Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 9/8 tsamba 20-22
  • Kupanikiza kwa Nyukliya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupanikiza kwa Nyukliya
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiitano kaamba ka Kuthetsa
  • Bomba monga Chochinjiriza
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kuopa Nyukiliya—Sikunathe Ngakhale Pang’ono
    Galamukani!—1999
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Kuopa Nyukiliya Kwatha?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 9/8 tsamba 20-22

Kupanikiza kwa Nyukliya

PAMWAMBA pa nsanja yaitali yaing’ono mu mbandakucha wa chipululu cha New Mexico panakolowekedwa chitsulo cholimba chozungulira chimene anthu anachitcha Gadget. M’maenje makilomita asanu ndi anayi kutali, akatswiri a zopangapanga, za mankhwala, odziŵa masamu, ndi asilikari anali osakhazikika, anayang’ana pa koloko zawo, ndipo anazizwitsidwa ngati Gadget ikakhozadi kugwira ntchito.

Inatero. Pa timphindi 15 isanakwane 5:30 a.m., Gadget inaphulika, ikumatulutsa mphamvu yake ya nyukliya pa miliyoni imodzi ya kamphindi. Iyo inaponya laŵi la moto lomwe likakhoza kuwonedwa kuchokera ku pulaneti ina ndi kupangitsa kuphulika komwe kunamvedwa makilomita 300 kutali. Kutentha kwa kuphulika kwa Gadget—kotentha kwambiri cha pakati pake kuposa pakati pa dzuŵa—kunapangitsa mchenga wa m’chipululu chifupifupi kilomita imodzi kukhala mphete yofiira ya galasi la radioactive. Ena analumbira kuti dzuŵa linatuluka kaŵiri tsiku limenelo.

Pa August 6, 1945, masiku 21 pambuyo pake, bomba la atomu lachiŵiri linaphwanya mzinda wa ku Japan wa Hiroshima, potsirizira pake likumapangitsa imfa za anthu oyerekezedwa pa 148,000. Mbadwo wa nyukliya unayambika.

Zimenezo zinali zaka 43 zapitazo. Zida kufika ku nthaŵi 4,000 zamphamvu koposa zakhala zikuyesedwa chiyambire pamenepo. Mphamvu zosanganizidwa za zida zonse zadziko zayerekezedwa kufika ku unyinji wonse pamodzi wa 20 biliyoni tons ya TNT—kuposa nthaŵi miliyoni imodzi ya mphamvu yakupha ya bomba la Hiroshima!

Chiitano kaamba ka Kuthetsa

Molingana ndi phunziro la 1983 la World Health Organization, nkhondo yotheratu ya nyukliya ikakhoza kupha anthu biliyoni imodzi kotheratu. Biliyoni yachiŵiri ikakhoza kufa pambuyo pake chifukwa cha kuphulikako, moto, ndi mbaliŵali. Maphunziro a posachedwapa ali ngakhale onkitsa. Momvekera, kenaka, kufuula kwakwezedwa kaamba ka kuthetsedwa kotheratu kwa zida za nyukliya.

Ngakhale kuli tero, si kufuula konse kaamba ka kuthetsa izo komwe kuli pa maziko abwino a umunthu. Ena amatsutsa kuti zida za nyukliya ziri kokha kapena ziribiretu phindu mu nkhondo yeniyeni. Chifukwa cha mphamvu zake za kupha zowopsya, kokha kuputidwa konkitsa kungakhoze kokha kulungamitsa kugwiritsira ntchito izo. Chotero, United States sinazigwiritsire ntchito izo mu Korea kapena Viet Nam, anthu a ku Britain sanazigwiritsire ntchito izo mu Falklands, kapena ngakhale anthu a ku Soviet sanagwiritsire ntchito izo mu Afghanistan. Mlembi wakale wa Chitetezero wa U.S. Robert McNamara wanena kuti: “Zida za nyukliya sizimatumikira chifuno cha nkhondo mpang’ono pomwe. Izo ziri zopanda ntchito kotheratu—kusiyapo kokha kuletsa mdani wa wina ku kuzigwiritsira ntchito izo.”

Mofananamo, zida za nyukliya ziri zopanda kugwiritsiridwa ntchito kokulira monga zomenyera malire kaamba ka kuwopsyeza kapena kusonkhezera mitundu ina. Mphamvu zazikuluzo ziri zosalimba kotheratu. Ndipo ponena za mphamvu zopanda zida za nyukliya, iwo kaŵirikaŵiri amayedzamira pa kuimirira ku mphamvu zazikulu ndi mantha ochepera a kubwezera mwa kugwiritsira ntchito zida za nyukliya.

Potsirizira pake, pali zotaika. Molingana ndi phunziro lofalitsidwa mu Bulletin of the Atomic Scientists, mkati mwa zaka za 1945-85 United States yokha inatulutsa chifupifupi zida za nyukliya 60,000.a Zotaika? Chifupifupi $82,000,000,000—ndalama zochulukira kwambiri kaamba ka chinachake chimene sanayembekezere kugwiritsira ntchito.

Bomba monga Chochinjiriza

Lingaliro la kuchinjiriza liri mwinamwake lakale monga mmene iliri mbiri ya kuwombana. Koma mumbadwo wa nyukliya, kuchinjiriza kwatenga mbali zatsopano. Mtundu uliwonse womwe ukuyang’anizana ndi kuwukiridwa kwa nyukliya umatsimikiziridwa za kubwezera kwa nyukliya kosakaza ndi kwa mwamsanga.

Kazembe B. L. Davis, wolamulira a nkhondo wa U.S. Strategic Air Command, chotero akunena kuti: “Nkhani yokhutiritsa ingapangidwe yakuti zida za nyukliya . . . zapangitsa dziko kukhala malo achisungiko koposa. Izo sizinakhoze kuthetsa nkhondo mpang’ono pomwe; zikwi zingapo zikupitirizabe kufa chaka chirichonse m’kukanthana komwe sikuli kwakung’ono ku mitundu yokhudzidwayo. Koma kulowereramo kwa mphamvu zazikulu m’kukanthana koteroko kukupendedwa mosamalitsa kotero kuti apewe kufikira kwachindunji chifukwa cha kuwonekeratu kwa kugwera m’moto wokulira—nyukliya kapena chitungu chokulira.”

M’nyumba iriyonse yodzala ndi mfuti, ngakhale ndi tero, nthaŵi zonse pamakhala ngozi yakuti winawake adzalasidwa mwangozi. Lamulo limodzimodzilo limakhala lowona m’dziko lodzala ndi zida za nyukliya. Nkhondo ya nyukliya chotero ingakhoze kuphulika pansi pa mikhalidwe yotsatirayi:

(1) Cholakwika cha kompyuta kapena kusagwira ntchito bwino kwa chiŵiya chomwe chingapangitse dziko kuganizira kuti liri pansi pa kuwukiridwa kwa nyukliya. Kuyankha kungakhoze kukhala kubwezera kwa nyukliya.

(2) Zida za nyukliya zingakhoze kupezedwa ndi munthu wonkitsa kapena mphamvu za uchigaŵenga zomwe zingakhale zoletsa mochepera ku kugwiritsira ntchito izo kuposa mmene ziliri mphamvu zamakono za nyukliya.

(3) Kukula kwa nkhondo yochepera m’dera limene zikondwerero za mphamvu zazikulu zikuphatikizidwa—monga ngati Gulf ya Persia.

Mosasamala kanthu za ngozi zoterozo, mitundu pakali pano yasungirira lamulo la chisungiko kupyolera m’kudzichinjiriza. Komabe, m’dziko lomwe likukula ndi zida za nkhondo, anthu sakudzimva osungika. Kulinganizidwa kwa mphamvu kuli motsimikizirikadi kulinganizidwa kwa uchigaŵenga, lamulo la kudzipha ku limene mabiliyoni a dziko ali minkhole yosadzifunira. Ngati zida za nkhondo ziri monga lupanga la Damocles, kuchinjiriza kuli tsitsi limodzi lomwe likuchinjiriza ilo. Koma bwanji ngati chochinjirizacho chalephera? Yankho liri lowopsya kuyang’anizana nalo.

[Mawu a M’munsi]

a Chifukwa chakuti ziŵiya za nyukliya zimatha mphamvu, zida zakale zimafunikira kulowedwa m’malo ndi zatsopano.

[Bokosi patsamba 6]

MPHAMVU YA BOMBA LA MEGATON IMODZI

Mbaliŵali za Chitungu (Kuwala ndi Kutentha): Kuphulika kwa nyukliya kumapanga kung’anima kokulira kwa kuwala komwe kumapangitsa kukhala wa khungu kapena kupangitsa anthu kusawona bwino cha kutali kuchoka pa malo ophulitsidwira—kufika ku makilomita 21 m’masana ndi makilomita 85 usiku m’kuphulika kumodzi kwa megaton.

Pa malo kapena pafupi ndi pomwe paphulitsidwira (malo omwe aphulitsidwapo bomba), kutentha kokulira kwa malaŵi a moto kungasungunule anthu. Kutali kwambiri (kufika ku makilomita 18), anthu amavutika ndi kupsya kwa ukulu wa nthaŵi ziŵiri kapena zitatu pa khungu lowunikiridwalo. Zovala zimayaka moto. Makapeti ndi mipando zimayaka. Pansi pa mikhalidwe ina, m’kuntho wotentha moposerapo umatulukapo, ukumakuta anthu mu imfa.

Kuphulitsa kwa Mumlengalenga: Kuphulitsa kwa nyukliya kumayambitsa mphepo za mkuntho. Pomwe paphulitsidwira bomba, chiwonongeko chimakhala chotheratu. Ku malo akutali, anthu m’manyumba amatswanyidwa ndi madenga omagwa kapena makoma; ena amavulazidwa kapena kuphedwa ndi zidutswa zomawuluka ndi mipando. Enabe amafa ndi kulephera kupuma kochititsidwa ndi dothi lokulira la manyumba ophwanyidwa kapena njerwa. Kukuntha kopambanitsa kwa mphepo kumapangitsa chiwalo cha m’khutu kuvulazika kapena kukha mwazi kwa m’mapapo.

Mbaliŵali: Kuphulika kokulira kwa maneutrons ndi cheza cha gamma kumatulutsidwa. Kuwunikiridwa kwakung’ono kumapangitsa matenda ozindikiridwa ndi nseru, kusanza, ndi kulefuka. Kuvulazika ku maselo a mwazi kumachepetsa kuchinjiriza kwa kuyambukira kwa matenda ndipo kumachedwetsa kuchiritsidwa kwa kuvulala. Kuwunikiridwa kokulira ku mbaliŵali kumapangitsa kulefuka, manjenje, kulobodoka kwathupi, ndi kuwodzera. Imfa imatsatira mkati mwa ora limodzi kufika ku 48.

Opulumuka okanthidwa ndi mbaliŵali amakhala owunikiridwa ku kansa. Iwo mwachidziŵikire kwambiri alinso okhoza kupatsira kulemala kwawoko kwa ana awo, kuphatikizapo kuchepetsedwa kwa kubala, kutaya mimba, ana opangidwa olemala kapena obadwa akufa kale, ndi kufooka kwina kobadwa nako kosazindikiridwa bwino.

Magwero: Comprehensive Study on Nuclear Weapons, yosindikizidwa ndi Mitundu Yogwirizana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena