Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 11/8 tsamba 22-23
  • Allan Kardec—Ngwazi ya Kukhulupirira Mizimu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Allan Kardec—Ngwazi ya Kukhulupirira Mizimu
  • Galamukani!—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tiyenera Kukhulupirira Mizimu Pofuna Zinthu Zauzimu Zenizeni?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mizimu Yoipa Njamphamvu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Polimbana ndi Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 11/8 tsamba 22-23

Allan Kardec—Ngwazi ya Kukhulupirira Mizimu

Ndi mlembi wa “Galamukani!” mu Brazil

“NDINE m’Kardec.” Nthaŵi ndi nthaŵi Mboni za Yehova mu Brazil zimamva mawu amenewa pamene zikupanga maulendo awo a kunyumba ndi nyumba. Ambiri amauza Mboni m’njira yaubwenzi: “Ndimaŵerenga uthenga kulingana ndi kukhulupirira mizimu. Mumudziŵa—Allan Kardec!” Chifupifupi nthaŵi zambiri kukambitsirana kotentha ndi kwa umoyo kumayambika.

Koma kodi Allan Kardec ndani? Maencyclopedia achinenero cha Chingelezi ambiri alibe kulongosola kwambiri pansi pa dzina limeneli, komabe kwa mazana angapo a zikwi iye ali ngwazi ndi m’chikirizi wa kukhulupirira mizimu mu mkhalidwe wake wamakono. Zolemba zake ziri zolandiridwa monga kulongosola kwamphamvu zosakhala za umunthu—makamaka mu Brazil, mmene mabukhu ake amasangalala ndi kuperekedwa kokulira.

Grande Enciclopédia Delta Larousse ndi Enciclopédia Mirador Internacional, maencyclopedia aŵiri odziwika kwambiri m’chinenero cha chiPortuguese, amatiuza ife kuti Allan Kardec liri dzina lopeka la wolemba wa chiFrench Hippolyte Léon Denizard Rivail, yemwe anakhalako kuchokera mu 1804 kufika ku 1869. Wobadwira mu Lyons, pa msinkhu wa zaka khumi iye anatumizidwa kukaphunzitsidwa mu Switzerland kumene anakakhala wophunzira wa munthu wokonzanso maphunziro Pestalozzi. Chaka cha 1824 chinampeza iye ali mu Paris, kumene anadzipereka iyemwini ku ntchito yophunzitsa ndipo, m’kupita kwanthaŵi, anadzakhala chiwalo cha France’s Royal Academy of Natural Science.

Mu chaka cha 1854, Rivail anadziŵitsidwa ku choseketsa chofala cha pakati pa zana la 19: Kuyesayesa kulankhula ndi mizimu yosakhala ndi thupi. Chaka chotsatira, iye anachitira umboni wa kugubuduzidwa kwachilendo kwa matebulo ndi kalembedwe ka anthu olankhula ndi mizimu. Iye anadzakhala wokhutiritsidwa za kukhalako kwa dziko la mizimu lokhalidwa ndi miyoyo yosakhoza kufa ya anthu akufa ndi kuthekera kwa kulankhuzana nawo. Magwero a mizimu yosawoneka sanachedwe kum’gwiritsira ntchito iye monga chiwiya.

“Mzimu wozolowereka” wake unamudziŵitsa iye kuti m’nthaŵi yakumbuyo, m’nthaŵi ya Druids, iye anali anakhalapo mu Gaul ndikuti dzina lake linkatchedwa Allan Kardec. Ndiponso, mizimu inalengeza kupyolera mwa olankhula ndi mizimuyo kuti “nthaŵi zokhazikitsidwa ndi Mulungu kaamba ka kuvumbulutsidwa kwa dziko lonse kunali kutafika ndi kuti, monga atumiki a Mulungu ndi ogwiritsiridwa ntchito a chifuno chake, [linali] thayo lawo kuphunzitsa ndi kuwunikira anthu, kutsegula nyengo yatsopano ya kubweretsanso mbadwo wa mtundu wa Anthu.”

Atakondweretsedwa mokulira ndi zonsezi, Rivail anayamba kugwira ntchito kuti aike mwadongosolo zinthu zochulukira zonsezo za kalembedwe ka anthu olankhula ndi mizimu zoperekedwa kwa iye ndi anzake okhulupirira mizimu. Iye anayamba kupezeka pa misonkhano ya mizimu mokhazikika, wokonzekeretsedwa nthaŵi zonse ndi mpambo wa mafunso omwe anayankhidwa kupyolera mwa olankhula ndi mizimu m’njira “yolondola, yakuya ndi mkhalidwe weniweni.” Zinthu zonsezi, “zitaŵerengedwa kaŵiri” motsimikiza ndi “Mzimu wa chowonadi” wogwira ntchito kupyolera mwa wolankhula ndi mizimu, zinafalitsidwa mu 1857 m’bukhu lake loyamba O Livro dos Espíritos (Bukhu la Mizimu), pansi pa dzina lakuti Allan Kardec.

Kuchokera pa chiyambi, Rivail anachipangitsa icho kukhala chowonekera “kuti Mizimu, pokhala kokha miyoyo ya anthu, iri mwina ndi chidziŵitso chopambana kapena nzeru zopambana; kotero kuti luntha lawo linadalira pa kupita patsogolo kumene iwo anapanga ndi kuti lingaliro lawo siliri chirichonse kuposa kokha lingaliro laumwini.” Kupyola mu kalembedwe ka mizimu kake konse, iye amapanga katchulidwe ka mizimu yapamwamba ndi yapansi, mizimu yabwino ndi yoipa, mizimu yodzichepetsa, yoipa ndi mizimu yowukira, mizimu yoyendayenda, mizimu yovuta ndi mizimu yabodza. Iyi imazidziŵikitsa iyo yokha kwa anthu olankhula ndi mizimu ndi maina odziŵika bwino lomwe onga ngati Socrates, Julius Caesar, Augustine, Charlemagne, George Washington, Mozart, ndi Napoleon. Mu bukhu lake What Spiritism Is, Rivail akuvomerezanso kuti mizimu ina iri “yabodza, yonyenga, yachiwawa, yoipa ndi yolakalaka kuvulaza,” ndipo yokhala ndi chinenero choipa.

Chotero, nchifukwa ninji, anthu amadzivuta kuphunzira kukhulupirira mizimu? Rivail akuyankha kuti: “Kuti atsimikize, mwa ziwiya, kukhalako kwa dziko lauzimu.” Koma ichi chinali kutalitali ndi kukhala choyenera. Zaka zikwi zingapo asanakhaleko Rivail, okhulupirira Baibulo anadziŵa kukhalako kwa dziko la mizimu loterolo.

Mulungu amene Akristu amalambira ali Mzimu Waukulu. Yesu iyemwini ananena kuti: “Mulungu ndiye Mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mu mzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:24) Akristu amene amatumikira Mulungu ameneyu ndi mtima wawo wonse amakumana ndi kusonkhezera kwake m’miyoyo yawo ndipo alibe kukaikira kulikonse kwa kukhalapo kwake. Akristu amadziŵanso za kukhalapo kwa mizimu ina—Yesu Kristu ndi khamu la angelo ake, angelo amene amachita chifuniro cha Mulungu.

Kulingana ndi ofalitsa a kufalitsidwa kwa chiPortuguese kwa bukhu la Rivail, “mbali yochitidwa ndi The Book of Spirits iri ija yothandiza zipembedzo zina zonse kulimbikitsa chikhulupiriro cha kusafa kwa moyo.”

Koma chiri chosathekera kwa kalongosoledweka kukhala kowona. Baibulo limalongosola kuti moyo wa munthu siuli wosafa. “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Baibulo lirinso ndi chenjezo lamphamvu kwambiri: “Moyo wochimwawo—ndiwo udzafa.”—Ezekieli 18:4.

Chotero, ndani, amene anali mizimu imene Rivail anakumana nayo? Pali kokha yankho lothekera limodzi: Mizimu imeneyi iyenera kukhala ya mbali ina yaufumu wa mizimu—ziwanda. Umu ndi mmene wophunzira Yuda akulongosolera ziwanda: “Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pawo pawo.” (Yuda 6) Inde iwo ali angelo amene anaukira Mulungu.

Mofananamo, mu Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Israyeli, iye analetsa mwamphamvu Aisrayeli kukhala ndi kugwirizana kulikonse ndi olankhula ndi mizimu onga aja amene Rivail anali nawo. (Levitiko 19:31) Chenicheni chakuti chinenero chawo nthaŵi zina chingakhale chinali chokongola, kulongosola malingaliro apamwamba sikumasintha chirichonse. Mtumwi Paulo anapereka chenjezo lakuti: “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wakuwunika.”—2 Akorinto 11:14.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Mizimu ina iri “yabodza, yonyenga, yachiwawa, yoipa ndi yolakalaka kuvulaza,” ndipo yokhala ndi chinenero choipa

[Chithunzi patsamba 22]

Allan Kardec, wogwiritsiridwa ntchito ndi magwero a mizimu yosawoneka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena