Masiku Otsiriza—‘Maufumu Molimbana ndi Maufumu’
“Kuwombana kwa mitundu kuchokera mu 1914 mpaka 1918 sikunali ‘mphekesera yosakhala yeniyeni ya nkhondo ina.’ Kulimbana kunabweretsa kachitidwe katsopano ka nkhondo, nkhondo ya dziko lonse yoyamba m’chokumana nacho cha mtundu wa munthu. Kukhalitsa kwake, kuwawa, ndi ukulu unapambana chirichonse chomwe chinadziŵidwa kalelo kapena chomwe chinayembekezeredwa mwa chisawawa. Tsiku la kupha kwa mkhalidwe wa nkhondo kosaŵerengeka kunafika.”—The World in the Crucible, lolembedwa ndi Bernadotte E. Schmitt ndi Harold C. Vedeler.
NKHONDO ya mu 1914-18 inali yaikulu kwambiri m’kuwononga ndi kutaika kwa moyo chakuti mu France kufikira lerolino, mungapeze mawu ozokotedwa pa miyala operekedwa kwa akufa mu La Grande Guerre, Nkhondo Yaikulu. Wolemba wa ku America Ernest Hemingway pambuyo pake anaitcha iyo “yaikulu koposa, yakupha, kusakaza kosalamulirika komwe sikunachitikepo padziko lapansi.” Nkhondo Yaikuluyo inatchedwanso Nkhondo ya Dziko I pamene dziko linawunikiridwa ku Nkhondo ya Dziko II (1939-45).
Nkhondo ya Dziko I inali yapadera kuchoka ku nkhondo zina zapapitapo m’njira zambiri. Magulu ankhondo mamiliyoni ochulukira anaphana lina ndi linzake m’dziko ndi m’nkhalango za Western Europe. Mfuti ya makina inapeza kukantha kwakukulukulu pamene inasakaza unyinji wokulira wa gulu lankhondo loyenda pansi. Monga mmene Gwynne Dyer analongosolela m’bukhu lake War: “Mkati mwa miyezi iŵiri [ya kuyamba kwa nkhondo], oposa amuna miliyoni imodzi anali akufa. . . . Zida za makina—ziwiya zokanthira mofulumira ndi mfuti za makina zikumatulutsa zipolopolo mazana asanu ndi limodzi pa mphindi imodzi—zinadzaza mpweya ndi zidutswa za zitsulo zosakaza.” Kasinja, sitima ya m’madzi, ndi ndege zinasintha kulingalira ndi kachitidwe. Tsopano imfa inadza kuchokera m’thambo ndi kumatuluka kuchokera m’madzi.
Nkhondo za m’mbuna, zokhala ndi kuwonjezereka kwa kugwiritsira ntchito mpweya waululu, zinasonkhezera anthu ku mlingo wa kupirira, kuvutika, ndi kugwa kwa makhalidwe. Nkhondo Yaikulu inali yapadera m’njira ina: “Iyi inali nkhondo yoyamba mu imene andende anafika ku chiŵerengero cha mamiliyoni (8,400,000 onse pamodzi) ndipo anasungidwa kwa nyengo yaitali ya nthaŵi.” (The World in the Crucible) Inalinso nkhondo yoyamba yomwe inaphatikizapo kwenikweni chiŵerengero chonse cha anthu wamba, kaya m’kuchinjiriza ndi kutulutsa zida za nkhondo kapena kukhala minkhole ya kuwukiridwa ndi kukantha.
Mboni za Yehova kumbuyo kumeneko mu 1914 zinawona mu nkhondo yoipa imeneyo chiyambi cha kukwaniritsidwa kwa maulosi ofikapo a Yesu. Koma zoipirapo zinkabwera.
Nkhondo ya Dziko II—Mphamvu Yosakaza Yapadera
Umboni wina wakuti, ngakhale m’kawonedwe ka munthu, amenewa angakhale masiku otsiriza uli kuthekera kwa munthu kwa kudziwononga kwaumwini. Dr. Bernard Lown analongosola m’nkhani yake ya Kupatsa Mphoto ya Mtendere kuti: “Nkhondo Yachiŵiri ya Dziko inayambitsa nkhondo ya dziko lonse—yopanda ulamuliro m’kachitidwe, yopanda polekezera m’chiwawa, ndipo yosasankha minkhole. Ng’anjo za Auschwitz ndi kuwawa kwa atomiki ya Hiroshima ndi Nagasaki kunalongosola nthaŵi yoipabe m’mbiri ya kusakaza kwa munthu.”
Kodi mtundu wa anthu unaphunzira chikondi ndi chifundo kuchokera ku chokumana nacho choipachi? Iye akupitiriza kuti: “Kuwawa kotalikira komwe kunasiya 50 miliyoni akufa [chifupifupi cholingana ndi chiŵerengero chonse pamodzi cha Britain, France, kapena Italy] sichinapereke maziko okhulupirira kaamba ka kumvana kwa kanthaŵi molimbana ndi kuipa. M’malomwake, ankhondowo mwamsanga anatulukira ndi zida zokhoza kusakaza mbadwo zolingana ndi za zikwi zochulukira za Nkhondo ya Dziko ya II.”—Kanyenye ngwathu.
Nchosakaikiritsa ponena za icho, tawona ‘mtundu ukulimbana ndi mtundu ndi ufumu ndi ufumu wina,’ ndipo wokwera pa kavalo wofiira wa Chivumbulutso watsanulira kupha modutsa dziko lapansi. (Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:4) Koma kodi ndi umboni wowonjezereka wotani umene kutulukiridwa ndi kupangidwa kwa zida za nyukliya kuli nako kaamba ka “masiku athu otsiriza”?—2 Timoteo 3:1.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
“Zana la 20 ladziŵikitsidwa ndi mlingo womakulakula wa chiwawa cholinganizidwa ndi mazana aŵiri apitawo. . . . Zana la 20 liri kale ndi zolembedwa za nkhondo 237, uko ndiko kuti kuwukirana komwe kunatulukapo mu imfa zoyerekezedwa 1,000 kapena kuposerapo pa chaka chimodzi.”
“Osati kokha kuti pali nkhondo zochulukira komanso kuwononga kwake kwakula. Nkhondo m’zana la 20 pakali pano zapha anthu mamiliyoni 99, kuchulukira nthaŵi 12 kuposa m’zana la 19, kuchulukira nthaŵi 22 kuposa zana la 18. . . . M’zana lapita kunali nkhondo ziŵiri ndi imfa zoposa pa 1 miliyoni; m’zana lino pali nkhondo 13 zoterozo.”—World Military and Social Expenditures 1986, lolembedwa ndi Ruth Leger Sivard.
[Mawu a Chithunzi]
U.S. Army photo