Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 9/8 tsamba 19
  • Chiwopsyezo cha Nyukliya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiwopsyezo cha Nyukliya
  • Galamukani!—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kuopa Nyukiliya—Sikunathe Ngakhale Pang’ono
    Galamukani!—1999
  • Anthu Akufunafuna Zothetsera
    Galamukani!—1988
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 9/8 tsamba 19

Chiwopsyezo cha Nyukliya

TANGOLINGALIRANI anyamata aŵiri ali m’garaji yotsekedwa, ataimirira pansi podzazidwa ndi petulo. Aliyense atanyamula bokosi la machisa . . .

Ichi chikuchitira chitsanzo bwino lomwe mkhalidwe womwe ulipo lerolino pakati pa mphamvu zazikulu ziŵiri. Zonse ziŵirizo ziri ndi mosungira zida za nyukliya zodzetsa mantha zomwe zitagwiritsiridwa ntchito zingakhoze kutulukamo mu chiwonongeko chotheratu. Mamissile awo aima okonzekeretsedwa mowonekera kaamba ka kupha, ziŵiya za chitsogozo cha dongosolo lawo zikuzungulira mofulumira.

Zikwi za athenga a imfa amenewa zimabisala kunsi kwa nthaka mkati mwa maenje a konkiriti. Mazana ena owonjezereka amalalira mkati mwa masitima a m’madzi a nkhondo ndipo komabe zochulukirabe zimapezeka m’mapiko okhotera kumbuyo a ndege za jet. Dziko lowopsyezedwa limadabwa kuti, Kodi nchiyani chimene chidzachitika ngati zidazo zitagwiritsiridwa ntchito?

Kazembe wamkulu akuyankha. Iye akunena kuti nkhondo ya nyukliya ikakhoza kukhala “tsoka lalikulu koposa m’mbiri lochititsidwa ndi malamulo a akulu ochuluka.” Wasayansi mmodzi akuwonjezera kuti: “Pali ngozi yenieni ya kuthetsedwa kwa munthu.”

Mwambi wakale wa Chigriki umanena za munthu wotchedwa Damocles yemwe anapangitsidwa kukhala kunsi kwa lupanga lolenjekedwa ndi kachingwe kamodzi ka tsitsi. Lupanga limenelo lingaimire bwino lomwe zida za nyukliya, ndipo Damocles, anthu onse. Chotsani lupangalo, ena anganene tero, ndipo Damocles adzakhala wosungika. Koma kodi chiyembekezo choterocho chiri chotsimikizirika? Kupita patsogolo m’zaka za posachedwapa kwapereka chiyembekezo kwa ambiri:

March 1983: Prezidenti Reagan wa U.S. ayambitsa Strategic Defense Initiative, kufufuza kwa sayansi kolinganizidwa kupanga zida zankhondo kukhala “zopanda ntchito ndi zachabe.”

January 1986: Mtsogoleri wa Soviet Mikhail Gorbachev ayambitsa za kuthetsa zida zonse za nyukliya podzafika pamapeto a zana lino. Iye pambuyo pake akulongosola kuti: “Tiri okonzekera kukambitsirana osati kokha pa kuthetsa mpikisano wa zida, komanso pa kuthekera kwakukulu koposa kwa kuchepetsa zida zankhondo, kufika ku kuleka kugwiritsira ntchito zidazo kwa chisawawa ndi kotheratu.”

December 1987: Gorbachev ndi Reagan anasaina chimvano cha kuchepetsako mamissile. Mogwirizana ndi nkhani yochitiridwa ripoti, “ndi nthaŵi yoyamba chiyambire mbandakucha wa Mbadwo wa Atomic pamene mphamvu zazikulu za dziko zavomerezana osati kokha kuchinjiriza zida za nyukliya koma kuchotsapo dongosolo lonse.”

Kodi ndi chotsimikizirika chotani chimenecho, ngakhale ndi tero, kuti kupita patsogolo kwa posachedwapa kumeneku kudzakhoza kutulukamo dziko lopanda zida za nyukliya? Kodi ndi zokhumudwitsa zotani zimene zikuima m’njira ya chipambano?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena