Kulankhula ndi Kupenya Kupyolera M’galasi
KUWALA—chizindikiro chakale cha chinsinsi, nzeru ndi luntha—tsopano sikulinso kokha chizindikiro. Mu zaka zaposachedwapa iko kwatenga mwamsanga ndi mwakachetechete ntchito yake yolondola ndipo kwakhala chonyamula chenicheni cha mitundu yonse ya chidziŵitso. Kuti kuwala kufikiritse kufunika kwake kwenikweni kaamba ka kutumiza nzeru pa mtunda wautali kwenikweni, zopangidwa ziŵiri zinkafunika: (1) mtundu wapadera wa kuwala ndi (2) mtundu wapadera wa chotsogoza kuwala.
Posachedwapa, mwakugwiritsira ntchito zopangidwa zodabwitsa zatsopano, tikutumiza tsopano unyinji waukulu wodabwitsa wa nzeru za mitundu yonse pa mtunda waukulu ndipo pa liwiro lokulira mwakugwiritsira ntchito cheza cha kuwala. Inde, tsopano chiri chothekera kulankhula, kuwona, ndi kumvetsera paliwiro lochititsa kakasi ndi kukhoza, mwakugwiritsira ntchito cheza chaching’ono cha kuwala komayenda kupyolera mu timipukutu tagalasi tonga tsitsi. Monga ude wa kangaude, timipukutu tagalasi timeneti tochinjirizidwa mu nthambo za mawaya, tayamba kale kupititsidwa pakati pa mizinda mu United States, mu Europe, ndi mu Japan. Ito tsopano tiri m’njira ya kufalikira m’nyanja, kumapita kuchokera ku kontinenti kufika ku kontinenti.
Kodi ichi chiri chothekera motani, popeza kuti tonsefe timadziŵa kuti kuwala kumangoyenda m’mizere yowongoka? Kodi nchiyani chimene chimachipangitsa kukhala chothekera kwa cheza chochepera cha kuwala kukhala mu timipukutu tagalasi pamene tikhota mozungulira ngodya? Kodi cheza chimenechi chimapita pa utali wotere motani ndi kunyamula chidziŵitso chochulukira chotere? Chiri mtundu wapadera wa kuwala umene umachipangitsa icho kukhala chothekera—kuwala kolongosoka.
Kuwala Kolongosoka Kopambana
Ubwino wa cheza cha kuwala kolongosoka pa cheza cha kuwala kwanthaŵi zonse kaamba ka kutumiza kwa nzeru kungathe kuchitiridwa chitsanzo ndi mbalawali za kuwala zomayenda kupyola mu nthambo za galasi mwa kuyerekezedwa ndi anthu omayenda mu msewu. Tiyeni tilingalire cheza cha kuwala kwanthaŵi zonse monga ngati kuti chinali gulu la anthu a misinkhu yonse, onse akumayenda mosiyanasiyana ndi kusokonezana wina ndi mnzake pamene akuyenda. Kumbali ina, cheza cha kuwala kolongosoka chingakhoze kulinganizidwa ndi asilikari onse a msinkhu umodzi, onse ali ngakhale m’mizere, ndiponso onse akumayendera pamodzi. Kuyendera pamodzi popanda kusokonezana kungakhoze ndithudi kuyendetsa anthu ambiri pa mtunda wautali ndi kulongosoka kokulira ndiponso kokhala ndi kusoweka kochepa kwa mphamvu. Chotero ndi mmenenso ziriri ndi kuwala kolongosoka.
Pansonga imeneyi ena anganene kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji kugwiritsira ntchito kumeneku kwa kuwala kwachedwa motero kubwera? Nchifukwa ninji palibe wina aliyense amene analingalira icho poyamba?’ M’chenicheni, iko sikuli kwenikweni kwatsopano. Chifupifupi munthu mmodzi, Alexander Graham Bell, anawona phindu la kulankhula mwa kugwiritsira ntchito kuwala ndipo anafalitsa pepala mu 1880 lokhala ndi mutu wakuti “Selenium and the Photophones.”
Lingaliro limeneli linasonyeza kuwoneratu kwapasadakhale, koma popanda kuwala kolongosoka kupeza kwake kukanakhala kokha ndi kupita patsogolo kokhala ndi polekezera. Sichinali, ngakhale kuli tero, kufikira mu 1960 ndi kupangidwa kwa LASER (Light Amplification by Stimulated Emission of Radiation) kuti kufunika koyenerera koyamba kunapezedwa. Bell anasowanso kufunika kwakukulu kwina, chotsogoza kuwala cholongosoka kwenikweni chofunika kutumizira chidziŵitso.
Zitsogozo Zaluso za Kuwala kwa Galasi Zimenezo—Kodi Zimagwira Ntchito Motani?
Pamene kugwira ntchito kunkapitirizidwabe ndi kupangidwa kwa zothandizira kuwala, ena ankapeza ndi kupanga zinthu za galasi zokhala ndi kuwonetsa bwino ndi kupangidwa kwaluso kumene kunalola zothandizira kuwala kolongosoka kuti kuyende pa mtunda wautali kwenikweni. Zinthu zimenezi chotero zinachepetsedwa kumlingo wa nthambo zonga tsitsi.
Ambiri a ife tingakumbukire kukhala titawonapo nthambo zowunikira za galasi zikugwiritsiridwa ntchito kaamba ka kucheutsa maso, ndi kukometsera thebulo kwa luso. Kuti apange kukometsera kumeneku, mipukutu ya galasi kapena nthambo za pulasitiki zimalekanitsidwa momwazikana monga mu mkhalidwe wa maluŵa ndi kuwunikiridwa kuchokera ku malekezero a kunsi. Mu kusonyeza kumeneku kokha kuwala kwanthaŵi zonse kumagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri kaamba ka kuwunikira kwa nthambo. Ichi chimachitira chitsanzo, chifupifupi, mmene kuwala kungachititsidwire kuyenda kupyola mu timipukutu tagalasi ndi mozungulira zokhota m’malo mwakungopita kokha m’mizere yowongoka monga mmene imachitira nthaŵi zonse. Mu zisonyezero zimenezi kuwala kumayenda kupyola mu mitunda yayifupi kwenikweni.
Kupangitsa kuwala kuyenda pa mitunda yaitali kuposa ndi zimene ziri zofunika mu zisonyezero zaluso, zokuta zapadera zagalasi kapena pulasitiki zapangidwa. Zokuta zapadera zimenezi zimapangitsa cheza cha kuwala chirichonse chimene chingafune kutuluka mwa kuchipangitsa kukhota ndi kubwerera kulowa mu galasi ndipo chotero kutetezera kachiŵirinso kuthawa kwa kuwala. Pali chiŵerengero ndithudi cha kusiyanasiyana kwaluso mu kapangidwe ndi kamangidwe ka zokutazi. Komabe, kusiyanasiyana kumeneku, chimodzi ndi chimodzi m’njira yake ndi pansi pa mikhalidwe yake yapadera, kumathandizira kuwonjezera mtunda umene kuwala kumayenda.
Ngakhale kuti timipukutu tagalasi timeneti, kapena nthambo, zawongolera kwakukulukulu mphamvu zathu za kutumiza ndi kutsogoza kuwala, chiri choyenererabe kulowetsa kuwala mu timipukutu pa kukhota kovuta kapena kocheperako. Tingamvetsetse lamulo la mmene ichi chimagwirira ntchito pamene tikumbukira kuti mbali yodekha ya mtsinje ingagwire ntchito monga kalilole. M’chenicheni, mitengo yomwe iri m’mbali mwa mtsinje nthaŵi zina ingawonedwe monga mu kalilole pansi pake. Kuyambukira kwa kalilole kumeneku kuli kothekera chifukwa chakuti kuwala komwe kumadza m’maso athu kumachokera ku kukhota kochepera kwenikweni. Pa kukhota kolunjikitsidwa kokha kumeneku, komwe kumatchedwa kukhota kovuta, mbali ya madzi imawunikira kuwala konga kalilole. Mu mkhalidwe umodzimodziwo, pamene kuwala kwalowetsedwa mu timipukutu tagalasi pa kukhota kovuta kapena kucheperapo, iyo mkatimo ikuwunikira mkati mwanthambo, zonga kalilole, zokhala ndi kuwunika kochepera kukutuluka kunja.
Chikuyembekezeredwa kuti cheza chimenechi chidzakhala chokhoza kuyenda kufika ku mamailosi 25 (40 km) kapena kuposerapo kupyola mu timipukutu tochepa timeneto popanda kufunika kwa kulowetsanso kuwala. Ziyembekezo zamtsogolo zirinso zolimbikitsa kwenikweni. Kulingana ndi ripoti laposachedwapa, nthambo zochepetsa kutuluka kwa kuwala kotheratu zapangidwa “zimene zingatumize chidziŵitso zikwi za mamailosi popanda kufunika kwa kubwereza.”
M’malo mofuna kuchinjiriza zosungitsa kuwala zodabwitsazi, chiri chofunika kuika zigawo mozizungulira ndi zomangira za kutetezera zinthu. Ndiponso, nthambo za mphamvu zapamwamba ndi mawaya, kuphatikizaponso ndi zosungitsa za magetsi, zimawonjezeredwa kaŵirikaŵiri kuti zipange nthambo za mawaya zazing’ono. Pamene zachinjirizidwa mkati mwa nthambo zamawaya, nthambo zagalasi zimenezi zimapereka kulongosoka kwa kutumizidwa kwa chidziŵitso kwakukulu kotero kuti mphamvu za magetsi zomayenda pamawaya a mkuwa a nthaŵi zonse sizingathe kupikisana nazo. Ichi chiri makamaka chowona kaamba ka mitunda yaitali. Koma kodi chidziŵitso, zithunzithunzi, ndi mawu a anthu zimanyamulidwa motani ndi mtundu wapadera umenewu wa kuwunika kupyola mu nthambo zagalasi zazing’ono zimenezo?
Mmene Tinthambo Tating’ono Timanyamulira Katundu Wawo Wamkulu
Ngakhale kuti mtundu wapadera wa cheza cha kuwala ndi nthambo zagalasi zaluso zimatikondweretsa, njira mu imene cheza chimanyamulira kwenikweni katundu wawo wamkulu wanzeru iri mofananamo yokondweretsa. Chinsinsi chimodzi chachikulu chiri paliwiro lalikulu lakuwala, chifupifupi mamailosi 186,000 pa kamphindi kamodzi (300,000 km/sec). Ina iri chiŵerengero chapamwamba kwenikweni cha kuyenda kwa kuwala, komwe kumadzatanthauza kubwerezabwereza kwa mabiliyoni pakamphindi kamodzi. Chifukwa cha ziŵerengero zapamwamba zanthaŵi zimenezi, ndipo mwakuzindikiritsa mphamvu zakuwala, unyinji wokulira wa nzeru ungadzazidwe mu cheza cha kuwala chomayenda kupyola m’nthambo zazing’ono. Tiyeni tilingalire chitsanzo chimodzi, kulankhula ndi kumvetsera mwa kugwiritsira ntchito kuwala.
Kulankhula ndi Kumvetsera mwa Kugwiritsira Ntchito Kuwala
Kulankhula ndi kumvetsera, kuphatikizaponso ndi kuwona, mwa kugwiritsira ntchito kuwala kumaphatikizapo cholowanecholowane wambiri wa nzeru za zopangapanga za m’tsiku lathu. Tiyeni, ngakhale kuli tero, tipite kokha m’mbali zoŵerengeka zimene zimachitika m’kulankhula ndi kumvetsera mwakugwiritsira ntchito kuwala kuti tipeze kuyamikira kochepera kwa kachitidweko.
Ngakhale kuti kuwala kumagwiritsiridwa ntchito kaamba ka kutumiza, njira yeniyeni imangoyamba monga mmene ziri, kulankhula pa telefoni. Kunthunthumira kwa mawu kochokera m’mawu athu kumasinthidwabe mu zotumizira mawu za magetsi zolingana nazo mu telefoni. Ndiyeno zizindikiro za zotumizira mawu za magetsi zimenezi “zimalekanitsidwa mu zidutswa” paliwiro lalikulu kwenikweni. Kachitidweka kamalingana ndi camera yowonetsa kanema, imene ndithudi imatenga mpambo ungapo wa zithunzithunzi zosakhoza kuyenda, kapena zidutswa, za seŵero. Zithunzithunzi zimenezi chotero zimawonetsedwa, galasi ndi galasi, m’kutsatizana kwaliwiro kuti zipatse wopenyerera lingaliro lakuti zikuyenda. Mofananamo, zidutswa zamagetsi zimenezi zimachotsedwa ndi kuzindikiritsidwa mu mkhalidwe watsatanetsatane wochulukira ndiyeno kusinthidwira mu mphamvu za kuwala. Mphamvu zozindikiritsidwa za kuwala mwakutero zimayenda kupyola mu mpukutu wagalasi kufika ku malekezero olandirira. Pamene zifika pamalekezero olandirira, izo zimasinthidwa mwakubwezedwa ndi njira zobwezera mu liwu lonthunthumira mu zinthu zoika m’makutu za telefoni. Kodi ndi mapindu otani omwe alipo kwa ife? Kodi ziyembekezo zamtsogolo nzotani?
Ena a Mapindu Omwe Alipo
Monga momwe tangoyamba kulandira ndi kuyamikira cholowanecholowane wa kukambitsirana kwa dziko lonse komwe kulipo, dongosolo latsopano lathunthu lawonekera. Nthambo za optics zikulonjeza kulowa m’malo zosungitsa zambiri za nthambo zamawaya a telefoni, cholowanecholowane wochepetsa wa kunthunthumira kwa mawu, ndipo ngakhale malo ena a satellite, komabe zokhala ndi unyinji wa mapindu owonjezereka.
◼ Kulankhuzana Popanda Kusokonezedwa. Imodzi ya mapindu ofunika kwambiri a kutumiza kwanthambo za optics kaamba ka wogwiritsira ntchito telefoni iri yakuti kwakukulukulu imachotsapo mitundu yambiri ya kusokoneza imene takhala ozolowerana nayo. Bingu, mphamvu za magetsi, majenareta—zonsezi zatikalipitsa ife ndi kusokoneza ndi phokoso. Ngakhale zosungitsa zokutidwa ndi mkuwa sizingakhoze kuchinjiriza kwina kwa kusokoneza kumeneku kuchitika.
Ngati kulankhuzana kwanu kwa pa telefoni kunatumizidwa mbali imodzi ndi satellite, inu mungakhale mutamvapo kamphindi kakuchedwa kwa kulankhuzana kapena kumvapo ziyambukiro za mawu ozungulira. Mu nthaŵi zakumbuyo, chiwunda chinkakhalapo. Nthambo za optics zimayesa kuchepetsako kuchedwa kodziŵika ndi kupereka kulandira komvekera bwino, ndipo kosasokonezedwa.
◼ Kulankhuzana Kokhala ndi Chisungiko. Chisungiko chotheratu chiri chimodzi cha mapindu a nthambo za optics. Chotero, kulankhuzana kolowerera kumathetsedwa, ndi kulumikiza mawaya kopanda lamulo kuli kwenikweni kosathekera. Palibe njira ina yomwe pakali pano yapangidwa kulumikiza mawaya pa cheza chakuwala, chifupifupi osati popanda kuchepetsa kwakukulukulu zolandirira ndipo motero kupereka chenjezo.
◼ Kulongosoka Kwakukulu. Kulongosoka kwabwino kwambiri kwa kutumizira chidziŵitso mwa kugwiritsira ntchito kuwala kungamvedwe pamene tilingalira kuti kulankhuzana kwa zikwi zikwi kwa pa foni kunganyamulidwe ndi mbali imodzi yokha ya nthambo za kuwala. Kuyerekeza kuli kwakuti zamkati zonse za Webster’s unabridged dictionary zingatumizidwe mamailosi zikwi mu timphindi tisanu ndi imodzi kupyola mu kampukutu kamodzi kokha ka galasi.
◼ Malo Ochepa—Zikhoza Kuchita ndi Malo Ozungulira Ovuta. Malo ambiri ayamba kale kupindula kuchokera ku kupangidwa kwatsopano kumeneku. Mbali za Mizinda Yaikulu zikupindula mu, chiwunda chapamwamba chatsopano cha kulankhuzana chokhala ndi kufunikira kochepera kwa ziwiya. Zipinda zonse zodzala ndi ziwiya zoyatsira zakale zingakhoze tsopano kulowedwa m’malo ndi ziwiya zanthambo za optic zomwe zimangofuna kokha malo ochepa. Ndiponso, malo akutali onga ngati Florida Keys tsopano amasangalala ndi kachitidwe kopanda phokoso. Mkhalidwe wovuta wa madzi a m’chere mu Keys ndi malo ofanana nawo zinali zokhoza kupangitsa kuchepa kwamphamvu za magetsi ndi kuzimiririka kwa zamankhwala. Komabe, ndi nthambo za optics, pali ziyambukiro zochepera.
Kuyang’ana Mtsogolo
Mtsogolo kaamba ka kupangidwa kwatsopano mumawonekera kukhala molonjeza. Kusintha kwayamba kale kutenga malo mofulumira kwenikweni kuposa ndi mmene kunanenedweratu ndi ena. Kukusimbidwa kuti limodzi la mavuto akulu koposa liri kusankha dongosolo lomwe silidzakhoza kuyerekezedwa panthaŵi imene lidzaikidwa.
◼ Liwu, Video, ndi Makompyuta Kuchokera Kumbali Imodzi. Magazini ya High Technology m’kope lake la February 1986 yachitira ripoti pansi pa mutu wakuti “Business Outlook” kuti “Nthambo za Optics zakhala mbali yolakalakidwa kwambiri ya kutumizira mawu, chidziŵitso, ndi video mu U.S.—makamaka kupyola pa mtunda wautali.” Nkhaniyo yapitiriza ndi kuchitira ndemanga kuti: “Tikuyamba kukulitsa cholowanecholowane wanthambo zimene zidzafikira m’nyumba. Mwakugwiritsira ntchito mbali imodzi imene ingakhoze kukhala ndi mawu, video, ndi . . . kufunsira mbali ya magwero a chidziŵitso kaamba ka mawu.” Ichi chikutsegula mwaŵi kwa chifupifupi anthu ena kugula, kuika ndalama ku banki, ndi kugula matikiti a ndenge, ndi kukhala ndi mwaŵi wina wa malaibulale panyumba zawo. Iwo ayenera kukhala okhoza ngakhale kuwona mabwenzi awo pamene akulankhula pa foni—zonsezi kupyolera mu nthambo za galasi zodabwitsa zimenezo.
[Zithunzi patsamba 16]
Kuwala komayenda kupyola m’nthambo za galasi kumawunikira mkati ndipo sikumatuluka kupyola khoma
Nthambo zamphamvu kwenikweni ndi mawaya zimapereka chitetezero
Mbali za galasi kapena pulasitiki zimachepetsako unyinji wa kuwala kothawa
[Chithunzi patsamba 18]
Nthambo za mawaya a optic zazing’ono izi zimanyamula kukambitsirana kochulukira kwa pa telefoni kuposa nthambo za mawaya zazikulu zotumizira mawu izi