Thupi—Lopangidwa Modabwitsa Kuti Tisangalale ndi Moyo!
ASAYANSI amavomereza kuti thupi la munthu linapangidwa modabwitsa, ndithudi chozizwitsa cha kulinganizidwa ndi kapangidwe. Pamene mbali zathu zonse za thupi zikugwira ntchito mwachibadwa, tingakhoze kuchita ndi kusangalala ndi zinthu zimene, ziri zozizwitsa kotheratu.
Mwachitsanzo, yang’anani pa manja anu. Iwo analinganizidwa mosangalatsa kukwaniritsa zinthu zochulukira mu ntchito kapena maseŵera. Tsopano lino, kodi manja anu agwira magazini ino yomwe mukuŵerenga? Ngati ndi tero, ndiko kuti mikono yanu iri yokhota kokha pa kukhota kolondola kuti isunge magaziniyi pa utali woyenera kuchokera ku maso anu. Zala zanu zikupereka mphamvu zofunika kuti zichinjirize iyo kugwa kuchoka m’manja anu. Ndipo zala zimenezo zikulamuliridwa ndi ubongo kuti zichite chimene kwenikweni mukufuna kuti izo zichite pamene mukutembenuza tsamba. Chikanakhala tsoka chotani nanga tikanakhala opanda manja!
Maso anu akuphatikizidwanso m’kuŵerenga masamba amenewa. Cholowanecholowane wozizwitsa wa mitsempha ndi mbali zina za thupi zimagwira ntchito kuti zitenge zifaniziro za mawu ndi zithuthunzi kuchoka pa tsamba kupita m’diso lanu ndipo kenaka kupita mu ubongo wanu. Mphamvu za magetsi zotulutsidwa ndi diso zimaperekedwa ku ubongo, kumene zimagwiritsiridwa ntchito kupanga zifaniziro zowoneka zofanana ndi zokhala patsambalo. Kupenya kwathu kuli kofunika chotani nanga, ndipo iri ngozi yotani nanga pamene kwasoŵeka!
Ubongo wa munthu umalemera kokha chifupifupi mapaundi atatu ndipo uli waung’ono mokwanira kulinga m’dzanja lanu. Koma uli chozizwitsa, chimodzi cha zilengedwe zocholowanacholowana m’chilengedwe. umatheketsa ife kulingalira, kuwona, kukhudza, kulankhula, ndi kugwirizanitsa kayendedwe kathu. Tiyamikira ubongo wathu wocholowanacholowana, tingasangalale ndi kulowa kwa dzuŵa kokongola, zakudya zokoma, kuwomba kwa mphepo ya m’dzinja pa maso pathu, kawonedwe kokongola ka mapiri owopsya, kuseka kwa khanda, kununkhira kwa duŵa, kugwira kwa winawake yemwe timakonda—ndipo zambiri za izi popanda kuyesayesa kodziŵika kulikonse ku mbali yathu. Popanda ubongo wodabwitsa umenewu, sitingakhoze kusangalala ndi chirichonse.
Ali olondola chotani nanga mawu a wamasalmo: “Chipangidwe changa nchowopsya ndi chodabwitsa”!—Masalmo 139:14.
Komabe, ndi chiwiya chabwino chonsechi, nthaŵi imafika pamene thupi potsirizira pake limaleka kugwira ntchito. Timadwala ndi kukalamba, ndipo kenaka timafa. Pali zoipa zambiri m’dziko lotizungulira chakuti ngakhale pamene tiri ndi umoyo wabwino, kusangalala kwathu ndi moyo kumathetsedwa. Kodi mikhalidwe yosavomerezeka imeneyi idzakhalapo nthaŵi zonse? Kapena kodi matupi athu analinganizidwa ndithudi kukhala kosatha—popanda matenda osakaza, ukalamba, ndi imfa—kusangalala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi m’lingaliro lotheratu kuposa chirichonse chimene tsopano tingakumane nacho?
Galamukani! idzasanthula nkhani zimenezi m’makope atatu miyezi ikudzayo. Mbali yoyambirirayi, tidzakambitsirana kokha zochepera za ziwalo za thupi lathu zozizwitsazo: dzanja, diso, ndi ubongo.