Kodi Mudzalabadira Machenjezo a Tsoka Lomwe Likudzalo?
MATSOKA ena achibadwa amapangitsa kuwononga miyoyo ya anthu; ena, kuwonongedwa kwakukulu kwa moyo ndi zinthu. Kaŵirikaŵiri, ngakhale kuli tero, zinthu zotero zimayambukira mbali yochepa ya dziko ndi anthu ake pa nthaŵi ina iriyonse. Mbadwo wathu watsopano, ngakhale kuli tero, ukuyang’anizana ndi tsoka la dziko lonse ku ukulu womwe udzayambukira mtundu wonse wa anthu.
Ayi, siiri nkhondo ya nyukliya pakati pa mphamvu zazikulu, ngakhale kuti limenelo lingakhale tsoka lalikulu. Mmalo mwake, tikulankhula za chifuno chotsimikiziridwa cha Mulungu kuchotsa zinthu zonse zoipa pa nkhope ya dziko lapansi.
Ukulu wa tsoka limeneli unalongosoledwa ndi Yesu mu ulosi wake wolozera kumapeto kwa dongosolo iri la zinthu: “Pomwepo padzakhala masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense.”—Mateyu 24:3, 21, 22.
Anapulumutsa Miyoyo Yawo
Yesu anayerekezera tsoka la dziko lonse limeneli ndi vuto la dziko loyambirira, chigumula cha tsiku la Nowa, akunena kuti: “Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37) Baibulo limalongosola kuti m’masiku pambuyo pa chigumula “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” Yehova ananena kuti: “Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi.”—Genesis 6:5-8.
Ponena za Nowa, timaŵerenga pa Ahebri 11:7 kuti: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” Nowa, mkazi wake, ndi ana ake amuna ndi akazi awo anasungidwa amoyo kupyola chigumula.
Mtundu wonse wa anthu wina wotsala, ngakhale kuli tero, unanyalanyaza chenjezo lopatsidwalo. Monga m’mawu a Yesu, anthu m’masiku aja chisanafike chigumula “analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa; ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza chinapululutsa iwo onse.”—Mateyu 24:38, 39.
M’masiku a Loti, Mulungu anafuna kubweretsa nzika za m’Sodomu ndi Gomora kuchiwonongeko chifukwa cha mkhalidwe wawo woipitsitsa. Komabe, anapitiriza ‘kudya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, anabzala ndi kumanga nyumba,’ monga ngati panalibe chirichonse chidzachitika. Ngakhale kuti Loti anachenjeza akamwini ake, ‘m’maso awo anawoneka monga ngati mwamuna wongoseka.’ Koma Mulungu anatsogoza moto ndi sulfure kuvumba kuchokera kumwamba, kuwononga iwo onse. Loti ndi ana ake akazi analabadira chenjezolo ndipo anapulumutsa miyoyo yawo.—Luka 17:28, 29; Genesis 19:12-17, 24.
Chenjezo m’Tsiku la Yesu
M’tsiku la Yesu anthu Achiyuda anakana Mawu a Mulungu ndi kukonda mwambo wawo, ndiponso anakana Mwana wa Mulungu monga Kristu, kapena Mesiya. Mulungu analingalira kupereka chiweruzo chake pa iwo ndi mzinda wawo wokoma, Yerusalemu, mwanjira ya magulu ankhondo a Roma. Yesu anapatsa chenjezo ponena za ichi ndi kuuza ophunzira ake mmene akapulumukira chiweruzocho. Iye anati:
“M’mene mukadzawona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli mneneri, chitaima m’malo oyera . . . pomwepo iwo ali m’Yudeya athawire kumapiri.” Ndi kuti: “Koma pamene pali ponse mudzawona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m’kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo; Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike.” (Mateyu 24:15, 16; Luka 21:20-22) Iyo ikakhala nthaŵi yakachitidwe kofulumira, munthu sakatenga nthaŵi kusunga zinthu zake zakuthupi. Yesu ananena kuti: “Lolani iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m’nyumba asabwere kutenga chopfunda chake.”—Mateyu 24:17, 18.
M’chaka cha 66 C.E., Yerusalemu anazingidwa ndi magulu ankhondo Achiroma pansi pa Cestius Gallus, m’kukwaniritsa ulosi wa Yesu. Aroma, amene anali kuderera linga la kachisi mwa kuimirira pa malo oyera a Ayuda, anali chinachake chonyansa kwa Ayuda. Chenjezo linaliko koma kunalibe mwaŵi wa kuthaŵa. Kenaka Cestius Gallus mwadzidzidzi anachotsa ankhondo ake. Akristu anayamba kuthaŵira ku mapiri. Ambiri a anthu, ngakhale kuli tero, anakhalabe mu mzinda, ndipo Ayuda ena anapitirizabe kubwera mu iwo kaamba ka mapwando awo achipembedzo.
Mu 70 C.E., pamene mzinda unadzazidwa ndi anthu ochita mapwando a Paskha, ankhondo Achiroma pansi pa kazembe Titus akufuna kubwezera choipa anazinga Yerusalemu. M’kupita kwa nthaŵi malinga anagwetsedwa, kachisi ndi mzinda wonse unawonongedwa, ndipo kulingana ndi wodziwa za mbiri yakale Josephus, anthu 1,100,000 anamwalira, ndipo opulumuka 97,000 anagulitsidwa monga akapolo ku Igupto ndi ku maiko ena. Ichi chinali malipiro a awo omwe analephera kulabadira chenjezo la Yesu. Aja omwe anathaŵa kuchoka mu mzinda, monga mmene Yesu analamulira, anapulumutsa miyoyo yawo.
Labadirani Chenjezo Tsopano
Ulosi wa Yesu, monga mmene unalembedwera mu Mateyu 24, Marko 13, ndi Luka 21, unayenera kukhala ndi kukwaniritsidwa kwakukulu. Kumbukirani, Yesu analinso kuyankha funso la ophunzira ake la chizindikiro cha kukhalapo kwake, chimene Baibulo limagwirizanitsa ndi mapeto a dziko lonse la dongosolo iri la zinthu. (Danieli 2:44; Mateyu 24:3, 21) Yesu anasonyeza kuti kubwera kwake, kapena kukhalapo kwake, kudzakhala kosawoneka, kudzaikidwa chizindikiro chomwe chidzaphatikizapo nkhondo, kuperewera kwa zakudya, zivomezi, matenda, kuwonjezereka kwa kusayeruzika, kuzunzidwa kwa ophunzira ake, kuukirana kwa mitundu, anthu akukomoka ndi mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.—Mateyu 24:7, 8, 12; Luka 21:10, 11, 25, 26.
Kodi ndani amene angakane kuti mbadwo chiyambire Nkhondo ya Dziko I wawona kuwonjezereka kwa miliri iyi yamatsoka? Kotero kuti anthu amvetsetse kufunika kwa zinthuzi, Yesu analosera kuti: “Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova mwachangu zalalikira mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu m’maiko oposa 200 mu zinenero zosiyanasiyana 200, kuchenjeza anthu za kulandira kwa chiweruzo cha Mulungu chikhudzacho. M’kulozera kwa aja omwe adzawona chiyambi cha zowawa za matsoka, chomwe chinayamba ndi Nkhondo ya Dziko I, Yesu ananena kuti: “Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.”—Mateyu 24:34.
Njira ya kulabadira chenjezo la Yesu iri, osati mwa kuthamangira kumapiri enieni kapena kuthamangira ku malo ena adziko, koma mwakutembenukira kwa Mulungu wowona, Yehova, ndi kuphunzira za kakonzedwe kake ka kupulumutsa moyo. Mungachite ichi mwakufikira awo amene akupereka chenjezoli, Mboni za Yehova, kuwalola iwo kuphunzira Baibulo ndi inu, ndi kugwirizana nawo.
Ngati kulabadira chenjezo kunali kofunika kwambiri kwa zikwi khumi za anthu a ku Japani amene anathaŵa chiwonongeko kuchokera ku thanthwe lotentha la pansi pa nthaka, ndi chofunika koposa chotani nanga kwa ife kuchitapo kanthu tsopano kuti tikalandire chinjirizo la Yehova kuchokera ku chiwonongeko cha dziko m’nthaŵi ino yamapeto!
[Chithunzi patsamba 25]
Mwa kulabadira machenjezo, Loti ndi ana ake akazi anathaŵa chiwonongeko