Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 22
  • Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri
  • Nkhani Zina
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa chiyani anthu ena atopa ndi mliri?
  • N’chifukwa chiyani kutopa ndi mliri n’koopsa?
  • Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri?
  • Mavesi a m’Baibulo amene angakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri
  • Kodi Moyo Udzabwereranso Mwakale?—Mmene Baibulo Lingakuthandizireni M’nthawi ya Mliri
    Nkhani Zina
  • Thandizo la Zaumoyo—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?
    Nkhani Zina
  • Tizithandiza Mtsogoleri Wathu Yesu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kupereka Chithandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mliri
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
Onani Zambiri
Nkhani Zina
mrt nkhani 22
Bambo wakhala pampando atagwira makiyi a galimoto ndi chophimba kunkhope.

Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri

Kodi mwatopa chifukwa choyesetsa nthawi zonse kupewa mliri wa COVID-19? Ngati zili choncho, si inu nokha. Kwa miyezi yambiri, anthu padziko lonse anafunika kusintha zinthu pa moyo wawo chifukwa cha mliriwu. Hans Kluge, yemwe ndi dailekitala wa ku Europe wa Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse ananena kuti anthu ambiri “adzimana zinthu zambiri pofuna kuthandiza kuti mliri wa COVID-19 usafalikire. Zimenezi zingatitopetse komanso kutigwetsa ulesi.”

Ngati nanunso mwatopa ndi mmene mliriwu wasinthira zinthu pa moyo wanu, limbani mtima. Baibulo likuthandiza anthu ambiri kuti apirire nthawi yovutayi ndipo lingakuthandizeninso.

  • N’chifukwa chiyani anthu ena atopa ndi mliri?

  • N’chifukwa chiyani kutopa ndi mliri n’koopsa?

  • Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri?

  • Mavesi a m’Baibulo amene angakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri

N’chifukwa chiyani anthu ena atopa ndi mliri?

Anthu akafunika kusintha zinthu pa moyo wawo kwa nthawi yaitali chifukwa chofuna kupewa mliri, akhoza kutopa kwambiri. Kutopa ndi mliri kungakhudze anthu mosiyanasiyana koma anthu ambiri angakhale ndi zizindikiro izi:

  • Kusafuna kuchita chilichonse

  • Kuvutika kudya kapena kugona, apo ayi kudya kapena kugona kwambiri

  • kusachedwa kupsa mtima

  • Kuda nkhawa chifukwa cha ntchito zimene mumatha kugwira mosavuta

  • Kuvutika kuika maganizo pa zinthu

  • Kukhumudwa kwambiri mpaka kufika pomaona kuti zinthu sizingasinthe

N’chifukwa chiyani kutopa ndi mliri n’koopsa?

Kutopa ndi mliri kungaike moyo wanu komanso wa anthu ena pa ngozi. Zili choncho chifukwa kungachititse kuti musiye kutsatira malangizo otetezera ku COVID-19. Pang’ono ndi pang’ono, mungayambe kuona kuti mliriwu si woopsa ngakhale kuti ukufalikirabe komanso kupha anthu. Chifukwa chotopa ndi ziletso zimene zabwera ndi mliriwu, mungayambe kufuna ufulu wambiri. Ndipo zimenezi zingaike moyo wanu ndi wa anthu ena pa ngozi.

Pa nthawi yovutayi, anthu ambiri akuona umboni wa mawu a m’Baibulo akuti: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miyambo 24:10) M’Baibulo muli mfundo zimene zingatithandize kupirira mavuto monga mliri wa COVID-19.

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri?

  • Muzichezabe ndi anthu koma musamayandikane nawo

    Zimene Baibulo limanena: ‘Bwenzi lenileni linabadwira kuti likuthandize pakagwa mavuto.’—Miyambo 17:17.

    Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Anzathu enieni amatilimbikitsa. (1 Atesalonika 5:11) Koma tikhoza kudwala ngati timapewa anthu.—Miyambo 18:1.

    Tayesani izi: Pitirizani kucheza ndi anzanu pa vidiyokomfelensi, pa foni kapena polemberana mameseji. Muzicheza nawo pamene mukuvutika komanso muziona pafupipafupi ngati iwowo ali bwino. Muziuzana zimene zikukuthandizani kupirira pa nthawi ya mliriyi. Mukakhala wokhumudwa, muzipeza njira zochitira anzanu zinthu zabwino ndipo nanunso mudzasangalala.

    Zimene anthu ena ananena

    Meagan.

    “Ndimayesetsa kucheza pa vidiyokomfelensi ndi anzanga. Nthawi zina ndimachita zimenezi ndi mnzanga mmodzi basi. Koma nthawi zina, ndimasangalala kuchita masewera kapena kucheza ndi gulu la anthu. Zimandithandiza kwambiri ngakhale kuti si chimodzimodzi ndi kukumana nawo pamasom’pamaso. Tonse tikuvutika chifukwa cha mliriwu. Choncho kucheza ndi anzako n’kumawauza mmene ukumvera mumtima mwako n’kofunika kwambiri. Kuchita zimenezi kungakhale kovuta koma tonse timafunikira kuthandizidwa.”—Meagan, ku Canada

    Nathan ndi Emma limodzi ndi ana awo, Eli ndi Hope.

    “Tasowa kwambiri achibale komanso anzathu koma timapeza njira zowasonyezera kuti timawakonda. Monga banja, tinapanga makadi komanso mphatso zina n’kulembapo vesi lolimbikitsa kenako tinawapatsa kuti adziwe kuti tikuwaganizira. Tinasangalala kwambiri pochita zimenezi. Tikamachita zinthu zothandiza anthu ena timaiwala mavuto ndi nkhawa zathu.”—Emma limodzi ndi mwamuna wake, Nathan, ndi ana ake, Eli ndi Hope, ku United States.

  • Muzichita zimene mungathe

    Zimene Baibulo limanena: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:16.

    Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu kungakuthandizeni kuti muziona zinthu moyenera m’malo moda nkhawa kwambiri.—Luka 12:25.

    Tayesani izi: M’malo moganizira zimene simungathe kuchita, muziyesetsa kuona zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, kodi pali ntchito kapena zosangalatsa zimene panopa muli ndi nthawi yozichitira? Kapena kodi mungacheze kwambiri ndi am’banja lanu?

    Zimene anthu ena ananena

    Evan ndi Samantha limodzi ndi ana awo, Eli ndi Adam.

    “Takhala tikuchita ntchito zambiri zapakhomo ngati kudzala masamba osiyanasiyana komanso kukongoletsa nyumba yathu.”—Evan limodzi ndi mkazi wake, Samantha, ndi ana awo, Eli ndi Adam, ku South Africa.

    Ivan ndi Eve.

    “Ine ndi mkazi wanga takhala ndi nthawi yambiri yocheza kuposa nthawi ina iliyonse pa zaka zonse 30 zimene takhala m’banja. Zatithandiza kukondana kwambiri chifukwa chodziwana bwino zofooka komanso zabwino. Panopa takonzeka kuti tidzathe kuthandizana kwambiri tikadzakumana ndi mavuto ena.—Ivan limodzi ndi mkazi wake, Eve, ku Italy.

  • Muzikhala ndi ndandanda

    Zimene Baibulo limanena: “Zinthu zonse zizichitika . . . mwadongosolo.”—1 Akorinto 14:40.

    Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Anthu ambiri amakhala osangalala komanso amakhala ndi mtendere wamumtima akakhala ndi ndandanda yochitira zinthu.

    Tayesani izi: Mukhale ndi ndandanda yogwirizana ndi mmene zinthu zilili panopa pa moyo wanu. Muzikhala ndi nthawi yochitira ntchito zanu zakusukulu, ntchito zapakhomo komanso zinthu zauzimu. Muzikhalanso ndi nthawi yochezera ndi a m’banja lanu, masewera olimbitsa thupi komanso zinthu zina zosangalatsa zimene mungachite panja. Nthawi zina, muzionanso ndandanda yanu kuti muone ngati muyenera kuisintha.

    Zimene anthu ena ananena

    Kgaogelo.

    “Mliri utayamba, sindinasinthe kwenikweni zimene ndimachita tsiku ndi tsiku. N’zoona kuti ndimachita masewera olimbitsa thupi m’malo mwa zinthu zina zimene ndinkachita m’mbuyomu, koma ndimadzukabe nthawi yofanana ndi kale. Zimenezi zimandithandiza kuti ndiziganizira achibale ndi anzanga m’malo modandaula kwambiri chifukwa cha mliriwu.”—Kgaogelo, ku South Africa.

    Carmel.

    “Ndimakonda kudzuka n’kumapanga khofi ndi kuphika chakudya ngati mmene ndinkachitira mliri usanayambe. Kenako, ndimavala n’kupesa ngati kuti ndikupita kwinakwake. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizisangalala komanso kuti ndiziganiza bwino.”—Carmel, ku France.

  • Muzichita zinthu mogwirizana ndi mmene nyengo ilili

    Zimene Baibulo limanena: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.”—Miyambo 22:3.

    Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Malinga ndi kumene mumakhala, nthawi zina nyengo ingakhale yoipa kwambiri moti simungakhale padzuwa kapena kupuma mpweya wabwino mokwanira. Zimenezi zingakhudze thanzi komanso maganizo anu.

    Tayesani izi: Ngati nyengo yozizira ikuyamba, sinthani zinthu m’nyumba yanu kuti dzuwa lizilowa. Muziyesetsa kuchita zinthu zina panja ngakhale kuti kukuzizira. Ngati zingatheke, pezani zovala zotenthera kuti muzitha kuchita zinthu panja.

    Ngati nyengo yotentha yafika, anthu ambiri azichita zinthu panja. Choncho muziyesetsa kukhala otetezeka. Muzisankha bwino malo komanso nthawi imene mungapite kumaloko n’cholinga choti musamakumane ndi anthu ambiri.

    Zimene anthu ena ananena

    Sameena.

    “Kumene ndimakhala kumagwa mvula pafupipafupi. Choncho ndi bwino kukhala wokonzeka kusintha zimene ukufuna kuchita pa tsiku. Ndikangoona kuti kuli dzuwa, ndimayesetsa kupita panja kuti ndikayende kapena kukwera njinga. Kukhala pa dzuwa, ngakhale pa nthawi yochepa, kumandithandiza kukhala ndi maganizo abwino.—Sameena, ku France.

    Tiffany.

    “Sindinavutike kwenikweni m’nyengo yotentha chifukwa ndinkatha kuchita zinthu zambiri panja. Koma popeza nyengo yozizira ikubwera, ndikulemba ndandanda ya zinthu zimene ndingachite m’nyumba.”—Tiffany, ku Canada.

  • Pitirizani kutsatira malangizo otetezera ku mliri wa COVID-19

    Zimene Baibulo limanena: “Wopusa amapsa mtima ndiponso amakhala wodzidalira.”—Miyambo 14:16.

    Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Mliri wa COVID-19 ndi woopsa ndipo tikasiya kutsatira malangizo tikhoza kudwala.

    Tayesani izi: Nthawi ndi nthawi muziona malangizo amene akuperekedwa kwanu kuti muone ngati mukuwatsatira bwinobwino. Muziganizira mmene zochita zanu zingakhudzire inuyo, a m’banja lanu komanso ena.

    Zimene anthu ena ananena

    Daryn.

    “Ndikuchita zimene ndingathe kuti mliriwu usafalikire. Ngakhale kuti anthu ena amanyalanyaza malangizo, ndikuyesetsa kuchita zimene ndingathe kuti ndiziteteza ineyo komanso banja langa.”—Daryn, ku South Africa.

  • Muzilimbikitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu

    Zimene Baibulo limanena: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

    Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Mulungu angakuthandizeni kupirira vuto lililonse.—Yesaya 41:13.

    Tayesani izi: Muziwerenga mavesi ena a m’Baibulo tsiku lililonse. Njira yowerengera Baibulo imeneyi ingakuthandizeni kuti muyambe kuliwerenga tsiku ndi tsiku.

Mungachite bwino kufunsa a Mboni za Yehova kuti akuuzeni zimene akuchita kuti apitirize kusonkhana pamodzi ngakhale pa nthawi ya mliri wa COVID-19 imeneyi. Mwachitsanzo, padziko lonse ambiri akhala akugwiritsa vidiyokomfelensi kuti azipanga misonkhano yawo yampingo, mwambo wa pa chaka wokumbukira imfa ya Yesu komanso msonkhano wachigawo.

Zimene anthu ena ananena

Roberto.

“Ndakhala ndikugwiritsa ntchito nthawi yowonjezereka imene ndili nayo kuti ndiziwerenga Baibulo. Zimandithandiza kukhulupirira komanso kudalira kwambiri malonjezo a Yehova.a Ndimadziwa kuti zinthu zidzakhala bwino kwambiri m’tsogolo.”—Roberto, ku Italy.

Alta ndi Jannie.

“Ine ndi mwamuna wanga timawerenga limodzi Baibulo komanso kuloweza pamtima malemba. Kupemphera, kuwerenga Baibulo, komanso kuuza anthu ena malonjezo a m’Baibulo kumatipatsa mphamvu zotithandiza kupirira nthawi yovutayi.”—Alta limodzi ndi mwamuna wake, Jannie, ku South Africa.

a Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.—Salimo 83:18.

Mavesi a m’Baibulo amene angakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri

Yesaya 30:15: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”

Mfundo yake: Kukhulupirira malangizo a Mulungu kungatithandize kukhala ndi mtendere wamumtima pa nthawi ya mavuto.

Miyambo 15:15: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”

Mfundo yake: Kuganizira zinthu zabwino kungatithandize kukhala osangalala pa nthawi ya mavuto.

Miyambo 14:15: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”

Mfundo yake: Tizitsatira malangizo otetezera ku matenda ndipo tisafulumire kukhulupirira kuti malangizowo ndi osafunika.

Yesaya 33:24: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

Mfundo yake: Mulungu walonjeza kuti adzathetsa matenda onse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena