Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 July tsamba 4-5
  • July 15-21

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • July 15-21
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 July tsamba 4-5

JULY 15-21

MASALIMO 63-65

Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Chikondi Chanu Chokhulupirika N’chabwino Kuposa Moyo”

(10 min.)

Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi moyo (Sl 63:3; w01 10/15 15-16 ¶17-18)

Kuganizira mozama mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kumatichititsa kuti tizimukonda kwambiri (Sl 63:6; w19.12 28 ¶4; w15 10/15 24 ¶7)

Kuyamikira chikondi chokhulupirika cha Yehova kumatichititsa kuti tizimutamanda mosangalala (Sl 63:4, 5; w09 7/15 16 ¶6)

Zithunzi: Mlongo akuwerenga Baibulo. 1. Akulalikira mosangalala ndi mlongo wina. 2. Akuyankha pamisonkhano.

ZOMWE MUNGACHITE PA KULAMBIRA KWA PABANJA: Kambiranani mmene Yehova wakusonyezerani chikondi chokhulupirika.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 64:3—Kodi vesili likutilimbikitsa bwanji kuti tizilankhula bwino? (w07 11/15 15 ¶6)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 63:1–64:10 (th phunziro 12)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba salankhula chilankhulo chanu. (lmd phunziro 3 mfundo 4)

5. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Mwasiya kulankhula ndi munthu musanamulalikire. (lmd phunziro 2 mfundo 4)

6. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Pezani nkhani yomwe ingasangalatse munthuyo ndipo konzani zoti mudzakumanenso. (lmd phunziro 1 mfundo 5)

7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(4 min.) Chitsanzo. ijwfq 51​—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amabwereranso Kunyumba za Anthu Omwe Anakana Kuti Awalalikire? (lmd phunziro 4 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo 154

8. Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Mulungu?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka.” (Sl 86:15) Munthu amene ali ndi ‘chikondi chokhulupirika’ amakonda kwambiri munthu wina n’kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa iye zivute zitani. Ngakhale kuti Yehova amasonyeza chikondi kwa anthu onse, iye amasonyeza ‘chikondi chokhulupirika’ makamaka kwa atumiki ake omwe amakhala nawo pa ubwenzi wapadera. (Sl 33:18; 63:3; Yoh 3:16; Mac 14:17) Nafenso tingasonyeze kuti timayamikira chikondi chokhulupirika cha Yehova tikamamukonda. Tingachite zimenezi tikamamvera malamulo ake, kuphatikizapo lakuti “mukaphunzitse anthu.”—Mt 28:19; 1Yo 5:3.

Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha mu Utumiki. Kenako funsani mafunso awa:

Kodi chikondi chingatilimbikitse bwanji kulalikira uthenga wabwino pamene

    Zithunzi za muvidiyo yakuti “Muzisonyeza Chikondi Chosatha mu Utumiki.” Bambo wagona pampando atangofika kuchokera kuntchito.
  • tatopa?

  • Zithunzi za muvidiyo yakuti “Muzisonyeza Chikondi Chosatha mu Utumiki.” Mwininyumba akukalipira bambo yemwe akulalikira limodzi ndi mwana wake.
  • tikutsutsidwa?

  • Zithunzi za muvidiyo yakuti “Muzisonyeza Chikondi Chosatha mu Utumiki.” Mayi ndi mwana wake akulankhula ndi munthu wogwira ntchito mushopu.
  • tikuchita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku?

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 12 ¶14-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 79 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena