JUNE 17-23
MASALIMO 51-53
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi Mungatani Kuti Mupewe Kuchita Machimo Akuluakulu?
(10 min.)
Musamadzidalire; munthu aliyense akhoza kulakwitsa (Sl 51:5; 2Ak 11:3)
Muzichita zimene zingakuthandizeni kukhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova (Sl 51:6; w19.01 15 ¶4-5)
Muziyesetsa kuti musamalakelake kapena kuganizira zinthu zoipa (Sl 51:10-12; w15 6/15 14 ¶5-6)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 51:1-19 (th phunziro 12)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 7 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 4 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’phunzitseni za dzina la Mulungu. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
7. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 115
8. Zomwe Mungachite Kuti Mukonze Zomwe Mwalakwitsa
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Ngakhale titayesetsa bwanji, tonsefe timalakwitsa zinthu zina. (1Yo 1:8) Ndiye zikachitika, tisamalole kuti manyazi kapena mantha atilepheretse kubwerera kwa Yehova kuti atikhululukire komanso atithandize. (1Yo 1:9) Nthawi zonse kupemphera kwa Yehova kumakhala chinthu choyamba chomwe munthu angachite kuti akonze zomwe walakwitsa.
Werengani Salimo 51:1, 2, 17. Kenako funsani funso ili:
Kodi mawu a Davidewa angatilimbikitse bwanji kubwerera kwa Yehova kuti atithandize pamene tachita tchimo lalikulu?
Onerani VIDIYO yakuti Moyo Wanga Wachinyamata—Ndingatani Kuti Ndikonze Zomwe Ndinalakwitsa M’mbuyo? Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:
Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa Thalila ndi José kuti alakwitse zinthu?
Kodi anachita zotani kuti akonze zimene analakwitsazo?
Kodi kuchita zimenezo kunawathandiza bwanji?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 11 ¶5-10, bokosi patsamba 89