CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 106-109
‘Muziyamikira Yehova’
N’chifukwa chiyani Aisiraeli anaiwala mwamsanga zimene Yehova anawachitira?
Anasiya kuganizira za Yehova n’kuyamba kuganizira mavuto komanso zofuna zawo
Kodi tingatani kuti tizithokoza Yehova komanso kuti tisamaiwale zomwe watichitira?
Tiziganizira zinthu zonse zimene Yehova watichitira
Tiziganizira zimene Mulungu walonjeza kudzatichitira m’tsogolo
Tizithokoza Yehova tikaona kuti watichitira zomwe tinapempha