Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 May tsamba 5-16
  • May 20-26

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May 20-26
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 May tsamba 5-16

MAY 20-26

MASALIMO 40-41

Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuthandiza Ena?

(10 min.)

Tikamathandiza ena timakhala osangalala (Sl 41:1; w18.08 22 ¶16-18)

Yehova amathandiza anthu amene amathandiza ena (Sl 41:2-4; w15 12/15 24 ¶7)

Tikamathandiza ena timachititsa kuti Yehova atamandike (Sl 41:13; Miy 14:31; w17.09 12 ¶17)

Mlongo wachitsikana akuthandiza mlongo wachikulire kugwiritsa ntchito tabuleti.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi pali aliyense mumpingo wathu amene ndingamuthandize kudziwa mmene angamagwiritsire ntchito JW Library?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 40:5-10​—Kodi pemphero la Davide limatiphunzitsa chiyani zokhudza kuzindikira udindo womwe Yehova ali nawo monga Wolamulira Wamkulu? (it-2 16)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 40:1-17 (th phunziro 12)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yambani kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti akusangalala. (lmd phunziro 2 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yambani kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti wakhumudwa. (lmd phunziro 3 mfundo 5)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 14 mfundo 6. Kambiranani mfundo imodzi yopezeka mu nkhani yakuti “Tizitamanda Yehova Mumpingo” yomwe ili pa gawo lakuti “Onani Zinanso” ndi wophunzira amene amazengereza kuyankha pamisonkhano. (th phunziro 19)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 138

7. Tizichitira Zabwino Anthu Achikulire

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova amayamikira kwambiri zonse zimene achikulire okhulupirika amachita mumpingo, choncho ifenso tiyenera kumawayamikira. (Ahe 6:10) Kwa zaka zambiri, iwo achita zambiri pophunzitsa, kuthandiza komanso kulimbikitsa Akhristu anzawo. Sitikukayikira kuti inunso mukukumbukira mmene anakuthandizirani. Kodi mungawasonyeze bwanji kuti mumawayamikira chifukwa cha zonse zomwe akhala akuchita mumpingo?

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Tizichitira Zabwino Abale ndi Alongo Athu.” Abale ndi alongo akuthandiza M’bale Ho-jin Kang kukonza zinthu panja pa nyumba yake.

Onerani VIDIYO yakuti Tizichitira Zabwino Abale ndi Alongo Athu. Kenako funsani omvera mafunso awa:

  • Kodi Ji-Hoon anaphunzira chiyani kuchokera kwa M’bale Ho-jin Kang?

  • Kodi achikulire a mumpingo wanu mumawayamikira chifukwa cha zinthu ziti?

  • Kodi tingaphunzirepo chiyani kuchokera mu fanizo la Msamariya Wachifundo?

  • N’chifukwa chiyani mukuona kuti anali maganizo abwino kuti Ji-Hoon azikhala ndi anthu ena akamathandiza M’bale Ho-jin Kang?

Tikamaganizira kwambiri zimene anthu achikulire mumpingo wathu amafunikira, tikhoza kupeza njira zambiri za mmene tingawathandizire. Mukaona kuti enaake akufunika thandizo, muziganizira zimene mungachite kuti muwathandize.​—Yak 2:15, 16.

Werengani Agalatiya 6:10. Kenako funsani omvera funso ili:

  • Kodi ndi zinthu zabwino ziti zomwe mungachitire achikulire a mumpingo wanu?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 10 ¶1-4, bokosi patsamba 79

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena