Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 May tsamba 14-15
  • June 24-30

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • June 24-30
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 May tsamba 14-15

JUNE 24-30

MASALIMO 54-56

Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Mulungu Ali Kumbali Yanu

(10 min.)

Mukamachita mantha, muzidalira Yehova ngati mmene Davide anachitira (Sl 56:1-4; w06 8/1 22 ¶10-11)

Yehova amayamikira kwambiri mukamapirira ndipo adzakuthandizani (Sl 56:8; cl 243 ¶9)

Yehova ali kumbali yanu. Iye sadzalola kuti chilichonse chikuwonongeni (Sl 56:9-13; Aro 8:36-39; w22.06 18 ¶16-17)

Mlongo amene ali ndi nkhawa akupemphera mochokera pansi pa mtima.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 55:12, 13​—Kodi Yehova anakonzeratu kuti Yudasi adzapereka Yesu? (it-1 857-858)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 55:1-23 (th phunziro 10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Muuzeni kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za phunziroli. (th phunziro 11)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 7 mfundo 4)

6. Nkhani

(5 min.) w23.01 29-30 ¶12-14​—Mutu: Kukonda Khristu Kumatichititsa Kukhala Olimba Mtima. Onani chithunzi. (th phunziro 9)

Mlongo ali m’basi ndipo akuchita chidwi ndi mtsikana wina amene akuoneka wankhawa. Mlongoyo ali ndi kapepala kakuti “Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?”

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 153

7. Tikhoza Kumasangalalabe Ngakhale Kuti . . . Tikuopsezedwa ndi Lupanga

(5 min.) Nkhani yokambirana.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Tikhoza Kumasangalalabe Ngakhale Kuti . . . Tikuopsezedwa ndi Lupanga.” M’bale Dugbe akukumbukira zomwe zinamuchitikira.

Onerani VIDIYO. Kenako funsani omvera funso ili:

  • Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zomwe zinachitikira M’bale Dugbe zimene zingakuthandizeni pamene muli ndi mantha?

8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya June

(10 min.) Onerani VIDIYOYI.

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 11 ¶11-19

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 70 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena