Bongo Wodabwitsa Umenewo wa Khanda!
ALI odabwitsa kungoyambira pachiyambi pawo penipeni. Milungu itatu pambuyo pokhala ndi pakati, amayamba ndi maselo 125,000 ndipo pambuyo pake amawonjezeka mu unyinji wa maselo 250,000 pamphindi imodzi. Bongo laling’ono lirilonse limapitiriza ndi kutukuka kwa kukula kwake kufikira pa kubadwa pamene maselo ake amafikira chiŵerengero cha 100,000,000,000—unyinji monga mmene ziriri nyenyezi mu Mlalang’amba!
Koma miyezi ingapo chisanachitike chimenecho, pamene lidakali m’mimba, bongo la khanda limayamba ntchito. Ilo likusonkhanitsa mphamvu za kuzindikira kuchokera ku malo ake ozungulira a madzi okhaokha. Ilo limamva, kulawa, limazindikira kuwunika, limayankha ku kugwiridwa, limaphunzira, ndi kukumbukira. Malingaliro a mayi wake angaliyambukire ilo. Mawu okhazikika kapena nyimbo zopanda phokoso zimalimvetsa bwino ilo. Kalankhulidwe kaukali kapena nyimbo zarock zimalikalipitsa ilo. Phokoso la kugunda kwa mtima wa mayi wake kumalitonthoza ilo. Koma ngati mantha awiritsa mtima wawo, mwamsanga mtima wa khanda umagunda mofulumira kuŵirikiza kaŵiri. Mayi wonyansidwa amayambukitsa kudera nkhaŵa ku khanda limene liri m’mimba mwake. Mayi wa mtendere amanyamula khanda la mtendere. Mayi wosangalala angapangitse khanda m’mimba mwake kulumpha kaamba ka chisangalalo. Zonsezi ndi zowonjezereka zimasunga bongo la khanda kukhala lotanganitsidwa. Ngakhale m’mimba limakhala lodabwitsa.
Kodi mitsempha yaikulu ya bongo yowonjezereka imapangidwa pambuyo pa kubadwa? Kufufuza kwa posachedwapa kumati ayi. Mosakaikira, ngakhale kuli tero, mitsempha yaikulu ya bongo imapitirizabe kukula kwadzawoneni m’mlingo, pamene ipanga matriliyoni a kugwirizanitsidwa kwatsopano ku ina ndi inzake. Bongo la khanda pa kubadwa limakhala kokha mbali imodzi mwa zisanu mu ukulu kulinganizidwa ndi wa achikulire, koma umadzaŵirikiza katatu m’mlingo mkati mwa chaka chake choyamba. Ilo limafikira kulemera kwa la achikulire kwa mapaundi atatu (1.4 kg) zaka zingapo isanafike mu zaka zaunyamata. Icho sichimatanthauza kuti limakhala ndi chidziŵitso cha achikulire. Chidziŵitso sichimalinganizidwa ndi kulemera kwa bongo kapena chiŵerengo cha maselo ake. Mosiyanako, chimawoneka kukhala chogwirizanitsidwa ku chiŵerengero ndithudi cha kulumikizidwa, chotchedwa popitira mphamvu za kuzindikira (synapses), zomwe zimapangidwa pakati pa mitsempha yaikulu ya bongo.
Ndipo chiŵerengero chimenecho chiri chodabwitsa! Kuzizwitsa kwa kulumikizanitsidwa kwa quadriliyoni imodzi potsirizira pake kungapangidwe—uko ndiko kuti 1 wotsatiridwa ndi mazero 15! Koma kokha ngati bongo lasonkhezeredwa molemerera bwino ndi zolowetsedwamo kuchokera ku kuzindikira kusanu kapena koposerapo. Malo ozungulira ayenera kusonkhezera zonse ziŵiri mphamvu za maganizo ndi za malingaliro, popeza kuti izo ndi zimene zimapanga cholowanecholowane wabwino wa kukula kwa timitsempha tabongo tolandira zizindikiro (Dendrites). Timitsempha tabongo tolandira zizindikiro (Dendrites) tili tinthu tating’ono tonga mizu tomwe timafikira kuchokera ku mitsempha yaikulu ya bongo ndi kukalumikiza ku mitsempha ina yaikulu ya bongo (neurons).
Palinso kupenda nthaŵi kolowetsedwamo m’kupanga kulumikizanitsidwa kumeneku: Izo zimapangidwa mofulumira kwambiri kwa achichepere kuposa kwa achikulire. Mwambi wakuti, “Simungaphunzitse galu wakale maluso atsopano,” siuli wowona. ‘Koma chiri chovuta kuphunzitsa galu wakale maluso atsopano.’ Kwa achikulire, kulumikizanitsidwa pakati pa mitsempha yaikulu ya bongo (neurons) kumapangidwa mochedwa ndipo kumatha mwamsanga. Mtengo wa kupangidwa kwawo uli chimodzimodzi monga mmene uliri mu khanda—kuvumbulidwa ku malo ozungulira olemerera, ndi osonkhezera. Malingaliro afunikira kupitirizabe kukhala achangu! Palibe kutopa konga kutha kwa maganizo! Palibe kuleka kwa kugwira ntchito kwa malingaliro!
Koma kukula kumene kuli kodabwitsa kuli mu bongo wa ana. Kuli monga chinkhupule chomwe chimagwira zomwe ziri pamalo ochizungulira! Mu zaka ziŵiri khanda limaphunzira chinenero chovuta, kokha mwakungowunikiridwa ku icho. Ngati ilo limamvetsera ku zinenero ziŵiri, ilo limaziphunzira zonsezo. Ngati zitatu zikulankhulidwa, ilo limaphunzira zitatu zonsezo. Mwamuna wina anaphunzitsa ana ake achichepere zinenero zisanu zonse panthaŵi imodzi—chiJapanese, chiItalian, chiGerman, chiFrench, ndi Chingelezi. Mkazi wina anawunikira mwana wake wamkazi ku zinenero zosiyanasiyana, ndipo podzafika nthaŵi pamene mwanayo anali ndi zaka zisanu, iye anali wokhoza kulankhula zinenero zisanu ndi zitatu bwino lomwe. Kuphunzira zinenero kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kwa achikulire koma kwa makanda zimangobwera kokha mwachibadwa.
Chinenero chiri kokha chitsanzo chimodzi cha mphamvu zomwe mwachibadwa zimakonzekeretsedwa mu bongo la khanda. Mphamvu za kuyimba nyimbo ndi luso la kudziŵa zinthu, kugwirizanitsa mphamvu, kufunika kwa tanthauzo ndi chifuno, chikumbumtima ndi makhalidwe abwino, kulemekeza ena ndi chikondi, chikhulupiriro ndi chisonkhezero cha kulambira—zonsezi zimadalira pa dongosolo lapadera mu bongo. (Onani Machitidwe 17:27.) M’mawu ena, cholowanecholowane wokhazikitsidwa mwachibadwa wa mitsempha yaikulu ya bongo ali wokonzekeretsedwa mwapadera kuyankha ku kukula kwa mphamvuzi ndi zofunika.
Mvetsetsani, ngakhale kuli tero, kuti pa kubadwa izi ziri kokha zofunika, mlingo wamphamvu, kuwunikiridwa kwa pasadakhale. Pafunikira kukhala zolowetsedwa kuti zipangitse izi kukula. Zifunikira kuwunikiridwa ku zokumana nazo zabwino kapena malo ozungulira kapena maphunziro kuti zikhale zenizeni. Ndipo palinso ndandanda yolongosoka kaamba ka zowunikira zoterezi kuti zigwire ntchito bwino, makamaka kwa achichepere.
Koma pamene zinthu zozungulira ziri zabwino ndipo kusunga nthaŵi kuli kolondola, zinthu zozizwitsa zimachitika. Osati kokha kuti zinenero zimaphunziridwa koma ziwiya zoyimbira nyimbo zimaseweredwa, maluso a za masewera amayambitsidwa, zikumbumtima zimaphunzitsidwa, chikondi chimamwerekera, ndipo maziko a kulambira kowona amapangidwa. Zonsezi ndi zina zochulukira, zochulukira kwambiri, monga bongo wa khanda zimabzyalidwa ndi mbewu zabwino ndi kuthiliridwa ndi chikondi cha ukholo.