Kumvera Kunawapulumutsa
YESU KRISTU anachenjeza nthaŵi isanafike za mapeto a dongosolo la zinthu lachiyuda limene zinthu zake zambiri zinkachitikira pa kachisi ku Yerusalemu. Sanatchule tsiku limene mapetowo adzafike. Koma anafotokoza zinthu zimene zidzachitike nthaŵi ya kuwonongekako ikadzayandikira. Analimbikitsa ophunzira ake kudikira ndi kuthaŵa pa malo angozi.
Yesu ananeneratu kuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira.” Ananenanso kuti: “Mukadzaona chonyansa cha kupululutsa . . . chitaima m’malo oyera, . . . pomwepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.” Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti asadzabwerere m’mbuyo kukapulumutsa katundu wawo. Kuti apulumuke, anafunika kuthaŵa msanga.—Luka 21:20, 21; Mateyu 24:15, 16.
Pofuna kuthetsa kuukira kumene kunachitika kwa nthaŵi yaitali, Seshasi Galasi anatsogolera asilikali a Aroma pokalimbana ndi Yerusalemu mu 66 C.E. Analoŵa mpaka m’kati mwa mzindawo n’kuzinga kachisi. Mu mzindamo munali chisokonezo. Anthu amene anadikira akanatha kuona kuti tsoka linali pafupi. Koma kodi akanatha kuthaŵa? Mwadzidzidzi, Seshasi Galasi ndi asilikali ake anachoka. Ayuda oukirawo anawatsatira. Tsopano inali nthaŵi yothaŵa ku Yerusalemu ndi m’dziko lonse la Yudeya!
M’chaka chotsatira, asilikali a Aroma anabweranso motsogozedwa ndi Vasipashani ndi mwana wake Tito. Nkhondo inafalikira paliponse m’dzikomo. Kumayambiriro kwa 70 C.E. Aroma anamanga mpanda wa mitengo yosongoka kuzungulira Yerusalemu. Sizikanathekanso kuthaŵa. (Luka 19:43, 44) Anthu a magulu otsutsana m’kati mwa mzindawo anaphana. Anthu otsala anaphedwa ndi Aroma kapena anatengedwa ukapolo. Mzindawo ndi kachisi wake anaziwonongeratu. Malinga ndi zimene ananena Josephus, wolemba mbiri wachiyuda wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Ayuda opitirira wani miliyoni anazunzika ndi kufa. Kachisiyo sanamangidwenso mpaka pano.
Akristu akanakhalabe mu Yerusalemu mu 70 C.E. akanaphedwa kapena kutengedwa ukapolo limodzi ndi anthu ena onse. Komabe, olemba mbiri akale amanena kuti Akristu anamvera chenjezo la Mulungu ndipo anathaŵa ku Yerusalemu ndi m’dziko lonse la Yudeya n’kuloŵera ku mapiri a kum’maŵa kwa mtsinje wa Yordano. Ena anakhazikika ku Pella, m’chigawo cha Perea. Anathaŵa ku Yudeya ndipo sanabwererekonso. Kumvera chenjezo la Yesu kunawapulumutsa.
Kodi Mukamva Machenjezo Odalirika Mumachitapo Kanthu?
Anthu ambiri amanyalanyaza machenjezo onse chifukwa chakuti amva machenjezo ambiri a zinthu zimene sizinachitike. Komabe, kumvera machenjezo kungapulumutse moyo wanu.
Ku China, mu 1975, anachenjeza kuti kuchitika chivomezi. Akuluakulu a boma anachitapo kanthu. Anthu anamvera ndipo ambiri anapulumuka.
Ku Philippines, mu April 1991, anthu okhala m’midzi yapafupi ndi phiri la Pinatubo ananena kuti anaona nthunzi ndi phulusa zikutuluka m’phirilo. Ataunika phirilo kwa miyezi iŵiri, a bungwe loona za mapiri ophulika la Philippine Institute of Volcanology and Seismology anachenjeza kuti kuchitika ngozi posachedwa. Nthaŵi yomweyo, anthu masauzande ambiri anasamutsidwa kuchoka ku deralo. M’maŵa pa June 15, phirilo linaphulika mochititsa mantha kwambiri ndipo chiphalaphala choti chingadzaze mu chithanki chachikulu cha makilomita aŵiri m’litali mwake, makilomita aŵiri m’lifupi mwake, ndi makilomita aŵiri kuya kwake chinathovokera m’mwamba n’kutsika pansi kukuta dera lonse lozungulira phirilo. Kumvera kunapulumutsa anthu ambiri.
Baibulo limachenjeza za mapeto a dongosolo la zinthu lilipoli. Tsopano tikukhala m’masiku otsiriza. Pamene mapeto akuyandikira, kodi mukudikira? Kodi mukuchitapo kanthu kuti muthaŵe pa malo angozi? Kodi mukuchenjeza ena mwachangu kuti achite zomwezo?
[Chithunzi patsamba 20]
Kumvera chenjezo kunapulumutsa anthu ambiri pamene phiri la Pinatubo linaphulika n’kutulutsa chiphalaphala
[Chithunzi patsamba 21]
Akristu amene anamvera chenjezo la Yesu anapulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.