Kudzipereka Nsembe Kumabweretsa Mphoto Zolemera
‘Lynette, wokondedwa wanga,
‘Ndangofuna kukusiira iwe chidziŵitso cha kukuyamikira kaamba ka kukhala mwana wamkazi wa pamtima, wokondedwa kwa ine. Chidzakhala chovuta kwa iwe kukhala wopanda amayi, wokondedwa, koma ena adzathandiza, ndipo Atate wako adzatenga chisamaliro chabwino kwambiri cha iwe. Thandiza ang’ono ako achichepere—ndikudziŵa kuti udzatero—popeza kuti adzayang’ana kwa iwe mochulukira. Ndikufuna kunena kuti zikomo wokondedwa wa pamtima kaamba ka zonse zimene wachita kwa ine ndi pokhala mtsikana wachichepere wabwino chotere, womvera, wosandipatsa ine kudera nkhaŵa kulikonse. Ndipemphera kuti Yehova adzandikumbukira ine ndi kuti tidzakumananso tonsefe m’Dziko Latsopano.
‘Ndi chikondi chochulukira kuchokera kwa Amayi wako wokondedwa,’
NDINALI wa zaka 13 zakubadwa pamene Amayi anafa ndi kansa mu January 1963. Chifupifupi miyezi itatu imfa yawo isanachitike, anandilola ine limodzi ndi ang’ono anga achichepere kudziŵa kuti iwo anali kufa. Ndinali woyamikira kuti iwo sanasunge nkhanizo mwachinsinsi koma analongosola mkhalidwewo mwachikondi ndipo kenaka kutenga njira ya kutikonzekeretsa ife kaamba ka masinthidwe omwe ankadza.
Ngakhale kuti iwo anali pakama lawo lodwalira, Amayi anandiphunzitsa ine kuphika, ndipo ndinakonzekera chakudya chonse pansi pa chitsogozo chawo. Iwo anandisonyezanso mmene ndingagwiritsire ntchito makina osokera zovala, kumeta tsitsi la banja, kukonzekera zakudya za pamasana za opita ku sukulu, ndi kuchita ntchito zina zambiri. Iwo analongosola kuti kukhala popanda iwo, ndikafunikira kudzipereka kwaumwini kuti ndithandize ang’ono anga achichepere.
Ndimakumbukira kukhala wodabwitsidwa pa mmene Amayi anali otsimikiza. Ndimadziŵa tsopano kuti ichi chinali chifukwa cha chidaliro chawo chozama m’kuukitsidwa kolonjezedwa. Masiku oŵerengeka pambuyo pa imfa yawo, Atate anapatsa mmodzi ndi mmodzi wa atsikanafe kalata imene Amayi analemba kwa ife mwamsanga asanafe. Yomwe inalembedwa kwa ine ikuwoneka, m’mbali, pamwambapo. Inu mungayerekeze misozi yanga pamene ndinaŵerenga kalata imeneyo, koma inandilimbikitsa ine mwauzimu mosasamala kanthu za zaka zanga za chikondizo. Kokha miyezi ingapo pambuyo pa chimenecho, ndinapanga kudzipereka kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa mu August 1963.
Kukulitsa Chikhulupiriro
Makolo anga anakhala Mboni za Yehova mu 1956, chaka chimodzi pambuyo pa kusamuka kuchoka pa munda wa ng’ombe zotulutsa mkaka kupita ku Sydney, Australia. Mwatsoka, ndinakulitsa chikaikiro, chifupifupi mkhalidwe wokana Mulungu chifukwa cha njira mu imene nkhani za Baibulo zinkaperekedwera pa sukulu yochitidwa pa Sande. Ndinagwirizanitsa mwamalingaliro zochitika za m’Baibulo ndi nthano ndi nthanthi zina zomwe ndinadziŵa kuti sizinali zowona. Ndinadzakhoza ngakhale kuwona Mulungu monga kokha munthu wina wa nthanthi. Komabe, kuwona mtima kwa Mboni kunayamba kundikondweretsa ine, ndipo ndinayamba kulingalira kuti ngati iwo ndi amayi anga anakhulupirira mwa Mulungu ndi Baibulo, pafunikira kukhala chinachake ku icho.
Pamene ndinali wa zaka 11 za kubadwa, mpingo unayamba kuphunzira bukhu la “Your Will Be Done on Earth”—ndi kulongosola kwake kwa ndime ndi ndime za mbali ya bukhu la Baibulo la Danieli. Maulosi amenewa ndi njira mmene iwo anakwaniritsidwira m’tsatanetsatane wotero ndithudi anandikondweretsa ine. Misonkhano ina ya mpingo inachita ndi kugwirizana kwa Baibulo ndi sayansi yowona. Zina za zikaikiro zanga zinayamba kutha, ndipo pang’onopang’ono ndinapeza chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu.
Kudzipereka Nsembe kwa Mtundu Wina
Monga mmene Amayi ananenera, kutenga mathayo a banja ndi kuthandiza alongo achichepere aŵiri sizinali nthaŵi zonse zopepuka. Wina wa ubwana wanga unataika. Ngakhale kuli tero, chomangira chathithithi chosakhala cha nthaŵi zonse chomwe chinakula pakati pa atsikana atatufe ndi chidaliro chimene atate anga anasonyeza mwa ine chinaposa pa kulipira kokha kaamba ka ichi. Komabe panali kudzipereka nsembe kwa mtundu wina komwe kunkadza.
Mkati mwa zaka za ku sukulu, ndinakulitsa chikondi cha nyimbo ndi kuseŵera zitsanzo. Banja lathu linali lokonda nyimbo. Anafe tinkakhoza kuseŵera piano, kuimba, kuvina, ndi kuyamba makonsati kufikira titatopetsedwa. Ndinapatsidwa malo autsogoleri mu zochitachita za pa sukulu chiyambire pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Aphunzitsi anandisonkhezera ine kulembetsa m’sukulu ya zitsanzo. Koma ndinakumbukira mawu a nyimbo yomwe tinkayimba pa misonkhano yathu ya mpingo: “Monga mphatso zathu ndi maluso ku ntchito Yake timazibweretsa.” Chotero ngakhale kuti sichinali chopepuka kuchita tero, ndinapewa kusonkhezera kwawo.
Ndinasangalalanso ndi kuphunzira ndipo, monga chotulukapo, ndinalandira zotulukapo za maphunziro apamwamba. Komabe, pamene ndinasankha molimbana ndi maphunziro a pa yuniversite mwa kusankha kugwiritsira ntchito nthaŵi yanga yonse m’ntchito yolalikira, ndinaperekedwa pamaso pa nduna yoyang’anira za maphunziro a ku koleji. “Chikuwoneka monga kungotaya chabe nthaŵi,” iye anatero pamene anayesera kundisonkhezera ine kutsatira ntchito ya za mankhwala. Komabe sindinamverepo chisoni chosankha changa.
Pambuyo pa kuchoka ku sukulu, ndinagwira ntchito kwa chaka chimodzi ndi theka m’gawo latsopano la makompyuta a dipartimenti ya boma. Pamene ndinapereka kalata yanga yolekera ntchito, ndinalonjezedwa malipiro kuwirikiza kaŵiri ndi malo autsogoleri mu dipartimenti imeneyo. Uku kunali kupatsidwa koyesa, makamaka kwa munthu wa zaka 17 zakubadwa! Koma ndinamamatirabe ku chonulirapo changa ndipo ndinayamba utumiki wa nthaŵi zonse monga mpainiya wokhazikika pa June 1, 1966.
Gawo Latsopano
Pamene ndinaikidwa monga mpainiya wapadera April wotsatira, ndinasangalatsidwa mokulira kulandira gawo mu mpingo wa kumudzi kwathu mu Sydney. Ichi chinandilola ine kukhala ndi ang’ono anga kwa nthaŵi yaitali pang’ono. Ndinali woyamikira kaamba ka ichi, popeza ndinayembekeza kukhala ndi banja langa kapena pafupi ndi iwo kufikira ang’ono anga onse atakwatiwa ndi kukhazikika.
Mu 1969 ndinapatsidwa gawo ku Mpingo wapafupi wa ku Peakhurst pamodzi ndi Enid Bennett yemwe akakhala mpainiya wapadera mnzanga kwa zaka zotsatira zisanu ndi ziŵiri. Zaka ziŵiri pambuyo pake, atate wanga anasamuka kukatumikira monga mkulu kumene kunali kusowa m’mzinda waung’ono wokongola wa ku Tumut, mtunda wochepera chakum’mwera, kumadzulo kwa Sydney. Sosaite mwachikondi inagawira Enid ndi ine kumenekonso. Pa nthaŵi imeneyi mng’ono wanga wachichepere kwambiri Beverley anayamba kuchita upainiya, ndipo anatumikira limodzi nafe.
Chisoni Choipa Kuposa Imfa
Panali chifupifupi panthaŵiyi pamene chochitika cha chisoni koposa cha moyo wanga chinachitika. Mng’ono wanga Margaret ndi wotomerana naye wake anachotsedwa mu mpingo Wachikristu. Iyi inali nthaŵi yovutitsa mtima, popeza kuti tsopano chomangira chodabwitsa chomwe ndinakhala nacho ndi Margaret chiyambire imfa ya amayi wathu chinadzawonongedwa. Ndinadziŵa kuti Amayi anali m’chikumbukiro cha Yehova, malo a chisungiko kwambiri kukhalamo. Komabe mng’ono wanga—kokha panthaŵiyo—anataya chivomerezo cha Yehova. Ndinakhoza kupemphera kwa Yehova mowona mtima kuti ndigonjetse kuvulazika kwa malingaliro anga kotero kuti ndingakhoze kumtumikira iye ndi chisangalalo china, ndipo iye anayankha pemphero langa.
Kudzilekanitsa ife eni kotheratu ku kuyanjana ndi Margaret kunayesa umphumphu wathu ku makonzedwe a Yehova. Chinapatsa banja lathu mwaŵi wa kusonyeza kuti ndithudi timakhulupirira kuti njira za Yehova ziri zabwino. Ku chisangalalo chathu, chifupifupi zaka ziŵiri pambuyo pake Margaret ndi mwamuna wake anabwezeretsedwa mu mpingo. Tinazindikira zochepa ponena za chiyambukiro cha chosankha chathu champhamvu chomwe chinali nacho pa iwo, popeza kuti Margaret pambuyo pake anandiuza kuti:
“Ngati iwe, Atate, kapena Bev munawona kuchotsedwa kwathu mopepuka, ndikudziŵa motsimikizirika kuti sindikanakhoza kutenga njira kulinga ku kubwezeretsedwanso mofulumira monga mmene ndinachitira. Kukhala wolekanitsidwa kotheratu kwa okondedwa ndi kusagwirizana mwathithithi ndi mpingo kunapanga chikhumbo champhamvu cha kulapira. Mwakukhala ndekha, ndinadzazindikira kokha mmene inaliri yolakwika njira yanga ndi mmene chinaliri chowopsya kutembenukira Yehova.”
Tinadalitsidwa kachiŵirinso mwa kukhala ndi banja lonse pamodzi likutumikira Yehova. Tiri achiyamikiro chotani nanga kaamba ka chisangalalo cha potsirizira pake chomwe chinatulukapo mu kumamatira mokhulupirika ku malamulo a Baibulo!
Ukwati ndi Ntchito Yoyendayenda
Pambuyo pake ndinakumana ndi Alan, mpainiya ndi mkulu Wachikristu. Tinakwatirana mu November 1975, miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pa ukwati wa mng’ono wanga Beverley. Pambuyo pa kuchita upainiya kwa zaka ziŵiri, mu January 1978, tinaitanidwa kukagawana m’ntchito yoyendayenda, kuchezera mipingo yosiyanasiyana mlungu uliwonse kuwathandiza ndi kuwalimbikitsa mwauzimu. Gawo lathu latitenga ife kuchoka pa malo okhala ndi kayendedwe kabwino a mizinda ya Queensland kupita ku malo ovuta okhala ndi anthu osiyanasiyana a ku Melbourne ndi Sydney.
Kwa ine, kuyendayenda ndi masutikesi ndi kukhala m’nyumba zosiyanasiyana mlungu uliwonse chinalidi chitokoso. Koma kenaka ndinalingalira kuti: ‘Ndiyenera kukhala wosangalala kuti tiri ndi masutikesi ndi zinthu zoikamo. Anthu ambiri alibiretu ngakhale zimenezi.’ Kusoweka kwa kuyanjana kwa mwamuna wanga usiku wambiri pamene iye ankasamalira mathayo a mpingo sichinakhale chopepuka nachonso. Komabe, akazi ambiri, ndinalingalira tero, samayanjana ndi amuna awo nkomwe, ndipo m’nkhani zambiri icho sichiri chifukwa cha kudziloŵetsa kwawo m’ntchito yabwino ya Ambuye.
Mkhalidwe wovuta kwambiri wa yonse wa kuchita nawo, ngakhale kuli tero, wakhala umoyo wanga woipa. Chiyambire ku ubwana, ndakhala ndi kuyang’anizana ndi zironda zopitirizabe za pa m’mero, mavuto amphamvu ndi m’mawondo, mavuto a chifuŵa cha befu, ndi kudzimva kwa chisawawa kwa kusoweka mphamvu. Adokotala ndi akatswiri odziŵa za chibadwa sanakhoze kuzindikira vutolo.
Pamene zaka zinapitabe, zizindikiro zomwe ziri pamwambazo zinaipirako, ndi kutsagana ndi kuwawa kwa msana kopitirizabe ndi kuwawa kwa khosi, kumva mphepo, kutopa kopitirira malire, zironda za m’thupi, kutupa kwa ziwalo, kumva mseru kopitirira, ndi kukhala ndi zironda za mu chikhodzero. Ndinayamba kuganizira kuti matenda oterewa anali mbali ya umoyo wabwino womwe ukafunikira kupiriridwa, chotero sindinadandaule.
Mkhalidwe umodzi wotere unayamba mwamsanga pambuyo pa kulandira gawo lathu loyamba la mdera. Nthaŵi iriyonse pamene ndinayenda koposa ora limodzi, ndinavutika ndi kutuluka kwa mwazi, ndipo ichi chinakhoza kupitirira kufikira nditakhala pansi. Popeza kuti ndandanda yathu inaitanira kaamba ka chifupifupi maora atatu akuyenda m’mawa uliwonse m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, ndinadabwa mmene ndikakhozera kuchita nazo. Ndinapemphera ponena za icho. Chotulukapo chake?
Uli wonse wa m’mawa umenewo—kwa miyezi itatu yonse—ndinafunsidwa kulowa mnyumba ndi kuitanidwa kukhala pansi. Pamene vuto la thupi linaleka, kunateronso kuitanidwako! Popeza kuti sichiri chamwambo kwa anthu a ku Australia kuitanira mnyumba anthu odzacheza osakhalitsa, ndimadzimva kuti ichi chinachitika koposa ndi zongokumana nazo.
Umoyo Wanga Uyipirako
Panthaŵi imene ndinali ku mayambiriro kwa ma 30 anga ndipo nditakhala mu ntchito yoyendayenda kwa zaka zingapo, umoyo wanga unaipa mowonjezereka. Icho chikatenga milungu iŵiri kapena kuposerapo kuchira ku masiku oŵerengeka a kubindikiritsidwa pa msonkhano. Kokha kuchedwa kwa usiku umodzi kunakhoza kundiletsa ine kwa milungu ingapo. Kuchitira umboni kwa m’mawa kunakhala monga mtolo wonga phiri. Kufika pa 10 koloko m’mawa uli wonse, ndinali wotopetsedwa. Podzafika 11 koloko ndinadzimva wolefuka mkati, ndipo kusagwira ntchito kwa malingaliro kunatsatira. Podzafika masana ndinali wosangalala kugona pansi. Kenaka panalinso madzulo ofunikira kuyang’anizana nawo. Ena anawonekera kukhala okhoza kuchita nazo mopepuka ndi kukhala ndi mphamvu kaamba ka zochitachita zowonjezereka. Nchifukwa ninji osati ine?
Ndinachepetsedwa ku mapaundi 93 (42 kg), ndipo ngati sindinali m’kama kaamba ka chimfine, ndinakhala ndi kudzimva kwa zizindikiro za chimfine kosalekeza. Sindinakhoze kugona usiku wonse popanda kusokonezeka nthaŵi 20 kapena kuposerapo chifukwa cha vuto la chikhodzero. Ndinafuna kupita kukagona ndipo osauka! Nthaŵi zambiri ndinadandaula m’pemphero kuti: “Chonde, Yehova, ndimadziŵa kuti sindiyenerera chirichonse, koma ndimangofuna umoyo wanga kukutumikirani. Kodi munganditsogoze ku mavuto anga? Ngati sitero, chonde ndithandizeni ine kupirira.”
Ndinali wotsimikiza kusaleka utumiki wa nthaŵi zonse mopepuka. Chotero ndinapanga kufunsa kwachindunji kwa Yehova kaamba ka thandizo, choyamba kuti tipeze caravan (ngolo), popeza kuti ndinadzimva kukhala wosowa kwenikweni malo ogonamo a pambali. Sindinatchule pempho langa kwa Alan, koma pa msonkhano wotsatira weniweniwo mbale anatifikira ife ndi kutipatsa ngolo yake. Pempho langa lotsatira linaphatikizapo kusinthidwa kupita ku gawo lozizirako, ndipo mwamsanga pemphero limeneli linayankhidwanso pamene tinagawiridwa ku Sydney.
Kodi mungakhulupirire kuti mkati mwa miyezi iŵiri ya kufika kwathu ku Sydney, ndinapatsidwa bukhu lolongosola zizindikiro zomwe zinawonekera kukhala zikugwirizana ndendende ndi zanga? Mozizwitsa, bukhu limeneli linalembedwa ndi dokotala yemwe kugwira ntchito kwake kunali m’gawo lathu ladera. Pambuyo pa kuyesa kochulukira, ndinaphunzira kuti ndinali ndi shuga yochepa m’mwazi ndi kuti zinthu zambiri zinali zoipa kwa ine, kuphatikizapo, bowa, zotupitsa mkate, fungo lina la mankhwala, mphaka, agalu, ndi zakudya zambiri.
Chinatenga miyezi yotopetsa isanu ndi itatu pansi pa chisamaliro cha dokotala ameneyu kupeza zakudya zanga zosafunikazo kufikira pamene ndinalibe zizindikiro. Chiri chovuta kulongosola chotulukapo chomwe ichi chakhala nacho pa umoyo wanga wa kuthupi ndi pakawonekedwe kanga konse ka umoyo. Misonkhano ya utumiki ndi mpingo inakhala chisangalalo chachikulu kachiŵirinso. Ndinadzimva monga ngati kuti “ndinaukitsidwa” kuchokera ku imfa yomwe inkayandikira! Mwamsanga ndinapezanso kulemera, ndipo aja omwe sanandiwonepo kwanthaŵi yotalikirapo anali odabwitsidwa pa kusinthaku.
Mphoto Zolemelera
Ndi mofulumira chotani nanga mmene zaka 24 zapitira kuchokera pa imfa ya Amayi! Ndipo ndiri wa chisangalalo chotani nanga kukhala nditawononga zaka 21 zimenezo m’ntchito ya nthaŵi zonse! Ndi zowona kuti, pakhala mavuto, koma popanda awa mwina sindikanakhoza kukulitsa mlingo umodzimodziwo wa kuyamikira kaamba ka chikondi cha Yehova.
Nditalinganiza, kudzipereka kwanga nsembe komwe ndapanga kumawonekera kukhala kochepera kutalinganizidwa ndi mphoto zomwe zangolandiridwa kale. Pakati pa izi uli unansi wamtengo wapatali ndi mabwenzi achikondi ambiri ndipo makamaka banja langa lenilenilo. Kuchitira chitsanzo, mng’ono wanga Margaret anandilembera mwamsanga pambuyo pakuti Alan ndi ine tinayamba ntchito yoyendayenda:
“Ndikuyamikani kwambiri pa kukhala anthu omwe muli. Sindiganiza kuti ndakhala nditanenapo izi chiyambire, ndipo ndiri wachisoni ngati sindinatero, koma ndikuyamikani kaamba ka kuchita kwanu ubwino wa kulera Bev ndi ine ndi kaamba ka kutenga malo a Amayi. Ndimazindikira tsopano kuti chinatenga unyinji wa chikondi ndi kuyesayesa ndi kudzipereka nsembe kwaumwini kumbali yanu. Ndakhala kaŵirikaŵiri ndikulingalira ponena za zaka zimenezo ndi kupemphera kuti inu mukhale odalitsidwa. Ndikudziŵa kuti nanunso mwakhala mukutero.”
Kenaka pali mphoto zamtsogolo—makamaka chiyembekezo cha mtengo wapatali cha kuukitsidwa kwa okondedwa athu ogona. Inde, misozi yoŵerengeka imagwabe pamene ndiŵerenganso kalata yotsazika ya Amayi. Pemphero langa lirinso monga lawo, “kuti Yehova adzawakumbukira [iwo] ndi kuti tonsefe tidzakumana m’Dongosolo Latsopano.”—Monga momwe yasimbidwira ndi Lynette Sigg.
[Mawu Otsindika patsamba 26]
Ndinadziŵa kuti Amayi anali m’chikumbukiro cha Yehova, malo osungika kwenikweni kukhalamo
[Chithunzi patsamba 25]
Kuchokera ku lamanzere: Lynette, Margaret, ndi Beverley, zaka zitatu amayi awo asanafe
[Chithunzi patsamba 28]
Lynette ndi mwamuna wake, Alan, akutumikira mu Australia pakali pano