Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 9/15 tsamba 3-4
  • Kodi Ndinu Atcheru ndi Zochitika za m’Nthaŵi Yathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndinu Atcheru ndi Zochitika za m’Nthaŵi Yathu?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitapo Kanthu Kunapulumutsa Miyoyo
  • Kuthaŵa Ngozi Yochititsidwa ndi Anthu
  • Kumvera Kunawapulumutsa
    Dikirani!
  • Ino Ndiyo Nthaŵi Yabwino Yokhala Tcheru!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kulabadira Chenjezo Kungapulumutse Moyo Wanu
    Galamukani!—1988
  • Kukhala Pafupi ndi Chimphona Chimene Chili M’tulo
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 9/15 tsamba 3-4

Kodi Ndinu Atcheru ndi Zochitika za m’Nthaŵi Yathu?

KUKHALA watcheru ndi ngozi inayake kungapulumutse moyo. Tingafanizire zimenezi ndi zimene zinachitika pazisumbu zina ziŵiri zopangidwa ndi volokano.

Phiri la Pelée, volokano yomwe inapha anthu ochuluka koposa m’zaka za zana la 20, linaphulika pa May 8, 1902, pachisumbu cha ku Caribbean cha Martinique. Linapha pafupifupi anthu onse 30,000 okhala ku Saint Pierre, mzinda umene uli m’tsinde mwa volokanoyo.

Phiri la Pinatubo linaphulika m’June 1991, ndipo kuphulika kumeneko mwina ndiko kwakukulu koposa m’zaka za zana lino. Zimenezi zinachitikira kumalo ena a ku Philippines komwe kuli anthu ambiri zedi ndipo linapha anthu pafupifupi 900. Komabe, panthaŵiyi zinthu ziŵiri ndizo zinapulumutsa miyoyo zikwizikwi: (1) kukhala tcheru ndi ngoziyo ndiponso (2) kumvera chenjezo mofunitsitsa.

Kuchitapo Kanthu Kunapulumutsa Miyoyo

Phiri la Pinatubo linali lisanaphulikepo kwazaka mazana ambiri mpaka mu April 1991 pamene linayamba kusonyeza zizindikiro zoti lingaphulike nthaŵi iliyonse. Nthunzi ndi mpweya wa sulfur dioxide zinayamba kutuluka pansonga ya phirili. Anthu okhala pafupi anamva zivomezi zingapo, ndipo mulu wa matope oopsa unayamba kutuluka m’phirimo. Asayansi ogwira ntchito m’bungwe loona za volokano ndi zivomezi la Philippine Institute of Volcanology and Seismology anayamba kufufuza za chochitikacho ndipo kenaka anauza akuluakulu aboma kuti asamutse anthu 35,000 okhala m’matauni ndi m’midzi yoyandikana ndi malowa.

Nthaŵi zambiri anthu samafuna kusamuka m’nyumba zawo popanda chifukwa chodziŵika bwino. Choncho, pofuna kuthetsa vuto la kuzengereza, anthu anasonyezedwa vidiyo yosonyeza zinthu zoopsa zimene zingachitike volokano itaphulika. Anthu miyandamiyanda anayamba kusamuka mwamsanga. Patapita masiku aŵiri, phirilo linaphulika mwamphamvu zedi moti matope a ukulu wa makyubiki kilomita 8 anathovoka. Kenako matope oyenderera pansi kapena kuti ma lahar, anapha anthu mazanamazana. Komabe, mwina anthu zikwi zambiri anapulumuka chifukwa chakuti anachenjezedwa za ngoziyo ndipo iwo anamvera machenjezowo.

Kuthaŵa Ngozi Yochititsidwa ndi Anthu

M’zaka za zana loyamba za Nyengo Yathu, Akristu okhala mu Yerusalemu anafunikiranso kulingalira zoti kaya asiye nyumba zawo kapena angokhala. Kuthaŵa mumzindawu mu 66 C.E. kunawapulumutsa pachiwonongeko chimene chinagwera okhalamo ena ndi Ayuda zikwizikwi amene anabwera ku Yerusalemu kudzachita Paskha ya 70 C.E. Anthu oposa miliyoni imodzi anali mkati mwa mzinda wa linga umenewo kudzachita Paskha ndipo asilikali achiroma anazinga mzindawu moti palibe ndi mmodzi yemwe amene anathaŵa. Njala, kulimbirana ulamuliro, ndiponso kuthiridwa nkhondo ndi Aroma kosalekeza zinapha anthu oposa miliyoni imodzi.

Nkhondo imeneyi yomwe inathetseratu chipanduko cha Ayuda motsutsana ndi Aroma inali italengezedwa kale. Zaka makumi angapo zimenezi zisanachitike, Yesu Kristu anali ataneneratu kuti Yerusalemu adzazingidwa ndi ankhondo. Iye anati: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) Malangizo ameneŵa anali omveka bwino, ndipo otsatira a Yesu sananyalanyaze.

Wolemba mbiri wa m’zaka za zana lachinayi Eusebius wa ku Kaisareya analongosola kuti Akristu onse a ku Yudeya anatsatira chenjezo la Yesu. Pamene Aroma anazinga Yerusalemu mu 66 C.E. nachokapo osachita chilichonse, Akristu ambiri achiyuda anasamukira kumzinda wa Akunja wotchedwa Pella, wokhala m’chigawo cha Aroma cha Pereya. Chifukwa chokhala tcheru ndi zochitika za m’nthaŵi yawo ndiponso mwa kutsatira chenjezo la Yesu, iwo anathaŵa chomwe chatchedwa “kuzinga malo kwa asilikali koopsa koposa komwe kwachitikapo m’mbiri yonse.”

Lerolino, kukhala tcheru kofananako nkofunika monganso kuchitapo kanthu moyenerera. Nkhani yotsatira idzafotokoza chifukwa chake.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Godo-Foto, West Stock

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena