Kugwiritsira Ntchito Mutu Wanu—Njira ya chiAfrica!
Ndi mlembi wa “Galamukani!” mu Sierra Leone
KODI nchiyani chimene anthu amanyamula pa mutu pawo? Mutafunsa ana opita ku sukulu funso limenelo, m’mbali zambiri za dziko iwo angayankhe kuti: “Zisote zawo.” Ndipo chimenecho mwachidziŵikire chikakhala kutha kwa ndandanda yawo.
Komabe, pamene kwenikweni tinafunsa funso limenelo kwa achichepere ena a ku Africa, iwo anayankha kuti: “Anthu amanyamula pa mutu migomo ya madzi, nthochi, mabukhu, matumba a mchere, nkhuni, mawailesi a kanema, nsomba, matumba a simenti, matumba a mpunga, zoziziritsa zakudya, madengu a ndiwo za masamba, miyala, monyamulira zakumwa zoziziritsa . . . ” Ndandanda yawo inangopitirizabe osatha.
Kuzungulira kontinenti yonse ya Africa, kunyamula mitokoma pa mutu kuli kofala. Iko kwakhalapo kwanthaŵi yaitali. Baibulo limatidziŵitsa ife kuti kubwerera m’mbuyo m’masiku a Yosefe, opanga mkate a ku Aigupto ankanyamula mkate pa mitu yawo. Ndipo chimenecho chinali zaka 3,700 zapitazo!—Genesis 40:16, 17.
Kodi Mungadendekere?
Kodi mwakhala mutawonapo kale anthu omwe ali akatswiri pa kusenza pamutu? Kwa iwo chiridi chosavuta monga kunyamula chinthu ndi dzanja.
Koma kuyeseni iko. Mwachitsanzo, ikani bukhu pa mutu wanu ndipo yeserani kuyenda. (Tingapereke malingaliro akuti mugwiritsire ntchito bukhu lomwe simungasamale ngati litagwedezedwa pang’ono.) Ngati inu muli wophunzira, inu mwachiwonekere mudzayenda pang’onopang’ono, mowongoka, mosamala kwenikweni, kotero kuti musasokoneze kukhazikika kovutako. Phazi limodzi . . . aŵiri . . . Mofulumira! Gwirani bukhulo lisanagwere pansi!
“Koma,” inu mungatsutse, “mutu wanga suli wosalala. Kodi mungandiyembekezere ine bwanji kukhazikitsa bukhu losalala pa mutu wowulungana?” Yankho limodzi liri: Kuzoloŵera! Yankho lina liri: Gwiritsirani ntchito nkhata. Nkhata iri nsalu kapena masamba omwe amapindidwa ndi kuzungulitsidwa kuti apange chinthu chozungulira monga mphete. Iyo imaikidwa pakati pa katundu ndi mutu kuti itumikire monga chotetezera ndi kuthandiza kukhazikitsa katundu wolimba, wonga ngati nkhuni. Kaamba ka zinthu zofewa, monga ngati matumba a ufa, nkhata simakhala yoyenera chifukwa chakuti thumbalo lidzakhala bwino pa mutu.
Kaya mumagwiritsira ntchito nkhata kapena ayi, chiri chofunika kunyamulira zinthu pakati pa mutu wanu. Edward, wa ku Sierra Leone, amakumbukira masiku ake oyambirira: “Pamene choyamba ndinayamba kusenza, ndinanyamulira nkhuni zolemera mbali imodzi pa mutu wanga. Pamene katunduyo analemera, khosi langa linayamba kuŵaŵa kaamba ka kupanikizako. Koma vuto lenileni linadza pamene ndinayamba kusenza migomo ya madzi. Popeza kuti simungakhazikitse madzi bwino lomwe kusiyapo kokha ngati mutu wanu uli wosalala, madzi anakhoza kugavikira pansi, ndipo zovala zanga zinanyowetsedwa. Ndinachida chimenecho. Kunali kunyowetsedwa, koposa china chirichonse, komwe kunandipangitsa ine kuwongokera.”
Komabe, pali zambiri ku luso kuposa kukhazikitsa bwino chinthu pakati kuti chinyamulidwe. Wonyamulira pa mutu wozolowera adzasunga zinthu m’malo mwake pa mutu pake mwanjira zosiyanasiyana, ndi kugwedeza khosi pang’ono kwa kuwongolera. Kuli monga kuyesa kulinganiza chikuni chowongoka pa chala chanu. Inu simumangochiika pamenepo ndi kuyembekezera kuti sichidzagwa. M’malo mwake, inu mufunikira kusinthasintha kakhazikitsidwe ka chala chanu mopitirizabe kuti mugwirizane ndi kuyendayenda kwa chikunicho. Ndipo monga mmene chikuni cholemera chiriri chothekera kuchikhazikitsa kuposa chopepuka, choteronso katundu wolemera amakhala wopepuka kaŵirikaŵiri kukhazikitsa pamutu.
Anthu a ku Africa ambiri amaphunzira ntchito mofulumira m’moyo mwa kutsatira ana a akulu ndi achikulire. Emmanual ali ndi chaka chakubadwa chimodzi ndi theka ndipo wosakhozabe kuyenda bwino. Pamene anapatsidwa m’gomo waung’ono wa madzi kuti anyamule, iye anawuika pamutu pake ndi manja ake onse aŵiri. Iwo unagwedera uku ndi uko, ndipo ena a madzi anagwera pansi, koma chinali chowonekera kuti iye anadziŵa lingaliro. Panthaŵi imene adzakhala wa zaka zisanu, madzi sadzagavira. Pa zaka zisanu ndi ziŵiri iye adzakhala katswiri.
Luso Lopindulitsa, Lokhoza Kugwirirapo Ntchito
Kutalitali ndi kukhala njira ya maseŵera ya kunyamula zinthu, kunyamula zinthu pa mutu liri luso logwira ntchito kaamba ka umoyo wa mu Africa. The Cambridge Encyclopedia of Africa yalongosola kuti: “Kunyamula zinthu kwa munthu . . . mosakaikira kukalidi chimodzi cha zothandiza za ku Africa za kunyamulira zinthu pamlingo wa kumaloko.” Ndipo kwa awo omwe ali ozoloŵerana ndi iyo, katundu amanyamulidwa mopepuka kwambiri pamutu.
Woyang’anira woyendayenda mmodzi wa Mboni za Yehova akulongosola kuti: “M’mizinda yambiri ndi m’midzi kumene ndimachezera kungafikiridwe ndi magalimoto, koma ina singathe. Iyi ingangofikiridwa kokha ndi ngolo. Nthaŵi zambiri, Mboni zinzanga kumeneko zimadzakumana ndi ine ndi kundithandiza kunyamula zola zanga ndipo njira yopepuka kwambiri ya kunyamulira izo iri pamutu. Panthaŵi zina, pamene ndikuyenda pandekha, ndimanyamula chola m’dzanja lina ndipo kukoloweka china ndi nthambo zake pa phewa lina la mkono wina, koma chola chachikulu koposa chimapita pamutu panga.”
Pambali pa kunyamula zinthuzi mopepukira, kuika zinthu pamutu kumasiya manja anu kukhala aufulu. Inu mungakhale ndi mthunzi kuchokera ku dzuŵa kapena kuchinjirizidwa ku mvula.
Wonjezerani ku ichi mapindu akuthupi: chisomo, kukhazikika, ndi mphamvu. Bukhu lakuti Tropical Surgery lalongosola kuti: “Anthu a m’dziko [kumbali yotentha], omwe kaŵirikaŵiri ali ozoloŵerana ndi kuyenda ndi katundu ali pamutu, akulitsa bwino lomwe mphamvu za kumsana ndi kaimidwe kabwino. Iwo samavutika kaŵirikaŵiri ndi kuŵaŵa kwa msana.”
Mwachiwonekere, kunyamulira pamutu si luso lofunikira kunyalanyazidwa. Mwamuna wachichepere mu Freetown anadzimva kuti: “Ndingakhoze kuika botolo pamutu panga ndi kuthamanga ndi ilo popanda kuligwira ilo ndi manja anga.” Kuchitira chitsanzo kuthamanga kwake ndi katundu woteroyo pamutu pake kunatsimikizira kuwona kwa mawu ake. Koma kusiyapo kokha ngati muli katswiri, musakuyesa iko!