Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 September tsamba 4
  • September 9-15

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September 9-15
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 September tsamba 4

SEPTEMBER 9-15

MASALIMO 82-84

Nyimbo Na. 80 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Mmodzi wa ana a Kora akuyang’ana mosirira chisa cha namzeze chomwe chili m’bwalo la kachisi

1. Tiziyamikira Mwayi wa Utumiki Umene Tili Nawo

(10 min.)

Timayamikira mwayi wa utumiki umene tili nawo (Sl 84:​1-3; wp16.6 8 ¶2-3)

Tizisangalala ndi utumiki umene tikuchita panopa, m’malo momaganizira kwambiri za utumiki umene timalakalaka (Sl 84:10; w08 7/15 30 ¶3-4)

Yehova ndi wabwino kwa anthu amene amamutumikira mokhulupirika (Sl 84:11; w20.01 17 ¶12)

Zithunzi zosonyeza Alevi akugwira ntchito zosiyanasiyana. 1. Akuthira madzi m’beseni lakopa kuchokera mu mtsuko. 2. Akukoka ngolo yodzadza ndi mitsuko. 3. Wanyamula mtsuko.

Utumiki uliwonse umakhala ndi madalitso ake komanso mavuto ake. Tikamaganizira madalitso amene timapeza, tikhoza kumasangalala ndi utumiki uliwonse.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 82:3—Kodi kusonyeza chikondi “ana amasiye” mumpingo n’kofunika bwanji? (it-1 816)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 82:1–83:18 (th phunziro 2)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Kukhala Achifundo—Zomwe Yesu Anachita

(7 min.) Nkhani yokambirana. Onerani VIDIYO, kenako kambiranani kabuku ka lmd phunziro 9 mfundo 1-2.

5. Kukhala Achifundo—Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

(8 min.) Nkhani yokambirana kuchokera m’kabuku ka lmd phunziro 9 mfundo 3-5 ndi “Onaninso Malemba Awa.”

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 57

6. Zofunika Pampingo

(15 min.)

7. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 15 ¶8-12, bokosi patsamba 118

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 130 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena