Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 2-3
  • Lemba la Chaka cha 2015

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lemba la Chaka cha 2015
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Nkhani Yofanana
  • Yamikani Yehova Ndipo Adzakudalitsani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Khalani Akuyamika”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • ‘Muziyamikira Yehova’
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Khulupirirani Yehova, “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njira Iliyonse”
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 2-3
Chithunzi pamasamba 2, 3

Lemba la Chaka cha 2015

“Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.”​—Salimo 106:1

Yehova anapulumutsa Aisiraeli pa Nyanja Yofiira pamene Farao ndi asilikali ake ankawathamangira. Apa Aisiraeliwo anali ndi zifukwa zambiri zowachititsa kumuyamikira. Ifenso tiyenera kuyamikira Yehova. N’zoona kuti timakumana ndi mavuto komanso timakhumudwa. Koma izi zikachitika, kukumbukira madalitso amene tili nawo kukhoza kutilimbikitsa.

Posachedwapa Yehova adzatidalitsa kwambiri. Iye adzatimasula n’kuthetsa mavuto athu onse. Kaya tikumane ndi vuto lotani, tiyenera kudziwa kuti Yehova sadzatisiya. Iye amatipatsa zinthu zonse zotithandiza kuti tizimutumikira mokhulupirika. Nthawi zonse amakhala “pothawira pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.” (Sal. 46:1) Kukumbukira zimenezi kungatithandize kuti tipirire mavuto oopsa kwambiri. Choncho m’chaka chonse chikubwerachi, tiyeni tiziganizira madalitso athu ‘n’kumayamika Yehova chifukwa iye ndi wabwino ndipo kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.’—Sal. 106:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena