Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 2/8 tsamba 5-10
  • “Kodi Ndingakhale Bwanji ndi Chisoni Changa?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Ndingakhale Bwanji ndi Chisoni Changa?”
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chisoni Chimatenga Utali Wotani?
  • Nchifukwa Ninji Kudzimva wa Mlandu, Wokwiya, ndi Wopatsa Mlandu?
  • Kuyang’anizana ndi Kutaikiridwa kwa Mwana Wobadwa Wakufa Kale
  • Chinsinsi ndi Chisoni cha Imfa ya Mwadzidzidzi
  • Agogo Nawonso Amamva Chisoni
  • Kodi Nkwachibadwa Kumva Mwanjira Imeneyi?
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • Kodi Ndingakhale Motani ndi Chisoni Changa?
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • Mavuto Amene Mungakumane Nawo
    Galamukani!—2018
  • Mfundo Zothandiza Amene Aferedwa
    Galamukani!—2018
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 2/8 tsamba 5-10

“Kodi Ndingakhale Bwanji ndi Chisoni Changa?”

NGOZI inakantha Bob ndi Diane Krych zaka 18 zapitazo. Mwana wawo wamwamuna wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa, David, anali ndi vuto lobadwa nalo la mtima. Diane akulongosola nkhaniyo:

“Dokotala analingalira kuti tichite kufufuza mkati mwa chaka chimodzi kapena kuposerapo, ku chimene tinavomereza. David anali wodzala ndi umoyo, chifupifupi wachangu moposerapo. Ndimakumbukira kuti panali pa January 25, ndipo David ankavuta mlongo wake, kusokoneza zinthu m’chipinda chake. Pamene iye anafunsa ngati akakhoza kupita kunja kukaseŵera, ndinamlola iye kupita.

“Nthaŵi ina pambuyo pake ndinamva ambulansi, ndipo kenaka bwenzi la pafupi nane linadza likuthamanga, ndi kufuula kuti, ‘Diane, ali David, ungachite bwino utadza!’ Ndinapita kunja, ndipo ndinamuwona pamenepo ali gone wotambalala pa mpando wa galimoto yomwe inamugunda iye. Sindinakhoze kuyenda. Ndinadzimva monga ngati kuti ndinali ndi ziwalo zosagwira ntchito. Anapita naye mu ambulansiyo. Koma chonsecho chinali pachabe. Mtima wake waung’onowo unaleka kugwira ntchito ndipo anafa.”

Galamukani!: “Kodi kutaikiridwa koipaku kunakuyambukirani motani?”

Diane: “Ndinapita mu unyinji wa zochitika—kusalankhula, kusakhulupirira, kudzipatsa mlandu, ndi kukalipa kulinga ku mwamuna wanga ndi dokotala kaamba ka kusalingalira kuwopsya kumene mkhalidwe wake unali. Ndinali wokwiitsidwa kwambiri ndi David tsiku limenelo. Ndinali ndi alendo omwe ankadza kudzadya ndi khanda la milungu khumi ya kubadwa lofunikira kusamalira. Izo zinalidi zochulukira. Ndipo kenaka chinthu chotsatira ndinadziŵa, chinali chakuti ankatenga David wanga ku chipatala.

“Sindinakhulupirire kuti iye anafa. Sindinakhoze kulandira mawu akuti ‘kufa’ ndi ‘imfa.’ Kwa ine, iye anali atapita kutali paulendo. ‘Iye ali wamoyo mu chikumbukiro cha Mulungu ndipo adzabwera,’ ndinalingalira tero. Chotero chifupifupi milungu isanu ndi iŵiri pambuyo pa kufa kwake, ndinayamba kulemba makalata kwa iye. Ndinalemba makalata amenewo kwa zaka 13!”

Kodi Chisoni Chimatenga Utali Wotani?

Dongosolo la chisoni chotalikira la Diane limachirikiza chimene Dr. Arthur Freese amalongosola mu bukhu lake lakuti Help for Your Grief: “Akatswiri ambiri amadzimva kuti kutaikiridwa kwa mwana kumatulutsa kutaikiridwa kosatha mwa makolo, makamaka amayi.”

“Chisoni chimabweranso ndi kusinthasintha kwa zaka” kunali kulongosola kodzimva kwa Shelley wolemba ndakatulo. Zokumbutsa za chaka ndi chaka za wokondedwa wakufayo zimakonzanso chatsopano kuŵaŵako. Anthu mamiliyoni angapo lerolino angatsimikizire chimenecho ndi kufunsa kuti, m’chenicheni, ‘Kodi ndingakhale bwanji ndi chisoni changa?’ Komabe chisoni chiri dongosolo la kuchira pang’onopang’ono, ngakhale kuti mwinamwake sichimatha. Chisoni choŵaŵa chimatha, ngakhale kuti malingaliro akutaikiridwa amakhalabe.

Lingaliro limeneli latsimikiziridwa ndi Harold ndi Marjorie Bird a ku Britain omwe anataikiridwa mwana wawo wa mwamuna wa zaka zakubadwa 19, Stephen, pamene anamira m’madzi zaka khumi zapitazo. Kupangitsa nkhaniyo kuipirako, iye anali mwana wawo wobadwa yekha, ndipo mtembo wake sunapezedwe. Harold akunena ponena za dongosolo la chisoni kuti: “Chanenedwa kuti nthaŵi imachiritsa, koma m’chenicheni imangodzetsa chikumbukiro cha wokondedwayo. Kuchiritsa kokha kudzadza pamene tidzakumana naye kachiŵirinso mu chiukiriro.”

Phunziro la sayansi limodzi la kuferedwa linalongosola dongosolo la chisoni monga zotsatirapozi: “Woferedwayo angasinthe kwadzawoneni ndipo mwamsanga kuchokera ku mkhalidwe wa kudzimva kwina ndi kupita ku unzake, ndipo kupewa zokumbutsa za woferedwayo kungasinthane ndi kukulitsa mwadala zikumbukiro pa nyengo ina ya nthaŵi. Anthu mwachisawawa amayenda kuchokera pa mkhalidwe wa kusakhulupirira ku kulandira kwapang’onopang’ono kwa zenizeni za kutaikiridwa.”

Dr. Freese wabweretsa kuwunikira m’nkhani yovutayi. “Wina afunikira nthaŵi zonse kupezanso chiyembekezo—kuzindikira kuti unyinji wa omwe amavutika ndi chisoni ndi kuchita ndi kuferedwa . . . amadza kudzera kumbali ina, kuchira ndi kupitirizabe m’mkhalidwe wa kuthupi umodzimodziwo mu umene kuŵaŵa ndi kuvutika kwa chisoni kunayambira.”

M’chenicheni, m’nkhani zambiri munthu angangopyola wamphamvu. Nchifukwa ninji zimenezo ziri tero? Chifukwa chakuti chokumana nacho cha chisoni chaphunzitsa kumverera chifundo—kumvetsera kwabwino ndi kuzindikira kwa awo omwe aferedwa. Ndipo popeza kuti kumvera chifundo kumapitirira pa kumvera chisoni, wopulumuka kuvutika maganizoko amadzakhala chuma, m’phungu, wotonthoza ena omwe amavutika ndi kutaikiridwa kwa wokondedwa. Monga chitsanzo, Bob, yemwe mwana wake David anafa kaamba ka kulephera kwa mtima, ananena kuti: “Tapeza kuti kuthandiza ena kupirira ndi katundu wawo wa kuvutika mtima kwapeputsanso kwathu komwe.”

Nchifukwa Ninji Kudzimva wa Mlandu, Wokwiya, ndi Wopatsa Mlandu?

Katswiri m’chigawo cha za chisoni watsimikizira kuti zochitika za kudzimva wa mlandu, kukwiya, ndi kupatsa mlandu zomwe kaŵirikaŵiri zimagwirizanitsidwa ndi woferedwa ziri zoyenera kaamba ka mkhalidwewu. Opulumuka amayesa kupeza zifukwa pamene kaŵirikaŵiri palibe zirizonse zomwe ziri zokhazikika kapena zanzeru. ‘Nchifukwa ninji icho chinayenera kuchitika kwa ine? Kodi ndachitanji kotero kuti ndichiyenerere? Ngati kokha ndikana . . . ’ kuli kuyankha komwe kuli kofala. Ena amatembenukira Mulungu ndi malingaliro onga ngati, ‘Nchifukwa ninji Mulungu anachilola ichi kuchitika? Nchifukwa ninji Mulungu anachita ichi kwa ine?’

Pano yankho la Baibulo limabwera ku malingaliro, “Nthaŵi ndi zochitika zosawonedweratu zimagwera iwo onse.” Ngozi ingachitike kulikonse, panthaŵi iriyonse, ndipo imfa iribe tsankho. Ndithudi Mulungu wa chikondi sangakhoze kusankha aliyense mwakutenga mwana wake.—Mlaliki 9:11; 1 Yohane 4:8.

Agustín ndi Valentina, omwe atchulidwa m’nkhani yathu yotsegulira, analirabe pamene anakambitsirana imfa ya Jonathan ndi Galamukani! Kodi iwo anali ndi kupatsa mlandu kulikonse? Valentina akuyankha kuti: “Sindinakhoze kuvomereza kuti apite ku Long Island m’galimoto la winawake. Ndifunikira kukhala wowona mtima. Ndinaika mlandu pa Agustín. Tsopano ndikuzindikira kuti kunali kuyankha kosasankha, koma panthaŵiyo ndinapitirizabe kulingalira kuti, ‘Ngati kokha Atate wake sanamulole iye kupita, iye akanakhalabe wamoyo.’ Ndinapitirizabe kumpatsa mlandu. Ndinafunikira kuchitulutsa chifukwa chakuti chinandivulaza kuchisunga mkati.”

Ukali wa Diane Krych pa imfa yosayembekezereka ya David unakhoza ngakhale kudzilongosola wokha mu kukalipira zinyama. Iye anauza Galamukani!: “Nditawona galu kapena mphaka akuyenda m’khwalala, ndinadzimva kuti, ‘nyama imene ija iri ndi mtima wabwino womwe ukugunda mkati mwake. Nchifukwa ninji mwana wanga wamwamuna sanakhale ndi mtima wabwino? Nchifukwa ninji nyama ingadziyenda uku ndi uko ndipo osati David wanga?’”

Akatswiri anatitsimikizira ife kuti zotulukapo zonsezi, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri zimakhala zosasankha, ziri zachibadwa. Kufunsa kuli mkhalidwe wa kulinganiza, mbali ya dongosolo la kugwirizanitsa ndi zenizeni. Potsirizira pake, kawonedwe kokhazikika kamapezedwa, ndipo nzeru zenizeni zimafalikira. Monga mmene Dr. Freese wachiikira icho kuti: “Kuyesa kwa chisoni chabwino—kwa kugwira mokwanira pa mavuto a malingaliro a kulira ndi chisoni, akulandira imfa ndi kuyang’ana mowona mtima pa malingaliro onse omwe amapita ndi izo—kuli kwakuti wolira potsirizira pake amangolekerera nthaŵi zoipa zimenezi ndi kuŵaŵa kopitirira kapena kokha ndi malingaliro ochepa, ozirara, a chisoni.”

Ichi chimatsogolera ku kutha kwake. Dr. Freese akupitiriza kuti: “Zenizeni ziri kudzibweza ndi malingaliro osangalatsa, ndi mphamvu za kulankhula ponena za wakufayo m’mkhalidwe wowona mtima ndi wachikondi, potsirizira pake kutenga malo oŵaŵawo ndi kumvera chisoni ndi mavuto.” Pa nsongayi, zikumbukiro zimasonkhezera chikondi mokulira kupambana kumvera chisoni.

Kuyang’anizana ndi Kutaikiridwa kwa Mwana Wobadwa Wakufa Kale

Ngakhale kuti anali kale ndi ana ena, Monna ankayang’ana kutsogolo ndi chikondi ku kubadwa kwa mwana wake wotsatira. Ngakhale pamene kubadwa kusanachitike, iye anali “khanda lomwe ndinakhoza kuseŵera nalo, kulankhula nalo, ndi kulilota.”

Dongosolo la chomangira la pakati pa amayi ndi mwana wosabadwa linali lamphamvu. Iye akupitiriza kuti: “Rachel Anne anali khanda lomwe linakhoza kukantha mabukhu m’mimba mwanga, linandisunga ine kukhala wogalamuka usiku. Ndingakhozebe kukumbukira kumenya kwake kwakung’ono koyambirirako, konga kukankha kofewa, ndi kwa chifundo. Nthaŵi iriyonse pamene iye anayendayenda, ndinadzazidwa ndi chikondi choterocho. Ndinamudziŵa iye bwino kwambiri chakuti ndinadziŵa pamene iye ankamva kuŵaŵa, pamene iye anali kudwala.”

Monna akupitiriza nkhani yake kuti: “Dokotala sanakhoze kundikhulupirira, kufikira pamene chinali kuchedwa. Iye anandiuza ine kusadera nkhaŵa. Ndimakhulupirira kuti ndinamumva iye akufa. Iye anangotembenuka mwachiwawa. Tsiku lotsatira anafa.”

Chokumana nacho cha Monna sichiri chochitika cha pa kanthaŵi. Kulingana ndi akonzi Friedman ndi Gradstein, m’bukhu lawo Surviving Pregnancy Loss, chifupifupi miliyoni imodzi ya akazi chaka chirichonse mu United States mokha amavutika ndi mimba zowonongeka. Anthu kaŵirikaŵiri amalephera kuzindikira kuti kupita padera kapena kubala mwana wakufa kale kuli ngozi kwa mkazi, ndipo amakhala ndi chisoni—mwinamwake moyo wake wonse. Mwachitsanzo, Veronica, wa ku New York City, yemwe tsopano ali m’zaka zake za ma-50, amakumbukira kutaya mimba kwake ndipo amakumbukira makamaka mwana yemwe anabadwa wakufa kale yemwe anali wa moyo m’mwezi wa chisanu ndi chinayi ndipo anabadwa wolemera mapaundi 13 (6 kg). Iye anamunyamula ali wakufa mkati mwake kwa milungu iŵiri yolekezera. Monga mmene iye ananenera: “Kubala mwana wakufa chiri chinthu choipa kwa amayi.”

Zotulukapo za amayi okhumudwitsidwawa sizimamvetsetsedwa nthaŵi zambiri, ngakhale ndi akazi ena. Dokotala wa odwala maganizo yemwe anataikiridwa mwana wake mwa kupita padera analemba kuti: “Chomwe ndaphunzira m’njira yoŵaŵa kwambiri chinali chakuti pamene ichi chisanachitike kwa ine, ndithudi ndinalibe lingaliro la chimene mabwenzi anga ankapirira. Ndinali wosalingalira ndipo mbuli kulinga kwa iwo monga mmene tsopano ndikudzimverera mmene anthu aliri kwa ine.”

Vuto lina kwa mayi womva chisoni liri kawonedwe kakuti mwamuna wawo sangakhoze kumva kutaikiridwa monga mmene iye amachitira. Mkazi wina anachilongosola icho mwanjirayi: “Ndinagwiritsidwa mwala kotheratu ndi mwamuna wanga panthaŵiyo. Kulingana ndi mmene iye anadziŵira, panalibe mimba. Iye sanakumane ndi chisoni chimene ine ndinkapitamo. Iye anali womvera chifundo ku mantha anga koma osati ku chisoni changa.”

Kuyankha kumeneku kuli mwinamwake kwachibadwa kwa mwamuna—iye samakumanizana ndi chomangira chimodzimodzi chakuthupi ndi cha malingaliro chimene mkazi wake wa mimbayo amakhala nacho. Ngakhale kuli tero, iye amavutika ndi kutaikiridwa. Ndipo chiri chofunika kwambiri kuti mwamuna ndi mkazi azindikire kuti iwo akuvutikira pamodzi, ngakhale kuti chiri m’njira zosiyana. Iwo ayenera kugawana chisoni chawo. Ngati mwamuna achibisa icho, mkazi wake angalingalire kuti iye sakulingalira. (Onani tsamba 12.) Chotero gawanani misozi yanu, malingaliro, ndi kumpsompsonana. Sonyezani kuti mumafunana wina ndi mnzake kuposa ndi kalelonse.

Chinsinsi ndi Chisoni cha Imfa ya Mwadzidzidzi

Amayi mamiliyoni angapo amakhala ndi chinsinsi, cha mantha a tsiku ndi tsiku. Monga mmene mayi wina anachilongosolera icho: “Ndimapemphera usiku uliwonse kuti ndipeze khanda langa liri lamoyo m’mawa.” Chimene iwo amawopa chiri imfa ya mwadzidzidzi, kapena SIDS (Sudden Infant Death Syndrome). Dr. Marie Valdes-Dapena, profesala wa zizindikiro za matenda pa Yuniversite ya Miami, Florida, walongosola kuti pali matenda 6,000 kufika ku 7,000 a SIDS chaka chirichonse mu United States mokha. Iye wawonjezera kuti: “Palibe chikaikiro chirichonse chakuti iri liri vuto lenileni la umoyo waunyinji.”

Imfa ya mwadzidzidzi imatenga makanda usiku, kaŵirikaŵiri pakati pa mwezi wachiŵiri ndi mwezi wachinayi wa moyo. Sayansi sinabwerebe ndi kulongosola kokwanira, ndipo ngakhale ofufuza mitembo alephera kupereka chifukwa kaamba ka imfa ya mwadzidzidzi. Iyo ikukhalabe chinsinsi.a

Chotulukapo ku imfa ya mwadzidzidzi chiri kaŵirikaŵiri kudzimva koipa kwa kupatsidwa mlandu. Chotero, kodi nchiyani chimene chidzathandiza makolo m’nkhani za imfa ya mwadzidzidzi? Choyamba cha zonse, iwo ayenera kuzindikira kuti iwo sakanakhoza kupewa tsokalo. SIDS iri yosaloseredwa ndipo kaŵirikaŵiri simapewedwa. Chotero, palibe chifukwa chirichonse cha kukhalira ndi malingaliro akudzipatsa mlandu. Chachiŵiri, kuchirikiza kwa makolo kwa ku mtima, kudalira, ndi kumvetsetsa kudzathandiza onse aŵiri kuchita ndi chisoni chawo. Lankhulani ponena za khanda lanu ndi ena. Gawanani malingaliro anu.

Agogo Nawonso Amamva Chisoni

Agogo amavutika nawonso, m’njira yapadera. Monga mmene atate woferedwa wina analongosolera icho kuti: “Iwo amayankha osati kokha ku imfa ya m’dzukulu komanso ku chisoni cha mwana wawo.”

Komabe pali njira zina za kupangitsira kutaikiridwa kwa agogo kukhala kopepuka. Choyamba, alingalireni iwo. M’dzukulu wawo anali mbali ya iwo nayenso. Chotero agogo ayenera kulandiridwa m’dongosolo la kumva chisoni m’njira yawo yeniyeni. Ndithudi, icho sichimatanthauza kuti iwo afunikira kupitiriza popanda chivomerezo cha makolo. Koma ngati iwo afuna kuti aphatikizidwemo ndipo nthaŵi zambiri iwo amatero, afunikira kulandiridwa.

Mu kukwaniritsidwa kwachidule kwa kumva chisoniku, tayesera kumvetsetsa kudzimva kwa oferedwa. Koma padakali mbali ina yomwe tiyenera kulingalira. Kodi ndimotani mmene ena angathandizire, makamaka ndi kalankhulidwe kawo? Ndipo kodi ndimotani mmene amuna angalongosolere kumva chisoni kwawo? Chonde onani nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Kope lakutsogolo la Galamukani! lidzalongosola SIDS mwatsatanetsatane.

[Bokosi patsamba 7]

Dongosolo la Chisoni

Ichi sichimalingalira kuti kumva chisoni kuli ndi ndandanda yokhala ndi polekezera kapena programu. Zochitachita za kumvera chisoni zingapitirire ndipo zingatenge utali wosiyanasiyana wa nthaŵi, kudalira pa munthuyo.

Zotulukapo zoyambirira:

Kuwopsya koyambirira, kusakhulupirira, kukana; kusalankhula; malingaliro opatsidwa mlandu; ukali

Chisoni chachikulu chingaphatikize:

Kusoweka kwa chikumbu mtima ndi kusowa tulo; ulesi waukulu; kusintha kwamwadzidzidzi kwa makhalidwe; chiweruzo ndi kulingalira kophophonya; nyengo za kufuna kulira; kusinthasintha kwa chilakolako cha zakudya, ndi kusoweka kwa kulemera kwa thupi kapena kukupeza; zizindikiro zosiyanasiyana za kusokonezeka kwa umoyo; kusoweka kwa chikondwerero; kuchepetsedwa kwa mlingo wa kugwira ntchito; kuwona zideruderu—kudzimva; kumvera, ndi kuwona wakufayo

Nyengo ya kutha kwa chisoni:

Kukalipa ndi kudzimva wodwala; zikumbukiro zosangalatsa za wakufayo, zokhoza kusonkhezeredwa ngakhale ndi nthabwala

(Zozikidwa pa Help for Your Grief, lolembedwa ndi Dr. Arthur Freese, masamba 23-6.)

[Bokosi patsamba 9]

Njira za Kukuthandizani Kugonjetsa Chisoni Chanu

Munthu aliyense afunikira kugwira ntchito ndi chisoni m’njira ya iyemwini. Njira yofunika kwambiri iri kupewa kusowa chochita kodzidalira ndi kudzimvera chifundo. Malingaliro ena ozikidwa pa zokumana nazo za anthu oferedwa ofunsidwa ndi Galamukani! ali:

◼ Dzisungeni otanganitsidwa ndi kupitiriza kugwira ntchito kwanu kwa nthaŵi zonse ndi zochitachita. Awo omwe ali Mboni za Yehova amagogomezera makamaka phindu la kupezeka pa misonkhano Yachikristu ndi kukhala wodzilowetsa mu utumiki. Ambiri alongosola chithandizo chachikulu chomwe alandira kuchokera ku pemphero.

◼ Lolani chisoni chanu chidziwonetsere icho cheni; musayese kuchisungirira mkati. Kufulumira kumene mudzamvera chisoni ndi kulira, kudzakhala kufulumiranso komwe inu mudzapyola nyengo ya kumva chisoni kowopsyako.

◼ Musadzipatule inu eni; sanganizanani ndi anthu ndipo aloleni kusanganizana ndi inu. Ngati chingakuthandizeni, lankhulani mwaufulu ponena za wokondedwa wanu wakufayo.

◼ Mwamsanga monga momwe chingathekere, khalani ndi chikondwerero mu anthu ena ndi mavuto awo. Yesani kuthandiza ena, ndipo mudzazithandiza inu eni.

[Bokosi patsamba 10]

Kodi Ena Angachitenji kuti Athandize?

Alembi a Galamukani! anafunsa makolo ambiri oferedwa m’maiko osiyanasiyana. Otsatirawa ali malingaliro ena omwe anapangidwa kaamba ka kuthandiza mabanja a chisoni. Ndithudi, pafunikira kukhala kukhazikika pa kuwagwiritsira ntchito, kudalira pa kudzimva kwa oferedwawo.

1. Chezerani ndi banja kuchokera pa tsiku loyambirira lenilenilo, ndiponso aitaneni iwo ku malo anu. Konzekerani chakudya kaamba ka iwo. Pitirizanibe kuchita ichi ku utali womwe ungafunike, osati kokha milungu ingapo yoyambirira.

2. Lolani makolo asankhepo kaya angafune zovala ndi zokumbutsa zina za mwana wakufayo kuti zisungidwe kapena kuikidwa kwinakwake.

3. Lankhulani ponena za mwana wakufayo mwa kumutchula dzina ngati woferedwayo akuwonetsa kukhala ndi chikhumbo chotero. Kumbukirani mbali zosangalatsa ndi zachimwemwe za umunthu wa mwanayo ndi umoyo. Musakhale chete. Makolo angakhale akufuna kulankhula ponena za wokondedwa wawo.

4. Ngati muli kutali kwambiri osakhoza kupereka chithandizo mwaumwini, lembani makalata omwe angakhoze kulimbikitsa ndi kutonthoza. Musapewe nkhani ya munthu wakufayo.

5. Pamene kuli koyenera, limbikitsani makolo kukhala achangu ndi kusungirira kachitidwe kawo koyambirira. Aloleni iwo kuchoka panyumba ndi kuchita zinthu zina kaamba ka ena.

[Bokosi patsamba 10]

Gogo Wachikazi Akulemba kuti:

“Kukhala nditataikiridwa mu imfa makolo anga okondedwa, mbale, mlongo, mnzanga wodzipereka kwanthaŵi yaitali, mwamuna wanga bwenzi lokondedwa la pamtima, Jim wanga, yemwe ndinakumana naye ndi kukonda pa zaka zakubadwa 13, ndi m’dzukulu wanga wam’ng’ono wofunika kwambiri Stuart Jamie—ndingakhoze kunena kuti palibe chisoni, palibe kuŵaŵa, palibe chisoni chozunza, chomwe chimasefukira pa ine ngakhale pamene ndilemba, monga imfa ya mwana.”

—Edna Green, England, pa imfa ya m’dzukulu wake, yemwe anali ndi zaka ziŵiri ndi miyezi isanu ndi inayi ya kubadwa.

[Chithunzi patsamba 8]

Mwa kugawana mowonekera chisoni chanu, mumathandizana wina ndi mnzake kuchita nacho

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena