Kuchokera kwa Aŵerengi Athu
Kupita Patsogolo kwa za Mano
NDINAIKIDWA msomali wa mazinga wa mawonekedwe onga fupa m’mano anga, kachitidwe kolongosoledwa mu nkhani yakuti “Kupita Patsogolo Kokulira mu Zamano,” kodziŵika monga kubzyalidwa kwa chitsulo chofewa mu mafupa momwe munazulidwa mano. (November 22, 1986, Chingelezi) Ine ndikuti, Musakuchite iko. Katswiri amene anandifufuza ine mu 1985 ananena kuti kachitidweka kali kutalitali ndi ubwino, ndipo kuti pakhale kupewa kucholowanacholowana kowopsya, kafunikira kugwiritsiridwa ntchito kokha kwa anthu omwe ali aumoyo wabwino mwakuthupi ndi mwamalingaliro. Magazini a zamankhwala afunikiranso kulola odwala omwe akhala ndi zokumana nazo zoipa kudzilongosolera iwo eni.
C. L., Federal Republic of Germany
Pamakhala kufunika nthaŵi zonse kwakusamala pamene mugwiritsira ntchito zinthu zachilendo ziri zonse mu thupi lanu, ndipo padzakhala maperesenti angapo akulephera. Nkhani yathu inakamba ponena za kugwiritsira ntchito zitsulo zofewa. Kulingana ndi kuphunzira kwina kwa zaka 20, njira imeneyi yakhala ndi mlingo wa kukhoza wa chifupifupi maperesenti 90. Osati kokha kuti zitsulo zofewa zakhala ziri kugwiritsiridwa ntchito koma zateronso vitreous carbon (galasi), sapphire, ndi ceramic. Pamene kuli kwakuti sitikuyamikira mankhwala aliwonse mwachindunji, ife tinafalitsa chidziŵitsocho kaamba ka phindu la aŵerengi athu. Chiri chabwino kupatsa kulingalira kosamalitsa ku ziyambukiro za pambali zothekera musanavomereze mankhwala aliwonse.—ED.
Kungosemphana?
Ndinasangalala ndi nkhani yanu yakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndani Akuti Kuli Kungosemphana?” (January 8, 1987, Chingelezi) Inadandaulira anthu achichepere komabe inachenjeza kuti kuganizira malingaliro oipa kuli kolakwa. Ndinali ndinasemphana ndi wina wake pa nkhani za pa wailesi ya kanema. Usiku wosagona ndi zoganizira zofika patali zonsezo zinalipo. Koma choipitsitsa chinali pamene ndinamlembera mkaziyo ndiyeno ndinalandira chithunzithunzi chongotsanzira! Ndinalingalira kuti ndinamkonda. Sindingayembekeze kaamba ka nkhani yanu yotsatira.
W. H., England
Onani kope lathu la January 22, 1987.—ED.
Chigwetsa Ntsamiro Wochedwa Usiku
Ndinayamikira kwenikweni kukambapo kwanu mu “Kumaliyang’ana Dziko” pansi pa mutu wakuti “Chizoloŵezi Chovulaza.” (January 8, 1987, Chingelezi) Iyo inalongosola kuti chigwetsa ntsamiro wakudza mochedwa usiku angakhale wovulaza, makamaka ngati munthu mobwerezabwereza amapita kukagona ora limodzi kapena kuposapo pambuyo pakudya. Vuto langa linali lakukhala ndi kusokonezeka kwenikweni kwa kugona usiku chifukwa cha kusagayidwa kwa zakudya mu thupi. Ndakhala kaŵirikaŵiri ndikulingalira kuti, ‘Kodi mchitidwe wa vuto la kugona kwanga ungakhale wochititsidwa ndi kudya chigwetsa ntsamiro usiku?’ Chabwino, pambuyo pa kuŵerenga nkhani yanu, ndinasintha malingaliro anga kusadya chigwetsa ntsamiro chirichonse pambuyo pa chakudya changa cha madzulo. Kuyambira pamenepo, ndakhala ndikupeza tulo tabwino usiku uliwonse, ndipo kwakhala phindu lowonjezereka: Ndataya mapaundi oŵerengeka osafunika.
M. G., United States
Nkhwazi Yokongola?
M’kope lanu la November 22, 1986, Chingelezi, munafalitsa nkhani yokhala ndi mutu wakuti “‘Wotsomphola’ Akhalira ku Dzina Lake.” Chithunzithunzi pa tsamba 20 la nkhaniyi, chimene chinaperekedwa ndi Zoological Society of San Diego, sichiri Nkhwazi Yokongola. Iyo iri Nkhwazi ya ku Guiana yokhala ndi Tsumba. Nkhwazi Yokongola iri nkhwazi yaikulu padziko lonse, ndipo mwaichititsa manyazi mwakusonyeza chithunzithunzi cha mbalame yokhala ndi miyendo yitali yowonda, yakudya njoka.
N. R., United States
Talandira zotsatirazi kuchokera ku Zoological Society of San Diego: “Ndiri wachisoni kusimba kuti chithunzithunzi chomwe munaika kukhala Nkhwazi Yokongola chiri ndithudi Nkhwazi yokhala ndi Tsumba, Morphnus yokhala ku guiana. Mwachiwonekere, mbalame ziŵirizi ziri zofanana kwenikweni m’mawonekedwe . . . Chimatenga diso loyang’anitsitsa kwenikweni kulongosola kusiyana kwake . . . [Ife] tikupepesa kaamba ka kusazindikiritsa bwino. Timapanga kuyesayesa kokulira kuzindikiritsa bwino lomwe zithunzithunzi zathu ndipo timachiyamikira chitabweretsedwa ku chisamaliro chathu ngati pali kukaikira kuli konse.”—ED.