AIDS ndi Makhalidwe
KODI nchiyani chomwe chinachitika m’ma-1960 ndi m’ma-1970 chimene chinatsogolera kukuulika kwa AIDS m’ma-1980? Kunali kuvomerezedwa kwa “mkhalidwe watsopano” wakuti chirichonse nchovomerezeka wa ufulu wa zakugonana. Pochitira ndemanga zimenezi mkonzi wa New York, Ray Kerrison analemba kuti:
“Kuulika kwa mwadzidzidzi kwa AIDS kungafulumizitsenso chitaganya ku kupendanso zofunika zake, zimene zakhala zikumanyentchera mwamsanga koposa galimoto yothamanga.
“Kwazaka zambiri, andale zadziko ndi mabwalo a mirandu akhala akumafalitsa chidziwitso chonama chowopsacho chakuti zochita zamtseri zochitidwa ndi nzika zamtseri siziri ndi kanthu ndi wina aliyense kusiyapo iwo eni.
“Mawu a mtundu umenewu mwachisawawa angathe kutchedwa kuti chiphunzitso cha chigwirizano. Kunena zowona, iwo amanena kuti, anthu awiri kapena oposa angachite monga momwe akufunira pokhapokha ngati sizidodometsa zoyenera za enawo.
“Chotero, ziletso zamakhalidwe abwino zonse motsatizanatsatizana zachotsedwa, zikumayambitsa funde la kudzisungira kolekerera ndi kuvomerezedwa kwa miyezo imene sinalingaliridwe konse zaka 30 zapitazo.
“Tsopano zotuta zomvetsa chisoni ziri pa ife.”
Ogonana ndi a ziwalo zofanana nawo ndiwo amene avutika mwapadera, ndipo zimenezi ziri chifukwa cha kugonana kwawo kosasankha mopambanitsa ndi mtundu wa machitachita a zakugonana ofala pakati pawo. Science Digest ikunena kuti: “Mapendedwe amodzi a CDC [Centers for Disease Control] anasonyeza avareji ya ogonana aŵiriaŵiri 1 100 mkati mwa moyo wa odwala nthenda ya AIDS ophunziridwa.”
Koma ogonana ndi aziwalo zofanana nawo sindiwo okha amene ali ogonana mosasankha—chitaganya chonse chatenganso kudzisungira kwakuti chirichonse nchoyenerera. Monga choturukapo, Harvey V. Fineberg, mkulu wowona za kudzisungira kwabwino wa ku Harvard School of Public Health, akunena kuti AIDS ikufalikira “mwapang’onopang’ono komabe mosapeweka m’chitaganya cha ogonana ndi aziwalo zosiyana.”
Makamaka, mu Afirika, nthendayo ikukantha chiwerengero cha anthu wamba. November wa chaka chatha, Lawrence K. Altman, mlembi wa zamankhwala wa The New York Times analemba kuti: “AIDS ikuwonekera kukhala ikumafalitsidwa ndi kugonana kwadzoma pakati pa anthu ogonana aziwalo zosiyana nawo m’Afirika ndipo ikukantha akazi pafupifupi ochuluka mofanana ndi amuna, malinga ndi kunena kwa ofufuza kunoku.”
Ngati mkazi agwidwa ndi AIDS kuchokera kwa mnzake wachimuna, iye sangadziwe konse kuti wayambukiridwa nayo. Mwachisoni, makanda obadwa kwa azimayi okhala ndi kachirombo ka AIDS nthawi zina amafikira kukhala mikhole yopanda liwongo. Ndipo amuna ogonana ndi akazi amene ali mahule angagwidwe ndi nthendayo.
Kulikonse anthu akuwopa. Kodi nchiyani chimene chidzachitika?
Kusintha m’Kudzisungira?
“Mosakaikira kudzathetsa mkuntho wa zakugonana,” akuneneratu motero Dr. Donald Francis wa pa CDC m’United States. Iye akunena kuti: “Inu mungathe kupewa nthenda yochita matuza ndi yotupa chiwindi B, koma simungathe kupewa kugwidwa ndi imeneyi.”
Dr. Walter R. Dowdle wa pa CDC akuwonjezera kuti: “Tiyenera kumvetsetsa kuti tonsefe tiyenera kusintha njira yathu ya moyo.” Mogwirizana ndi Dowdle, “limeneli sindilo funso la zamakhalidwe. Chiri chenicheni cha sayansi ya zamoyo.”
Chikhalirechobe, iri yoposa chenicheni cha sayansi ya zamoyo—makhalidwe abwino akuphatikizidwa. Miyezo yamakhalidwe abwino imene chitaganya chasankha kunyalanyaza siinayambidwe ndi anthu. Nzeru yapamwamba inaichititsa kuti ilembedwe kalekale. Ndipo kumzindikira kwathu monga Mfumu ndiko kumene kudzatithandiza kugwirizana nayo.
Koma kodi ndimiyezo yotani, kapena malamulo a kudzisungira, amene iye wapereka? Kodi ndimotani mmene kuwamvera kungatitetezerere?
[Bokosi patsamba 26]
Kuimika Kufalikira kwa AIDS
June Brown, polemba mu The Detroit News, anafotokoza mmene zimenezi ziliri zotheka: “Kuchiritsa kwachiwonekere kumene kungachepetse mofulumira mlingo wa chiwonjezeko ndiko kusintha mu zizolowezi za kugonana za mafuko. Ngati aliyense anasankha mnzake wogonana naye wathanzi labwino ndi kukhalabe wokhulupirika kufikira imfa, AIDS pafupifupi ikanazimilirika. Zimenezi zingamvekere mofanana ndi chiphunzitso Chabaibulo. Koma monga zatsopano, nthenda zopatsirana mwa kugonana zikupitirizabe kuwonekera, iriyonse ikumakhala yakupha koposa yoyambayo, chiphunzitso chaumulungu chonyalanyazidwa kwambiri ponena za kukhulupirika m’zakugonana mwadzidzidzi chimawonekera kukhala choyenerera mogwirizana ndi lingaliro lamakono la zathanzi.”