Kuchokera pa Kukangalikira Chinazi Kufikira pa Kukhala Woyang’anira Wachikristu
“TAMVERANI! Penyani bwino! Kagulu ka Achichepere ka Hitler, chigawo cha Böblingen, kakusimba.” Ha mmene ndinaimilira “anyamata anga” monyadilira nanga kwa akulu athu pa maphunziro oyeseza, mkati mwa perete, ndi pa zochitika zina. Kumvera kwawo ndi kulondola zinandichititsa chidwi. Ndinagwidwa mkuchita chidwi kwa nyengo yatsopano. Kuchiyambiyambi kwa ma-1930, panalibe chikaikiro chakuti tinaifunikira.
Jeremani anali atavutika kwambiri ndi ziyambukiro za pambuyo pake za Nkhondo Yadziko I, ndi zaka zambiri za kusakhazikika ndi magawano andale zadziko. Ulova unakula mofulumira. Panthawiyo, ndinali kugwirira ntchito wosoka pa Stuttgart, yemwe anali kundilipira ndalama zokwanira Mamarks anayi pamlungu umodzi, pafupifupi yokwanira chakudya chofisula ndi chakudya chamadzi chamasana. Ndipo mkhalidwe wangawo sunali wachilendo. Sikodabwitsa kuti Jeremani anali kuvutika ndi kusakhazikika kwa zinthu. Mtsogolo munawonekera kukhala mopanda chiyembekezo kwambiri.
Ndipo kenako “iye” anadza! Potsirizira, mwamuna yemwe anadziwa zomwe anali kuchita! Ndithudi, sialiyense yemwe anavomerezana naye, koma palibe aliyense yemwe akanakhoza kukana kuti iye anatsogoza ndi ulamuliro ndi kuti anapeza zoturukapo. Mkhalidwe wachuma unawongokera; ulova unali utachepa. Palibe aliyense yemwe anali kumva njala. Zinthu zinali kuwongokera. Ichi chinali chipambano, ndipo chinadzetsa thamo ku zimene ananena.
Kupereka Chichirikizo Chachangu
Ndinabadwa ndi kuleredwera m’Holzgerlingen, mudzi waung’ono kunja chapafupi ndi Stuttgart, Jeremani. Ndinali chiwalo cha kagulu kathu ka zamasewera kamomwemo, ndipo pamene ochuluka a ziwalo zake anafikira kukhala ochilikiza Hitler, ndinagwirizana nawo. Ndiiko komwe, iye anandichititsa chidwi, ndipo mwayi wa kukhala ndi phande m’kuwongolera mikhalidwe unali wokopa.
Pamene Hitler anatenga ulamuliro mu 1933—ndinali wausinkhu wa zaka 24 panthawiyo—ndinali kale chiwalo cha Chipani cha Nazi. Powona changu changa, mabwenzi anga mwamsanga anali kunena kuti: “Willi, ungathe kukhala wabwino kutenga ntchito iyi kapena iyo.” Chotero pafupifupi m’nthawi yochepa, ndinatenga malo athayo osiyanasiyana asanu ndi amodzi m’chipanicho. Ndinaulingalira kukhala ulemu.
Mwachitsanzo, ndinaikidwa pamalo a kutsogolera ma-Brownshirts athu a mchitaganyacho—monga momwe timagulu ta chipani chathu tinali kutchedwera. Zimenezi pambuyo pake zinatsogolera ku kuikidwa kwanga pa kukhala woyang’anira Anyamata a Hitler okwanira 2 000. Ha mmene kunaliri kochititsa nthumanzi nanga kutumikira ndi mtima wonse m’chipani choyenda mofulumira chimene maprogramu ake aliyense anali wotsimikiza kupindula nawo! Changu changa chinali chachikulu kufikira pa kukhala wokangalika mopambanitsa. Tsoka kwa aliyense yemwe anali wolimba mtima kutsutsa malingaliro anga!
Chotero taganizirani, ngati mungathe, kuchititsidwa kwanga nthumanzi pamene ndinagawiridwa kukafika pamadyerero a ku Stuttgart kumene Führer iyemwiniyo akakhalapo. Ha mmene chinaliri chochitika chachikulu nanga! Amuna okhala m’magulu ndi Anyamata a Hitler Achinazi okwanira 70 000 ataima m’mizeremizere atavala yunifomu yodera, akumayenda mofanana ndi makina amodzi. Ndiyeno panali pachimake pamene, patsogolo pa khamu lalikuru limeneli, ndinapatsidwa mwayi wa kukagwira m’manja “mwake” mwenimweni!
Kulekeka kwa Ntchito Imene Inali Kuyenda Bwino
Martha ndi ine tinakwatirana mu 1932. Ha mmene ndinaliri wachimwemwe kukhala ndi mnzanga yemwe anali ndi phande mzochita zanga! Zonse zinayenda bwino kufikira pamene iye anayamba kusagwirizana ndi zinthu zimene ndinkachita. Wina wake anali ataipitsa zinthu, ndipo sikunali kovuta kuzindikira yemwe anali atatero—Mina, mlamu wanga. Iye anali atafikira kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo sanaleke kuuza mlongo wake zonse zonena za “chowonadi chopezedwa chatsopano” chakecho. Mosakaikira zimenezi sizinandiyendere bwino ineyo, Mnazi.
Unansi wathu waukwati unafikira kukhala wovuta kwambiri. Mwachitsanzo, ndikukumbukira, pamene ndinabwerera kunyumba kuchokera ku msonkhano m’Stuttgart, nditachititsidwa nthumanzi kwambiri pokhala nditagwira m’manja Führer. Martha anangomwetulira ndi kunena kuti: “Kodi zimenezi zitanthauza kuti simudzasambanso m’manja mwanu?” Zimenezo zinandikhumudwitsa. Kodi angasekerenji ulemu wotero, mwayi wotero? Kodi iye sanamvetsetse?
Kaŵirikaŵiri ndinadzipeza kukhala ndikumamkalipira, koma iye ankachita mwabata, zimene zinkandikwiyitsa koposa ndi kalelonse. Poyang’anizana ndi mkwiyo ndi kuchitiridwa molakwa, kodi nkuti kumene anapeza nyonga yamkati yochitira mwanjirayo? Kamodzi ndinamthamangitsiradi kunja kwa nyumba. Zimenezo, ndithudi, sizinawongolere nkhanizo, ndipo sindinathe kugona usiku wonse. Tsiku lotsatira, mosasamala kanthu za kunyada kwanga kovulazidwako, ndinambweretsanso panyumba. Kudzisungira kwake kunapitirizabe monga poyamba—kukhala wopanda liwongo.
Kodi kungakhale kwakuti ine, osati iye, ndine amene ndinali wolakwa? Ngakhale lingalirolo linali lomvetsa chisoni. Eya, kukanatanthauza kutha kwa malingaliro angaanga, kutha kwa dziko langa.
Maora Atatu Omwe Anasintha Moyo Wanga
Tsiku lina ndinabwerera kunyumba kuchokera ku masewera ozolowezetsa magulu a anyamata nditadwala ndi malungo. Ndinapita kukagona nindinapeza Baibulo la mkazi wanga litaikidwa pambali pa bedi pa thebulo. Zimenezo zinali zachilendo chifukwa chakuti iye anadziwa kuti kunali kwachiwonekere kuti ndikanalitentha ndi moto mkukhala kwanga wachangu mokangalika. Ngakhale kuti ndinalingalira kukhala wolemekezeka kwambiri kosakhoza kutero, kaamba ka chifukwa chakutichakuti ndinatenga Baibulolo nindinayamba kuliwerenga. Pamenepo, m’Chivumbulutso 17 ndi 18, ndinawona pamene panali kunena za mkazi wachigololo wamkulu wotchedwa Babulo Wamkulu. Liwulo linali lozolowereka chifukwa chakuti ndinali nditamva Martha akumaligwiritsira ntchito pasadakhale, koma ndinali wonyada kwambiri kosakhoza kufunsa kuti andifotokozere. Tsopano pafupifupi ndinadziwa kumene linachokera. Koma sindinadziwebe zimene linatanthauza.
Potsimikiza kuti ndidziwe, ndinamtenga mchipinda china. Iye anawonekera kukhala wamantha kundiwona nditagwira Baibulo lake, akumawopera chitetezo chake. Pokhalabe wonyada kosakhoza kumvetsera kwa mkazi wa ine mwini, ndinafunsa mokakamiza kuti: “Kodi ungakanditengere Mina kotero kuti adzandifotokozere amene Babulo ameneyu ali?”
Mlongo wakeyo angakhale atalingalira bwino lomwe kuti unali msampha umene ukanatsogolera ku kubindikiritsidwa kumsasa wachibalo. Mosasamala kanthu za zimenezo, akumalimba mtima kuthetsa mantha aliwonse amene angakhale anali nawo, anadza. Ndipo tinalankhulana. Tinalankhula kwa maora atatu, maora atatu amene kwenikweni anasintha moyo wanga.
Ndinaleredwera m’Chiprotestante ndipo ndinali kufika ku tchalitchi mwakamodzikamodzi. Koma ine sindinali kwenikweni wopembedza. Komabe, tsopano, ndinayamba kuzindikira kuti zimene Baibulo linanena ponena za Babulo Wamkulu mowonadi zinali kufotokoza kophiphiritsira matchalitchi. Mwapang’onopang’ono ndinayamba kuzindikira mmene anthu ndi mitundu anakhalira mikhole ya “vinyo wa . . . chigololo chake” ndi mmene “mafumu adziko [anali atachitira] naye chigololo.” (Chivumbulutso 18:3) Ndipo zimenezi zinaphatikizapo ngakhale Jeremani Wachinazi!
Pamene Mina anafotokoza mowonjezereka, ndipamenenso ndinkatha kumvetsetsa bwinopo mawu a Baibulo ndi kugwira kwawo ntchito kwamakono. Kodi ndimotani mmene zonsezi zikanakhalira zitaloseredwa zaka mazana ambiri pasadakhale? Zinandilimbikitsa kwambiri. Tsopano ndinadziwa mmene mtumwi Paulo ayenera kukhala atalingalirira—eya, ichi chinali chowonadi! (Machitidwe 9:1-19) Sizinanditengere nthawi yaitali kuti ndifikire chosankha.
Patsiku lotsatira, ndiri chidwalirebe ndi malungo, ndinadzuka nindinapita kukatula pansi umembalashipi wanga ponse paŵiri kuchipanicho ndi kutchalitchi. Ndithudi, zimenezi zinaphatikizapo, kuleka maudindo onse asanu ndi umodzi athayo m’Chipani cha Nazi. Linali sitepe losonyeza kulimba mtima kwambiri lolitenga chifukwa chakuti Anazi anali kulamulira kotheratu, ndipo chirichonse chimene sichinali choyenerera m’ziphunzitso zawo chinali kuperetsedwa mopanda chifundo kuti chisakhalepo. Ndipo ndinali ndi chifukwa chabwino chodziwira izi, pakuti kodi inemwinine kufikira patsopano sindinali wochilikiza wachangu wa mchitidwe umenewowo? Kodi tsopano nchiyani chimene chikanachitikira ntchito yanga? Kodi nchiyani chimene chikanandichitikira?
Mayeso a Umphumphu
Milungu itatu yokha pambuyo pooti ndadzipangitsa inemwini kukhala wapamwamba koposa onse ndi yemwe anali kukambidwa za iye m’mudzimo, Martha ndi ine tinasangalala ndi kubadwa kwa mwana wathu woyamba. Koma chisangalalo chathu chinali chakanthawi; zothetsa nzeru zinalowerera, ndipo mwanayo anafa milungu iŵiri pambuyo pake. Moyo wa Martha unali wosalongosoka kwa masabata ena owonjezereka. Kodi chimenechi chinali chilango chochokera kwa Mulungu? Ena angakhale atalingalira motero, koma ife sitinatero. Zinatibwezeretsa pafupi ndi Yehova, Mulungu wachikondi, yemwe analola Martha kuchira ndi yemwe analimbikitsa chikhulupiriro chathu m’chiukiriro, akumatipatsa chiyembekezo champhamvu chodzawona Esther wachichepereyo kachiŵiri.
Pakali pano, anthu a m’mudzi wamomwemo, ngakhale makasitomala anga okhulupirika koposa kwanthawi yaitali, anayamba kutsutsa sitolo yanga yosokera. Koma iwo anadziwa kuti nthawi zonse ndinawatumikira bwino, ndinali wowona mtima, ndipo ndinali nditachita ntchito yabwino. Chotero pambuyo pa milungu yowerengeka, kutsutsako kunayamba kutha. Makasitomala anayamba kubwerera, ngakhale kuti ena ankatero usiku kotero kuti asawonedwe ndi ena. Pasanapite nthawi yaitali, bizinesi langa linayamba kuchita bwinopo ngakhale koposa poyamba!
Panthawi ndi nthawi tinalandira mabukhu a Mboni, omwe tinaŵaŵerenga mofulumira ndiyeno nkuwapatsira ena mwamsanga. Koma popeza kuti mabukhu amenewa anali ataletsedwa, tinayenderedwanso ndi Agestapo kwanthawi ndi nthawi ali ndi cholinga cha kudzapeza ena a iwo mnyumba mwathu. Magulu aŵiri a Agestapo anafika mosayembekezereka masana ena pafupifupi pa ora lachiŵiri. Ndi panthawi yonse yodzafika! Tsiku limodzi lokha zimenezo zisanakhale, tinali titalandira kabukhu koti ndidzapatsire ena madzulo amenewo. Iwo anayamba kufufuza kwawo, koma kenako mwadzidzidzi anatembenuka ndi kupita, osawona chomwe chinali chitaikidwa pamwamba pa wailesi pafupifupi pamaso pawo penipeni—kabukhuko!
Ife nthawi zonse tinali muupandu wa kumangidwa. “Willi, kodi ukudziwa zimene ukuchita? Uyenera kukhala ukupenga” ndizo zimene mkulu wamomwemo Wachinazi anandiuza pamene ndinachoka m’chipanicho. Koma popeza kuti mbale wake anakwatira mmodzi wa alamu anga, zomangira zabanja mwachiwonekere zinamletsa kuti asandipereke. Ena mu tawunimo amene anandidziwa bwino lomwe, omwe anazindikira kuwona mtima kwanga ndi amene anandilemekeza, anawonekera kukhala pafupifupi atafika pa kuchita chinyengo mwakachetechete.
Sindidzaiwala konse chotchedwa kuti matsankho aufulu a mu 1935. Chifukwa cha kukhulupirika ku Ufumu wa Yehova, tinakhalabe achete, tikumakana kuphatikizidwa m’ndale zadziko. Madzulo amenewo pafupifupi paora lachisanu ndi chitatu, kagulu ka Anazi okwanira 80 kanaguba chakutsogolo kwa nyumba yathu, kakumafuula madzulowo kuti onse amve mwakumati: “Awo okhala muno ali apereki ku mtundu wa Jeremani. Jeremani alibe malo kaamba ka anthu onga inu. Muyenera kunyongedwa. Pitani kwa Mdyerekezi monga momwe Yudase anachitira!”
Monga yemwe kale anali Mnazi, sindinasangalale kutchedwa kukhala mpereki. Koma zimene Yesu anali atanena: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.” (Yohane 15:18) Chotero udani umenewu unangotsimikizira kokha kuti tinali kuchita bwino. Ochuluka a magulu amenewa pambuyo pake anathetsa miyoyo yawo mchochitikacho. Komabe, aŵiri amene anali chikhalirebe amoyo pambuyo pa nkhondoyo, anadza mwachindunji kudzapempha chikhululukiro kaamba ka zimene anali atachita.
Kugalamutsidwira ku Zochita
Mwamsanga pamene chidodometso chaboma Lachinazi chinali kutha, Mboni za Yehova kuzungulira Jeremani yense zinayamba kulinganizidwanso. Ndakhala ndi moyo kuwona kagulu kathu kakang’ono m’Holzgerlingen kakumakula kuchokera kwa okwanira asanu ndi mmodzi okha panthawiyo kufikira pa oposa zana limodzi lerolino. Ndipo ha mmene chakhalira chisangalalo nanga kukhala nditawona anthu okwanira 28 akumatenga ntchito yolalikira mothandizidwa ndi banja lathu lokha.
Kwazaka pafupifupi 40 tsopano, ndasangalala ndi kukwaniritsa mathayo a kuyang’anira mpingo. Mwachiwonekere osati m’mawu olamulira ndi ouma khosi a mtsogoleri Wachinazi amene ndinkagwiritsira ntchito, koma mumzimu wa kutumikira wachikondi ndi chifatso wofunikira abusa aang’ono Achikristu.—Mateyu 23:10, 11; 1 Petro 5:2, 3.
Kuyambira pa October wa 1934, pamene ndinadziyeretsa inemwini kusiyana ndi Chinazi ndi Babulo Wamkulu, papita zaka zoposa makumi asanu. Zaka zambiri pambuyo pake, ndinadzaphunzira kuti m’mwezi weniweniwo mipingo ya Mboni za Yehova kuzungulira padziko lapansi inatumizira Hitler uthenga wapalamya, umene unawerengedwa kuti: “Kuchitira nkhanza kwako Mboni za Yehova kukuipira anthu onse abwino a padziko lapansi ndipo kumaluluzitsa dzina la Mulungu. Uleke kupitirizabe kumazunza Mboni za Yehova; apo phuluzi Mulungu adzawononga iwe ndi chipani chako cha mtundu wonsewo.” Ndinakhala ndi moyo kuwona mawu amenewo akumakwaniritsidwa.
Ha mmene ndiliri wosangalala nanga kukhala nditawona manenanena okopa onyenga Achinazi ndi mawu awo adzoma munthawi yake! Chotero ndinadzipewetsa ku manyazi a kugawanamo m’machimo ake ndipo pambuyo pake ululu wa kulandira mbali ya miliri yake, monga momwe ambiri a mabwenzi anga akalewo anachitira.—Monga momwe yasimbidwira ndi Willi Wanner.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
Kawirikawiri ndinadzipeza kukhala ndikumakalipira mkazi wanga, koma iye nthawi zonse ankachita mwabata
[Chithunzi patsamba 28]
Mabwezi a kalabu ya zamasewera mu 1928, omwe anali kale Achinazi. Wachichepereyo pamwamba kulamanzere ndi ine (patsogolo chapakati) tinadzakhala Mboni za Yehova
[Chithunzi patsamba 31]
Willi Wanner, mkazi wake Martha, ndi mlongo wake Wilhelmine