Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 6/8 tsamba 20-22
  • Ndalama—Kapolo Wanu Womvera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndalama—Kapolo Wanu Womvera
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kasungidwe ka Ndalama
  • Chofunika China
  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
    Galamukani!—2015
  • Ndalama
    Galamukani!—2014
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 6/8 tsamba 20-22

Ndalama—Kapolo Wanu Womvera

“PAKATI pa 1968 ndi 1986 chiŵerengero cha achikulire mu Great Britain okhala ndi akaunti yosungira ndalama ku building society chinakula kuchokera pa 15% kufika ku 64%,” inachitira ripoti tero Glasgow Herald. Mosiyanako, pepalalo linawona kuti: “Chiŵerengero cha anthu omwe ali a Tchalitchi cha Chikristu chagwa.”

Ndalama, kapena Chuma, chakhala chikulingaliridwa kwa nthaŵi yaitali kukhala chotsutsana ndi Mulungu, mosakaikira chifukwa cha mawu a Yesu akuti: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo . . . Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma.”—Mateyu 6:24, King James Version.

Pa nthaŵi imodzimodziyo, ngakhale kuli tero, Baibulo limanena kuti, “Ndalama zichinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Kapena monga mmene munthu wa m’nthaŵi zamakono akuchiikira icho, “Ndalama zimalankhula nzeru m’chinenero chimene mitundu yonse imachimva.”

Koma kodi ndimotani mmene tingawonere ku icho kuti ndalama zikutipindulitsa m’malo mwa kutilamulira? Zomwe ziri pamwambazo ziri zofunika. Inu mumazifunikira izo kuti mukhale wachimwemwe. Monga mmene Baibulo limanenera kuti: “Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” Inu ndithudi simufunikira zochulukira. “Pakuti sitinatenge kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano.”—1 Timoteo 6:7, 8.

Komabe, bwanji ngati ndalama zimene mumalandira siziri zokwanira kukupatsani zomwe mumalingalira kukhala zofunikira? Kenaka inu mungakhumbe kusamukira ku malo komwe malipiro anu adzakwaniritsa zosowa zanu. Koma pano ndi pamene mufunikira kusanthula mkhalidwewo mowona mtima ndi mosamalitsa, popeza kuti Mawu a Mulungu amapitiriza kuchenjeza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi mumsampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitaiko.”—1 Timoteo 6:9.

Labadirani chenjezo limeneli mwanzeru! Mvetserani ku mtumwi wa Chikristu Paulo yemwe analimbikitsa kuti, “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma.” (Ahebri 13:5) Dzisanthuleni inu eni, mukumadzifunsa kuti: ‘Kodi ndiri wokwaniritsidwa ndi zofunika zokha? Kapena kodi ndimalakalaka kaamba ka zosangalatsa?’

Zowona, ndalama zingapereke zosangalatsa zowonjezereka. “Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo,” Baibulo limatero, “ndipo ndalama zivomera zonse.” Komabe, zowonjezereka zimene ndalama zingagule siziri zofunika ku chimwemwe chowona.—Mlaliki 10:19.

Kasungidwe ka Ndalama

Nchiyani, kenaka, chimene mungachite kusunga ndalama m’malo ake abwino, monga kapolo? Chiri chofunika kwambiri kwa munthu kukhalira moyo ndi zimene angakhoze kupeza. Mwachitsanzo, Liz, yemwe watchulidwa poyambirirapo, wanena kuti: “Ndikuzindikira tsopano kuti magwero a mavuto a banja langa pamene ndinali wachichepere anali kasungidwe koipa ka ndalama. Tinkagula pa ngongole, ndipo chotero nthaŵi zonse tinkakhala ndi ngongole zikumatiyembekezera. Ichi chinabweretsa kudera nkhaŵa.”

Inu mudzafunikira, ndithudi, kusanthula mosamalitsa kokha ndi ndalama zingati zimene muli nazo. Pa kulandira malipiro anu, choyamba ikani pambali ndalama za kulipira kaamba ka zofunika. Mwanjirayi, ndalama zanu zidzakhala kapolo wochinjiriza, monga mmene Mlaliki 7:12 wanenera kuti zingakhale.

Chidziŵitso cholunjika cha pasadakhale chiri mbali yoyenera ya kasungidwe kabwino ka ndalama. Ikani pambali unyinji wofunikira kusamalira kaamba ka zowonongedwa zomwe zikudza. Koma, kumbukirani, kudera nkhaŵa kopambanitsa kaamba ka mtsogolo mosungika mwa ndalama kuli mkhalidwe wovulaza kwenikweni wa chuma cha kuthupi.

Kumbukirani, kachiŵirinso, kuti zina za ndalama zomwe muli nazo sizingakhale kwenikweni zanu. Kodi mumakumbukira pamene Yesu anafunsidwa ponena za nkhani ya kulipira msonkho? Iye anapempha kobiriyo ndi kufunsa, “Chithunzithunzi ichi ndi chirembo chake ziri za yani?”

“Za Kaisara,” linali yankho.

“Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara,” Yesu anayankha tero.

Chotero, maboma oikidwa mwalamulo amafuna ndalama za msonkho molondola kulipira kaamba ka ntchito zonga ngati kusamalira umoyo, maphunziro, ndi ziwiya zoyendera. Ngati inu mukukhumba chiyanjo cha Mulungu, kenaka inu muli pansi pa thayo la kulipira unyinji wolembedwa wofunidwa kaamba ka msonkho.—Marko 12:13-17.

Chofunika China

Pambali pa chakudya, zovala, ndi nyumba, pali chofunika china chimene sitinganyalanyaze popanda kudzichititsa ife eni mavuto okulira. Kodi mungadziŵe chimene chofunika chimenechi chiri kuchokera ku mawu a Yesu awa: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m’mahema osatha”?—Luka 16:9.

Chuma chimalephera. Ponena za chimenecho ambiri a ife timadziŵa bwino lomwe pamene tipeza mphamvu zogulira za ndalama zathu zitathetsedwa ndi kusakhazikika kwa mtengo. Chotero, kenaka, malinga ngati tiri ndi moyo, tidzafunikira kugwiritsira ntchito ndalama zathu m’njira imene idzapanga mabwenzi omwe angatilandire ife “m’malo osatha.” Kodi ndani omwe ali olandira chumawa?

Yesu Kristu iyemwini anapereka yankho pamene ananena mu pemphero lake kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Inde, ngati tifuna kukhala ndi moyo kupyola kukhalapo kwathu kwamakono kochepa, kodzala ndi mavuto, chiri chofunika kotheratu kuti tikhale mabwenzi a Mlengi wathu, Yehova Mulungu, ndi Mwana wake, Yesu.

Koma, inu mungafunse, ndimotani mmene ndingachitire chimenechi? Kodi icho chidzanditengera ine chiyani? Kodi icho chidzabweretsa chimwemwe chenicheni?

[Zithunzi patsamba 21]

Kukwanira Ndi Zofunika za Moyo

Zakudya

Zovala

Nyumba

[Chithunzi patsamba 22]

Kuphunzitsa kwa Yesu kwa ‘kupereka zinthu za Kaisara kwa Kaisara’ kumaika thayo pa ife lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena