Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 May tsamba 8-9
  • June 3-9

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • June 3-9
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 May tsamba 8-9

JUNE 3-9

MASALIMO 45-47

Nyimbo Na. 27 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesu wagwira dzanja mkwatibwi wake wophiphiritsa ndipo akuyang’ana dziko lapansi kuchokera kumwamba.

Yesu ali ndi mkwatibwi wake omwe ndi a 144,000

1. Nyimbo ya Ukwati wa Mfumu

(10 min.)

Salimo la nambala 45 limafotokoza za ukwati wa Mfumu yomwenso ndi Mesiya (Sl 45:1, 13, 14; w14 2/15 9-10 ¶8-9)

Ukwati wa Mfumuwu udzachitika pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo (Sl 45:3, 4; w22.05 17 ¶10-12)

Anthu onse adzalandira madalitso chifukwa cha ukwatiwu (Sl 46:8-11; it-2 1169)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mtima wanga “umasangalala” kulengeza uthenga wabwino wonena za Mfumu yathu, Yesu Khristu?’​—Sl 45:1.

Azimayi ndi azibambo akusangalala ndi moyo m’Paradaiso.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 45:16​—Kodi vesili likutiphunzitsa chiyani zokhudza mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso? (w17.04 11 ¶9)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 45:1-17 (th phunziro 5)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 1 mfundo 3)

5. Nkhani

(5 min.) ijwbv 26​—Mutu: Kodi lemba la Salimo 46:10 limatanthauza chiyani? (th phunziro 18)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(4 min.) Chitsanzo. g 12/10 22-23​—Mutu: Kodi Nkhani ya Maukwati a Amuna Kapena Akazi Okhaokha Mumaiona Bwanji? (lmd phunziro 6 mfundo 5)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 131

7. Pitirizani Kusonyezana Chikondi M’banja Lanu

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Mungatani Kuti Banja Lanu Lizisangalala?: Muzisonyezana Chikondi.” Mwamuna wakhala pampando ndi mkazi wake ndipo akumukisa pa chipumi.

Ukwati umakhala wosangalatsa kwambiri. (Sl 45:13-15) Nthawi zambiri, tsiku la ukwati limakhala lamtengo wapatali kwambiri kwa amene akwatiranawo. Koma kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti apitirizebe kukhala osangalala kwa moyo wawo wonse?​—Mla 9:9.

Kusonyezana chikondi ndi kumene kumachititsa kuti anthu akhale ndi banja losangalala. Anthu okwatirana ayenera kumatengera chitsanzo cha Isaki ndi Rabeka. Baibulo limatiuza kuti atakhala m’banja kwa zaka zoposa 30, iwo ankapitirizabe kukondana kwambiri. (Ge 26:8) Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti nawonso azikondana chonchi?

Onerani VIDIYO yakuti Mungatani Kuti Banja Lanu Lizisangalala?: Muzisonyezana Chikondi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:

  • Kodi n’chiyani chingachititse kuti mwamuna ndi mkazi wake asamakondane kwambiri?

  • Kodi mwamuna ndi mkazi omwe ndi okwatirana angatani kuti aliyense azichititsa mnzake kumva kuti amamukonda komanso kumuganizira?​—Mac 20:35

8. Zofunika Pampingo

(5 min.)

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 10 ¶13-21

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 111 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena