Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 25
  • Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?
  • Nkhani Zina
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi anthu angapulumutse dzikoli?
  • Tingayembekezere zinthu zabwino
  • Kodi Dzikoli Lidzatha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Anthu Apitiriza Kuwononga Dzikoli N’kufika Poti Silingakonzedwenso?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino
    Galamukani!—2023
  • Mphatso Yosatha Yochokera kwa Mlengi
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nkhani Zina
mrt nkhani 25
Mtsikana akuthirira duwa. Kumbuyo kwake, mafakitale akutulutsa mpweya woipa wowononga chilengedwe.

Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?

Anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa choti amaganiza kuti anthu akuwononga dzikoli komanso moyo wapadzikoli. Akatswiri ena a zachilengedwe amanena kuti zimene anthu akuchita panopa zikhoza kuwonongeratu mitundu ina ya zinyama ndi zitsamba.

Kodi n’zoona kuti anthu adzawononga dzikoli? Kapena kodi adzatha kukhala bwinobwino padzikoli popanda kuwononga zinthu?

Kodi anthu angapulumutse dzikoli?

Akatswiri ambiri amaona kuti anthu akhoza kuteteza dzikoli n’kumachita zinthu popanda kuliwononga. Koma akatswiri ena amanena kuti anthu ayenera kusintha zinthu zambiri pa nthawi imodzi kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino padzikoli. Zinthu zina zimene ziyenera kusinthidwa ndi izi:

  • Kusintha mmene timasamalirira nkhalango, madambo, nyanja ndi malo ena.

  • Kusintha njira zolimira komanso mmene timapangira mphamvu za magetsi ndi zina zotere.

  • Kuyamba kudya masamba ambiri n’kuchepetsa nyama ndi nsomba zimene timadya. Kuchepetsanso chakudya chimene timadya komanso kutaya.

  • Kuzindikira kuti kukhala ndi moyo wabwino sikudalira kukhala ndi zinthu zambiri

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi n’zotheka kuti maboma, mabizinezi komanso anthu onse azigwirizana posintha zinthuzi? Kapena kodi mukuganiza kuti makhalidwe oipa amene anthu amasonyeza monga dyera, kudzikonda komanso kusaganizira zam’tsogolo angalepheretse zimenezi?​—2 Timoteyo 3:1-5.

Tingayembekezere zinthu zabwino

Baibulo limalonjeza kuti dziko lathu silidzatha. Limafotokozanso kuti zimene anthu angachite sizingapulumutse dzikoli. Koma limafotokoza zinthu zimene ziyenera kusintha komanso mmene zinthuzi zidzasinthire.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene anthu angachite paokha sizingapulumutse dzikoli? Yehovaa Mulungu analenga dzikoli ndipo anapatsa anthu udindo wolisamalira. (Genesis 1:28; 2:15) Koma anthu akanatha kukwaniritsa udindowu pokhapokha ngati akanadalira Mulungu kuti aziwatsogolera komanso kumvera malangizo ake. (Miyambo 20:24) Koma anthu anakana kumvera Yehova ndipo anayamba kuchita zimene ankafuna. (Mlaliki 7:29) Paokha anthu sangasamalire dzikoli ndipo akayesetsa bwanji sangakwanitse kusinthiratu zinthu.​—Miyambo 21:30; Yeremiya 10:23.

Zinthu zimene ziyenera kusintha. Mulungu sadzalola kuti anthu awononge dzikoli. (Chivumbulutso 11:18) Iye sadzangokonza maboma ndi mabungwe amene akuwononga dzikoli koma adzawachotsa. (Chivumbulutso 21:1) N’chifukwa chake Yehova ananena kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”​—Chivumbulutso 21:5.

Mmene zinthuzi zidzasinthire. Yehova adzachotsa maboma a anthu n’kuika boma lakumwamba lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Boma limeneli lotsogoleredwa ndi Yesu Khristu lizidzalamulira dzikoli.​—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.

Ufumu wa Mulungu uzidzaphunzitsa anthu kuti azitsatira mfundo zachilungamo za Mulungu. Anthu akadzayamba kutsatira malangizo a Mulungu, adzatha kuchita zinthu mogwirizana ndi chilengedwe, osachiwononga. (Yesaya 11:9) Baibulo limafotokoza kuti boma la Mulungu lidzathandiza anthu ake kuti akhale ndi moyo wabwino kwambiri popanda kuwononga dzikoli. Lidzachita zinthu zotsatirazi:

  • Kupereka chakudya chokwanira anthu onse.​—Salimo 72:16.

  • Kubwezeretsa zinthu zimene zawonongedwa padzikoli.​—Yesaya 35:1, 2, 6, 7.

  • Kuonetsetsa kuti anthu azikhala mwamtendere ndi zinyama​—Yesaya 11:6-8; Hoseya 2:18.

  • Kuthetsa ngozi zachilengedwe.​—Maliko 4:37-41.

Tingayembekezere kuti Ufumu wa Mulungu udzachita zinthu zimenezi posachedwapa. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti ““Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?”

a Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.

Kodi tingachite chiyani panopa polemekeza dziko lathuli?

N’zoona kuti timadalira Ufumu wa Mulungu kuti udzathetseretu mavuto padzikoli. Koma panopa tingachite zinthu zina posonyeza kuti timalemekeza dzikoli. Mwachitsanzo, tingapewe kutaya zinthu zambiri komanso tingatsatire malamulo am’dera lathu okhudza mmene tingatayire zinthu.​—Yohane 6:12, 13; Aroma 13:1, 5.

  • Brett.

    Brett ankagwira ntchito yosamalira zachilengedwe koma pano anapuma pa ntchito. Zimene ankadziwa zokhudza chilengedwe zinamuthandiza kuzindikira kuti kuli Mlengi amene sadzalola kuti dzikoli liwonongedwe. Werengani nkhani yake.

  • Anthu awiri akuyang’ana nyumba ziwiri zimene zinali zitangomangidwa kumene ku Likulu Lapadziko Lonse la Mboni za Yehova.

    Njira imodzi imene a Mboni za Yehova amalemekeza Mlengi wawo ndi kumanga maofesi awo motsatira njira zimene sizingawononge chilengedwe. Kuti muone zimene amachita, onerani vidiyo yakuti Nyumba Zabwino Kwambiri Zimene Zimalemekeza Yehova.

Mavesi a m’Baibulo okhudza dziko lapansi

Genesis 2:15: “Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalira.”

Mfundo yake: Mulungu anapatsa anthu udindo wosamalira dziko lapansi.

Genesis 1:28: “Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire. Muyang’anirenso nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.’”

Mfundo yake: Anthu anapatsidwa udindo wosamalira nyama.

Yesaya 45:18: “Yehova, Mlengi wa kumwamba, Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, amene analikhazikitsa mwamphamvu, amene sanalilenge popanda cholinga, amene analiumba kuti anthu akhalemo, wanena kuti: ‘Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.’”

Mfundo yake: Cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi sichinasinthe. Anthu adzakhala padzikoli ndipo adzakwaniritsa zimene Mulungu ankafuna poyamba.

Salimo 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”

Mfundo yake: Anthu amene amatsatira mfundo zachilungamo za Mulungu adzakhala ndi mwayi wokhala padzikoli mpaka kalekale.

Salimo 98:6-8: “Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova, chifukwa wapambana. Nyanja ndi zonse zili mmenemo zichite mkokomo, Chimodzimodzinso mtunda ndi zonse zokhala kumeneko. Mitsinje iwombe m’manja, Mapiri onse afuule pamodzi mokondwera.”

Mfundo yake: Ulamuliro wa Mulungu udzathandiza kuti dzikoli likhale labwino kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena