Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 9/8 tsamba 3
  • Kodi Kuopa Nyukiliya Kwatha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuopa Nyukiliya Kwatha?
  • Galamukani!—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kuopa Nyukiliya—Sikunathe Ngakhale Pang’ono
    Galamukani!—1999
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?
    Galamukani!—2004
  • Kupanikiza kwa Nyukliya
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 9/8 tsamba 3

Kodi Kuopa Nyukiliya Kwatha?

KWA zaka zopitirira 40, anthu akhala akuopa kuti dziko lidzaonongedwa ndi nyukiliya. Kenaka, mu 1989, Khoma la Berlin linagwa—kuyamba kwa kutha kwa Chikomyunizimu ku Soviet. Mosakhalitsa, mayiko amphamvu koposa anagwirizana kuti asamachalire kuphulitsana ndi zida zawo za nkhondo. “Armagedo” ya nyukiliya itaimitsidwa motero, kapena tingoti tsiku lake litasinthidwira m’tsogolo, dziko linangoti zinthu zakhala bwino.

Komabe, akatswiri ambiri akuona kuti ndibwino kulinda kaye madzi apite tisananene kuti tadala. Mu 1998 wotchi yotchuka yoonera chiwonongeko cha dziko ya magazini a The Bulletin of the Atomic Scientists anaikokera ndi mphindi zisanu, kuifikitsa pa kutatsala mphindi zisanu ndi zinayi kuti ikwane pakati pausiku—kusonyeza kuti, kuopa kuti zida za nyukiliya ziphulitsidwa kunali kulipobe.a Zoona, zochitika za dziko zasintha. Ano si masiku amene pali mayiko aŵiri okha amphamvu zofanana pa zida za nyukiliya zimene akukanika kumenyana nazo. Lero mayiko ambiri angapange zida za nyukiliya! Ndiponso, akatswiri akuopa kuti mwina zigaŵenga tsiku lina zidzapeza zipangizo zopangira zida zimenezi n’kudzapanga bomba langati la atomu.

Ndiponso, ngakhale kuti zida zambiri zachotsedwa, mayiko a United States ndi Russia ali ndi nkhokwe zambirimbiri za zida za nyukiliya. Malingana ndi gulu lina lofufuza zida za nyukiliya lotchedwa Committee on Nuclear Policy, zida za nyukiliya zokwanira 5,000 pakali pano ndi zotchera kale. Lipoti lawo likuti: “Motero ndi mmene zilili zinthu panopa, ngati pataperekedwa lamulo lakuti zida zimenezi azigwiritse ntchito, [mabomba oulutsidwa ndi kukaphulikira mu kontinenti ina] okwanira 4,000 (2,000 ochokera ku lililonse la mayiko aŵiriŵa) angathe kuulutsidwa kuti akaphulike kumalo ochaliridwa pamphindi zochepa chabe ndipo mabomba ena [otumizidwa kuchokera pa sitima zoloŵa pansi pa nyanja] zokwanira 1,000 zingathe kutumizidwa kumalo ochaliridwa mwakanthaŵi kochepa chabe pambuyo pake.”

Chifukwa chakuti pali nkhokwe zoterezi, n’kutheka kuti nkhondo yongochitika mwangozi kapena ngakhale yoikonzekera ingabuke. Wambalume wina wotchuka wa ku Russia Vladimir Belous anachenjeza kuti: “Mosiyana ndi zimene atsogoleri andale akufuna, mwatsoka ngozi ya zida za nyukiliya ingathe kuchitika imene ingathe kusokoneza dziko lonse.” Choncho ngakhale kuti nkhondo ya mawu inatha, kuopa nkhondo ya nyukiliya yoseseratu chilichonse sikunathe ayi. Koma kodi chiopsezo chimenechi ndi chachikulu bwanji? Kodi zida za nyukiliya zidzatheratu padziko lapansi? Nkhani zotsatirazi zilongosola zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

a Wotchi yoonera chiwonongeko cha dziko imene ili pa chikuto cha magazini ya The Bulletin of the Atomic Scientists ndi chizindikiro cha mmene anthu akuganizira kuti dziko layandikira “pakati pausiku” pa nkhondo ya nyukiliya. Kwa zaka makumi angapo m’mbuyomu, muvi wosonyeza mphindi wa wotchiyi wakhala ukusunthidwa kusonyeza mmene ndale zilili padziko.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Mabomba ophulitsidwa ali patsamba 2 ndi 3: U.S. National Archives Photo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena