Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 8/8 tsamba 30
  • Yochepera Koma Yokhala ndi Zitsogozo Zapadera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yochepera Koma Yokhala ndi Zitsogozo Zapadera
  • Galamukani!—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Malangizo Anachokera Kuti?
    Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri
  • Maselo Athu Ali Ngati Laibulale
    Galamukani!—2015
  • Kuchuluka kwa Zinthu Zimene DNA Imasunga
    Galamukani!—2013
  • Umboni Wakuti Kuli Mlengi
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 8/8 tsamba 30

Yochepera Koma Yokhala ndi Zitsogozo Zapadera

DEOXYRIBONUCLEIC ACID. Ochepera angalitchule ilo, ndipo osati ngakhale kulikumbukira ilo. Ambiri amalidziŵa ilo mwa kungotchula malemba oimira liwulo akuti: DNA. Magwero a DNA ali ochepera kwenikweni kotero kuti akatswiri a sayansi okhala ndi ziwiya zawo zamphamvu zokuzira zinthu m’chenicheni sanawonepo amodzi kufikira kokha posachedwapa. Komabe magwero oterowo ali ndi nkhokwe zochulukira za chidziŵitso chomwe chimayambukira miyoyo ya tonsefe. Msinkhu wanu, mtundu wa tsitsi, mtundu wa maso ndi khungu—zonsezi zimagamulidwapo pasadakhale, zolembedwa mu DNA yanu.

Koma choloŵanecholoŵane wopanga zigamulo ameneyu tsopano akugwiritsiridwa ntchito m’kupanga mtundu wosiyana wa chigamulo chakuti: kaya anthu adzakhala aufulu kapena kupita ku ndende, kukhala ndi moyo kapena kufa. Kusiyana kwapadera kwenikweni kwa DNA ya munthu aliyense kwatsegula njira ku kachitidwe katsopano kozindikiritsira munthu aliyense payekha, kotchedwa kusindikiza kwa DNA.

Popeza kuti DNA imapezeka m’chenicheni m’maselo onse a thupi ndi m’zamadzi zochulukira za thupi, apandu angazengedwe mlandu chifukwa chosiya kumbuyo tsitsi loŵerengeka kapena kachidutswa ka khungu, ngakhale chidutswa cha chungamu. Machenjera atsopano akhala okhutiritsa mwapadera molimbana ndi owukira a kugonana. Kalekale, ogwirira chigololo omwe anakana moumirira kukhala kwawo aliwongo azengedwa mlandu kupyolera mu DNA ya iwo eni. Mmodzi wakupha munthu anatumizidwa ku mpando wophera wa magetsi pa muyezo wa umboni woterowo.

Kusindikiza kwa DNA kumapangitsa maloya ochinjiriza kukhala osowa chochita. The National Law Journal ya ku United States ikugwira mawu wina kukhala akunena kuti: “Chiri chosakaza. Pamene katswiri aloŵa ndi kunena kuti pali kokha mwaŵi umodzi mu 700 miliyoni wakuti munthu wanu sali yemwe anatero [wopangitsa upandu]—zimangokukhwethemula.” Ku mbali ina, zosindikiza za DNA zingamasule munthu wozengedwa mlandu molakwika ndipo chotero zingachepetse ngozi ya kuika m’ndende kapena kupha munthu wopanda liwongo.

Chikhalirechobe, palibe njira yausayansi, mosasamala kanthu za kukhala kwake yamakono, yomwe ingathetse tsoka la chiwunda chonse la upandu. Pambali pa icho, maupandu ochulukira achiwawa samasiya umboni uliwonse wa DNA. Ayi, kokha tsiku lomwe lidzawona kuwonongedwa kwa oipa kuchoka pa dziko lapansi ndi limene lidzawona mapeto a upandu.—Salmo 37:10, 11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena