JANUARY 5-11
YESAYA 17-20
Nyimbo Na. 153 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Zimene Zidzachitikire Amene Akutilanda Zinthu”
(10 min.)
Baibulo limayerekezera anthu ndi nyanja yomwe imasinthasintha (Yes 17:12; w18.06 7 ¶16-mwbr)
Timayembekezera kuti anthu a m’dzikoli azitizunza chifukwa chosalowerera ndale (Yoh 15:18, 19; w16.04 28 ¶4-mwbr)
Posachedwapa Yehova atipulumutsa kwa “anthu amene akutilanda zinthu” (Yes 17:13, 14; ip-1 198 ¶20-mwbr)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 20:2—Kodi Yesaya ankayendadi ali maliseche kwa zaka zitatu? (w06 12/1 11 ¶1-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 19:1-12 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani ndi munthu amene ali pabanja mfundo imodzi ya choonadi yopezeka mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 2, mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 8, mfundo 4)
6. Nkhani
(5 min.) lmd zakumapeto A, mfundo 14—Mutu: Mulungu Amafuna Kuti Tizipemphera kwa Iye. (th phunziro 8)
Nyimbo Na. 148
7. “Muzikumbukira Thanthwe Limene Limakutetezani”
(10 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova ndi Thanthwe limene limatiteteza. (Yes 17:10) Iye amapulumutsa anthu amene amathawira kwa iye. (Sl 144:1, 2) Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene amachititsa kuti anthu asiye kutitsutsa, iye amapatsa mabwenzi ake zimene akufunikira kuti apirire.—1Ak 10:13.
Njira imodzi imene timasonyezera kuti tikukumbukira Yehova ndi kumumvera. Onerani VIDIYO yakuti Phunzirani Kwa Anzake a Yehova—Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Itanani ana amene munawasankhiratu kuti abwere papulatifomu ndipo muwafunse mafunso otsatirawa, kapena funsani omvera kuti:
Kodi Yehova anapulumutsa bwanji anzake?—Da 3:24-28
Kodi Hananiya, Misayeli ndi Azariya anasonyeza bwanji kuti anali anzake a Yehova?
Kodi ndi pa nthawi iti pamene zimakuvutani kumvera Yehova?
Kodi mungatani kuti muzimvera Yehova?
8. Tsiku Lililonse Muzipeza Nthawi Yophunzira kwa Anzake a Yehova
(5 min.) Nkhani yokambirana.
Mavidiyo akuti Phunzirani kwa Anzake a Yehova anakonzedwa kuti azithandiza ana amene akuphunzira kuwerenga. Iwo amaphunzira za anthu amene ankakonda Yehova. Vidiyo iliyonse imalimbikitsa anawa kuti ‘azipeza nthawi tsiku lililonse yophunzira kuchokera kwa anzake a Yehova.’
Kodi mungatani kuti muzipeza nthawi tsiku lililonse yophunzira za Yehova komanso anzake?
Kodi mungakonde kuphunzira zambiri zokhudza anthu ati otchulidwa m’Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 50, mawu oyamba a gawo 9, komanso mutu 51