JANUARY 12-18
YESAYA 21-23
Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Zimene Zinachitikira Sebina?
(10 min.)
Muzikhalabe odzichepetsa mukapatsidwa udindo (Yes 22:15-19; w18.03 25 ¶7-9-mwbr)
Mukachotsedwa pa udindo musamasiye kutumikira Yehova mwakhama (Yes 36:3; w18.03 25 ¶10-mwbr)
Makolo kapena akulu, muzipereka malangizo a m’Malemba potsanzira mmene Yehova anachitira zinthu ndi Sebina (w18.03 26 ¶11-mwbr)
Malangizo achikondi ndi njira imodzi imene Mulungu amagwiritsa ntchito potiumba
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 21:1—N’chifukwa chiyani Babulo akutchulidwa kuti “chipululu chimene chili ngati nyanja”? (w06 12/1 11 ¶2-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 23:1-14 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(1 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Popanda kutchula mfundo ya m’Baibulo, pezani njira yomwe ingathandize munthu amene mukukambirana naye kudziwa kuti ndinu wa Mboni za Yehova (lmd phunziro 2, mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo ya choonadi yopezeka mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 1, mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti watanganidwa. (lmd phunziro 7, mfundo 4)
7. Nkhani
(5 min.) ijwyp nkhani Na. 71-mwbr—Mutu: Kodi Ndingasankhe Bwanji Munthu Wabwino Woti Ndizimutsanzira? (th phunziro 9)
Kutengera munthu wachitsanzo chabwino kungatithandize kukwaniritsa zolinga zathu
Nyimbo Na. 124
8. Zofunika Pampingo
(15 min.)
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 52-53