Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 117
  • Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi zikumandivuta kupeza nthawi yochita zinthu zina chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?
  • Kodi ndikumalephera kugona chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?
  • Kodi malo ochezera a pa intaneti akumandisokoneza maganizo?
  • Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Gawo 1: Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Ndingatani Ngati Makolo Anga Sakundilola Kugwiritsa Ntchito Malo Ochezera a pa Intaneti?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Gawo 2: Kuphunzitsa Mwana Wanu Wachinyamata Kukhala Wosamala Pogwiritsa Ntchito Intaneti
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Katswiri wa za Umoyo Wachenjeza Kuti Achinyamata Angakumane Ndi Mavuto Pamalo Ochezera a pa Intaneti—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 117
Mtsikana akuyang’ana pafoni yake. Wazunguliridwa ndi ma imoji osiyanasiyana

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?

Kodi makolo anu amakulolani kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti? Ngati amakulolani, nkhaniyi ikuthandizani kuganizira mbali zitatu zofunika izi:

Patsamba lino mupeza izi

  • Kodi zikumandivuta kupeza nthawi yochita zinthu zina chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?

  • Kodi ndikumalephera kugona chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?

  • Kodi malo ochezera a pa intaneti akumandisokoneza maganizo?

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Kodi zikumandivuta kupeza nthawi yochita zinthu zina chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?

Kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kuli ngati kukwera hatchi yamphamvu kwambiri. Mungathe kuilamulira kapena ingakulamulireni.

“Ndikalowa pa intaneti ndimaganiza kuti ndingokhalapo kwa nthawi yochepa chabe, koma ndimangozindikira kuti ndakhalapo maola ambirimbiri! Malo ochezera a pa intaneti akhoza kutikomedwetsa komanso kutitayira nthawi.”​—Joanna.

Kodi mukudziwa? Malo ochezera pa intaneti ndi okomedwetsa chifukwa ndi mmene anawapangira basi. Anthu amene anapanga mawebusaiti amenewa amadziwa mfundo yakuti kuti webusaiti ikakhala yotchuka kwambiri anthu ambirinso amalowapo ndipo otsatsa malonda amalipiranso ndalama zochuluka.

Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zina ndimalephera kusunga nthawi chifukwa chokomedwa ndi kuona zinthu zosiyanasiyana pamalo ochezera a pa intaneti? Kodi ndingagwiritse ntchito nthawiyi kuchita zinthu zina zofunikira?’

Zimene mungachite. Dziikireni malire pa nthawi imene mumakhala pamalo ochezera a pa intaneti ndipo muzichokapo nthawiyo ikakwana.

Zithunzi zosonyeza mnyamata pa nthawi yopuma masana. 1. Wagona pabedi atavala mahedifoni m’makutu ndipo maso ake ali pafoni. 2. Akusangalala kusewera mpira ndi anzake panja.

Dziikireni malire pa nthawi imene mumakhala pamalo ochezera a pa intaneti

“Ndinaika malire a nthawi pafoni panga kuti nthawiyo ikakwana mapulogalamu ena amene ndimagwiritsa ntchito azitsekeka okha. Ndinachita zimenezi kwa kanthawi ndipo zinandithandiza kuti ndizigwiritsa ntchito bwino nthawi yanga pamalo ochezera a pa intaneti.”​—Tina.

Mfundo ya m’Baibulo: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—Aefeso 5:16.

Kodi ndikumalephera kugona chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti?

Akatswiri ambiri amanena kuti achinyamata amafunika azigona maola osachepera 8, koma ambiri amagona maola ochepa kuposa pamenepa. Chimodzi mwa zinthu zimene zikuchititsa zimenezi ndi kugwiritsa ntchito malo ochezera pa intaneti.

“Ndisanagone ndimakonda kuona zomwe zabwera pafoni panga, kenako ndimangozindikira kuti padutsa maola ambiri ndikuona zithunzi zimene anthu aika pamalo ochezera. Ndikuona kuti limeneli ndi vuto lomwe ndikufunika kusintha.”​—Maria.

Kodi mukudziwa? Kusagona mokwanira kungayambitse nkhawa komanso matenda amaganizo. Pulofesa wina woona zamaganizo a anthu, dzina lake Jean Twenge, ananena kuti chimodzi mwa zinthu zinthu zimene zimapangitsa kuti anthu asamamve bwino m’thupi komanso kuti asamasangalale ndi kusagona mokwanira. Iye ananenanso kuti “m’kupita kwa nthawi” munthu amene amavutika akhoza kupezeka ndi “matenda aakulu ovutika maganizo.”a

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimagona maola angati usiku uliwonse?’ ‘Kodi ndimangokhalira kuona zinthu pamalo ochezera a pa intaneti pa nthawi imene ndikufunikira kupuma kapena kugona?’

Zimene mungachite. Muziyesetsa kuika zipangizo zanu zamakono patali ndi bedi lanu mukamafuna kugona. Ngati n’zotheka, muzisiya kuyang’ana pasikirini yapazipangizo zanu kudakali maola awiri musanakagone. Ngati mukufuna kuti alamu ikudzutseni m’mawa, yesani kugwiritsa ntchito alamu yomwe sili mufoni kapena tabuleti yanu.

Zithunzi zosonyeza mtsikana akungodzuka kumene m’mawa. 1. Wakhala pabedi ndipo akuvutika kuchokapo. 2. Wakhala pabedi ndipo wakweza manja ake m’mwamba uku akusangalala.

Muzisiya kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kudakali maola angapo mukamafuna kugona

“Nthawi zina ndimagona mochedwa kwambiri kumangoyang’ana zinthu zomwe zabwera pafoni panga. Limeneli ndi vuto limene ndikuyesetsa kuti ndithane nalo. Ndikufunika ndichita zinthu monga munthu wamkulu zomwe zikuphatikizapo kumachita zinthu mwanzeru. Ndikufuna ndizigona mwamsanga n’cholinga choti tsiku lotsatira ndizichita zinthu zakupsa.”​—Jeremy.

Mfundo ya m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

Kodi malo ochezera a pa intaneti akumandisokoneza maganizo?

Kafukufuku wina anasonyeza kuti pafupifupi hafu ya atsikana akusekondale omwe anachita nawo kafukufukuyu ananena kuti “amakhala okhumudwa pafupipafupi kapenanso kusowa chiyembekezo.” Nthawi zina malo ochezera a pa intaneti ndi amene amapangitsa kuti azimva choncho. Dr. Leonard Saxb ananena kuti: “Ukamakhala nthawi yaitali uli pamalo ochezera a pa intaneti, umayamba kudziyerekezera ndi anthu ena ndipo zimenezi zimapangitsa kuti uzivutika ndi maganizo.”

“Ndi zofala kwambiri kuona achinyamata akudziyerekezera ndi anthu ena ndipo malo ochezera a pa intaneti amachititsa vutoli kukula kwambiri. Ukhoza kuona zithunzi za anthu ena kwa maola ochuluka n’kuyamba kuyerekezera moyo wako ndi wa anthuwo, kapenanso ungayambe kumasirira zimene anzako akuchita n’kumaona kuti ukumanidwa zinazake.”​—Phoebe.

Kodi mukudziwa? Ngakhale kuti kucheza pa intaneti kungakuthandizeni kulumikizana ndi anzanu, koma sikungafanane ndi kucheza nawo pamasom’pamaso. Dr. Nicholas Kardaras analemba kuti: “Tikamacheza ndi anthu pazipangizo zamakono sitimasangalala ngati mmene timasangalalira tikamacheza ndi anthu pamasom’pamaso. Sitingakhutire kuti tachezadi ndi mnzathu.”c

Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimamva kuti ndili ndekhandeka pambuyo poona zomwe anzanga akuchita?’ ‘Kodi ndimaona kuti moyo wanga ndi wobowa ndikayerekezera ndi zithunzi zimene anzanga amaika pamalo ochezera a pa intaneti?’ ‘Kodi ndimakhumudwa ngati anthu ochepa okha ndi amene alemba kuti akonda zomwe ndaika pamalo ochezera?’

Zimene mungachite. Yesani kupumira kaye kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kwa masiku, mawiki kapenanso mwezi. Wonjezerani nthawi yomwe mumacheza ndi anzanu pamasom’pamaso kapenanso kuwaimbira foni. Kenako muone ngati mwayamba kukhala ndi nkhawa zochepa komanso osangalala pa nthawi yomwe mwasiya kaye kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.

Zithunzi zosonyeza mtsikana. 1. Akuyang’ana zithunzi za anzake pafoni mokhumudwa. 2. Akucheza panja ndi anzake mosangalala uku akudya ice cream.

Kodi mungathe kuwonjezera nthawi yomwe mumacheza ndi anzanu pamasom’pamaso?

Pamene ndinkagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti ndinkangokhalira kuganizira zimene anthu ena akuchita. Koma nditadilita mapulogalamu amenewa ndinamva ngati ndatula chimtolo cholemera, kenako ndinkapeza nthawi yambiri yochitira zinthu zofunika kwambiri.”​—Briana.

Mfundo ya m’Baibulo: “Koma aliyense payekha ayese zochita zake kuti aone kuti ndi zotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi zimene akuchitazo, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”​—Agalatiya 6:4.

a Kuchokera m’buku lakuti, iGen.

b Kuchokera m’buku lakuti, Why Gender Matters.

c Kuchokera m’buku lakuti, Glow Kids.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Phoebe.

“Malo ochezera a pa intaneti ankandithera nthawi yambiri ndipo sankandithandiza kukhala wosangalala. Ndiye ndinasankha zosiya kuwagwiritsa ntchito. Kenako ndinazindikira kuti sindikumanidwa chilichonse. Panopa ndimasangalala kwambiri, ndimachita zinthu mokhazikika maganizo komanso mwaluso.”​—Phoebe.

Jacob.

“Nthawi zambiri ndimadilita kaye pulogalamu ya pa intaneti kuti ndisiye kaye kugwiritsa ntchito malo ochezera. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndizikumbukira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti n’kumathera nthawi pa zimenezo. Ndingagwiritse ntchito nthawi yanga m’njira zambiri zothandiza kusiyana n’kumangopita pamalo ochezera a pa intaneti popanda zifukwa zomveka.”​—Jacob.

Sienna.

“Nditha kudzayambiranso kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti m’tsogolo, koma panopa ndinasankha kusiya kaye. Ndikufuna kuti ndizithera nthawi yanga poganizira za moyo wanga, osati za moyo wa anthu ena.” N’zosavuta kuiwala zolinga zako komanso anzako enieni chifukwa cha malo ochezera a pa intaneti.”​—Sienna.

Mfundo zobwereza: Kodi malo ochezera a pa intaneti akundisokoneza pa moyo wanga?

  • Kodi zikumandivuta kupeza nthawi? Dziikireni malire a nthawi yomwe muzigwiritsa ntchito malo ochezera ndipo nthawiyo ikakwana muzisiya kuwagwiritsa ntchito.

  • Kodi ndikumalephera kugona? Muzisiya kuyang’ana pasikirini yapazipangizo zanu kudakali maola awiri musanakagone.

  • Kodi malo ochezera a pa intaneti akumandisokoneza maganizo? Muzisiya kaye kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti n’kumathera nthawi yambiri pocheza ndi anzanu pamasom’pamaso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena