Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 4/8 tsamba 3
  • Nchifukwa Ninji Zinthu Zoipa Zimachitika kwa Anthu Abwino?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Zinthu Zoipa Zimachitika kwa Anthu Abwino?
  • Galamukani!—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Ena Amalongosolera Kulolera Kuipa kwa Mulungu
    Galamukani!—1988
  • Ukalamba Sungatilepheretse Kutumikira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Zinthu Zosaiwalika pa Utumiki Wanga
    Nsanja ya Olonda—2014
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 4/8 tsamba 3

Nchifukwa Ninji Zinthu Zoipa Zimachitika kwa Anthu Abwino?

Cha pansi pa matanthwe otentha a pansi pa nthaka ya San Salvador mu El Salvador pali mzinda wa San Ramón. M’mawa mwa September 19, 1982, unakanthidwa ndi mafunde atatu akulu a matope. Mwakuchititsidwa ndi mathithi a mvula, funde loyamba linali laukulu wa chifupifupi nyumba zosanjikana zitatu mu utali ndipo linanyamula miyala yaikulu ndi nthambi za mitengo. Ikumapanga chigwa chakuya mamita 50 ndi ukulu wa mamita 75, inathira kunsi cha kumbali kwa matanthwe otentha a pansi pa nthaka, ikumapeza mphamvu ndi mlingo pamene inkayenda. Podzafika cha kunsi, iyo inakagunda mu nyumba za njerwa zowotcha mu njira yake.

Nyumba ya Ana inagwa kaamba ka funde losapumalo m’chochitika chowopsya chimodzi. Ana ake akazi anakumbata Ana ndi kulira, “Tipempherereni ife!” Kenaka matope anawaphimba iwo . . .

Mwamwaŵi, ngakhale kuli tero, chidutswa cha zophimba denga chinakadziimika icho chokha kutsogolo kwa nkhope ya Ana, chikumamusiyira iye mpata wopumira. “Ndinangopitirizabe kuitana ndi kuitana kaamba ka thandizo,” iye akutero. Chifupifupi maora anayi pambuyo pake, anansi anamva kulira kwake ndipo anayamba kumthandiza. Iye anapezedwa wofotseredwa m’matope kufika m’kwapa mwake, ndi matupi a ana ake akazi atapanikizidwa molimbana ndi iye m’matope othetsa mpweyawo.

ANTHU a ku San Ramón anali ofatsa ndi aubwenzi. Pakati pa akufawo panali chiŵerengero cha Akristu odzipereka, kuphatikizapo okwatirana chatsopano aŵiri, Miguel ndi Cecilia, ndi banja la anthu asanu omwe mitembo yawo inapezedwa itatsekeredwa mkati ali okumbatirana.

Tsoka, ngakhale kuli tero, silimasankha pakati pa abwino ndi anthu oipa, nsonga imene ambiri amaipeza kukhala yovuta kugwirizanitsa ndi chikhulupiriro m’kukhalako kwa Mulungu wachikondi. ‘Ali Mulungu wa mtundu wotani,’ iwo amafunsa, ‘yemwe angalole kutaika kosafunikaku kwa moyo kuchitika? Kapena kaamba ka chifukwa chimenecho, kodi ndimotani mmene Mulungu wamphamvuyonse akayang’anira munthu wachikulire akumapita popanda kuchinjirizidwa, mabanja ogwira ntchito mwamphamvu akumataikiridwa zofunika za moyo wawo, amuna achichepere ndi akazi m’chiyambiyambi cha moyo wawo akumaphedwa ndi kudwala kodzetsa imfa—ndipo osachita chirichonse?’

Harold S. Kushner, rabi wa Chiyuda, anafunsa mafunso oterowo pamene anadziŵa kuti mwana wake wamwamuna adzafa ndi matenda osakhala a nthaŵi zonse. Chisalungamo chothetsa nzeru cha ichi chinazizwitsa Kushner. “Ndinali munthu wabwino,” iye akukumbukira. “Ndinayesera kuchita chimene chinali chabwino m’maso mwa Mulungu. . . . Ndinakhulupirira kuti ndinali kutsatira njira za Mulungu ndi kuchita ntchito yake. Ndimotani mmene ichi chingachitikire banja langa?” M’kufufuza kwake kaamba ka mayankho kunadza bukhu lake lofala When Bad Things Happen to Good People.

Kushner ali kokha mmodzi wa akatswiri ophunzira zaumulungu ambiri yemwe wayesera kuyankha funso la chifukwa chimene Mulungu amalolera kuipa. M’chenicheni, munthu waika Mulungu pa chiyeso. Kodi ndi chigamulo chiti chimene Kushner ndi akatswiri ophunzira zaumulungu ena afikira? Kodi chigamulo chawo chiri cholungama?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena