Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb17 tsamba 84-88
  • Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Georgia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Georgia
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
yb17 tsamba 84-88
Dera lina lamapiri ku Svaneti m’dziko la Georgia

Dera lamapiri la Svaneti

GEORGIA

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Georgia

Bambo wanyamula basiketi ya zipatso za mphesa; zipatso za mphesa

Anthu amasangalala akamakolola zipatso za mphesa

Mmene Dzikoli Lilili: Kuli mapiri akuluakulu omwe amaoneka oyera pamwamba pake chifukwa cha sinowo [kapena kuti chipale chofewa]. Mapiri ena ndi aatali kufika mamita 4,500. Dzikoli linagawidwa m’zigawo ziwiri, chigawo chakum’mawa komanso chakumadzulo. M’zigawo zimenezi muli madera osiyanasiyana ndipo dera lililonse lili ndi nyengo, chikhalidwe, nyimbo, magule komanso zakudya zake.

Anthu: Ambiri mwa anthu okwana 3.7 miliyoni omwe amakhala m’dziko la Georgia ndi nzika za dzikoli.

Chipembedzo: Anthu ambiri m’dzikoli ali m’chipembedzo cha Orthodox. Anthu 10 pa 100 alionse ndi Asilamu.

Chinenero: Chinenero cha anthu a ku Georgia ndi chosiyana kwambiri ndi zinenero za anthu a m’mayiko ena omwe anayandikana ndi dzikoli. Zikuoneka kuti afabeti ya m’dzikoli inayamba kale kwambiri chisanafike chaka cha 1 C.E.

Ntchito Zawo: Anthu ambiri ndi alimi. Koma chaposachedwapa, dzikoli linayambanso kudalira kwambiri ntchito zokopa alendo.

Nyengo: Kum’mawa kwa dzikoli si kotentha kwambiri. Koma m’mbali mwa nyanja ya Black Sea, m’chigawo chakumadzulo kwa dzikoli, ndi kotentha ndipo kumakhala zipatso zambiri monga malalanje, mandimu ndi zina.

Anthu akukolola zipatso za mphesa

Akukolola zipatso za mphesa m’dera la Kakheti

Chakudya: Anthu a m’dzikoli amakonda kudya buledi m’mawa, masana komanso madzulo. Anthu ambiri amaphika okha buledi ndipo amagwiritsa ntchito mauvuni opangidwa ndi dongo. Amakonda supu wophikidwa ndi zinthu zosiyanasiyana komanso amamuthira zokometsera. Anthu a ku Georgia akhalanso akupanga vinyo kwa zaka zambiri. M’madera akumidzi amasunga vinyo m’mitsuko ikuluikulu kuti apese. Mabanja ambiri amalima mphesa ndipo amapanga vinyo wawo. Ku Georgia kuli mitundu ya mphesa pafupifupi 500.

Mayi akupanga buledi

Akupanga buledi

KUKULA KWAKE

26,900 (69,700 sq km)

KULI ANTHU

3,720,400

OFALITSA MU 2016

18,619

WOFALITSA ALIYENSE AFUNIKA KUPHUNZITSA ANTHU

200

OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO MU 2016

32,216

Mapu a dziko la Georgia
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena