Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 10/8 tsamba 14-15
  • Kodi Kukhulupirira Malaulo Kuli Kosavulaza?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kukhulupirira Malaulo Kuli Kosavulaza?
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kosavulaza kapena Kovulaza?
  • Kovulaza—Mu Mkhalidwe Wotani?
  • Zikhulupiriro—N’chifukwa Chiyani Zidakalipobe?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Mumakhulupirira Malodza pa Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Zikhulupiriro za Makolo N’zogwirizana ndi Baibulo?
    Galamukani!—2008
  • Yehova Amafuna Kuti Mukhale Otetezeka
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 10/8 tsamba 14-15

Lingaliro Labaibulo

Kodi Kukhulupirira Malaulo Kuli Kosavulaza?

PAMENE gulu la ophunzira za maganizo linayedzamitsa chikwerero kukhoma mu khwalala lotanganitsidwa la ku London, anthu opita mu njira anapanikizidwa: kukhala pambali pake ndi kupita pansi pa chikwerero, kapena kuchokapo pambali pake ndi kupewa kupitapo. Opita mu njira asanu ndi aŵiri mwa anthu khumi alionse anachipewa chikwererocho.

Ndithudi, anthu ambiri, atadidikizidwa, amavomereza kutembenukira ku kukhulupirira malaulo kumodzi kapena kuŵiri. Bwanji ponena za inu? Kodi nthaŵi zina mumadzimva kusonkhezeredwa kwa kufuna kugunda nkhuni, kupingasa zala zanu, kapena kupikisa mchere pamwamba pa phewa lanu la kumanzere? Ndipo ngati ndi tero, kodi munayambapo mwaima ndi kuganizira chifukwa ninji?

Kukhulupirira malaulo sikukuwonedwa monga kowopsya ndi ambiri. Monga mmene mkonzi Robertson Davies akulongosolera: “Maphunziro a maganizo aumwini, zouluka zosazindikirika, kuchiritsa kozizwitsa, kulingalira kwa kuya kwa mapangidwe a maganizo . . . ziri zoletsedwa, koma kukhulupirira malaulo kwangochitiridwa kokha chisoni.”

Ena amawona kukhulupirira malaulo monga kosakhala kwenikweni, kosawopsya nkomwe. “Tiyeni tikuwone iko mwakungokulekerera ndi kusangalala,” latero bukhu limodzi ponena za kukhulupirira malaulo. Anthu ambiri amatero. Iwo amalingalira kuti, ‘Ngati sikuchita chabwino, ndiko kuti kuli kosavulaza nkomwe.’ Koma kodi kuli tero?

Kosavulaza kapena Kovulaza?

“Mkhalidwe sumakhalapo popanda tanthauzo,” watero Dr. Alan Dundes, mphunzitsi wa mwambo wa pa yuniversite. “Anthu sangagwiritsire ntchito miyambo kusiyapo kokha ngati iwo atanthauza chinthu china chake ku malingaliro.” Zikhulupiriro za kukhulupirira malaulo zimenezi, akutero ofufuza, ziri osati china koma “zenera ku malingaliro.” Chotero nchifukwa ninji sitingatsegule “zeneralo” ndi kuwona zifukwa zimene ziri kumbuyo kwake?

Wodziŵa za maganizo Edward Hornick wanena kuti “kuwopa mizimu kuli chimodzi cha zochirikiza za moyo.” Koma kodi simuvomereza kuti mtengo wa chochirikiza, kapena chothandizira, umadalira pa mtundu wa maziko umene chiri nawo? Mwachitsanzo, mpando pansi pa kichini yanu yolimba umakhala pa maziko abwino, osavulaza. Koma kodi mungakhale pa mpandowo ngati ukanaikidwa pa mchenga wa m’madzi? Ndithudi ayi.

Nsonga yosiyanitsa imodzimodziyo ingagwirenso ntchito ku kukhulupirira malaulo, “kuchirikiza kwabwino kwamoyo.” Kodi maziko ake nchiyani? Kodi kwazikidwa pa maziko olimba a ziphunzitso za Baibulo kapena, mwinamwake, pa malingaliro a chipembedzo onga mchenga wa m’madzi?

‘Zimenezo zikumvekera kukhala zosamveka,’ inu mungalingalire. ‘Sindikuwona mmene kupewa chikwerero, kugunda nkhuni, kapena miyambo yoteroyo ingakhale ndi china chirichonse chochita ndi zikhulupiriro za chipembedzo.’ Komabe, pali kugwirizana. Tengani kukhulupirira malaulo kwa chikwerero monga chitsanzo.

Nthaŵi zina chimakhala chanzeru kuyenda mozungulira chikwerero kuti tipewe chinachake chomwe chagwa pansi, komabe kodi sichowona kuti ngakhale pamene chikwerero sichibweretsa ngozi iriyonse, anthu ena amachipewa icho kaamba ka kufuna kupewa “matsoka”? Koma kodi mwambowo wazikidwa pati? Chabwino, chikwerero choyedzekedwa ku khoma chimapanga chinthu cha ngodya zitatu. “Ndipo chinthu cha ngodya zitatu,” yalongosola tero Encyclopædia of Superstitions, “chakhala nthaŵi zonse chophiphiritsira Utatu.” Chotero, kuyenda pansi pa chikwerero kunafikira kukhala kuipsya Utatu, kulowerera kopanda lamulo m’malo oyera, ndipo kumeneko, kwadziŵitsa tero kulozera kumodzimodziko, kukakhala “kusewera m’manja a Woipa.” Komabe, kodi Utatu uli chiphunzitso chamaziko cha mu Baibulo?

Mosiyanako, kuphunzitsa kwa Utatu kunayambira mu zipembedzo zakale za chikunja. Mawu a Mulungu, ngakhale ndi tero, amatsutsa lingaliro la Utatu. Iwo amati Yehova ali wamkulu pa Kristu. (Yohane 14:28; 1 Akorinto 11:3) Chotero, kukhulupirira malaulo kwa chikwerero kwazikidwa pa malingaliro onama a chipembedzo. Chimodzimodzinso ndi kukhulupirira malaulo kwa kupikisa mchere pamwamba pa phewa lanu la kumanzere.

Mchere, wosungitsa zakudya, unadzaphiphiritsira moyo ndi mwayi wabwino. Ngati mwaupikisa iwo, molingana ndi kukhulupirira malaulo, inu muyenera kutonthoza mtima Mdyerekezi ndi ziwanda. Ndipo popeza kuti iwo amakhala nthaŵi zonse kumanzere kwanu, mbali ya manzere (sinister liri liwu la Chilatin la “kumbali ya kumanzere”), inu mufunikira kupikisa ungapo pamwamba pa phewa lanu la kumanzere. Kodi kutonthoza mtima sikumatanthauza kupanga kuvomereza? Inde, ndipo chimenecho chimabwera m’chigwirizano ndi kuchenjeza kwa Malemba kwakuti: “Kanizani Mdyerekezi,” “ndiponso musampatse malo Mdyerekezi,” ndi “imani nji molimbana ndi . . . Mdyerekezi.” (Yakobo 4:7; Aefeso 4:27; 6:11, NW) Chotero, kukhulupirira malaulo kumeneku kwazikidwanso pa zikhulupiriro zosiyana ndi Baibulo.

Kovulaza—Mu Mkhalidwe Wotani?

‘Zimenezo zingakhale zowona, koma pamene ndipewa chikwerero kapena kupikisa mchere sindikuganiza ponena za Utatu kapena Mdyerekezi, ndipo sindikuwalemekeza nkomwe iwo,’ inu mungatsutse tero. ‘Chiri kokha chizoloŵezi. Kodi chingandivulaze motani?’ Mwa njirayi: Ngati inu mudziŵa kuti miyambo ina ya kukhulupirira malaulo iri yozikidwa pa bodza, koma inu mupitirizabe kugwiritsira ntchito miyambo yoteroyo, mwakutero inu muli ngati munthu amene amadziŵa kuti mpando wake uli pa mchenga wa m’madzi koma amene anena kuti: ‘Ine sindidzangoganizira ponena za mchenga wa madziwu, chotero siudzandivulaza,’ ndipo mwakutero akhala pampando. (Chivumbulutso 22:15) Iye ali mu ngozi, ndipo inu mungakhalenso tero. Chifukwa ninji?

Inu mungayambe kudalira mopitirizabe pa kukhulupirira malaulo, ndipo musanachidziŵe icho, iko kungayambe kulamulira moyo wanu. Ndipo popeza kuti kukhulupirira malaulo kwazikidwa pa bodza, inu pambuyo pa kuyambukiridwa, mungakhale, kapolo wa “atate wabodza,” Satana. (Yohane 8:44) Chimenecho, pambuyo pake, chingatsogolere ku ukapolo wa kugwiritsira ntchito kwina kozikidwa pa bodza—kukhulupirira mizimu.

Zowona, pa kawonedwe koyambirira kukhulupirira malaulo kumawonekera kukhala kosavulaza nkomwe, koma kupatseni iko kawonedwe kena kabwino ndipo mudzazindikira chimene ndithudi iko kuli—mochepetsetsa kopanda pake ndipo kwakukulukulu kovulaza.

[Bokosi patsamba 14]

“Kumbukirani, kachiŵirinso, kuti kukhulupirira malaulo kumatsanulira kwa munthu wosakula chodzikhululukira cha kupatsa mlandu mphamvu zina zomposa iye kaamba ka matsoka ake.”—Superstitious? Here’s Why!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena