Khalani ndi Moyo Kuti Mudzawone Nkhalango Zikusangalala!
“Ndikhulupirira kuti sindidzawona
Ndakatulo yokongola monga mtengo. . . .
Ndakatulo zimalembedwa ndi anthu opusa monga ine,
Koma kokha Mulungu angapange mtengo.”
KU CHOWONADI chakuti “kokha Mulungu angapange mtengo,” wolemba ndakatulo wa chiAmerica Joyce Kilmer, amene moyo wake wa luso unafupikitsidwa ndi Nkhondo ya Dziko I, moyenerera chingakhale chinawonjezera lingaliro, ‘ndipo kokha Mulungu angasunge mtengo kukhala wa moyo.’
Mosasamala kanthu za kulira kwa nkhondo ya “Sungani Nkhalango Zathu,” zoyesayesa za anthu za kusunga nkhalango zikukumana ndi chipambano chochepa. Ngakhale “mbiri yabwino” yoperekedwa ndi ripoti la September 1986 liri la chitonthozo chochepa. Ilo limalankhula za “kukhazikitsa kwapamwamba,” kumene m’mawu okhweka kumatanthauza kuti Waldsterben akufutukukabe paliŵiro locheperapo kuposa mmene zinaliri zaka zapitazo.
Malinga ndi nyuzipepala yapamwamba ya mu German, lingaliro lomakula la kudzimva kwa kukhala opanda thandizo likupezeka pakati pa anthu asayansi. Ilo limagwira mawu a Professor Peter Schütt wa ku Munich’s Institute of Forestry, amene posachedwapa anauza khamu lokhudzidwa kuti: “Tiyeni tisadzinyengeze ife eni. Ndi kale lomwe tinafikira mapeto a kuthekera kwathu.” Iye anachenjeza kuti ngati zoyesayesa zatsopano za kuthetsa kuipitsa mpweya zidzalephera, “tidzasiidwa opanda china chirichonse chakuti tiyesere.”
Ndipo ndimotani mmene ziyembekezo za kuthetsa vuto la kuipitsa mpweya zingalongosoledwere? Zakuda, zomvetsa chisoni, kapena za mazizi—sankhani nokha. “Mtundu wa mpweya sunawongoleredwe,” ikutero nyuzipepala ya chiSweden Die Weltwoche. Pamene “akatswiri odziŵa za kapangidwe ka mitengo adakali okhudzidwa m’ntchito yatsatanetsatane, ya kutha nthaŵi, kuyesera kugamulapo kuti ndi choipitsa chiti chimene chikukantha mtengo uti ndipo ku ukulu wotani, . . . oyendetsa magalimoto amene pa nthaŵi imodzi anali osakhutiritsidwa akupezanso chidaliro chawo chaumwini chakale ndi kuyendetsa magalimoto mopitirira pa liŵiro limene iwo ayenera kuyendetsera. Kugulitsidwa kwa magalimoto okhala ndi catalytic converters kwaima . . . Palibe zambiri za chirichonse chomwe chasintha, kupatulapo kokha kumveka kwa kusangalatsidwa [ponena za Waldsterben] kuli kwakale.”
Yankho Lenileni Liri Pafupi
Kukhulupirira kuti Waldsterben ingathetsedwe mwa chipambano ndi anthu kuli kosalingalirika. Chifukwa ninji? Chifukwa iwo alibe chidziŵitso cholongosoka ponse paŵiri cha zoyambitsa zake ndi njira zokhutiritsa za kuthetsera iyo. M’kuwonjezerapo, anthu alibe mphamvu ya kulamulira mphamvu za chilengedwe monga ngati dongosolo la nyengo ndi kudalirana kwa zinthu za chilengedwe. Pambali pa icho, dyera la cholowa limaletsa iwo kutulutsa zikondwerero zaumwini mu chiyanjo chaubwino wa onse.
Komabe, pali zifukwa za kukhala ndi kawonedwe kabwino. Mbiri ya Baibulo ndi nsonga zakuthupi zimasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu wopemphereredwa kwanthaŵi yaitali uli pafupi. Boma lokhazikitsidwa limeneli linanenedweratu chifupifupi zaka 1,900 zapitazo m’mawu awa: “Tikuyamikani, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli nimunali, popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu. Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, [ndi nthaŵi yoikika, NW] . . . kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:17, 18) Mwamsanga, monga kunalonjezedwa, “nthaŵi yoikika” idzafika kaamba ka Mulungu “kuwononga iwo akuwononga dziko,” kuphatikizapo oipitsa omwe akuwononga nkhalango zake.
Pansi pa ulamuliro waumulungu, mtundu wa anthu omvera udzalangizidwa moyenerera mmene angapewere kuipitsa mpweya ndi chotulukapo chake chapambali cha Waldsterben. Tangolingalirani mmene dziko lapansi lidzasangalalira, kulankhula mophiphiritsira, pamene kulinganizika kwa chilengedwe kudzabwezeretsedwa ndi zotulukapo zabwino pa nyengo, za malimidwe, ndi umoyo. “Dziko lapansi lisekerere, [linene] mwa amitundu, ‘Yehova achita ufumu!’ . . . Panthaŵi imodzimodziyo lolani mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera.” (1 Mbiri 16:31-33) Yobwezeretsedwa ku mkhalidwe wa kukongola kokulira ndi wabwino koposa kalelonse, “mitengo ya m’nkhalango” idzakhalabe ndi chifukwa chirichonse cha “kufuula mokondwera.”
Koma nthaŵi imeneyo isanafike, Waldsterben ayenera kuipirapo. Mwachitsanzo, mu September 1986 nyuzipepala yotchulidwa pamwambapo inalemba kuti: “Mitengo yobzyalidwa m’malo otsika ikuyamba kuwonongeka; mitengo ya cherry kumpoto cha kumadzulo kwa Switzerland yataya mphamvu yawo, ndipo alimi akufunafuna uphungu kuchokera kwa nduna za malimidwe.” Mkhalidwe wofananawo mu Germany posachedwapa unatsogolera boma la Baden-Württemberg kuyamba kufufuza kugwirizana pakati pa kuipitsa mpweya ndi kuwonongeka kwa mitengo ya zipatso. Ngakhale kuti palibe ziŵerengero zomwe zapezedwa pakali pano, chikusimbidwa kuti asayansi akukhulupirira kuti zipatso zokhala ndi nthanga mwapadera ziri m’tsoka.
Maripoti onga ngati awa angakumbutse ophunzira Baibulo za Habakuku 3:17. Polankhula za tsiku lathu, ilo limati: “Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m’minda m’mosapatsa chakudya.”
Ngati, ngakhale kuli tero, muika chidaliro chanu mwa Mulungu ndi kuchirikiza ulamuliro wake wa Ufumu, inu, mofanana ndi Habakuku, simudzakhala ndi chifukwa chakuchitira mantha. (Habakuku 3:18) Mosiyanako, mudzakhala ndi chifukwa chirichonse chakuyang’anira kutsogolo ndi kawonedwe kabwino ndi kukondwera. Vuto la Waldsterben liri pafupi kuthetsedwa—mokhazikika ndi kotheratu. Inu, nanunso, mungakhale ndi moyo kudzawona nkhalango zikusangalala—limodzi ndi mtundu wonse wa anthu ndi iyo!