Dominican Republic
MU 1492, Christopher Columbus anapita m’mayiko ena amene ankaona kuti akhoza kupezako chuma ndi zinthu zina zabwino. Pa mayikowa, panali chilumba china chimene iye anachipatsa dzina loti La Isla Española kapena kuti Hispaniola. Panopa, mbali yaikulu ya chilumbachi ili m’dziko la Dominican Republic. Masiku ano, anthu ambiri a m’dzikoli atulukira zinthu zina zofunika kwambiri. Iwo aphunzira zoti dziko latsopano likubwera ndipo mudzakhala chilungamo chifukwa lizidzalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. (2 Pet. 3:13) Werengani nkhani yosangalatsa ya anthu amtima wabwino amene anaphunzira zinthu zimenezi.