka.” M’manda otseguka mumaikidwa anthu akufa komanso achinyengo, nawonso mmero wa anthu oipa umalankhula zakupha komanso zachinyengo.—Yerekezerani ndi Mt 15:18-20.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwfq 64
N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amakana Mwaulemu Kuchita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lawo?
A Mboni za Yehova amalemekeza maboma komanso zizindikiro zoimira dziko lawo. Timalemekeza zimene anthu ena amachita posonyeza kuti amakonda dziko lawo monga kulumbira, kuchitira sawatcha kapena kugwadira mbendera kapenanso kuimba nyimbo ya fuko lawo.
Komabe, a Mbonife timasankha kusachita nawo miyambo imeneyi chifukwa timakhulupirira kuti ndi yosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Choncho, nafenso timayamikira anthu ena akamalemekeza zomwe timasankha kukhulupirira.
Zimene zili munkhaniyi
Kodi timatsatira mfundo za m’Baibulo ziti?
Tingatani ngati boma linakhazikitsa lamulo loti tizichita nawo miyamboyi?
Kodi a Mboni za Yehova amakhala mbali ya mabungwe kapena magulu enaake a ndale?
Kodi timatsatira mfundo za m’Baibulo ziti?
Timatsatira mfundo za m’Baibulo ziwiri izi:
● Mulungu yekha ndiye woyenera kumulambira. Baibulo limanena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Luka 4:8) Nthawi zambiri malumbiro kapenanso nyimbo za fuko zimakhala ndi mawu osonyeza kuti munthu walonjeza kuti azikonda kwambiri dziko lake kuposa china chilichonse. Choncho, a Mboni za Yehova amaona kuti n’kulakwa kuchita nawo miyambo yotereyi.
A Mboni za Yehova amaonanso kuti kuchitira sawatcha mbendera kuli ngati kulambira mafano, ndipo Baibulo limaletsa kuchita zimenezi. (1 Akorinto 10:14) Olemba mbiri ena akuvomereza kuti mbendera za mayiko zimangofanana ndi zizindikiro za zipembedzo. Mwachitsanzo, a Carlton J. H. Hayes analemba kuti: “Kukonda dziko lanu kuli ngati chipembedzo ndipo chizindikiro chachikulu chomwe anthu amalambira m’chipembedzochi ndi mbendera.” Ponena za Akhristu oyambirira, wolemba mbiri wina dzina lake Daniel P. Mannix, ananena kuti: “Akhristu ankakana . . . kupereka nsembe ku mizimu ya olamulira [a ku Roma]. Masiku ano zimenezi zingafanane ndi kukana kuchitira sawatcha mbendera.”
Ngakhale kuti a Mboni za Yehova sachitira sawatcha mbendera, iwo sawononga, kuwotcha kapena kuchita china chilichonse chosonyeza kusalemekeza mbendera kapena zizindikiro zina zam’dziko lawo.
● Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana. (Machitidwe 10:34, 35) Baibulo limanena kuti “kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) Pa chifukwa chimenechi, a Mboni za Yehova amaona kuti ndi kulakwa kuona kuti gulu linalake la anthu kapena mtundu winawake ndi wapamwamba kuposa ena. Iwo amalemekeza anthu amitundu yonse posatengera kuti anachokera kuti.—1 Petulo 2:17.
Tingatani ngati boma linakhazikitsa lamulo loti tizichita nawo miyamboyi?
A Mboni za Yehova si otsutsa boma. Timakhulupirira kuti maboma omwe alipowa ndi “dongosolo la Mulungu” lomwe walilola kuti likhalepo. (Aroma 13:1-7) Timakhulupiriranso kuti Akhristu ayenera kumvera olamulira.—Luka 20:25.
Kodi a Mboni za Yehova amatani ngati olamulira akuwauza kuti achite zinthu zimene Mulungu amawaletsa? Nthawi zina zimatheka kupempha boma kuti lisinthe malamulo enaake. Ngati boma lakana kusintha, a Mboni za Yehova amachita zinthu mwaulemu posankha “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:29.
Kodi a Mboni za Yehova amakhala mbali ya mabungwe kapena magulu enaake a ndale?
Ayi. A Mboni za Yehova salowerera nkhani za mabungwe omenyera ufulu kapena nkhani za ndale. Timakana kuchita nawo miyambo monga kulumbira, kuchitira sawatcha mbendera komanso kuimba nyimbo ya fuko chifukwa timatsatira mfundo za m’Baibulo zomwe timakhulupirira osati chifukwa ndife omenyera ufulu wa anthu.
FEBRUARY 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 8-10
“Ndidzakutamandani Inu Yehova”
Muziyamikira Mwayi Wanu Wokhala M’banja la Yehova
6 Yehova anatipatsa malo abwino kwambiri oti tizikhalamo. Zaka zambiri asanalenge munthu woyambirira, iye anali atalenga dziko lapansili kuti anthu adzakhalemo. (Yobu 38:4-6; Yer. 10:12) Popeza kuti ndi wokoma mtima komanso wopatsa, Yehova anaikamo zinthu zambiri zabwino kuti anthu adzasangalale nazo. (Sal. 104:14, 15, 24) Nthawi zina, iye ankaganizira zinthu zimene analenga, ndipo ankaona kuti “zili bwino.” (Gen. 1:10, 12, 31) Yehova anasonyeza kuti amaona anthu kukhala ofunika ‘powapatsa mphamvu’ yoti alamulire zinthu zochititsa chidwi zimene analenga padzikoli. (Sal. 8:6) Cholinga cha Mulungu n’choti anthu angwiro azidzasangalala kusamalira zinthu zokongola zimene iye analengazi mpaka kalekale. Kodi mumamuthokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha zinthu zabwino zimene analonjezazi?
Kodi Timayamikira Zinthu Zimene Mulungu Anatipatsa?
10 Kukambirana ndi anthu amene amadabwa kuti n’chifukwa chiyani sitikhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha, ndi njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira mphatso ya kulankhula. (Sal. 9:1; 1 Pet. 3:15) Anthuwa amanena kuti dzikoli komanso zamoyo zinangokhalako zokha. Ngati tingagwiritse ntchito Baibulo komanso mfundo zomwe zafotokozedwa mu nkhaniyi, tikhoza kuthandiza anthu kudziwa za Atate wathu wakumwamba. Tingathandizenso anthu a maganizo abwino kuti adziwe chifukwa chake timakhulupirira kuti Yehova ndi amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.—Sal. 102:25; Yes. 40:25, 26.
Kodi Ndinu “Chitsanzo . . . M’kalankhulidwe”?
13 Muziimba ndi mtima wonse. Tikamaimba nyimbo za Ufumu, cholinga chathu chachikulu chizikhala kutamanda Yehova. Mlongo wina dzina lake Sara amaona kuti saimba bwino kwenikweni. Komabe amafuna kutamanda Yehova poimba nyimbo. Choncho amaona kuti n’zothandiza kukonzekera nyimbo ngati mmene amachitira ndi mbali zina zapamisonkhano. Iye amayeserera nyimbozo n’kuona mmene mawu ake akugwirizanira ndi zimene akaphunzire pamisonkhano. Anati: “Zimenezi zimandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri mawu a munyimboyo, osati luso langa loimba.”.
Mfundo Zothandiza
it-1 832
Chala
Baibulo limanena mophiphiritsira kuti Mulungu anachita zinthu pogwiritsa ntchito “chala” chake kapena “zala” zake. Mwachitsanzo, pamene analemba Malamulo Khumi pa miyala yosema (Eks 31:18; De 9:10), pamene anachita zozizwitsa (Eks 8:18, 19) komanso pamene analenga kumwamba (Sl 8:3). “Zala” zomwe anazigwiritsa ntchito polenga zinthu zikuimira mzimu wake woyera kapena kuti mphamvu yake. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino munkhani ya m’buku la Genesis yomwe imati mphamvu ya Mulungu inkayendayenda pamwamba pa madzi. (Ge 1:2) Komabe Malemba a Chigiriki amatithandiza kumvetsa mosavuta mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, buku la Mateyu limati Yesu ankatulutsa ziwanda pogwiritsa ntchito ‘mzimu woyera wa Mulungu’ pomwe Luka anafotokoza kuti ankagwiritsa ntchito “chala cha Mulungu.”—Mt 12:28; Lu 11:20.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
15 Kodi mumakumbukira nthawi imene munkachita mantha kuti mukhale wa Mboni za Yehova? Mwina munkaona kuti simungakwanitse kumagwira ntchito yolalikira. Mwinanso munkaopa kuti achibale komanso anzanu azikutsutsani. Ngati ndi choncho, ndiye kuti mungamvetse mmene wophunzira wanu angamvere. Yesu anavomereza kuti n’zotheka kuti munthu aziopa zimenezi. Komabe iye analimbikitsa otsatira ake kuti asamalole kuti mantha awalepheretse kutumikira Yehova. (Mat. 10:16, 17, 27, 28) Ndiye kodi Yesu anawathandiza bwanji, nanga tingatani kuti timutsanzire?
16 Nthawi zonse muziphunzitsa wophunzira wanu mmene angafotokozere kwa ena zimene amakhulupirira. Ophunzira a Yesu ayenera kuti ankachita mantha iye atawatumiza kuti akalalikire. Koma Yesu anawathandiza powauza uthenga komanso malo oti akalalikire. (Mat. 10:5-7) Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji Yesu? Tizithandiza wophunzira wathu kudziwa anthu amene angawalalikire. Mwachitsanzo, mungamufunse ngati akudziwa munthu wina amene mfundo inayake ya m’Baibulo ingamuthandize. Kenako mungamuthandize kukonzekera komanso kumusonyeza mmene angafotokozere zimenezo mosavuta. Mungamuthandize pogwiritsa ntchito tizigawo takuti “Zimene Ena Amanena,” komanso “Munthu Wina Angafunse Kuti,” tomwe tili m’buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale. Mukamachita zimenezi, muzimuphunzitsa mmene angagwiritsire ntchito Baibulo popereka mayankho mwaluso komanso mosavuta.
17 Muzithandiza wophunzira Baibulo wanu kuti azidalira Yehova. Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti Yehova adzawathandiza chifukwa amawakonda. (Werengani Mateyu 10:19, 20, 29-31.) Muzikumbutsa wophunzira wanu kuti nayenso Yehova azimuthandiza. Mungamuthandize kuti azidalira Yehova mukamatchula zolinga zake pamene mukupemphera naye. Franciszek, yemwe amakhala ku Poland ananena kuti: “Mphunzitsi wanga ankatchula zolinga zanga akamapemphera nane. Nditaona mmene Yehova ankayankhira mapemphero a mphunzitsi wangayo, mwamsanga inenso ndinayamba kumapemphera. Ndinaona kuti Yehova anandithandiza pamene ndinkapempha nthawi kuntchito imene ndinali nditangoyamba kumene, kuti ndikachite nawo msonkhano wachigawo komanso ndizipezeka pamisonkhano ya mpingo.”
18 Yehova amakonda kwambiri anthu amene timaphunzira nawo Baibulo. Amakondanso kwambiri Akhristu amene amachita khama kuphunzitsa ena kuti akhale naye pa ubwenzi ndipo amawayamikira chifukwa cha zimenezi. (Yes. 52:7) Ngati panopa simukuchititsa phunziro la Baibulo, mungathandizebe ophunzira Baibulo kupita patsogolo mpaka kufika pobatizidwa popita ndi ofalitsa ena kumaphunziro awo.
FEBRUARY 26–MARCH 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | SALIMO 11-15
Muziyerekezera Muli M’dziko Latsopano Lamtendere
Mfundo Zazikulu za Chigawo Choyamba cha Masalmo
11:3—Kodi ndi maziko otani amene akupasuka? Amenewa ndi maziko amene amanga anthu pamodzi—malamulo, bata, ndi chilungamo. Zimenezi zikasokonekera, pamakhala chisokonezo pakati pa anthu ndipo sipakhala chilungamo. Zikatero, munthu aliyense “wolungama” ayenera kudalira Mulungu ndi mtima wonse.—Salmo 11:4-7.
Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli?
Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu athetsa zachiwawa zonse padzikoli. Ndipo limatitsimikizira kuti anthu onse okonda zachiwawa adzaphedwa “m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:5-7) Pa nthawiyi sikudzakhalanso anthu ozunza ena. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu ndi wofunitsitsa kuthetseratu zachiwawa?
Baibulo limanena kuti “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Mlengi wathu amakonda mtendere ndi chilungamo. (Salimo 33:5; 37:28) N’chifukwa chake sadzalola kuti anthu ochita zachiwawa akhalepo mpaka kalekale.
Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?
15 Kodi n’chifukwa chiyani Davide anayembekezera moleza mtima? Yankho la funsoli tingalipeze pa zimene iye ananena mu Salimo lomwe lija limene anafunsa maulendo 5 kuti: “Kufikira liti?” Davide ananena kuti: “Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha. Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu. Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.” (Sal. 13:5, 6) Davide ankakhulupirira kuti Yehova ndi wokoma mtima kwambiri. Choncho sanakhumudwe koma ankayembekezera kuti Yehova adzamupulumutsa ndipo ankaganizira zinthu zabwino zimene Yehovayo anamuchitira. Davide ankadziwa ubwino wodikira moleza mtima.
Ufumu Udzakwaniritsa Zimene Mulungu Amafuna Padziko Lapansi
16 Chitetezo. Pamapeto pake, mawu olimbikitsa amene ali pa Yesaya 11:6-9 adzakwaniritsidwa komaliza. Amuna, akazi ndi ana adzakhala otetezeka kulikonse kumene angapite padziko lapansili. Sikudzakhala chinthu china chilichonse choopsa, kaya munthu kapena nyama. Taganizirani mmene mudzasangalalire nthawi imeneyo pamene dziko lonseli muzidzaliona ngati kwanu. Mudzakhala ndi ufulu wosambira m’mitsinje ndi m’nyanja komanso kuyenda m’mapiri ndi m’nkhalango popanda kuopa chilichonse ngakhale utakhala usiku. Pa nthawiyi mawu a pa Ezekieli 34:25 adzakhala atakwaniritsidwa ndipo zidzakhala zotheka kwa anthu a Mulungu ‘kukhala m’chipululu popanda chowaopsa ndiponso kugona m’nkhalango.’
Mfundo Zothandiza
Kodi Mwasandulika?
12 Anthu ambiri m’dzikoli alinso ndi ‘maganizo oipa.’ Mwina iwo amaganiza kuti n’zachikale zoti anthu ena aziuza anzawo mfundo zoti aziyendera. Aphunzitsi ndi makolo ambiri amaganiza kuti ana ayenera kukhala ndi ufulu wochita zimene akufuna. Iwo amaona kuti palibe mfundo zimene anthu onse ayenera kuyendera. Ngakhale anthu ambiri amene ali m’zipembedzo amaona kuti ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akuona kuti n’chabwino osaganizira zimene Mulungu amafuna. (Sal. 14:1) Maganizo amenewa akhoza kusokoneza mmene Akhristu ena amaonera zinthu m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, mwina sangafune kuyendera dongosolo la mpingo ndipo angayambe kudandaula ndi chilichonse chimene sakusangalala nacho. Kapena sangagwirizane ndi malangizo ochokera m’Baibulo pa nkhani ya zosangalatsa, kugwiritsa ntchito Intaneti kapena maphunziro a ku yunivesite.