Masiku Otsiriza—Kusoweka kwa Chakudya, Mliri, Kuipitsa—Ndi Kulalikira Ufumu
“Njala ikubwera mu mtundu wina. Iyo iri njira yokhazikika chakuti anthu oposa 700 miliyoni akuvutika. . . . Chaka chirichonse njala yaikulu yowonekera imeneyi imapha anthu ochulukira pa 18 kufika ku 20 miliyoni—kuwirikiza kuposa kaŵiri pa chiŵerengero cha awo omwe anafa chaka chirichonse mkati mwa Nkhondo ya Dziko II.”—World Hunger—Twelve Myths, lolembedwa ndi Frances Moore Lappé ndi Joseph Collins.
MONGA mmene Yesu ananeneratu, mbadwo wathu wakhalanso ndi mbali yake ya kusoweka kwa chakudya ndi kupereŵera kwa chakudya koma ndi kudzilungamitsa kochepera m’nkhani zina kuposa mibadwo yapita. Nchifukwa ninji tero? Chifukwa chakuti zopangapanga zamakono ndi njira za kukambitsirana ndi zonyamulira zikanakhoza kupanga kusoweka kwa chakudya kukhala chinthu chakumbuyo. Komabe, eni a dziko ndi andale zadziko agwiritsira ntchito anthu kukhala monga opanda pake, osasamala kanthu za kuvutika kowonjezedwa pa osauka ndi opanda dziko.
Njala ndi kusoweka kwa chakudya kukupitirizabe kukantha Africa. Posachedwapa mu September 1987, chenjezo linaperekedwa kuti Ethiopia inalinso pansi pa chipsyinjo pamene “njala inkafalikira mofulumira m’dziko la ku Africa losauka limenelo,” inasimba tero The New York Times. Nduna yakale ya ku Ethiopia yoyang’anira pa zinthu zosonkhedwa kaamba ka kusoweka kwa chakudya inalongosola kuti: “Chikuwonekera kuti pali tsopano chifupifupi anthu mamiliyoni asanu oyambukiridwa ndi kusoweka kwa chakudya, ndipo sitikudziŵa kuipa kumene icho chingatenge.”
Pa nthaŵi imodzimodziyo, maripoti kuchokera ku dziko lokulira la India akuperekanso chithunzi china choipa chochititsidwa ndi chirala. Nduna ya Boma kaamba ka Zamalimidwe inanena kuti: “Chifupifupi maperesenti 60 a chiŵerengero chathu chonse cha dziko adzavulazidwa ndi chirala chimenechi.” Iye anawonjezera kuti “chiŵerengero chimenechi chinali chokulira kwenikweni kuposa kuyerekeza kwa pasadakhale ndipo chinatanthauza kuti chifupifupi mamiliyoni 470 a chiŵerengero cha dziko cha mamiliyoni 780 anayambukiridwa.” Kodi ndithudi tingakhoze kuchita ndi kupenyerera ziŵerengero zimenezo ndi kuyambukira kwake pa mabanja a munthu?
Wonjezerani ku zungulirezungulire wokhazikika wa kusoweka kwa chakudya, chigumula, ndi zirala mitengo yowopsya yolipiridwa ku njala mkati mwa nkhondo ziŵiri zadziko ndi zochitika za pambuyo pake. Monga mmene wolemba mmodzi wa zochitikazo mu 1945-46 anasimbira kuti: “Panali kupereŵera kwa chakudya kwa dziko lonse monga chotulukapo cha nkhondo ndipo mkhalidwe kuzungulira Europe yonse . . . unali wowopsya. Mwamsanga pakadakhala kusoweka kwa chakudya kowopsya m’mbali ya Russia ndi Rumania ndipo mu Greece zikwi zingapo zikanavutika ndi njala ndi kufa. Ngakhale mu Britain mkate ukanafunikira kugawanidwa kwa nthaŵi yoyamba m’mbiri yadziko.”
Inde, kavalo wakuda wa kusoweka kwa chakudya, ndi wokwerapo wake akumatambasula muyeso m’mpweya, wapita kupyola m’mitundu ndipo akudumphabe pa mtundu wa anthu.—Chivumbulutso 6:5, 6.
Mliri wa Matenda ndi Mliri
Yesu analosera kuti mbali ya chizindikiro cha masiku otsiriza ikakhala “mliri wa matenda.” (Luka 21:11, NW) Kodi zana lathu la 20 lawona kugawana kwake kwa mliri wa matenda ndi mliri? Kuyamba ndi Spanish flu yomwe inakantha pamapeto a Nkhondo ya Dziko I ndi kutenga miyoyo mamiliyoni 20, mtundu wa anthu, mofanana ndi mibadwo ya kumbuyo, wakhala ukukanthidwa ndi matenda. Koma ngakhale ndi kupita patsogolo kwa sayansi ndi mankhwala m’masiku otsirizawa, kuwonjezeka kwa matenda ndi kufa kukupitabe patsogolo kufika ku chiŵerengero cha mamiliyoni chaka chirichonse.
M’dziko lolemera la Kumadzulo, timamva kufunsira kokhazikika kaamba ka ndalama ndi kuchiritsa kwa kansa, matenda a mtima, ndi AIDS. Zowona, mazana a zikwi akufa chaka chirichonse kuchokera ku matendawa ndi kukantha kwina. Komabe, pali matenda omwe akuthetsa mamiliyoni angapo chaka chirichonse mu Africa, Asia, ndi Latin America.
M’bukhu lake lakuti Mirage of Health, René Dubos analemba kuti: “Malungo, kuyambukiridwa kwina ndi protozoa, ndi kuyambukiridwa kwa nyongolotsi kuli maziko a kudzetsa chisoni kwa malingaliro ndi kwa ndalama m’mbali zambiri zopanda mwaŵi.” Monga chotulukapo, “mamiliyoni pa mamiliyoni a mtundu wa anthu mu Asia, Africa, ndi Latin America amavutika ndi kufa chaka chirichonse ku matenda a nyongolotsi yokangamira ku matumbo, matenda a tulo a ku Africa, kapena malungo.” Chisoni chochititsidwa ndi matendawa sichiri choyerekezedwa kokha ndi chiŵerengero cha awo omwe amafa monga chotulukapo cha iwo. Dubos walongosola kuti: “Matenda ochititsidwa ndi tizirombo tating’ono sanagonjetsedwebe.”
Dubos akupitiriza kuti: “Mosiyanako, dyera la [munthu woyera] limampangitsa iye kuphimba ndi ulemelero wa sayansi kupeza kulikonse komwe kumapezedwa pa kukhalapo kwa iyemwini.” Chotero, kugogomezera m’dziko la kumadzulo kuli pa kansa ndi matenda a mtima—ndipo chosafunikira kuiwalidwa chiri matenda opatsirana mwa kugonana. Magazini ya zamankhwala imodzi yalongosola kuti pamakhala chifupifupi matenda atsopano mamiliyoni atatu a chinzonono chaka chirichonse mu United States mokha.
Koma mosasamala kanthu zakuti tikufufuza maiko otukuka kapena maiko otukuka kumene, timawona umboni wa ‘kavalo wotumbuluka wa imfa ndi mliri wakupha,’ kavalo wachinayi wa Chivumbulutso.—Chivumbulutso 6:8.
Kuwononga Dziko Lapansi
Pa mlingo wa dziko lonse, munthu akuwononga kale ndi kusakaza mkhalidwe wosalimba wolinganizika wachibadwa m’mkhalidwe wochepa wochititsidwa ndi kuipitsa, kusakaza, kusasamala, ndi kugwetsa mitengo.
Mvula ya acid kapena kuchotsapo nthaka, kochititsidwa ndi mvula yosakanizana ndi chipale chofewa ndi utsi wotulutsidwa ku zopangidwa (nitrogen oxides ndi sulfur) kuchokera ku malasha ndi makampani otentha mafuta, kukuyambukira nyanja ndi nkhalango za ku Northern Hemisphere. Monga mmene olemba a bukhu la Earth alongosolera: “Chochititsa chimodzi cha kuchotsa nthaka kwa acid kwakhala kusintha kwa nyanja zambiri m’malo onga ngati New England ndi Scandinavia kuchokera ku dongosolo la zamoyo ndi malo ozizinga olemera otulutsa zochulukira kufika ku osauka, nthaŵi zina unyinji wosathandiza, wa madzi ochulukira. Mwachitsanzo, nsomba zonse zaphedwa m’mazana a nyanja mu Adirondacks, ndipo chifupifupi nyanja 50,000 za ku Canada zikuwopsyezedwa ndi tsoka loterolo.”
Ponena za nkhalango, ambiri akuvutika ndi “kufa kwa nkhalango.” “Zizindikiro za ‘kufa kwa nkhalango’ zawonedwa mu nkhalango za Kum’mawa kwa Europe, USSR, Italy, Spain, Canada, Britain ndi kumtunda kwa Midwest ya America.” Olemba amodzimodziwo akupitiriza kuti: “Mwanzeru, anthu akuchita ndi kuyesa kokulira, kuika ululu mopambanitsa ku limodzi la gawo lokulira (ndipo mwinamwake mbali zina za gawolo), kenaka kuyembekeza kuti awone chimene chidzachitika.”
Kudidikiza pa malo okhala zaumoyo kukuwonjezeka ndi nsonga yosakhoza kugonjetsedwa ina—chiŵerengero cha anthu cha dziko posachedwapa chapitirira pa mlingo wa mabiliyoni asanu. Akatswiri odziwa za zinyama Anne ndi Paul Ehrlich alongosola kuti: “Mwachiwonekere mtundu uliwonse wa zamoyo za padziko lapansi ukuvutika kuchokera ku kufutukuka kwa Homo sapiens.” Munthu amafutukuka ndi kudyera masuku pamutu. Mibadwo ya kutsogolo idzafunikira kudzisamalira iyo yokha.
Mitsinje, nyanja, ndi nyanja zazikulu zikuipitsidwa ndi kuipitsa kopanda malingaliro kwa munthu kwa chuma chimenechi. Zoipa, zapadzala, ndi mankhwala oipitsa zimaponyedwa m’nyanja monga ngati kuti zimenezi zinali motaira zinyalala za kumaloko, chothandizira chozizwitsa ku moyo wamunthu pa dziko lapansi.
Chotero, umenewu, uli mbadwo woyamba m’mbiri ya munthu womwe wakhoza kuwononga kwenikweni dziko lapansi. Tsopano, kwa nthaŵi yoyamba, ulosi wa Chivumbulutso 11:18, womwe umanena kuti Mulungu “adzawononga iwo akuwononga dziko,” ungakwaniritsidwe. Chimenecho chiyenera kuchitika pamapeto a “nthaŵi ya chimaliziro.”—Danieli 12:4.
Ntchito Yochenjeza Yapadera
Padakali mbali ina ya ulosi wa Yesu yomwe ikukwaniritsidwa m’njira yapadera. Iye ananeneratu kuti ntchito yaikulu yolalikira, ntchito yochitira umboni, idzachitidwa m’mitundu yonse mapeto asanadze. (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Ndipo ikachitidwa mkati mwa nthaŵi ya moyo wa mbadwo wa mu 1914. Ichi chakhala chothekera kokha m’zana la 20 limene kupita patsogolo kwamakono m’zoyendera, zokambitsirana, makompyuta, ndi kusindikiza kwalola Mboni za Yehova kukulitsa ntchito yawo yaikulu yophunzitsa m’zinenero 200 kuzungulira dziko lonse lapansi.
Tsopano Mboni zikutulutsa magazini ya Nsanja ya Olonda m’zinenero 103! Makope oposa mamiliyoni 13 a kope lirilonse akugawiridwa. Magazini imene mukuŵerenga ikufalitsidwa m’zinenero 54, ndipo oposa makope 11 miliyoni akusindikizidwa a kope limodzi ndi limodzi. Chifupifupi Mboni mamiliyoni atatu ndi theka zikulengeza mokhazikika mbiri yabwino ya boma la Ufumu wa Mulungu mu utumiki wawo m’maiko 210.
Ntchito yapadera imeneyi ikukwaniritsidwa mosasamala kanthu za chizunzo cha dziko lonse chimenenso Yesu ananeneratu kaamba ka otsatira ake owona. Inde, ntchito yeniyeniyo ndi kupulumuka kwa Mboni za Yehova pa mlingo wa dziko lonse kuli umboni weniweni wakuti tiri m’masiku otsiriza!—Marko 13:9, 10.
Pa Kaindeinde Payandikira
Chotero, m’kukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosi wa Yesu, zochitika zonsezi zimapanga chizindikiro chokhalamo zambiri cha kukhalapo kwa Yesu kosawoneka ndi maso ndi masiku otsiriza, kapena “mathedwe a dongosolo la zinthu.” (Mateyu 24:3) (Onani bokosi pa tsamba 11.) Izo zimagwirizana pamodzi monga zidutswa zolumikizidwa bwino, zikumapanga chithunzithunzi chathunthu chomwe chimanena kuti, “Awa ndi masiku otsiriza a dongosolo iri la zinthu.”—Onaninso 2 Timoteo 3:1-5, 12, 13.
Pamene kuli kwakuti yochulukira ya mikhalidwe yonenedweratu ndi Yesu yakhalaponso mwaumwini m’mibadwo yoyambirira, kusakanizika kwa yonseyo mu mbadwo umodzi sikunachitikepo ndi kale lonse. Monga mmene tawonera, ina sinachitikepo mu iriyonse ya mibadwo yapitayo, kapena sikatero. Ina ikali kuyembekezabe kukwaniritsidwa kotheratu mbadwo uno usanathe. Ndipo pali zochitika zina zimene Mboni za Yehova zikuyembekezera tsopano ndi chikondwerero chokulira. Zochitika zimenezo ziri zotsogolera ku kufutukula kwa kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu padziko lapansi lino. Chotero funso tsopano n’lakuti, Nchiyani chotsatira?
[Bokosi patsamba 7]
Kodi Ndimotani Mmene Inu Mungayankhire? Chiyambire 1914 . . .
1. Ndi nkhondo zazikulu zotani zomwe zamenyedwa?
2. Ndi zivomezi zazikulu zingati zomwe mungakumbukire?
3. Kodi mtundu wa anthu wavutika ndi matenda a akulu aliwonse ndi miliri?
4. Kodi ndi kusoweka kwa chakudya kwakukulu kotani ndi kuperewera kwa chakudya komwe kwakantha dziko?
5. Kodi aneneri onyenga ndi amesiya onyenga adzizindikiritsa iwo eni?
6. Kodi pali umboni uliwonse wa kuwonjezeka kwa chiwawa ndi kusaŵeruzika?
7. Kodi pakhala kusoweka kwa chikondi ndi kukonda mnansi?
8. Kodi gulu lina lirilonse ladzinenera ilo lokha kuti lidzabweretsa mtendere kudziko?
9. Kodi pali chisauko cha amitundu ndi mantha a mtsogolo?
10. Kodi mumawona chitsimikiziro cha ntchito ya kuchitira umboni Ufumu kwa dziko lonse?
(Kaamba ka mayankho, onani tsamba 11.)
[Bokosi patsamba 11]
Mayankho ku Mafunso omwe ali patsamba 7a
1. Mateyu 24:7—Nkhondo zadziko ziŵiri (1914-18; 1939-45); Nkhondo ya Anthu wamba ya chiSpanish (1936-39); Nkhondo ya ku Korea; Nkhondo za ku Vietnam; Iraq-Iran; Nkhondo za ku Middle East ndi zina.
2. Mateyu 24:7—Zivomezi: 1920 ndi 1932, Kansu, China, 200,000 ndi 70,000 anafa mosiyana; 1923, Kanto, Japan, 142,000 anafa; 1935, Quetta, Pakistan, 60,000 anafa; 1939, Chillán, Chile, 30,000 anafa; 1939, Erzincan, Turkey, 30,000 anafa; 1960, Agadir, Morocco, 12,000 anafa; 1970, Peru, 66,700 anafa; 1972, Managua, Nicaragua, 5,000 anafa; 1976, Mzinda wa Guatemala, Guatemala, 23,000 anafa; 1976, Tangshan, China, 800,000 anafa.
3. Luka 21:11—Matenda a mtima; kansa; AIDS; onchocerciasis (khungu lochititsidwa ndi tizirombo ta mumtsinje); malungo; matenda opatsirana mwa kugonana.
4. Luka 21:11—Kusoweka kwa chakudya: 1920-21, kumpoto kwa China, 20 miliyoni oyerekezedwa ayambukiridwa; ku India, 1943-44, 1,500,000 anafa; Nigeria, 1967-69, ana oposa 1,500,000 anafa; Kampuchea, 1975-79, imfa 1,000,000; 1983-87, Akuda a ku Africa, anthu 22 miliyoni ayambukiridwa.
5. Mateyu 24:11—Atsogoleri a chipembedzo a machitachita a kuchiritsa mwauzimu, amesiya a pa TV, ndi atsogoleri achipembedzo a chiHindu apitirizabe kusocheretsa mamiliyoni.
6. Mateyu 24:12; 2 Timoteo 3:13—Upandu, chiwawa, kusamvera, ndi kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka kukhala kofala m’mbali zambiri zadziko. Malonda a dziko lonse a anamgoneka atulutsa unyinji wa kugwiritsira ntchito anamgoneka osalamulirika ndi akupha.
7. Mateyu 24:12—Zitseko tsopano zikuikidwa akabali ndi zochinjiriza; agalu owopsyeza akugwiritsiridwa ntchito kuchinjiriza chuma; anansi athu ali kaŵirikaŵiri alendo.
8. Chivumbulutso 17:3, 8-11—Chigwirizano cha Amitundu ndi Mitundu Yogwirizana.
9. Luka 21:26—Nkhondo zadziko ziŵiri zipangitsa kuvutika kosaneneka ndi kusauka. Chiwopsyezo cha chiwonongeko cha nyukliya chiyambire 1945 chayambukitsa mantha ndi kusauka ku dziko lonse.
10. Mateyu 24:14—Oposa mamiliyoni atatu a Mboni za Yehova akulalikira ‘mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu’ m’zinenero 200.
[Mawu a M’munsi]
a Ndandanda imeneyi ikupereka zitsanzo za zochitika; iyo siiri yokwanira.
[Zithunzi patsamba 10]
Kusoweka kwa chakudya kukukantha mbali zambiri zadziko lapansi
Munthu akuipitsa malo okhalako omwe iye akugawana nawo ndi zolengedwa zamoyo zina zonse
Mamiliyoni a anthu akuyambukiridwa ndi matenda osiyanasiyana
Ntchito yochenjeza yapadera ikuchitidwa m’zinenero 200 kuzungulira dziko lonse
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
FAO photo