Mmene Ena Amalongosolera Kulolera Kuipa kwa Mulungu
MULUNGU—kodi ali waliwongo kapena wopanda liwongo la kuchititsa kuvutika kwa munthu? Funso limeneli limavutitsa mokulira pa ngozi zambiri, kaya zaumwini kapena zokulira zonga ngati za pa San Ramón. Yatero magazini ya Chibritish The Evangelical Quarterly: “Chimodzi cha zokhumudwitsa zokulira za kukhulupirira mwa Mulungu wamphamvuyonse, ndi wachikondi kuli kukhalapo kwa kuvutika kosafunika m’dziko.”
Ena mwakutero angakhoze kupatsa mlandu Mulungu kaamba ka kulekelera—ngati kwenikweni sikupangitsa—kuvutika. Walemba tero wophunzira zaumulungu John K. Roth: “Mbiri yakale yeniyeniyo iri kuswa lamulo la Mulungu. . . . Musatenge mopepuka chimene thayo la Mulungu limafunikira.”
Olingalira ambiri a chipembedzo chiyambire Augustine, ngakhale kuli tero, atsutsana mokulira kaamba ka kulongosoka kwa Mulungu. Wa nthanthi wa m’zana la khumi ndi zisanu ndi ziŵiri Leibniz anapeka kalongosoledwe ka kuyesayesa kumeneku kukhala: theodicy, kapena “kulungamitsa kwa Mulungu.”—Onani tsamba 6.
Maphunziro A Zaumulungu a Makono Atenga Kaimidwe ka Umboni
Kuyesayesa kwa kuchotsa liwongo pa Mulungu kwapitirizabe m’nthaŵi zamakono. Mary Baker Eddy, muyambitsi wa Sayansi ya Tchalitchi cha Chikristu, anayesa kuthetsa vutolo mwa kukana kuti kuipa kumakhalapo pa nthaŵi yoyamba! Mu Science and Health With Key to the Scriptures, iye analemba kuti: “Mulungu . . . sanapange munthu wokhala ndi uchimo . . . Komabe, kuipa kuli kokha chinyengo, ndipo kulibe maziko enieni.”—Kanyenye ngwathu.
Ena akhululukira Mulungu pa maziko a kukhala kwawo olungama m’kuvutika. Rabi wina pa nthaŵi imodzi ananena kuti: “Kuvutika kumadza kwa munthu wotchuka kwambiri, kuti kuyeretse malingaliro a kunyada kwake ndi kudzikometsera.” M’nsonga yofananayo, akatswiri a maphunziro a zaumulungu ena apanga nthanthi yakuti kuvutika padziko lapansi kuli “koyenerera kutikonzekeretsa ife monga anthu abwino kaamba ka moyo wa Ufumu wa kumwamba wa mtsogolo.”
Koma kodi chiri cholongosoka kukhulupirira kuti Mulungu amabweretsa kapena kulola ngozi kotero kuti ayeretse ndi kulanga anthu? Mwachiwonekere awo amene anaphedwa amoyo pa San Ramón anali ndi mwaŵi wochepera wa kuwongolera kakulidwe kawo kolongosoka. Kodi Mulungu anawapanga iwo zopereka kotero kuti aphunzitse opulumukawo? Ngati ndi tero, kodi ndi liti lomwe linali phunziro?
Chotero, momvekera, bukhu la Kushner When Bad Things Happen to Good People liri ndi kufikira kofala. Chifukwa chakuti mkonzi wake mwaumwini anadziŵa kuŵaŵa kwa kuvutika, iye anayesera kutonthoza aŵerengi ake, kuwatsimikizira iwo kuti Mulungu ali wabwino. Komabe, pamene chinadza ku kulongosola kokha chifukwa chimene Mulungu amalolera olungama kuvutika, kulingalira kwa Kushner kunatenga mbali yachilendo. “Mulungu amafuna olungama kukhala mumtendere, miyoyo ya chimwemwe,” analongosola tero Kushner, “koma nthaŵi zina ngakhale Iye sangakhoze kuchibweretsa chimenecho.”
Kushner chotero akulongosola Mulungu yemwe sali woipa koma wofooka, Mulungu yemwe mwinamwake sali wamphamvuyonse. Mwa chikhumbo, ngakhale kuli tero, Kushner analimbikitsabe aŵerengi ake kupemphera kaamba ka chithandizo chaumulungu. Koma ponena za kokha mmene Mulungu woyerekezedwa kukhala ndi polekezera ameneyu akakhalira wa chithandizo chenicheni chirichonse, Kushner sali wotsimikiza.
Kutsutsana kwa Makedzana
Chotero olingalira a chipembedzo cha dziko alephera kuwunjika kuchinjiriza kokhutiritsa kaamba ka Mulungu ndi kupereka chitonthozo chenicheni ku minkhole ya kuvutika. Mwinamwake amene afunikira kukhala pa kuyesedwa sali Mulungu koma maphunziro a zaumulungu! Popeza kuti nthanthi zosagwirizana zimenezi zimangodzetsa kokha malingaliro opanda maziko omwe analongosoledwa chifupifupi zaka zikwi zinayi zapitazo. Panthaŵi imeneyo kutsutsana kunachitika kozikidwa pa kuvutika kwa munthu wowopa Mulungu wotchedwa Yobu, munthu wachuma ndi wotchuka wa Kum’mawa yemwe anadzakhala nkhole wa matsoka otsatizanatsatizana. M’kutsatizanatsatizana kofulumira Yobu anavutika ndi kutaikiridwa kwa chuma chake, imfa ya ana ake, ndipo, potsirizira pake, iye anakanthidwa ndi matenda oipa.—Yobu 1:3, 13-19; 2:7.
Atatu otchedwa mabwenzi anabwera ku chithandizo cha Yobu. Koma m’malo mopereka chitonthonzo, iwo analimbana naye ndi maphunziro a zaumulungu. Nsonga ya kutsutsa kwawo inali: ‘Ali Mulungu amene wachita chimenechi kwa iwe, Yobu! Ndithudi iwe ukulangidwa kaamba ka kuchita chinthu chinachake cholakwika! Pambali pa icho, Mulungu alibe chikhulupiriro ndi chimodzi chomwe mwa atumiki ake.’ (Yobu 4:7-9, 18, NW) Yobu sanakhoze kumvetsetsa chifukwa chimene Mulungu mwachiwonekere anakhoza ‘kumuika iye kaamba ka kukhala nkhole ya iyemwini.’ (Yobu 16:11, 12) Ku ubwino wake, Yobu anasungilira umphumphu wake ndipo sanakhoze kupereka choipa mwachindunji kwa Mulungu.
Komabe, otonthoza a Yobu, m’chenicheni, ‘analengeza Mulungu kukhala woipa,’ mwakutanthauza kuti wovutika aliyense wa tsoka ankapatsidwa chilango kaamba ka kuchita choipa. (Yobu 32:3) Koma Mulungu mwamsanga anawongolera kawonedwe kawo kolakwa.