Kupeza Gulu Lankhondo Labwino
MUNALI MU 1944, mkati mwa nkhondo ya dziko yachiŵiri. Monga wandende wa Chigerman wosungidwa ndi Allies, lingaliro langa la kuthaŵa linakula kufikira litakhala lingaliro loipa. Palibe china chirichonse chimene chinandidetsa nkhaŵa. Ichi ndi chifukwa chake andende anzanga 13 ndi ine tinangotenga tsoka kuchoka mu sitima lothamanga mwaliwiro pafupi ndi malire a Spanish Morocco.
Modabwitsa, pambali pa kukhuluzika kwakukulu, tonsefe tinapulumuka. Komabe, ufulu wathu unali wa nthaŵi yochepa. Masiku anayi pambuyo pake tinagwiridwanso ndi apolisi a ku Arabia ofufuza anthu othawa. Koma chilakolako cha kufuna ufulu chinapitirizabe kumakula. Chikatenga koposa thupi lokhuluzidwa, kuchititsidwa manyazi kwa kugwidwanso, ndi chilango chowawa kuchikankhira pambali.
Miyezi inapitapo, ndipo tinali andende mu Casablanca. Lingaliro linanso lakuthawa. Nthaŵiyi tinangotenga vuto la kukumba msima wa mapazi 65 (20 m). Chinatenga miyezi itatu ya kuvutika kopweteka msana, koma potsirizira pake usiku wa kuthawa unafika. Kachiŵirinso, tonsefe tinakhoza!
Panalinso chisangalalo cha ufulu wa pa kanthaŵi kochepa, koma tinagwidwanso masiku ochepa pambuyo pake. Panthaŵiyi chilango chathu chinali cholekanitsidwa mu ndende zapadera ndi kugwira ntchito ya kalavula gaga kwa mwezi umodzi. Pambuyo pake tinamasulidwa kupita ku msasa wa ndende wa nthaŵi zonse.
Ndinali kokha wa zaka 19, ndipo zokumana nazo zimenezo zinasiya kawonedwe kosatha. Panthaŵiyo ndinali wotsimikiza kuti ndinali m’gulu lankhondo labwino, limene linapanga kuyesayesa konse kuwonekera kukhala kophulapo kanthu.
Kuphunzitsidwa Koyambirira
Ndinabadwa mu September 1925, pafupi ndi Bremen, cha kumpoto kwa Germany. Atate wanga anali katswiri wosewera m’mpira, kusambira, ndi wothamanga pa madzi oundana, chotero ndinakula wokhala ndi chikondwerero cha changu cha masewera. Koma ndinakondanso kuŵerenga. Makolo anga ankapita ku tchalitchi kokha pa Krisimasi, kukapezeka ku maliro, kapena panthaŵi zina zapadera. Pamene ndinapita ku tchalitchi, ndinakhala wodabwitsidwa kuwona mmene anthu ochulukira anagona mkati mwa kupereka uthenga kwa mbusa.
Pamene ndinakula, ndinaŵerenga nkhani zochita ndi masewera ndipo ndinakhala wokondweretsedwa kuphunzira ponena za maiko ena. Ndikumbukira kuŵerenga bukhu ponena za Torres Strait—kutalika kwakukulu kwa nyanja pakati pa Papua New Guinea ndi Australia. Mtundawu, umene uli mbali yosangalatsa ya dziko lapansi unandikondweretsa ine, ndipo ndinali ndi ziyembekezo zolakalaka kuti tsiku lina ndikakhoza kuchezera malo akutali amenewa.
Tinali ndi bukhu la nazonse, ndipo mu ilo ndinaŵerenga ponena za zipembedzo zambiri za dziko ndi milungu yawo yosiyanasiyana. Ndinadabwitsidwa panthaŵi zina ngati kuti pakati pa zonsezi panalidi Mulungu wowona. Kupyolera m’makalata, Atate nthaŵi zonse ankalandira kapepala kotchedwa Der Stürmer. Ndinasangalatsidwa ndi dzina losakhala lanthaŵi zonse lakuti Yehova logwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri m’mawu ake ogwidwa kuchokera mu Baibulo. Atate analongosola kuti iri linali dzina la Mulungu wa Ayuda. Ndinali nditaŵerengapo ponena za milungu yambiri yakale, yonga ngati Odin, Thor, ndi Frigga, ndiponso ndi milungu ya Chihindu Siva, Vishnu, ndi Brahma, koma ndinali ndisanakumanepo ndi dzina lakuti Yehova ndi kale lonse.
Kulawa Koyamba kwa Umoyo wa mu Gulu la Nkhondo
Mwakukulira pansi pa ulamuliro wa Chinazi, ndinadzakhala mbali ya gulu la Achichepere la Hitler. Podzafika 1939 Nkhondo ya Dziko II inali itayamba, ndipo ngakhale kuti ndinali wa zaka 14, ndinaphunzitsidwa za mkhalidwe wa nkhondo. M’kupita kwanthaŵi, kumenya nkhondo kwa m’mlengalenga kunadzakhala njira ya moyo. Panthaŵi imodzi, ndinadzutsidwa mwadzidzidzi pamene bomba la moto linagwa kupyola pa denga lathu, kudzagwera pafupi ndi kama yanga. Ndinalizima ilo ndi matumba a mchenga ndipo mwanjirayo ndinapulumutsa nyumba yathu.
Mu 1943 ndinagwirizana ndi asilikari olumpha mu ndege ndipo ndinatumizidwa ku France kaamba ka kuphunzitsidwa. Pambuyo pa kuphunzitsidwa kwakukulu ndinatumizidwa ku maiko apatsogolo ku Nettuno ndi Anzio mu Italy. Mwendo wanga unalasidwa ndi chipolopolo, ndipo ndinaikidwa mu chipatala kwa milungu isanu ndi umodzi pa Bologna. Ndinabwereranso ku ntchito wachangu ndipo mosapita nthaŵi pambuyo pake ndinatengedwanso wandende pafupi ndi Siena, Italy.
Panali pamene ndinatengedwa ndi sitima ku French Morocco pomwe anzanga 13 ndi ine tinapanga makonzedwe athu oyamba akuthawa. Pambuyo pogwidwanso tinatengedwa ku ndende ya chibalo cha ankhondo mu mapiri a High Atlas pafupi ndi Sahara Desert. Kumeneko ndinaphunzira mmene amapangira njerwa kuchokera ku nthaka ndi zinthu zosanganizidwa ndi madzi. Pambuyo pake tinasinthidwira ku ndende ya ku Casablanca. Kunali kumeneko kumene tinapanga makonzedwe athu akuthawa achiŵiri mwakukumba msima.
Malo Achilendo a Chifrench
Ngakhale kuti nkhondo inatha mu 1945, tinasungidwa monga andende mu Morocco. Mu 1947 tinaperekedwa ku France, kumene ndinakhala wandende kufikira 1948. Ntchito yanga yoyamba pambuyo pa kumasulidwa inali ya kudula mitengo mu Pyrenees. Komabe pambuyo pake, mu 1950, ndinagwirizana ndi French Foreign Legion kumenyera molimbana ndi chikomyunizimu. Poyamba ndinatumizidwa ku Sidi-bel-Abbès mu Algeria ndiyeno pambuyo pake ku Phillipy kukakhala msilikari wolumpha mu ndege mu gulu lankhondo la Chifrench.
Potsatira ndinatumizidwa kukamenya nkhondo mu Indochina. Kumeneko ndinapwetekedwa mu kulalira kumene kokha aŵiri a ife tinathawa amoyo. Panthaŵiyi ndinaikidwa mu chipatala mu Hanoi kwa milungu isanu ndi umodzi. Pambuyo pa kuchira, ndinabwezedwanso kukamenya nkhondo mu nkhalango ndi m’minda ya mpunga. Zonse pamodzi, ndinapanga kulumpha 20 monga msilikari wolumpha mu ndege.
Potsirizira pake ndinadwala ndi nthenda ya chikasu kotero kuti odziŵa za mankhwala a gulu lankhondo anavutika ndi moyo wanga. Ndinakhala bwino koma ndinanenedwa kukhala wosayenera kaamba ka ntchito yamphamvu. Komabe sindinapatsidwe kumasulidwa kolemekezeka. Mwamwaŵi, ndinali pafupi kupita kutchuthi chachitali, chotero ndinapempha kubwerera ku North Africa.
Pamene ndinali kumeneko, ndinakonza kaamba ka kuthawa kwina koma panthaŵiyi ndinali ndekha. Ndinazindikira kuti pa chifupifupi 100 omwe anathawa, 99 anagwidwanso. Chotero makonzedwe anga anali abwino. Ndinatha kufika ku Port Lyautey ndi kupeza sitima yonyamula anthu ya Chigerman. Mwamsanga pamene ndinali pa nyanja zazikulu ndi ulendo woloza ku Germany, ndinachinjirizidwa.
Kubwerera ku Germany, ndinali wogwirizana mwachimwemwe ndi banja langa pambuyo pa kukhala kutali kwa zaka khumi. M’nzanga wakale wa pa sukulu anakonza kaamba ka ine kuti ndigwirizane ndi mbali ya German ya gulu la nkhondo la Chibritish, kuchipangitsa icho kukhala gulu lankhondo lachitatu limene ndakhala ndi kukhalamo. Ndinali kulandira ndalama zabwino koma ndinakula wotopa mowonjezereka ndi umoyo wa mu gulu lankhondo.
Moyo Watsopano mu Dziko Latsopano
Mwaŵi wa kupita ku Canada kapena Australia unandibwerera. Ndinasankha Australia, ndipo mu June 1955 ndinafika mu Sydney, mzinda waukulu wa New South Wales. Ndinaphunzira kuti ntchito inaliko pa large hydroelectric irrigation scheme mu Snowy Mountains chifupifupi mamailosi 300 (480 km) Kumwera cha kumadzulo kwa Sydney. Ndinadziŵa kuti iyi ikakhala ntchito yoyipa, komabe malipiro anali abwino, ndipo ndinamva kuti kunali anthu a Chigerman ambiri kumeneko ndi ogwira ntchito ochokera ku Europe pa ntchitoyo.
Chiyambire nkhondo sindinalingalirepo kwambiri ponena za chipembedzo. Kuchokera pa chimene ndinawona mkati mwa nkhondo, ndinanyengedwa ndi icho. Sindinamvepo ponena za Mboni za Yehova, koma mmodzi wa ogwira nawo ntchito amene anati anali Mboni anakamba kwa ine kaŵirikaŵiri ponena za chochiritsa cha mikhalidwe ya dziko, ndipo chimene anakamba chinapanga nzeru kwambiri. Komabe, mwamsanga pambuyo pake iye anabwerera ku Sydney, ndipo ndinasowa kugwirizananso naye.
Panthaŵiyi ndinakumana ndi kukwatira Christa. Ndinauza mkazi wanga ponena za zinthu zimene Mboni inandiuza ine, ndipo iye, nayenso, anakonda zimene anamva. Chotero pa ulendo wopita ku Sydney, ndinakakumananso naye. Ngakhale kuti nayenso anali m’German, iye ankakhoza kuwerenga ndi kulankhula Chingelezi bwino lomwe ndipo anatipatsa bukhu la m’Chingelezi, Kuchokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezedwanso. Popeza kuti tonse Christa ndi ine tinali tikali kuphunzirabe Chingelezi, sitinakhoze kumvetsetsa chirichonse chimene bukhulo linanena, ngakhale kuti tinamvetsetsa zambiri kuchokera mu zithunzi.
Pamene Mboni inatiuza kuti bukhulo linaliko mu Chigerman, kothera kwa mlungu wina pamene mvula inali kugwa tinafulumira kupita ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ya mu Australia pa Strathfield. Kumeneko tinatenga bukhu mu Chigerman, ndi kuliŵerenga ilo lonse mu usiku umodzi. Tinabwerera ndi kukapezeka ku msonkhano pa Nyumba ya Ufumu ya pa Strathfield. Aliyense anali wa chibwenzi kwambiri, ndipo chinawoneka kwa ife kukhala chibwenzi chowona, osati chakungopanga. Tinachoka ku msonkhanowu okhala ndi mipukutu yambiri ya magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiponso ndi mabukhu ena mu chinenero cha Chigerman.
Ndimapitirizabe ndi Kusamala
Ngakhale kuti zimene tinkaphunzira zinawoneka kukhala zabwino, ndinali wosamala ponena za kudziyika inemwini mu njira iriyonse. Ichi chinali mwapambali chifukwa cha chokumana nacho cha amayi wanga ndi chipembedzo cholinganizidwa. Mu 1936 iwo anachoka ku chipembedzo cha Lutheran chifukwa chakuti anagwiritsidwa mwala ndi zinthu zimene anamva ndi kuwona zikuchitidwa. Komabe sanasiye chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndipo nthaŵi zina ankalankhula kwa ine ponena za icho.
Ndiyeno pamene ndinagwirizana ndi gulu la nkhondo mu 1943, tonsefe tinapita ku tchalitchi ndi kumvetsera kwa ansembe akupereka nkhani. Iye anatitsimikizira ife kuti ngati tikanaphedwa mu kumenyana, tikapita kumwamba mwamsanga kukagwirizana ndi anzathu a mu nthaŵi za kumbuyo. Pambuyo pake, mu migula ndi m’migodi ya nkhandwe, ndinawona kuti asilikari ambiri anavala mitanda kaamba ka chitetezero. Bwenzi langa linali lovala chimodzicho pamene iye anamenyedwa ndi kuphedwa pafupifupi ndi ine. Pambuyo pakuchira kuchoka ku chozizwitsacho, lingaliro langa loyamba linali lakuti: ‘Kodi mtanda wake unachitanji kwa iye?’
Ndinali wodabwitsidwa pamene ndinawona andende a nkhondo a Chingelezi nawonso ovala mitandayo. Ndinalingalira kuti: ‘Ngati ichi chinali Chikristu, ndiye kuti palibe chipembedzo Chachikristu chirichonse kwa ine.’ Nkulekelanji, popeza kuti amuna odzitcha kukhala Akristu anali kumbali zonse ziŵiri—kuphana wina ndi mnzake!
Nthaŵi yotsatira ndinawona wansembe, ndinamufunsa ponena za ichi. Iye anati pamene nkhondo ikumenyedwa, uyenera kumenyera kaamba ka dziko lako, koma nkhondo itatha, onse afunikira kubwerera ku matchalitchi a iwo eni. Ichi chinali chokwanira kwa ine! ‘Pali china chake cholakwika kwambiri,’ ndinalingalira. Tsopano ndinamvetsetsa chifukwa chimene amayi wanga anachokera ku tchalitchi.
Chotero ndinali wosamala momvetsetsa. Komabe mwamsanga ndinadzakhutiritsidwa kuti uthenga wa Baibulo ponena za chowonadi unali wosiyana. Chinyengo cha zipembedzo zolinganizidwa sichinali chimene Baibulo linaphunzitsa. Tsopano ndinakhoza kuwona chifukwa chimene panali kusokonezeka koteroko ndi matsoka pa dziko lapansi. Ndipo ndinasangalatsidwa kuphunzira potsiriza pake amene Yehova ali. Iye ali Mulungu wowona wa onse, osati kokha wa Ayuda monga mmene atate ananenera.
Ndiponso, ndinaphunzira mmene Yesu Kristu analingira. Iye ali Mwana wokondedwa wa Yehova, ndipo Yehova anamutuma iye ku dziko lapansi kudzatisonyeza ife chimene tingachite ndi kupereka dipo kotero kuti tingathe kupeza moyo wosatha. Ndinadzapeza kuti Ufumu wa Mulungu udzapanga dziko lapansi kukhala paradaiso ndipo, chomwe chiri choposa, chiri chakuti adzakhala kosatha.
Gulu Lankhondo Labwino Potsirizira Pake!
Mwamsanga tinazindikira kuti kuti tipezeke ku misonkhano Yachikristu mokhazikika, kukhala kwathu mu misasa kwa kothera kwa milungu kukafunikira kulekedwa, kapena kungochotsedwapo. Vuto lina limene ndinali nalo linali kusuta kokulira. Kwa zaka 16 ndakhala ndikusuta ndudu 40 kufika ku 60 pa tsiku limodzi, ndiponso ndi ndudu ya pakanthaŵi ndi kaliwo. Pamene chinasonyezedwa kwa ine kuti kuipitsa koteroko kwa thupi la munthu sikumamkondweretsa Mulungu, ndinasiya chizoloŵezi choipacho m’tsiku limodzi.
Mu February 1963 Christa ndi ine tinadzisonyezera ndi ubatizo wa m’madzi kudzipereka kwathu kwa Yehova. Mwamsanga pambuyo pake tinayamba utumiki wa nthaŵi zonse monga apainiya, ndipo mu January 1965 tinasankhidwa monga apainiya apadera. Tsopano ndinali msilikari mu “gulu lankhondo” Lachikristu la Yehova.
Mu 1967 tinapita ku Papua New Guinea, kumene tinatumikira poyamba mu Port Moresby ndipo pambuyo pake ku Poppendetta. Tinabwerera ku Australia kwanthaŵi yochepa ndiyeno mu 1970 tinabwerera ku Papua New Guinea, kumene tinatumikira mpaka September 1981. M’kupatsidwa kwa gawo kwathu kumodzi, tinathandizira kumanga Nyumba za Ufumu ziŵiri ndipo tinathandiza ambiri kuphunzira chowonadi cha Baibulo. Tinayenda ndi bwato ku malo ambiri—tikugwiritsira ntchito magalimoto opanda denga. Mu zaka zitatu ndi theka, anthu 29 omwe tinathandiza anabatizidwa.
Tonsefe tinagwidwa ndi malungo owopsya. Ndinakomoka kwa maora 48 ndipo sindinayembekezeredwe kukhalanso ndi moyo. Potsirizira pake, mu 1981, tinagamulapo za kubwerera ku Australia, kumene tinapitiriza monga apainiya apadera mu Brisbane ndipo pambuyo pake mu Cairns, kumpoto kwa Queensland. Kupatsidwa gawo kwathu kwa posachedwapa kuli pa Thursday Island, mu Torres Strait, kokha chakumbali kwa kumpoto kwenikweni kwa dziko lalikulu la Australia. Kuli ku malo akutaliwo kumene ndinakhala ndikuŵerenga ponena za iko pamene ndinali kokha wachichepere, osakhulupirira kwenikweni kuti ndikakhoza kufikako.
Kuyang’ana m’mbuyo kwa zaka zathu zoposa 23 za kuchita upainiya, sitiri achisoni ponena za kuphatikizidwa mu “gulu lankhondo” limeneli. Mitima yathu imasangalala kudziŵa kuti takhala okhoza kuthandiza anthu chifupifupi 60 kupereka miyoyo yawo kwa Yehova Mulungu. Timapeza chimwemwe chambiri mu ntchito yathu ya kulalikira ya nthaŵi zonse ndipo timalimbikitsa ena nthaŵi zonse kutenga ntchito yodalitsikayi.
Ndimayamika Yehova mopitirizabe, pambuyo pa kutumikira mu magulu a nkhondo a maiko atatu, okhala ndi kugwiritsa mwala kwambiri ndi kukhala pafupi ndi kufa kosiyanasiyana, ndinakhala wokhoza kuphatikizidwa mu gulu lake lankhondo logonjetsa monga msilikari wa Kristu Yesu. (2 Timoteo 2:3) Inde, potsirizira pake ndinapeza gulu lankhondo labwino ndipo ndimapemphera kuti ndipitirizebe kutumikira monga msilikari wokhulupirika ku nthaŵi zosatha.—Monga momwe kwanenedwera ndi Siegmar Soostmeyer.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Ndinadzutsidwa mwadzidzidzi pamene bomba la moto linagwa kupyola pa denga lathu
[Mawu Otsindika patsamba 13]
Amuna odzinenera kukhala Akristu anali kumbali zonse ziŵiri—kuphana wina ndi mnzake!
[Chithunzi patsamba 11]
Pamene ndinatumikira m’Malo Achilendo a Chifrench