JANUARY 26–FEBRUARY 1
YESAYA 28-29
Nyimbo Na. 28 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzilemekeza Yehova ndi Milomo Yanu Komanso Mtima Wanu
(10 min.)
Yesaya anadzudzula atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake chifukwa cha chinyengo (Yes 29:13; ip-1 299 ¶23-mwbr)
Yesu anagwiritsa ntchito mawu a Yesaya ponena za atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake (Mt 15:7-9; w21.05 9 ¶7-mwbr)
Yehova amayembekezera kuti anthu amene amamulambira ‘azimumvera mochokera pansi pa mtima’ (Aro 6:17; w24.06 10 ¶8-mwbr)
Yehova amaona komanso kuyamikira tikamachita zinthu mogwirizana ndi zimene timalalikira
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 29:1—N’chifukwa chiyani n’zomveka kutchula mzinda wa Yerusalemu kuti Ariyeli? (it-E “Ariyeli” ¶1; it-E “Ariyeli” Na. 3-mwbr)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 29:13-24 (th phunziro 2)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pezani nkhani yomwe ingamusangalatse. Konzani zoti mudzalankhulanenso. (lmd phunziro 1, mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Yankhani funso limene mwininyumba anafunsa pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9, mfundo 3)
6. Kuphunzitsa Anthu
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 10, mfundo 3)
7. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 89
8. “Ndimachita Zinthu Zimene Zimamusangalatsa Nthawi Zonse”
(8 min.) Nkhani yokambirana.
Pa nthawi ina Yesu ananena kuti: “Ndimachita zinthu zimene zimamusangalatsa [Yehova] nthawi zonse.” (Yoh 8:29) Potsanzira Yesu, timayesetsa kuchita zinthu m’njira imene Yehova amafuna. Ngakhale kuti nthawi zambiri kuchita zimenezi si kophweka, koma zinthu zimatiyendera bwino.
Onerani VIDIYO yakuti Kuchita Zinthu M’njira Imene Yehova Amafuna. Kenako funsani funso ili:
Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani yochita zinthu m’njira imene Yehova amafuna mukamazunzidwa, kukakamizidwa kuchita makhalidwe oipa komanso mukakumana ndi msampha wa kunyada?
9. Zofunika Pampingo
(7 min.)
10. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 56, mawu oyamba a gawo 10, komanso mutu 57