Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
MARCH 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 41-42
“Usachite Mantha”
ip-2 20 ¶10
Mawu Otonthoza Aulosi Amene Akukukhudzani
10 Ponyang’ana m’zaka ngati 200 kutsogolo, Yehova akufufuza zochitika padziko lapansi. Ankhondo amphamvu olamulidwa ndi Koresi akuyenda mofulumira, akugonjetsa onse amene akulimbana nawo. Mitundu ya anthu—ngakhale amene akukhala m’zilumba, okhala ku madera akutali kwambiri—akunjenjemera ndi kufika kwake. Chifukwa cha mantha iwo akugwirizana kuti alimbane ndi munthu amene Yehova wamuitana kuchokera kum’maŵa kudzapereka chiweruzo. Akuyesa kulimbikitsana akumati: “Khala wolimba mtima.”
ijwbv nkhani na. 5 ¶4-7
Yesaya 41:10—“Usachite Mantha, Pakuti Ndili Nawe”
“Ndili nawe.” Yehova anauza anthu omulambira kuti sayenera kuopa chifukwa sali okha. Popeza Yehova amaona zimene anthuwo akupirira komanso amamva mapemphero awo, zili ngati iye ali pamodzi nawo.—Salimo 34:15; 1 Petulo 3:12.
“Ine ndine Mulungu wako.” Yehova anakhazikitsa mtima pansi anthu omulambira powakumbutsa kuti iye amaonabe kuti ndi Mulungu wawo ndipo iwo ndi anthu ake. Sayenera kukayikira kuti iye adzawathandiza zivute zitani.—Salimo 118:6; Aroma 8:32; Aheberi 13:6.
“Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” Yehova anagwiritsa ntchito mfundo zitatu pofuna kutsindika mfundo imodzi yakuti iye sangalephere kuthandiza anthu ake. Anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa posonyeza zimene amachita anthu ake akafunika kuthandizidwa. Munthu akagwa, Mulungu angamupatse dzanja lake lamanja kuti amudzutse.—Yesaya 41:13.
Njira yaikulu imene Mulungu amalimbitsira komanso kuthandiza anthu ake ndi kugwiritsa ntchito Baibulo. (Yoswa 1:8; Aheberi 4:12) Mwachitsanzo, m’Baibulo muli malangizo anzeru othandiza anthu amene akukumana ndi mavuto monga umphawi, matenda kapena kuferedwa. (Miyambo 2:6, 7) Mulungu angagwiritsenso ntchito mzimu wake woyera, kuti azipatsa anthu ake mphamvu zopirira mavuto awo.—Yesaya 40:29; Luka 11:13.
“Usachite Mantha. Ineyo Ndikuthandiza”
Ngati mutawaganizira mawuwa mutha kuona kuti ndi olimbikitsa kwambiri. Mawuwa sakusonyeza kuti mwagwirana manja ndi Yehova n’kumayenda naye limodzi, wina apa wina apa. Zikanakhala choncho ndiye kuti dzanja lake lamanja likanagwira dzanja lanu lamanzere. Koma lembali likusonyeza kuti Yehova akutambasula ‘dzanja lake lamanja lachilungamo’ n’kugwira ‘dzanja lanu lamanja.’ Zili ngati kuti akukukokani kuti akuchotseni pamalo ovuta kwambiri. Ndiyeno pochita zimenezi akukulimbikitsani ndi mawu oti: “Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”
Kodi inuyo mumaona kuti Yehova ndi Atate wanu komanso Mnzanu amene angakuthandizeni mukapanikizika ndi mavuto? Iye amakuganizirani, amakufunirani zabwino komanso amafunitsitsa kukuthandizani. Yehova amakukondani ndipo amafuna kuti musamade nkhawa mukakumana ndi mavuto. Mpake kuti Baibulo limati iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Sal. 46:1.
Mfundo Zothandiza
Kodi Kukhulupirika Kumatanthauzanji?
Yehova anamuuza mnzake Abrahamu kuti: “Ine ndine chikopa chako.” (Genesis 15:1; Yesaya 41:8) Iye sanangonena mawuŵa koma anachitadi zimenezo. Anateteza ndi kupulumutsa Abrahamu ndi banja lake kwa Farao ndi kwa Abimeleki. Anamuthandiza Abrahamu kupulumutsa Loti m’manja mwa mafumu anayi amene anamugwira. Yehova anabwezeretsa mphamvu zobereka za Abrahamu amene anali ndi zaka 100 ndi za Sara amene anali ndi zaka 90 kuti Mbewu imene anailonjeza idzabadwe kudzera mwa iwo. Yehova ankalankhula ndi Abrahamu nthaŵi zonse kudzera m’masomphenya, maloto, ndi angelo amithenga. Inde, Yehova anakhulupirika kwa Abrahamu panthaŵi imene anali moyo ndiponso patapita nthaŵi yaitali iye atamwalira. Kwa zaka mazana ambiri, Yehova anasungabe malonjezo ake kwa mbadwa za Abrahamu, mtundu wa Israyeli, ngakhale kuti mtunduwu unali wopulupudza. Ubale wa Yehova ndi Abrahamu unasonyeza tanthauzo la kukhulupirika kwenikweni lomwe ndi kuchitapo kanthu chifukwa cha chikondi.—Genesis, machaputala 12 mpaka 25.
MARCH 9-15
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 43-44
Ulosi Umene Unalembedwa Kutatsala Zaka 200
Maulosi Amene Anakwaniritsidwa
16 Mu 539 B.C.E., nthaŵi ya ulamuliro wa Babulo monga ulamuliro womalamulira wa padziko lonse inatha pamene wolamulira wakhama Wachiperisi Koresi, motsagana ndi gulu lankhondo la Amedi, anaguba motsutsana ndi mzindawo. Komabe, chimene Koresi anapeza, chinali champhamvu. Babulo anazunguliridwa ndi mpanda waukulu ndipo anawonekera kukhala wosaloŵeka. Mtsinje waukulu Firate, nawonso, unayenda kudutsa mzindawo ndipo unathandizira kwambiri chitetezo chake.
17 Wolemba mbiri Wachigriki Herodotus akufotokoza mmene Koresi anathetsera vutolo: “Iye anakhazika mbali ina ya gulu lake lankhondo pamalo amene mtsinjewo umaloŵera mumzindawo, ndiyeno gulu lina kumbuyo kumene umatulukira, atalamula kuguba kukaloŵa m’tauniyo moyenda pansi pouma pa mtsinjewo, mwansanga pamene madziwo anakhala ochepa mokwanira . . . Iye anapambutsa Firate mwa ngalande yonkera mphepete [nyanja yopanga yokumbidwa ndi wolamulira wapapitapo wa Babulo], chimene panthaŵiyo chinali thaŵale, palimene mtsinjewo unazama kufika pamlingo wakuti mpangidwe wa pansi pamtsinjewo sipanakhale pakuya. Panopo Aperisi amene anasiyidwa kaamba ka chifuno chimenecho pa Babulo mphepete mwa mtsinjewo, analoŵa mumtsinjewo, umene tsopano unaphwa kotero kuti ukafike pakatikati pa ntchafu za munthu, ndipo motero anakafika m’tauniyo.”4
it-E “Koresi” ¶7
Koresi
Kugonjetsedwa Kwa Babulo. Koresi anali atakonzeka kukamenyana ndi mzinda wa Babulo womwe unali wamphamvu. Kuchokera panthawiyi, iye anayamba kukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Mu ulosi wa Yesaya wonena za kubwezeretsedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi, wolamulira wa Chiperisiyayu anatchulidwa kuti ndi amene Yehova anamusankha kuti akagonjetse Babulo komanso kumasula Ayuda kuti abwerere kwawo. (Yes 44:26–45:7) Ulosiwu unalembedwa kutatsala zaka zoposa 150 kuti Koresi ayambe kulamulira. Komanso Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo Koresi asanabadwe n’komwe. Ngakhale zinali choncho, Yehova anali ataneneratu kuti Koresi adzakhala “m’busa” wake yemwe adzathandize anthu ake. (Yes 44:28; yerekezerani ndi Aroma 4:17.) Chifukwa chakuti anali atasankhidwiratu, Koresi ankatchedwa “wodzozedwa” wa Yehova (mawu akuti wodzozedwa akufanana ndi a Chiheberi akuti ma·shiʹach, mesiya, ndi mawu a Chigiriki akuti khri·stosʹ, khristu). (Yes 45:1) Ngakhale kuti Mulungu ‘anamuitana pomutchula dzina’ (Yes 45:4) kudakali nthawi yaitali chonchi, sizikutanthauza kuti Mulungu anapatsa Koresi dzinali pa nthawi imene ankabadwa. M’malomwake, zikutanthauza kuti Yehova ankadziwa kuti kudzakhala munthu wodziwika ndi dzina limeneli ndiponso kuti Yehova adzamuitana pomutchula dzina lake lenileni.
it-E “Koresi” ¶17
Koresi
Ngakhale kuti Koresi sankalambira Yehova, iye anachita zinthu mogwirizana ndi Ayuda mosiyana ndi mmene olamulira ena omwenso sankalambira Yehova ankachitira. Koresi anabwezeretsa ziwiya za m’nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kupita nazo ku Babulo. Anaperekanso chilolezo choti Ayuda aitanitse matabwa a mkungudza kuchokera ku Lebanoni komanso kuti ndalama zothandizira pantchito yomanga zichokere m’nyumba yake yachifumu. (Ezr 1:7-11; 3:7; 6:3-5) Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa pamwala wina wofotokoza zokhudza Koresi (Cyrus Cylinder; CHITHUNZI, Vol. 2, tsa. 332), wolamulira wa Chiperisiyayu ankakomera mtima anthu amene agonjetsedwa ndi ufumu wake ndipo sankawachitira nkhanza. Pamwalawo pali mawu a Koresi akuti: “Ndinabweza mizinda yopatulika [ina yomwe yatchulidwa kale] yakutsidya lina la mtsinje wa Tigirisi, malo opatulika omwe anali bwinja kwa nthawi yaitali, ndiponso zifaniziro zomwe zinali kumalowo komanso kuzikonzera malo ena opatulika okhazikika. Ndinasonkhanitsanso anthu omwe ankakhala m’maderawo n’kuwabwezera malo awo okhala.”—Ancient Near Eastern Texts, p. 316.
Mfundo Zothandiza
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Chitsanzo chachiwiri ndi ulosi wokhudza Koresi, yemwe anamasula Ayuda ku ukapolo n’kulamula kuti akamangenso kachisi wa Yehova. (Yes. 44:26–45:4) Mfumu Koresi ya ku Perisiya inakwaniritsa ulosi umenewu. (Ezara 1:1-4) Komatu Koresi sankalambira Mulungu woona. Yehova anagwiritsa ntchito Koresi pokwaniritsa ulosiwu koma anamulola kugwiritsa ntchito ufulu wake wosankha yemwe akufuna kumulambira.—Miy. 21:1.
MARCH 16-22
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 45-47
“Ine Ndine Mulungu Ndipo Palibe Aliyense Wofanana ndi Ine”
“Dzina Lanu Liyeretsedwe”
14 Satana wakhala akuyesetsa kuti alepheretse cholinga cha Yehova koma walephera. Baibulo limafotokoza zimene Yehova wachita ndipo limasonyeza kuti iye ndi Atate wachikondi komanso Wolamulira wabwino. N’zoona kuti kusamvera kwa Satana komanso onse amene ali kumbali yake kumam’pweteka kwambiri. (Sal. 78:40) Komabe zimene wachita pa nkhaniyi, zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru, woleza mtima ndiponso wachilungamo. Wasonyezanso mphamvu zake m’njira zambiri. Koposa zonse, wasonyeza kuti ndi Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Yehova akupitirizabe kuyeretsa dzina lake.
‘Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri’
14 Monga mmene tionere, Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake polenga, powononga, poteteza komanso pobwezeretsa zinthu. Mwachidule tingoti pochita chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse zolinga zake. (Yesaya 46:10) Pa zochitika zina, Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kutiphunzitsa zinthu zofunika zokhudza iyeyo komanso mfundo zake. Chofunika kwambiri n’chakuti iye amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kukwaniritsa chifuniro chake, chomwe ndi kuyeretsa dzina lake pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya. Zimenezi zimasonyeza kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Ndipotu palibe chimene chingalepheretse cholinga chakechi.
it-E “Ayuda Omwe Anali ku Ukapolo ku Babulo Anabwerera Kwawo” ¶1
Ayuda Omwe Anali ku Ukapolo ku Babulo Anabwerera Kwawo
Mu 607 B.C.E., dziko la Yuda lomwe poyamba linali ndi chuma chochuluka, ‘linasanduka bwinja, lopanda wokhalamo,’ chifukwa Ayuda anagwidwa kupita ku ukapolo ku Babulo ndipo ena otsala anathawira ku Igupto. (Yer 9:11) Komabe Mulungu yemwe ndi wokoma mtima sakanasiya anthu ake ku ukapolo mpaka kalekale. Iye ananeneratu kuti iwo ‘adzatumikira mfumu ya ku Babulo kwa zaka 70,’ ndipo pambuyo pake iye adzapulumutsa Ayuda okhulupirika. (Yer 25:11, 12; 29:10-14) Ngakhale kuti mzinda wa Babulo unali wamphamvu kwambiri padziko lonse ndipo unkaoneka kuti sungagonjetseke, sukanachititsa kuti cholinga cha Mulunguchi chilephereke. Ayuda atabwerera kuchokera ku ukapolo ku Babulo, zinasonyeza kuti maulosi a Yehova amakwaniritsidwa ndendende.
Ndife Okondwa Kuti Yehova Amatisonyeza Njira Yake
18 Lerolino, monga kale, kuyenda m’njira ya Yehova kumafuna kukhulupirika—kutsimikiza mtima kuti tidzatumikira yekhayo basi. Zimafuna kum’khulupirira—chikhulupiriro chenicheni kuti malonjezo a Yehova n’ngodalirika ndipo adzachitikadi. Kuyenda m’njira ya Yehova kumafuna kumvera—kutsatira malamulo ake ndi kusawasiya ndiponso kusunga miyezo yake yapamwamba. “Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama.”—Salimo 11:7
19 Ahazi anayembekezera kupeza chitetezo kwa milungu ya Aaramu. Aisrayeli ku Igupto ankati “mfumu yaikazi ya kumwamba,” mulungu wamkazi amene anthu ambiri anali kum’lambira kalelo ku Middle East, adzawalemeretsa. Lerolino, milungu yambiri si mafano enieni. Yesu anachenjeza za kutumikira “Chuma” m’malo motumikira Yehova. (Mateyu 6:24) Mtumwi Paulo ananena za “chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.” (Akolose 3:5) Ananenanso za awo amene “mulungu wawo ndiyo mimba yawo.” (Afilipi 3:19) Inde, ndalama ndi zinthu zakuthupi ndiyo ina mwa milungu yaikulu imene ikulambiridwa lerolino. Kwenikweni, anthu ochuluka—kuphatikizapo ambiri opembedza—‘akuyembekezera chuma chosadziŵika kukhala kwake.’ (1 Timoteo 6:17) Ambiri amagwira ntchito ndi mtima wonse potumikira milungu imeneyi, ndipo ena amapinduladi—amakhala m’nyumba zokongola koposa, kukhala ndi zinthu zamtengo wapamwamba, ndi kudya zakudya zapamwamba. Koma si onse amene akupeza bwino chonchi. Ndipo ngakhale awo amene amapeza bwinowo m’kupita kwa nthaŵi amaona kuti zinthu zimenezi sizikuwakhutiritsa mwa izo zokha. N’zosadziŵika kukhala kwake, zosakhalitsa, ndipo sizikhutiritsa zosoŵa zauzimu.—Mateyu 5:3.
Mfundo Zothandiza
Kodi Mulungu Anadziwiratu Kuti Adamu ndi Hava Adzachimwa?
Malemba amasonyezanso kuti Yehova ndi “wanzeru yekhayo.” (Aroma 16:27) Angelo a Mulungu anaona zinthu zambiri zimene iye anachita zosonyeza kuti alidi ndi nzeru zopanda malire. Yehova atalenga zinthu zapadziko lapansi, iwo “anayamba kufuula ndi chisangalalo.” (Yobu 38:4-7) Ndi zosakayikitsa kuti angelo amenewa ankaonetsetsa mwachidwi zonse zimene zinkachitika m’munda wa Edeni. Angelo anaona Mulungu akulenga kumwamba ndiponso zinthu zochititsa chidwi kwambiri za padziko lapansi. Ndiye kodi zikanakhala zomveka kwa iwo kuona kuti kenako Mulungu wanzeru ameneyu, akulenganso anthu awiri koma akudziwiratu kuti anthuwo sapita patali? N’zoonekeratu kuti zimenezi zikanakhala zosamveka.
Komabe mwina wina anganene kuti, ‘Kodi zingatheke bwanji kuti Mulungu, yemwe ndi wanzeru zonse, asadziwiretu za m’tsogolo?’ N’zoonadi kuti Yehova ali ndi nzeru zazikulu ndipo amatha kudziwa “za mapeto kuyambira pa chiyambi.” (Yesaya 46:9, 10) Koma iye sakakamizika kugwiritsa ntchito nzeru zake zonse zodziwiratu zinthu monga mmene zilili kuti kawirikawiri sagwiritsira ntchito mphamvu zake zonse pochita zinthu. Yehova amasankha mwanzeru zinthu zimene akufuna kuzidziwiratu. Ndipo amachita zimenezo akaona kuti ndi pofunikira komanso ngati zikugwirizana ndi mmene zinthu zili pa nthawiyo.
MARCH 23-29
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 48-49
Mukamamvera Yehova Zinthu Zidzakuyenderani Bwino
it-E “Mphunzitsi, Kuphunzitsa” ¶2
Mphunzitsi, Kuphunzitsa
Mlengi wathu Yehova Mulungu, ndi Mlangizi Wamkulu, kapena kuti Mphunzitsi wa atumiki ake. (1Mf 8:36; Sl 27:11; 86:11; 119:102; Yes 30:20; 54:13) Chilengedwe chimatiphunzitsa kuti kuli Mulungu yemwe ndi wanzeru zonse ndipo chimatipatsa mwayi wofufuza zinthu zambiri, ngakhale kuti pofika pano ndi zochepa chabe zimene anthu akwanitsa kuzimvetsa. (Yob 12:7-9) Kuwonjezera pamenepo, Yehova anagwiritsa ntchito njira zina zapadera pophunzitsa anthu za dzina lake, zolinga zake komanso malamulo ake. (Yerekezerani ndi Eks 4:12, 15; 24:12; 34:5-7.) Njira zimenezi zimapezeka m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu ndipo zimathandiza anthu kudziwa zoona zokhudza cholinga chake. (Aro 15:4; 2Ti 3:14-17) Mzimu wa Mulungu nawonso umagwira ntchito ngati mphunzitsi.—Yoh 14:26.
ijwbq nkhani na. 44 ¶2-3
Kodi Baibulo Limati Mungasankhe Nokha Zochita Kapena Mulungu Analemberatu Tsogolo Lanu?
● Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Nyama zimangoyendera nzeru zachibadwa koma ife anthu timafanana ndi Mlengi wathu chifukwa chakuti timatha kusonyeza makhalidwe monga chikondi ndi chilungamo. Mofanananso ndi Mlengi wathu, tili ndi ufulu wosankha.
● Zimene timasankha zimakhudza tsogolo lathu. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tisankhe moyo mwa kumvera mawu a Yehova Mulungu,’ kapena kuti tisankhe kumvera malamulo ake. (Deuteronomo 30:19, 20) Tikanakhala kuti tilibe ufulu wosankha, mawu amenewa akanakhala osamveka ndipo tikananena kuti Mulungu ndi wankhanza kwambiri potiuza zimenezi. M’malo motikakamiza kuchita zimene iye amanena, Mulungu amatichonderera mokoma mtima kuti: “Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje.”—Yesaya 48:18.
‘Dzilimbitseni Pamaziko a Chikhulupiriro Chanu Choyera Kopambana’
8 Apa Yehova akutikumbutsa kuti tikamamumvera, timapindula ndi ifeyo. Iye akutilonjeza kuti tidzapindula m’njira ziwiri. Njira yoyamba, mtendere wathu udzakhala ngati mtsinje, womwe madzi ake amakhala abata, ochuluka ndiponso samauma. Yachiwiri, chilungamo chathu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja. Mukaima m’mphepete mwa nyanja ndikuona mafunde, mumadziwa kuti umu ndi mmene nyanja imakhalira nthawi zonse. Mumadziwa kuti mafundewo sadzasiya kufika m’mphepete mwa nyanjayo mpaka kalekale. Kwenikweni Yehova akukuuzani kuti mungathe kumachita chilungamo, kapena kuti kuchita zabwino pa moyo wanu mpaka kalekale. Ngati mukuyesetsa kukhala wokhulupirika, Yehova sadzakusiyani kuti mugonje mukakumana ndi mayesero. (Werengani Salimo 55:22.) Malonjezo olimbikitsa amenewa angakuthandizeni kwambiri kukhulupirira Yehova ndi malamulo ake olungama.
Mfundo Zothandiza
it-E “Nthawi Yovomerezeka” ¶1-3
Nthawi Yovomerezeka
Pa 2 Akorinto 6:2, mtumwi Paulo ananena zimene zili mu ulosi wa pa Yesaya 49:8, womwe umati: “Yehova wanena kuti: ‘Pa nthawi yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha. Ndipo pa tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Ndinkakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu, kuti ndikonzenso dzikolo, kuti anthuwo atengenso cholowa chawo chimene chinali bwinja.’” Zikuoneka kuti poyambirirapo, mawuwa ankapita kwa Yesaya yemwe ankaimira mtundu wa Isiraeli. (Yes 49:3) N’zoonekeratu kuti ulosiwu unali wonena za kubwezeretsa, n’chifukwa chake unakwaniritsidwa koyamba pa nthawi imene Aisiraeli anamasulidwa kuchoka ku Babulo. Pa nthawiyi, Aisiraeli omwe anali akaidi anaitanidwa kuti, “Tulukani.” Choncho iwo anabwerera kwawo n’kukamanga nyumba zawo m’dziko lomwe linali bwinja lija.—Yes 49:9.
Komabe, mawu akuti, “kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,” opezeka pa Yesaya 49:8, komanso mawu a m’chiganizo chomaliza cha mu vesi 6, onena za “mtumiki” wa Yehova kuti adzaperekedwa ngati “kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti chipulumutso [cha Mulungu] chifike kumalekezero a dziko lapansi,” akusonyezeratu kuti ulosiwu ndi wonena za Mesiya yemwe ndi Khristu Yesu “mtumiki” wa Mulungu. (Yerekezerani Yes 42:1-4, 6, 7 ndi Mt 12:18-21.) Popeza kuti “nthawi yosonyeza kukoma mtima” inali nthawi imene Yehova ‘anayankha’ komanso ‘kuthandiza’ mtumiki wake, ndiye kuti akunena za nthawi imene Yesu anali padziko lapansi pomwe “anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa ankaopa Mulungu.” (Ahe 5:7-9; yerekezerani ndi Yoh 12:27, 28; 17:1-5; Lu 22:41-44; 23:46.) Choncho limeneli linali “tsiku la chipulumutso” kwa Mwana wa Mulungu, pamene anali ndi mwayi wosonyeza kukhulupirika kwake monga munthu wangwiro mpaka mapeto. Pamapeto pake, iye anali woyenera kukhala “ndi udindo wopulumutsa kwamuyaya anthu onse amene amamumvera.”—Ahe 5:9.
Kuwonjezera pamenepo, mawu a ulosi omwe Paulo ananenawa, akuoneka kuti akunenanso za Akhristu amene iye anawalimbikitsa kuti ‘asalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkuphonya cholinga cha kukoma mtimako,’ komanso omwe anawauza kuti (pambuyo pogwira mawu a pa Yes 49:8): “Ndithudi, inoyo ndi nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Lero ndi tsiku lachipulumutso.” (2Ak 6:1, 2) Akhristuwa anakhala “Isiraeli wa Mulungu” wauzimu kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E. kupita mtsogolo (Aga 6:16), koma iwo ankafunika kusonyeza kuti ndi oyenera kusonyezedwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, n’cholinga choti ‘nthawi yovomerezekayi’ ikhaledi “tsiku lachipulumutso” kwa iwo.
APRIL 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 50-51
Muzimvera Yesu Yemwe Anaphunzitsidwa ndi Yehova
Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
5 Pa nthawi yake yoyenerera, Yehova anaphunzitsa Mwana wake za utumiki umene anafunika kudzachita padziko lapansi. Taonani ulosi umene umafotokoza mmene Mlangizi Wamkulu ankaphunzitsira Mwana wake woyamba kubadwa. (Werengani Yesaya 50:4, 5.) Ulosiwu unanena kuti Yehova ankadzutsa Mwana wake “m’mawa uliwonse.” Mawu amenewa akunena za mphunzitsi amene amadzutsa wophunzira wake m’mamawa kuti akamuphunzitse. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linanena kuti: “Yehova . . . ankamutenga Yesu ngati mwana wasukulu ndipo ankamuphunzitsa mfundo zoyenera kukalalikira komanso mmene angalalikirire.” Pa sukulu imeneyi, Yehova anaphunzitsa Mwana wake ‘zimene ayenera kunena ndi zimene ayenera kulankhula.’ (Yoh. 12:49) Yehova anaphunzitsanso Mwana wake mmene angaphunzitsire anthu. Ali padziko lapansi, Yesu anagwiritsa ntchito zimene anaphunzirazo, osati pochita utumiki wake wokha komanso pophunzitsa otsatira ake kukwaniritsa utumiki wawo.
“Ndimakonda Atate”
13 Mwanayu asanabwere padziko lapansi, anaphunzira zambiri kuchokera kwa Atate wake. Ulosi wopezeka pa Yesaya 50:4-6 umasonyeza kuti Yehova anaphunzitsa Mwana wake mwapadera kwambiri kuti akwaniritse udindo wake monga Mesiya. Ngakhale kuti zina mwa zinthu zimene anaphunzirazo zinali zokhudza mavuto amene Wodzozedwa wa Yehova adzakumane nawo, Mwanayu anaphunzirabe modzipereka. Kenako Yesu anabwera padziko lapansi ndipo ngakhale atakula, sanasiye kupita kunyumba ya Atate wake kukalambira komanso kukaphunzira zinthu zimene Yehova ankafuna kuti anthu azidziwe. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti nthawi zonse Yesu ankapezeka pakachisi ndiponso kusunagoge. (Luka 4:16; 19:47) Kuti tipitirize kukonda Yehova, nthawi zonse tiyenera kumapezeka pamisonkhano ya Chikhristu, pamene timalambira Yehova ndi kuphunzira zambiri zokhudza iyeyo.
Mfundo Zothandiza
it-E “Malo Okumbapo Miyala” ¶2
Malo Okumbapo Miyala
Kudzera mwa Yesaya, Yehova ananena mokuluwika pogwiritsa ntchito zimene zimachitika pa malo okumbapo miyala. (Yes 51:1) Malinga ndi Yesaya 51:2, “thanthwe” panthawiyo linali Abulahamu, yemwe anali tate wa mitundu yonse, ndipo “malo okumbapo miyala” anali Sara yemwe kuchokera m’mimba mwake anabereka Isaki, kholo la Isiraeli. (Yes 51:2) Komabe, popeza kuti Isaki anabadwa modabwitsa komanso mothandizidwa ndi Mulungu, mawu okuluwika onena za malo okumbapo miyala, ayenera kuti ali ndi tanthauzo lophiphiritsa lauzimu. Choncho lemba la Deuteronomo 32:18 limanena za Yehova kuti ndi ‘Thanthwe limene linabereka’ Isiraeli mawu omwenso anagwiritsidwa ntchito ponena za Sara pa Yes 51:2.
APRIL 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 52-53
Yesu Anatisonyeza Chikondi Chachikulu
Achinyamata, Pewani Kutengera Zochita za Anzanu
2 Kodi inu mumafuna kuchita zoti musangalatse anzanu? Ngati ndi choncho n’chifukwa chiyani? Kodi mwina mumafuna kuti iwo azikukondani? Maganizo amenewa paokha si olakwika. Ngakhale anthu akuluakulu amafunanso kukondedwa ndi anzawo. Palibe amene amasangalala akamasalidwa, kaya akhale wamng’ono kapena wamkulu. Komabe si nthawi zonse pamene anthu amakuyamikirani chifukwa chokana kuchita zoipa. Ngakhalenso Yesu anakumanapo ndi vuto limeneli koma iye ankachitabe zabwino. Anthu ena ankamutsatira ndipo anakhala ophunzira ake pomwe ena ankanyoza Mwana wa Mulunguyu ndipo ‘ankamuona ngati wopanda pake.’—Yes. 53:3.
ip-2 205 ¶25
Yehova Atukula Mtumiki Wake Waumesiya
25 Kodi Mesiya analolera kuvutika ndi kufa? Yesaya akuti: “Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha [“anali kulolera kuzunzidwa,” NW] osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa om’senga, motero sanatsegula pakamwa pake.” (Yesaya 53:7) Usiku womaliza wa moyo wake, Yesu akanatha kuitanitsa “mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri” kuti adzam’thandize. Koma iye anati: “Pakutero, malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?” (Mateyu 26:53, 54) M’malo mwake, “Mwanawankhosa wa Mulungu” sanavutevute. (Yohane 1:29) Pamene ansembe aakulu ndi akulu anam’neneza monama pamaso pa Pilato, Yesu “sanayankha kanthu.” (Mateyu 27:11-14) Sanafune kunena kalikonse komwe kakanasokoneza kuchitika kwa chifuniro cha Mulungu kwa iye. Yesu anali wokonzeka kufa monga Mwanawankhosa woperekedwa nsembe, akudziŵa bwino lomwe kuti imfa yake idzawombola anthu ku uchimo, matenda, ndi imfa.
Mfundo Zothandiza
it-E “Ziwiya” ¶2
Ziwiya
Mawu a Chiheberi akuti keliʹ ankanena za ziwiya zosiyanasiyana zomwe zinkagwiritsidwa ntchito pachihema. Zina mwa ziwiyazi ndi monga mbale, mitsuko, mafosholo, mbale zolowa, mafoloko, zopalira moto, zopanira zozimitsira nyale, mabeseni, ndi makapu. (Eks 25:29, 30, 39; 27:3, 19; 37:16, 23; 38:3; 1Mf 7:40-50; 2Mb 4:11-22) Ziwiyazi zinkakhala “zoyera” chifukwa chakuti zinkagwiritsidwa ntchito pa zinthu zopatulika. (1Mf 8:4) Popeza kuti Ayuda omwe anachoka ku Babulo mu 537 B.C.E., anali ndi mwayi wonyamula ziwiya zopatulika zimene Mfumu Nebukanezara inatenga ku Yerusalemu, iwo ankafunika kukhala oyera pa nkhani ya kulambira komanso makhalidwe awo. Choncho ulosi wina unawalamula kuti: “Chokanimo, chokanimo, tulukani [m’Babulo], musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa! Chokani pakati pake! Khalani oyera, inu amene mukunyamula ziwiya za Yehova.” (Yes 52:11) Kuti akhale oyera mwa njira imeneyi, iwo ankafunika kuchita zambiri kuposa kungokhala aukhondo, ankafunika kukhala oyera kuchokera mumtima. Pamene ankalembera Akhristu a ku Korinto, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu a pa Yesaya 52:11 posonyeza kuti Akhristu nawonso ayenera kuchotsa chinthu chilichonse choipitsa thupi ndi mzimu.—2Ak 6:14-18; 7:1.
APRIL 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 54-55
Kodi Inuyo Mupereka Chiyani?
Maphunziro Ochokera kwa Mulungu Ndi Opambanadi
3 Chifukwa chakuti Yehova ndi wabwino, amalakalaka kuphunzitsa anthu opanda ungwiro. Polosera za Akhristu odzozedwa, lemba la Yesaya 54:13 limati: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa “nkhosa zina” za Khristu. (Yoh. 10:16) Zimenezi zikuoneka bwino mu ulosi umene ukukwaniritsidwa masiku ano. Yesaya anaona m’masomphenya anthu a mitundu yonse akukhamukira ku kulambira koona. Iye anafotokoza kuti anthuwo akuuzana kuti: “Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yes. 2:1-3) Ndi mwayi waukuludi kuphunzitsidwa ndi Mulungu.
“Gula Choonadi Ndipo Usachigulitse”
6 Werengani Yesaya 55:1-3. Mawu amene Yehova anauzira Yesaya amatithandizanso kumvetsa tanthauzo la kugula choonadi. Pamavesi amenewa, Yehova anayerekezera mawu ake ndi madzi, mkaka ndi vinyo. Mofanana ndi madzi ozizira bwino, mfundo za choonadi zimatitsitsimula. Ndipo mofanana ndi mkaka umene umatipatsa mphamvu komanso kuthandiza ana kuti akule, mawu a Mulungu amatithandiza kuti tipeze mphamvu komanso tikule mwauzimu. Koma mawu a Yehova alinso ngati vinyo. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limasonyeza kuti vinyo amathandiza kuti munthu asangalale. (Sal. 104:15) Choncho pouza anthu ake kuti ‘agule vinyo,’ Yehova akungotsimikizira anthu ake kuti akamatsatira mawu ake adzakhala osangalala. (Sal. 19:8) Kunena zoona, mfundo za m’mavesi amene takambiranawa zikutithandiza kudziwa ubwino wophunzira komanso kutsatira mfundo za choonadi za mawu a Mulungu. Koma zimene munthu amachita kuti apeze choonadicho zili ngati ndalama zimene amapereka kuti achigule. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu 5 zimene tingalolere kuchita kuti tigule choonadi.
KODI MUNACHITA ZINTHU ZITI KUTI MUGULE CHOONADI?
7 Nthawi yathu. Pamafunika nthawi kuti munthu apeze choonadi. Mwachitsanzo, munthu ayenera kupeza nthawi yoti amve uthenga wa Ufumu, awerenge Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo, aziphunzira payekha, azikonzekera misonkhano komanso azipezeka pamisonkhanopo. Kuti zimenezi zitheke, munthu amafunika ‘kugula’ nthawi kapena kugwiritsa ntchito nthawi imene akanachitira zinthu zina zosafunika kwenikweni. (Werengani Aefeso 5:15, 16 ndi mawu ake am’munsi.) Kodi pamafunika nthawi yaitali bwanji kuti munthu aphunzire mfundo zoyambirira za m’Baibulo? Zimadalira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthuyo. Palibe malire ophunzirira nzeru za Yehova, njira zake komanso ntchito zake. (Aroma 11:33) Magazini yoyambirira ya Nsanja ya Olonda inayerekezera kupeza choonadi ndi kupeza kaduwa kokongola. Magaziniyo inati: “Zikanakhala kuti kaduwa kamodziko n’kokwanira si bwenzi pali enanso. Choncho tisamangokhutira ndi mfundo imodzi yokha ya choonadi. Nthawi zonse tizifufuza mfundo zina.” Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi maluwa a choonadi amene ineyo ndapeza ndi ochuluka bwanji?’ Ngakhale titalandira moyo wamuyaya padzakhalabe mfundo zambiri zokhudza Yehova zimene tingaphunzire. Chofunika panopa ndi kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi yathu kuti tiziphunzira mfundo zambiri za choonadi. Tiyeni tikambirane chitsanzo cha munthu wina amene ankafunitsitsa kupeza choonadi.
“Yang’anirani Mamvedwe Anu”
Pali zinthu zambiri zimene zimatilepheretsa kutchera khutu. Tingakhale ndi nkhaŵa m’maganizo mwathu. Phokoso komanso kuyendayenda kwa anthu m’katimo posonkhana kapena panja kungatidodometse. Kusamva bwino m’thupi kungatilepheretse kuika maganizo pa nkhani. Amene ali ndi ana aang’ono kaŵirikaŵiri amapeza kuti maganizo awo amadodometsedwa. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizisunga maganizo athu pa pulogalamu?
Kaŵirikaŵiri, maso ndiwo amatsogolera maganizo athu. Gwiritsani ntchito maso anu kuti akuthandizeni kusunga maganizo pamodzi mwa kuyang’ana wolankhulayo. Pamene atchula lemba m’Baibulo—ngakhale lodziŵika—litseguleni, ndipo m’tsatireni pamene akuŵerenga. Kanizani mutu wanu kucheukira phokoso lililonse kapena munthu amene akuyenda. Ngati maso anu akupereka zododometsa zambiri ku maganizo anu, mungaphonye zambiri zimene zikulankhulidwa ku pulatifomu.
Ngati “zolingalira” zina zikukulepheretsani kuika maganizo anu pa pulogalamu, pempherani kwa Yehova kuti akhazikitse pansi maganizo ndi mtima wanu kuti mutchere khutu. (Sal. 94:19; Afil. 4:6, 7) Chitani zimenezo mobwerezabwereza ngati kuli kofunika. (Mat. 7:7, 8) Misonkhano yampingo ndi chogaŵira cha Yehova. Khalani ndi chidaliro chakuti iyenso amafuna kuti mupindule nayo.—1 Yoh. 5:14, 15.
Mfundo Zothandiza
“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ine Ndine Mulungu Wako”
14 Choyamba, Akhristufe timayembekezera kuti anthu azidana nafe. (Mat. 10:22) Paja Yesu ananeneratu kuti ophunzira ake adzazunzidwa kwambiri m’masiku otsiriza. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20) Chachiwiri, ulosi wa Yesaya unasonyeza kuti adani athu sadzangodana nafe koma adzagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana polimbana nafe. Zina mwa zida zimene amagwiritsa ntchito ndi chinyengo, mabodza ankunkhuniza komanso kuzunza mwankhanza. (Mat. 5:11) Yehova saletsa adani athu kugwiritsa ntchito zida zimenezi polimbana nafe. (Aef. 6:12; Chiv. 12:17) Koma sitiyenera kuchita mantha. N’chifukwa chiyani tikutero?
15 Tiyeni tikambirane mfundo yachitatu imene tiyenera kuikumbukira. Yehova ananena kuti “chida chilichonse” chimene anthu angagwiritse ntchito polimbana nafe “sichidzapambana.” Mofanana ndi mmene khoma limatitetezera ku mphepo yamkuntho, Yehova amatitetezanso pamene “anthu ankhanza akuwomba” ngati mphepo. (Werengani Yesaya 25:4, 5.) Adani athu sangathe kutiwonongeratu.—Yes. 65:17.
APRIL 27–MAY 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 56-57
Timasangalala Kuti Yehova Ndi Mulungu Wathu
ip-2 269 ¶14-16
Yehova Amatsitsimutsa Mzimu wa Odzichepetsa
14 Komabe, nthaŵi ya kupirira kwa Mulungu idzatha. Polingalira za nthaŵi imeneyo, Yehova akulengeza kuti: “Ndidzaonetsa chilungamo chako ndi ntchito zako sudzapindula nazo. Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse.” (Yesaya 57:12, 13a) Yehova adzavumbula chilungamo chonamizira cha Yuda. Sadzapindula ndi ntchito zake zachinyengo. ‘Zosonkhanitsa’ zake, mafano omwe ali nawo, sadzamupulumutsa. Pamene tsoka lifika, milungu imene amaidalira idzauluzika ndi kuwomba chabe kwa mphepo.
15 Mawu a Yehova akuchitika mu 607 B.C.E. Chimenecho ndicho chaka chimene Mfumu Nebukadinezara ya Babulo ikuwononga Yerusalemu, ikuwotcha kachisi, ndi kutenga ukapolo anthu ena. “Motero anamuka nawo Ayuda andende kuwachotsa m’dziko lawo.”—2 Mafumu 25:1-21.
16 Mofananamo, mafano ambirimbiri a Matchalitchi Achikristu sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. (Yesaya 2:19-22; 2 Atesalonika 1:6-10) Matchalitchi Achikristu adzafafanizidwa limodzi ndi ‘Babulo Wamkulu’ yense, amene ndi zipembedzo zonse zonyenga za padziko lapansi. Chilombo chofiiritsa chophiphiritsa ndi nyanga zake khumi ‘zidzam’khalitsa [Babulo Wamkulu] wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzam’psereza ndi moto.’ (Chivumbulutso 17:3, 16, 17) Ndifetu okondwa kwambiri kuti tinamvera lamulo lakuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake”! (Chivumbulutso 18:4, 5) Tisabwererenso kwa iye kapena ku njira zake.
“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”
16 Kunena zoona anthuwa anachita bwino kwambiri kusintha chonchi. Paja Baibulo limayerekezera anthu m’dzikoli ndi nyanja yowinduka yomwe ikukanika kukhala bata. (Yes. 17:12; 57:20, 21; Chiv. 13:1) Nkhani zandale zimagawanitsa anthu ndiponso zimayambitsa chiwawa koma ifeyo timapitiriza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana. Popeza anthu ndi ogawikana m’dzikoli, Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona mgwirizano wa anthu ake.—Werengani Zefaniya 3:17.
it-E “Dziko” ¶21
Dziko
Mawu akuti dziko amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ponena za zinthu zolimba komanso zokhazikika zokhudza anthu. Pomwe kuwindukawinduka kwa nyanja kumaimira kusakhazikika kwa maulamuliro a anthu.—Yes 57:20; Yak 1:6; Yuda 13; yerekezerani ndi Chv 12:16; 20:11; 21:1.
it-E “Mtendere” ¶3
Mtendere
Kupeza Mtendere. Yehova ndi Mulungu wamtendere (1Ak 14:33; 2Ak 13:11; 1At 5:23; Ahe 13:20) komanso amene amapereka mtendere (Nu 6:26; 1Mb 22:9; Sl 4:8; 29:11; 147:14; Yes 45:7; Aro 15:33; 16:20), khalidwe limene anthu amakhala nalo mothandizidwa ndi mzimu wake woyera. (Aga 5:22) Choncho anthu amene ali pamtendere ndi Mulungu ndi amene amakhala ndi mtendere weniweni. Machimo akuluakulu angachititse kuti munthu asakhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso kuti azisowa mtendere. Wolemba masalimo wina anati: “Mʼmafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.” (Sl 38:3) Choncho amene amafunitsitsa kukhala pamtendere ayenera ‘kusiya kuchita zinthu zoipa n’kumachita zabwino.’ (Sl 34:14) Popanda chilungamo sipangakhale mtendere. (Sl 72:3; 85:10; Yes 32:17) N’chifukwa chake anthu oipa sakhala ndi mtendere. (Yes 48:22; 57:21; yerekezerani ndi Yes 59:2-8.) Komabe anthu amene amapatsidwa mtendere ndi amene amadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse, amakonda chilamulo chake (Sl 119:165), komanso amene amamvera malamulo ake.—Yes 48:18.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 2
56:6—Kodi ‘alendo’ ndani ndipo ‘agwira zolimba chipangano cha Yehova’ m’njira yotani? ‘Alendo’ ndiwo “nkhosa zina” za Yesu. (Yohane 10:16) Agwira zolimba chipangano chatsopano mwa kumvera malamulo okhudza chipanganocho, kuchita mogwirizana ndi zonse zimene zakonzedwa kudzera m’chipanganocho, kudya chakudya chauzimu chofanana ndi Akhristu odzozedwa, ndi kuwathandiza m’ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira.
Kulemekeza Misonkhano Yathu Yopatulika
YEHOVA wasonkhanitsa anthu ake, Akhristu odzozedwa ndi anzawo, kuti amulambire pa ‘phiri lake lopatulika.’ Akuwasangalatsa ‘m’nyumba yake yopemphereramo,’ yomwe ndi kachisi wake wauzimu, kapena kuti “nyumba yopemphereramo mitundu yonse.” (Yesaya 56:7; Maliko 11:17) Zochitika zimenezi zikusonyeza kuti kulambira kwa Yehova n’koyera, kosadetsedwa, ndi kokwezeka. Mwa kulemekeza moyenerera misonkhano yathu yomwe timaphunzirako ndi kulambirako, timasonyeza kuti timaona zinthu zopatulika monga mmene Yehova amazionera.