Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 95
  • Kodi Ndine Wopirira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndine Wopirira?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi munthu wopirira amatani?
  • N’chifukwa chiyani kukhala wopirira n’kofunika?
  • Kodi mungatani kuti mukhale wopirira?
  • Muziwaphunzitsa Kukhala Opirira
    Galamukani!—2019
  • Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
    Galamukani!—2018
  • Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha
    Galamukani!—2016
  • Mmene Mungathandizire Ana Anu Akamalephera Zinazake
    Mfundo Zothandiza Mabanja
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 95
Poyamba wachinyamata akuoneka wokhumudwa koma kenako akuyamba kusangalala chifukwa choti wapirira.

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndine Wopirira?

Kodi ndinu wopirira? Kodi zinthu zotsatirazi zinakuchitikiranipo?

  • Imfa ya munthu amene mumam’konda.

  • Matenda okhalitsa.

  • Ngozi yadzidzidzi.

Ochita kafukufuku amanena kuti si mavuto aakulu okha amene amafunika kuwapirira. Ngakhale mavuto omwe mumakumana nawo tsiku ndi tsiku akhoza kuwononga thanzi lanu. N’chifukwa chake muyenera kukhala wopirira kaya mukukumana ndi mavuto aakulu kapena aang’ono.

  • Kodi munthu wopirira amatani?

  • N’chifukwa chiyani kukhala wopirira n’kofunika?

  • Kodi mungatani kuti mukhale wopirira?

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Kodi munthu wopirira amatani?

Munthu wopirira ndi amene amatha kuthana ndi mavuto amene akukumana nawo komanso savutika kwambiri zinthu zikasintha pa moyo wake. Ngakhale kuti amakumananso ndi mavuto ngati wina aliyense, amakhalabe olimba.

Zithunzi ziwiri zosonyeza mtengo wa kanjedza. 1. Wawerama chifukwa cha mphepo. 2. Wadzukanso mphepo itatha.

Mofanana ndi mtengo umene wapirira chimphepo champhamvu ndipo wadzukanso, inunso mukhoza kupirira mukakumana ndi mavuto

N’chifukwa chiyani kukhala wopirira n’kofunika?

  • Aliyense amakumana ndi mavuto. Baibulo limanena kuti: “Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, . . . ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.” (Mlaliki 9:11) Tikuphunzirapo chiyani? Anthu abwino nawonso amakumana ndi mavuto, ndipo nthawi zina osati chifukwa choti anachita zinazake zolakwika.

  • Kupirira kungakutetezeni. Mlangizi wapasukulu ina ya sekondale ananena kuti: “Ophunzira ambiri amabwera mu ofesi mwanga ali okhumudwa chifukwa choti sanakhoze bwino mayeso kapena chifukwa choti munthu wina wawanena pamalo ochezera a pa intaneti.” Ngakhale kuti zimenezi zingaoneke zazing’ono, koma ngati mwana wa sukulu sangakwanitse kuthana nazo, “akhoza kuyamba kuvutika maganizo.”a

  • Kupirira kungakuthandizeni panopa komanso mukadzakula. Dokotala wina dzina lake Richard Lerner anafotokoza za zinthu zokhumudwitsa zomwe timakumana nazo. Iye analemba kuti: “Ngati umakwanitsa kupirira mavuto amene wakumana nawo, kapena kupeza njira zina kuti ukwanitse kuchita zimene umafuna, sungadzavutike ukadzakula ndipo zinthu zimakuyendera bwino.”b

Kodi mungatani kuti mukhale wopirira?

  • Muziona mavuto anu moyenera. Muzitha kusiyanitsa pakati pa mavuto aakulu ndi mavuto aang’ono. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa, koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.” (Miyambo 12:16) Choncho si mavuto onse amene ayenera kukusowetsani mtendere.

    “Kusukulu, anzanga ambiri amakonda kudandaula pa zinthu zosafunika n’komwe. Ndiye anzawo akakawachemerera pa intaneti, amaganiza kuti akuchita bwino, m’malo moti aone zinthu moyenera n’kupeza njira yothetsera vutolo.”—Joanne.

  • Muziphunzira kuchokera kwa ena. Mwambi wina wa m’Baibulo umanena kuti: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.” (Miyambo 27:17) Mukhoza kuphunzira zambiri kuchokera kwa anthu amene anapirira atakumana ndi mavuto aakulu pamoyo wawo.

    “Mukamacheza ndi anthu ena, mukhoza kupeza kuti nawonso anakumanapo ndi mavuto ambiri, koma anakwanitsa kupirira. Muzicheza nawo n’kuona zimene anachita komanso zimene sanachite kuti apirire.”—Julia.

  • Muzikhala woleza mtima. Baibulo limanena kuti: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” (Miyambo 24:16) Mukakumana ndi mavuto, pamatenga nthawi kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino, choncho musamadabwe ngati nthawi zina mukumakhala wokhumudwa. Chofunika n’choti ‘mudzukenso.’

    “Mukathana ndi vuto linalake, pamatenga nthawi kuti muyambirenso kusangalala. Ndipo ndaona kuti nthawi ikamapita m’pamene zinthu zimayambanso kuyenda bwino.”—Andrea.

  • Muzikhala ndi mtima woyamikira. Baibulo limanena kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akolose 3:15) Ngakhale mutakhala kuti mukukumana ndi mavuto aakulu, pamakhala zinazake zabwino zomwe mukhoza kuziyamikira. Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zitatu zomwe muli nazo pa moyo wanu.

    “Ukamakumana ndi mavuto, umadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chani zimenezi zikundichitikira?’ Koma munthu wopirira safunika kumangoganizira za mavuto ake. Chofunika ndi kuona zinthu moyenera, kuyamikira zomwe uli nazo komanso zimene ungakwanitse kuchita.”—Samantha.

  • Muzikhala wokhutira. Mtumwi Paulo ananena kuti: “M’zochitika zosiyanasiyana ine ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo.” (Afilipi 4:11) Paulo analibe mphamvu zothetsera mavuto amene ankakumana nawo. Koma akanatha kudziwa zoyenera kuchita akakumana ndi mavutowo. Choncho iye anasankha kukhala wokhutira.

    “Ndaona kuti ndikakumana ndi vuto linalake ndimachita zinthu mopupuluma. Ndiye panopa cholinga changa n’choti ndiziona vuto lililonse moyenera. Zimenezi zizithandizanso ngakhale anthu ena.”—Matthew.

  • Muzipemphera. Baibulo limanena kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” (Salimo 55:22) Sikuti kupemphera kumangokuthandizani kuti mungomva bwino basi. Koma ndi njira yomwe mumagwiritsa ntchito polankhulana ndi Mlengi wanu, amene “amakuderani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.

    “Sindingathane ndi mavuto anga pandekha. Ndiye ndimapemphera kwa Mulungu n’kumuuza mavuto omwe ndikukumana nawo komanso kumuthokoza chifukwa cha zabwino zomwe wandichitira. Ndikamaganizira za madalitso omwe Yehova wandipatsa ndimasiya kuganizira kwambiri mavuto anga. Pemphero ndi lofunika kwambiri!”—Carlos.

Zimene achinyamata anzanu amanena

Sarahi.

“Popeza kuti ndife anthu opanda ungwiro, tsiku lililonse timalakwitsa zinthu. Zimenezi sitingazisinthe, ndiye chofunika ndi kupirira komanso kuphunzirapo kanthu pa zomwe talakwitsazo. Ndipo ngati tingadzakumanenso ndi vuto ngati lomwelo ulendo wina, sitingadzavutike kudziwa zoyenera kuchita kuti zinthu ziyende bwino.”—Sarahi.

Isabelle.

“Ndimakonda lemba la Mateyu 6:27, pomwe Yesu anafunsa kuti: ‘Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?’ Nthawi zina ndimaganizira kwambiri za mavuto omwe ndikhoza kukumana nawo, koma zimenezi zimangondiwonjezera nkhawa. Ndiye ndimangoyesetsa kuganizira zimene zikuchitika pa nthawiyo, chifukwa kudera nkhawa zinthu zomwe sindingazisinthe sikungandithandize.”—Isabelle.

Mfundo zobwereza: Kodi Ndine Wopirira?

  1. 1. Muziona mavuto anu moyenera. Muzitha kusiyanitsa pakati pa mavuto aang’ono ndi mavuto aakulu.

  2. 2. Muziphunzira kuchokera kwa ena. Muzicheza ndi makolo anu kapena munthu wina wamkulu wodalirika amene anakumanaponso ndi mavuto.

  3. 3. Muzikhala woleza mtima. Mukakumana ndi mavuto, pamatenga nthawi kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino, choncho musamadabwe ngati nthawi zina mukumakhala okhumudwa.

  4. 4. Muzikhala ndi mtima woyamikira. Ngakhale mutakumana ndi mavuto aakulu bwanji, pamakhala zinazake zabwino zomwe mukhoza kuziyamikira.

  5. 5. Muzikhala wokhutira. Sitingasankhe mavuto oti tikumane nawo, koma tikhoza kusankha zimene tingachite tikakumana ndi mavutowo.

  6. 6. Muzipemphera. Pemphero ndi njira yomwe mumagwiritsa ntchito polankhulana ndi Mlengi wanu, amene “amakuderani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.

a Kuchokera m’buku lakuti, Disconnected, lolembedwa ndi Thomas Kersting.

b Kuchokera m’buku lakuti, The Good Teen—Rescuing Adolescence From the Myths of the Storm and Stress Years.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena