Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 September tsamba 6-7
  • September 23-29

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September 23-29
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 September tsamba 6-7

SEPTEMBER 23-29

MASALIMO 88-89

Nyimbo Na. 22 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Ulamuliro wa Yehova Ndi Wabwino Kwambiri

(10 min.)

Ulamuliro wa Yehova umalimbikitsa chilungamo chenicheni (Sl 89:14; w17.06 28 ¶5)

Ulamuliro wa Yehova umathandiza anthu kukhala ndi chisangalalo chenicheni (Sl 89:​15, 16; w17.06 29 ¶10-11)

Ulamuliro wa Yehova udzakhalapo mpaka kalekale (Sl 89:​34-37; w14 10/15 10 ¶14)

Zithunzi zosonyeza m’bale akuganizira za ulamuliro wa Yehova poyerekezera ndi maulamuliro a m’dzikoli. 1. Anthu akukangana pamsonkhano wandale. 2. Abale akupatsana moni mwansangala pa misonkhano yampingo.

Kuganizira za ulamuliro wa Yehova womwe ndi wapamwamba kwambiri, kungatithandize kusakhala mbali ya dziko andale akamafalitsa mabodza

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 89:37—Kodi kukhulupirika n’kosiyana bwanji ndi kudalirika? (cl 281 ¶4-5)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 89:​1-24 (th phunziro 11)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Pemphani kuti muziphunzira Baibulo ndi munthu amene si Mkhristu. (lmd phunziro 5 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti mumusonyeze mmene phunziro la Baibulo limachitikira. (th phunziro 9)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Nkhani. ijwbq 181—Mutu: Kodi m’Baibulo Muli Nkhani Zotani? (th phunziro 2)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 94

7. Mfundo za Yehova Ndi Zabwino Kwambiri

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Anthu ambiri amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana ndiponso ukwati ndi zopanikiza komanso zachikale. Kodi mumatsimikiza mumtima mwanu kuti kutsatira mfundo za Yehova nthawi zonse n’kwabwino kwa inuyo?—Yes 48:​17, 18; Aro 12:2.

    Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Zifukwa Zokhalira ndi Chikhulupiriro​—⁠Kodi Ndizitsatira Mfundo za Mulungu Kapena Zanga?” Hugo ndi Clara.
  • Pa nkhani ya makhalidwe abwino, n’chifukwa chiyani sitiyenera kumakhulupirira mfundo za anthu am’dzikoli? (Yer 10:23; 17:9; 2Ak 11:​13-15; Aef 4:​18, 19)

  • Zithunzi za muvidiyo yakuti “Zifukwa Zokhalira ndi Chikhulupiriro​—⁠Kodi Ndizitsatira Mfundo za Mulungu Kapena Zanga?” 1. Pa tabuleti pakuoneka chizindikiro cha jw.org. 2. Hugo ali mu sitima ndipo akuwerenga Baibulo pafoni. 3. Clara akupemphera.
  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira mfundo zamakhalidwe abwino za Yehova? (Yoh 3:16; Aro 11:33; Tit 1:2)

Baibulo limaphunzitsa kuti anthu amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu “sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.” (1Ak 6:​9, 10) Koma kodi timatsatira mfundo za Mulungu pa chifukwa chokhachi basi?

Onerani VIDIYO yakuti Zifukwa Zokhalira ndi Chikhulupiriro—Kodi Ndizitsatira Mfundo za Mulungu Kapena Zanga? Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mfundo zamakhalidwe abwino za Mulungu zimatiteteza bwanji?

8. Zofunika Pampingo

(5 min.)

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 15 ¶15-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 133 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena