JANUARY 19-25
YESAYA 24-27
Nyimbo Na. 159 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Uyu Ndi Mulungu Wathu”
(10 min.)
Tili ndi zifukwa zambiri zosangalalira kuti Yehova ndi Mulungu wathu (Yes 25:9; cl 15 ¶21-mwbr)
Yehova adzatipatsa madalitso ambiri m’dziko latsopano, kuphatikizapo chakudya chabwino (Yes 25:6; w24.12 6 ¶14-mwbr)
Iye adzatipatsa moyo wosatha (Yes 25:7, 8; w25.01 28-29 ¶11-12-mwbr)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Ndikamachita zinthu zanga za tsiku ndi tsiku mlungu uno, ndi ndani amene ndingamuuzeko zimene Mulungu analonjeza?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 24:2—N’chifukwa chiyani mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso, mawu a pavesili anawalemba mosiyana ndi Mabaibulo ena a m’mbuyomu? (w15 12/15 17 ¶1-3-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 25:1-9 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Pezani nkhani yomwe ingasangalatse munthuyo. Muuzeni mmene angapezere nkhani ndi zinthu zina pa jw.org. (lmd phunziro 1, mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo ya choonadi yopezeka mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 9, mfundo 4)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Chitsanzo. ijwbq nkhani na. 160-mwbr—Mutu: N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu? (th phunziro 3)
Nyimbo Na. 144
7. Muzidalira Yehova Mukamakonzekera Zoti Mudzachite Mukadzadwala Kapena Mukadzafunika Opaleshoni
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova amateteza anthu amene ‘amamudalira ndi mtima wonse.’ (Werengani Yesaya 26:3.) Tingasonyeze kuti timadalira Yehova ndi mtima wonse tikamagwiritsa ntchito zinthu zimene watipatsa kudzera m’gulu lake pokonzekera zimene tidzachite tikadzadwala.
Onerani VIDIYO yakuti Kodi Mwakonzekera Zimene Mudzachite Mukadzafunikira Thandizo la Chipatala? Kenako funsani mafunso otsatirawa:
Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize tikamakonzekera thandizo lachipatala?
Kodi mafomu a zachipatalaa amatithandiza bwanji?
Kodi nthawi yabwino yolankhulana ndi a M’komiti Yolankhulana ndi Achipatala ndi iti?
Kodi mumamva bwanji ndi zinthu zimene Yehova watipatsazi?
“Mtendere wosatha” umene Yehova anatilonjeza pa Yesaya 26:3, sutanthauza kuti adzatiteteza kuti tisadzadwale. M’malomwake, kudzera m’gulu lake amatipatsa zinthu zotithandiza tikadwala zomwe zimatithandiza kukhala ndi mtendere komanso kumva kuti ndife otetezeka.
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 54-55
Mawu Omaliza (3 min.) | ndi Pemphero
a Mungapemphe kwa akulu ngati mukufuna fomu ya Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401), fomu ya Mfundo Zofunika Kukumbukira Tikafunika Thandizo la Opaleshoni Kapena la Matenda a Khansa (S-407), komanso fomu ya Mmene Makolo Angatetezere Ana Awo Kuti Asapatsidwe Magazi (S-55).