Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 September tsamba 2-3
  • September 2-8

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September 2-8
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 September tsamba 2-3

SEPTEMBER 2-8

MASALIMO 79-81

Nyimbo Na. 29 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Tizikonda Dzina la Yehova Laulemerero

(10 min.)

Tizipewa makhalidwe amene amanyozetsa dzina la Yehova (Sl 79:9; w17.02 9 ¶5)

Tizitamanda dzina la Yehova (Sl 80:18; (ijwbv 3 ¶4-5)

Yehova amadalitsa anthu omwe ndi omvera amene amasonyeza kuti amakonda dzina lake (Sl 81:​13, 16)

M’bale akupereka khadi la jw.org kwa mnzake wakuntchito pa nthawi ya buleki.

Kuti zochita zathu zizisonyeza kuti timaimira Yehova, tizizidziwikitsa kuti ndife a Mboni za Yehova

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 80:1—N’chifukwa chiyani dzina la Yosefe nthawi zina linkagwiritsidwa ntchito pofotokoza za mafuko onse a Isiraeli? (it-2 111)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 79:1–80:7 (th phunziro 10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 4)

5. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 3)

6. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 3 mfundo 3)

7. Ulendo Wobwereza

(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani munthu amene anakanapo kuphunzira Baibulo m’mbuyomu kuti muziphunzira naye. (lmd phunziro 8 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 10

8. “Iwo Adzayeretsa Dzina Langa”

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Satana anayamba kunyoza dzina la Yehova m’munda wa Edeni. Kungoyambira nthawi imeneyo, kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova kwakhala nkhani yaikulu kwambiri kwa zolengedwa zonse zanzeru.

Tangoganizirani zitsanzo zochepa chabe za mabodza oipa kwambiri amene Satana wakhala akufalitsa okhudza Yehova. Iye amanena kuti Mulungu ndi wolamulira wankhanza komanso wopanda chikondi. (Ge 3:​1-6; Yob 4:​18, 19) Amanenanso kuti anthu amene amalambira Yehova samamukonda ndi mtima wonse. (Yob 2:​4, 5) Iye wachititsanso anthu mamiliyoni ambiri kuyamba kukhulupirira kuti Yehova si amene analenga dziko lokongolali.—Aro 1:​20, 21.

Kodi mumamva bwanji mukaganizira mabodza amenewa? Mosakayikira, mumafuna kuchitapo kanthu ndi kuteteza dzina la Yehova. Iye anadziwa kuti anthu ake adzakhala ofunitsitsa kumuthandiza kuyeretsa dzina lake. (Yerekezerani ndi Yesaya 29:23.) Kodi mungathandize bwanji?

  • Muzithandiza ena kuti adziwe Yehova komanso kuyamba kumukonda. (Yoh 17:​25, 26) Muzikhala okonzeka kufotokoza umboni woti iye alipodi komanso kuphunzitsa ena za makhalidwe ake ochititsa chidwi.—Yes 63:7

  • Muzikonda Yehova ndi mtima wanu wonse. (Mt 22:​37, 38) Muzimvera malamulo onse a Yehova, ngakhale amene samakusangalatsani, ndipo muzichita zimenezi chifukwa choti mumafuna kumusangalatsa.—Miy 27:11

Zithunzi za muvidiyo yakuti “Chikondi Chanu Chisathe Ngakhale Kuti . . . Mukukumana ndi Mavuto Kusukulu” 1. Ariel wakhala padesiki ndipo mnyamata wina m’kalasi mwawo akumuloza komanso kumufunsa chifukwa chake sachitira sailuti mbendera. 2. Akuphunzira Baibulo payekha pogwiritsa ntchito phunziro 61 la buku lakuti “Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo.” 3. Waima kutsogolo m’kalasi mwawo ndipo akufotokoza zimene amakhulupirira. 4. Diego akupatsidwa ndudu ya fodya ndi mnzake wa kusukulu. 5. Akufufuza pogwiritsa ntchito tabuleti. 6. Akuweruka kusukulu ali osangalala.

Onerani VIDIYO yakuti Chikondi Chanu Chisathe Ngakhale Kuti . . . Mukukumana ndi Mavuto Kusukulu. Kenako funsani mafunso awa:

  • Kodi Ariel ndi Diego anateteza bwanji dzina la Yehova?

  • Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kuti ateteze dzina la Yehova?

  • Kodi mungatsanzire bwanji chitsanzo chawo?

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 15 ¶1-7, ndi mawu ofotokoza gawo 6

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena