Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 2/8 tsamba 3-5
  • “Sichingakhale Chowona!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sichingakhale Chowona!”
  • Galamukani!—1988
  • Nkhani Yofanana
  • “Sizingakhale Zoona!”
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • Chiyembekezo Kaamba ka Akufa, Chitonthozo kwa Okhala ndi Chisoni
    Galamukani!—1988
  • Tikapirira Mavuto Tidzadalitsidwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Ena Angathandize Motani?
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 2/8 tsamba 3-5

“Sichingakhale Chowona!”

“MAY 31, 1982, linali tsiku lokongola. Dzuŵa linkawala, m’mwamba munalibe mitambo, ndipo ndinalingalira kuti uwu ukakhala mwaŵi wabwino wa kuyeretsa bwalo. Tinali titangodula kumene Chinese elm yakale, ndipo panali padakali timitengo ndi nthambi zosiidwa pa kapinga. Kenaka ndinakumbukira kuti bwenzi lathu George anali ndi chochotsera zinyalala chomwe chikakhoza kupangitsa ntchitoyo kukhala yopepuka, chotero ndinamutumira lamya.

“George anali woyendetsa ndege wozoloŵera, ndipo anakonda kuwuluka ndi ndege. Chotero sichinali chodabwitsa pamene iye anandiuza ine kuti ankapita kukatenga mabwenzi kupita nawo m’mwamba ndipo anatifunsa ngati tingakonde kukwerako ndegeyo. Mkazi wanga Dianne ndi ine tinalingalira kuti chikakhoza kupanga kusintha kwabwino pambuyo pa kuyeretsa bwalo lija. Tinapita ndi mwana wathu wamkazi wa zaka za kubadwa zitatu. Maria, mwana wokondedwa, wanzeru wokhala ndi tsitsi ndi maso osiira ndi akuda pang’ono, anali wosangalatsidwa.

“Pamene tinafika ku bwalo la ndege, bwenzi lina linkayembekezera kukweramo, chotero tonsefe tinadzipapatiza m’ndege yonyamula anthu anayiyo. Tinawuluka pamwamba pa nyanja ndi kuloza ku mapiri. Chinali chosangalatsa. Tinayang’ana kunja ndi kuwona malo ozoloŵereka. Anthu ena ankachita maseŵera pa phiri. Maria anali wosangalatsidwa. Kenaka, pamene tinkapita chapamwamba pa phiri, ndege inagwidwa ndi m’kuntho wokoka wa mphepo. Injini inaleka kugwira ntchito ndi kuzima, ndipo ndegeyo inagwa kuchokera m’mwamba!

“Chonse chomwe ndinalingalira chinali kuyesa kufika pamene panali mkazi wanga, yemwe anali ndi Maria pa manja ake, ndi mpando wa kutsogolo. Sindinakhoze kufikako—ndegeyo inakagunda pambali pa phiri.

“Ndinayesera kunyamuka koma sindinakhoze kuyenda. Ndinakhoza kumva Dianne akulira kaamba ka thandizo, koma sindinakhoze kuchita chirichonse. Chonse chomwe ndinakhoza kuchita chinali kufuula kaamba ka thandizo.

“Potsirizira pake, gulu lopereka mankhwala m’nthaŵi ya ngozi linabwera kudzatichotsa pa phirilo. Ngakhale kuti tinapanga kugwa kopanga mbiri, George ndi bwenzilo anafa. Otsalafe tinkavutika ndi kuvulala koipa. Maria anali ndi kuvulala kwa m’mutu ndi mkati. Apongozi anga achimuna anali ndi ntchito yovuta ya kubwera ku kama langa la m’chipatala kudzandiuza ine kuti iye anafa—icho chinali chopyoza ku mtima kwanga. ‘Nchifukwa ninji iye? Nchifukwa ninji sichinakhale ine? Sichiri chabwino kuti mwana wonga iye afe,’ ndinalingalira tero. Ngati kokha sindinavomere kukwera ndege kumene kuja . . .

“Dianne anali m’mkhalidwe wa kaya kaya ndi msana wothyoka. Milungu itatu pambuyo pa kugwa kumeneko, iye nayenso anafa. Ndinataikiridwa khanda langa ndi mkazi wanga pa chochitika chimodzi. Ndinalingalira kuti ndinataikiridwa chirichonse. Kodi ndikakhoza kupulumuka motani?”—Monga momwe yasimbidwira ndi Jess Romero, New Mexico, U.S.A.

“Mwana wanga wamwamuna Jonathan anapita kutali pa Long Island kuchezera mabwenzi. Mkazi wanga, Valentina, sanakonde kuti iye apite kutali kumeneko. Iye anali wa mantha nthaŵi zonse ponena za magalimoto. Koma mwanayo anakonda za magetsi, ndipo mabwenzi ake anali ndi malo ogwirirako ntchito komwe iye akakhoza kupeza kuyeneretsedwa kogwira ntchito. Ndinali panyumba mu West Manhattana. Mkazi wanga anali kutali kuchezera banja lake mu Puerto Rico.

“Ndinkawodzera kutsogolo kwa TV. ‘Jonathan adzabwera mwamsanga,’ ndinalingalira tero. Kenaka belu la pa khomo linalira. ‘Ameneyo afunikira kukhala iye motsimikizirika.’ Iye sanali. Anali apolisi ndi a dokotala owuluka ndi ndege.

“‘Kodi mukuizindikira laisensi yoyendetsera galimoto iyi?’ nduna ya apolisi inafunsa tero. ‘Inde, imeneyo iri ya mwana wanga, Jonathan.’ ‘Tiri ndi mbiri yoipa kaamba ka inu. Kunali kwachitika ngozi, ndipo . . . mwana wanu, . . . mwana wanu wamwamuna waphedwa.’ Kuyankha kwanga koyambirira kunali, ‘No puede ser! No puede ser!’—sichingakhale chowona!

“Ngozi imeneyo inatsegula bala m’mitima yathu lomwe likalipobe, chifupifupi zaka ziŵiri pambuyo pake.”—Monga momwe yasimbidwira ndi Agustín Caraballoso, New York, U.S.A.

“Kubwerera ku Spain mu 1960, tinali banja lachimwemwe—mosasamala kanthu za chizunzo cha chipembedzo kaamba ka kukhala Mboni. Panali María, mkazi wanga, ndi ana athu atatu, David, Paquito, ndi Isabel, a zaka zakubadwa 13, 11, ndi 9 onsewo.

“Tsiku lina mu March 1963, Paquito anabwera kunyumba kuchokera ku sukulu akudandaula za kumva mutu kuŵaŵa kwambiri. Tinadabwitsidwa ponena za chimene chikakhala chochititsa—koma osati kwa nthaŵi yaitali. Maora atatu pambuyo pake iye anafa. Kutha kwa mwazi wa munkolofupa kunatenga moyo wake.

“Imfa ya Paquito inachitika zaka 24 zapitazo. Ngakhale kuli tero, kuŵaŵa kozama kwa kutaikiridwa kumeneko kwakhalabe ndi ife kufikira ku tsiku lino. Palibe njira iriyonse imene makolo angataikiridwe mwana ndi kusadzimvera kuti iwo ataikiridwa chinachake cha iwo eni—mosasamala kanthu za unyinji wa kupita kwanthaŵi kapena ndi unyinji wa ana ena omwe iwo angakhale nawo.”—Monga momwe yasimbidwira ndi Ramón Serrano, Barcelona, Spain.

Izi ziri kokha zochepa za ngozi mamiliyoni angapo zomwe zimakantha mabanja kuzungulira dziko lonse. Monga mmene makolo okhala ndi chisoni ambiri adzachitira umboni, pamene imfa yatenga mwana wanu, iyo mowonadi imakhala mdani.—1 Akorinto 15:25, 26.

Koma kodi ndimotani mmene anthu oferedwa amenewa anakhozera m’nkhani zomwe zangotchulidwazo? Kodi umoyo wa nthaŵi zonse ungakhale wothekera nkomwe pambuyo pa kutaikiridwa koteroko? Kodi pali chiyembekezo chirichonse chakuti tingakhoze kuwona otaikiridwa okondedwa athu kachiŵirinso? Ngati ndi tero, ndi kuti ndipo motani? Awa ndi mafunso ena olinganako adzalingaliridwa m’nkhani zotsatirapozi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

The Daily Herald, Provo, Utah

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena