Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 10/8 tsamba 7-9
  • Nkhondo—Kuchita ndi Zotulukapo Zake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhondo—Kuchita ndi Zotulukapo Zake
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwopsyeza
  • Zotulukapo Zake
  • Kupeza Chothetsera
  • Mangilirani Chiyembekezo mu Malonjezo a Mulungu
  • Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhondo Yothetsa Ndhondo
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhondo—Kutsendereza ndi Zipsyera
    Galamukani!—1989
  • Chimene Chinandichititsa Kusiya Kukonda Nkhondo
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 10/8 tsamba 7-9

Nkhondo—Kuchita ndi Zotulukapo Zake

NDIMOTANI mmene anthu owopsyezedwa ndi nkhondo amachitira nazo? Kuti tizindikire nkhaniyi, Galamukani! inafunsa minkhole ina ya nkhondo.

Bob Honis anali pakati pa makumi a zikwi za Asilikali Apamadzi a ku U.S. omwe anamenya nkhondo mu nkhondo ya dziko yachiŵiri m’kukanthana kwa ku Iwo Jima kumadzulo kwa Pacific. Nkhani yake yasindikizidwa osati kuti iwopsyeze koma kuti isonyeze kuti nchotheka kwa ena kuchira ku zokumana nazo zowopsyezadi.

Kuwopsyeza

“Tinayamba kufikira kwathu ku Iwo Jima pa 8:30 a.m. pa February 19, 1945. Mfuti zazikulu za sitima yankhondo yotchedwa Tennessee zinandandamitsidwa kumbuyo kwathu, ndipo kenaka ndege yathu yotera inapasulidwa ndi kuponyeredwa zida kochitidwa ndi adani kuchokera ku chandamale. Titachititsidwa mantha, pa zochitika zomwe zinali kutsogolo, ndinafuula pakati pa phokoso lonselo ndi phokoso la kuphwanyaphwanyako kuti, ‘Tipulumutsirenkoni ena!’ pamene tinatsatira magulu ankhondo osakaza oyambirira.

“Nditafika pa gombe, chonse chomwe ndinakhoza kununkhiza chinali fungo lodwalitsa la wonga, phulusa la kuphulitsa, ndi ziŵiya zomapsya. Ndege yathu yotera inagundidwa. Woyendetsa anaphedwa pa nthaŵi yomweyo, ndipo ziŵiya zathu zonsezo zinawonongedwa.

“Sindidzaiŵala konse kawonekedwe ka asilikali apamadzi ena akufa. Winawake anafotseredwa mu mchenga. Nsapato zake zankhondo, zopanda chakunsi chake, zinakokedwera kumawondo, miyendo imene pa nthaŵi imodzi inali yamphamvu, yolimba. Nditayang’ana ku lamanja kwanga pamene ndinkakwawa m’nkhwimba ya nkhandwe yokumbidwa mofulumira, ndinawona msilikali wapamadzi wina ali woyedzamira kutsogolo mfuti yake itasindikizidwa pachifuwa pake, wopanda mutu. Gombelo linakhala loipitsidwa ndi asilikali apamadzi akufa, ambiri omwe anali odukaduka kosaneneka. Ichi chinali kokha chiyambi.

“Pa tsiku lachiŵiri ndinatumizidwa kukafufuza amodzi a malo athu. Ndi zomvetsa chisoni chotani nanga zomwe ndinawona! Mzinga wophulika unali utadula miyendo ndi mikono ya msilikali wapamadzi woyambirira yemwe ndinawona. Chisoti chake ndi nsambo ya kuchibwano zinali zidakali chikhalirebe. Maso ake anali otuzuka, akumayang’ana kutsogolo ngati kuti anali kusinkhasinkha. Owunjikanawunjikana uku ndi uko monga ziŵiya zoduka za zidoli, anali ziŵalo zina za gulu la mfutilo omwe sanali kanthu koma kokha minofu yonyotsoka yomwazikana m’phulusa lofeŵa, la kuphulitsidwako.

“Kuphako kunapitirizabe mpaka tsiku lachitatu. Kenaka akufa anayamba kuvunda mofulumira. Kununkhako kunakhala koipirako. Kunali paliponse. Panalibe pothaŵira.

“Pambuyo pa masiku anayi a kumenyana kwaukali, pa February 23 panali kukwezedwa komwe tsopano kuli kotchuka kwa mbendera ya ku Amereka pa Phiri la Suribachi. M’malo mosangalatsidwa, zonse zomwe ndinadzimva zinali kusoŵa pothaŵira. Akufa anali konsekonse. Moyo unawonekera kukhala wopepuka kwenikweni. Nkhondo yosakazayo inapitirizabe kufikira March 26, pamene potsirizira pake Iwo Jima inalandidwa, pambuyo pa milungu ingapo ya kupha kopanda malekezero. Unali mwazi wotani nanga—chiwonkhetso cha anthu 26,000 a ku Amereka ndi a ku Japan anaphedwa pa chisumbu cha makilomita makumi awiri okha mbali zonse zinayi!

Zotulukapo Zake

“Ikanakhala nthaŵi ya chisangalalo chokulira pamene ndinatumizidwa kuchokera kwa Asilikali Apamadzi ndi kukagwirizananso ndi banja langa. Komabe, m’malomwake, zomwe zinkachitika mkati mwanga tsopano zinawonekera—kusoŵa chochita kodzetsa mantha ndi lingaliro lopanda chisungiko.

“Mafunso anapitirizabe kundizunza ine. Ngati moyo uli wopepuka chotero, kodi ndi iti yomwe iri nsonga ya kukhala ndi moyo? Kodi pangakhaledi Mulungu yemwe amasamala? Kodi ndidzakhala ndikusautsidwa ndi zokumana nazo zanga kwa utali wa moyo wanga wonse? Ngakhale pambuyo pa kukwatira mkazi wanga, Mary, kusautsidwako kunapitirizabe. Sindinakhoze kuwona chiyembekezo chirichonse chokhalitsa, mtsogolo mwachimwemwe, kokhadi nkhondo ndi kupha kopanda nzeru, potsirizira pake, kuwonongedwa kwa dziko lapansi ndi miyoyo yonse yokhala pa ilo.

Kupeza Chothetsera

“Mwamsanga pambuyo pa kukwatirana kwathu, mkazi wanga ndi ine tinachezeredwa ndi Mboni za Yehova ziŵiri. Ichi chinandipatsa ine mwaŵi wa kufunsa ena a mafunso osanthula ponena za nkhondo, kuvutika, ndi chifuno cha moyo. Mayankho ku mafunso anga anadza mofulumira kuchokera m’Baibulo.

“Inde, pali Mulungu wachikondi yemwe amasamala ndi yemwe mofulumira adzachiritsa kuŵaŵa kwathu konse ndi chisoni. (Salmo 83:18; Chibvumbulutso 21:1-4) Ayi, Mulungu samaletsa nkhondo m’kufunafuna zonulirapo za ndale zadziko za anthu. (Salmo 46:9; Yesaya 2:4; Yohane 18:36) Ayi, dziko lapansi silidzawonongedwa m’chipululutso cha nyukliya. Ilo lidzakhala kosatha, monga mudzi wa paradaiso kwa onse omwe amafikitsa ziyeneretso za Mulungu.—Salmo 37:29; Yesaya 45:18; Chibvumbulutso 11:17, 18.

“Pamene phunziro langa la malonjezo othuzitsa mtima a Baibulo linapitirizabe, mphako yomwe inali mkati mwanga inadzazidwa mwa pang’onopang’ono. Ndinakhala ndi chidaliro chakuti Ufumu wa Mulungu ulidi chochititsa chotsimikizirika cha kubweretsa mtendere ndi chisungiko pa dziko lapansi. Potsirizira pake nkhondo ya Mulungu ya Armagedo idzachotsa kuipa konse pa dziko lapansi.—Danieli 2:21, 22; Mateyu 6:10; Chibvumbulutso 16:14-16.”

Mangilirani Chiyembekezo mu Malonjezo a Mulungu

Ena amavomereza kuti kuphunzira chowonadi chonena za chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi ndi zifukwa Zake za kulolera kuipa kosakhalitsa kwakhala chochititsa champhamvu cha kuwathandiza kuchita ndi zipsyera zotsala zankhondo.

Uku sindiko kulingalira kuti thandizo la ukatswiri wa mankhwala silingafunikire pa nthaŵi zina. Koma chiyembekezo chenicheni, chozikidwa pa malonjezo odalirika a Mulungu opezeka m’Baibulo, chimapatsa nyonga yamkati ya kupirira mavuto owopsya.

Komabe, inu mungakhale osayambukiridwa mwaumwini ndi zipsyera za nkhondo. Koma mungadziŵe winawake yemwe ali tero. Kodi nchiyani chimene mungachite kuti muthandize? “Khalani womvetsetsa ndi wolimbikitsa kwa awo omwe avutika m’njirayo,” akutero m’nkhole wina wa chipsyera cha nkhondo, Mary C  . “Thandizani oterowo kuyang’ana kutsogolo, kukhala m’malonjezo a Mulungu, osati masoka a zapitazo,” iye akulangiza tero. Inde, khalani oleza mtima ndi achifundo. Lolelani. Ndipo yeserani kuwathandiza kumangirira chiyembekezo cha mtsogolo.

‘Koma,’ inu mungatero, ‘kodi ndimotani mmene zingakhalire kuti awo omwe avutika kupyola m’zipsyera zankhondo, nkhondo ina, Armagedo, idzakhalanso chothetsera?’ Armagedo, yomwe iri nkhondo ya Mulungu motsutsana ndi kuipa konse, idzakhala nkhondo yopanda minkhole yosakhala ndi liwongo. Iyo sidzaswa malamulo a makhalidwe abwino a chilungamo ndi ubwino. Iyo idzachitidwa ‘m’chilungamo,’ mu imene kokha oipa ndiwo adzafa.—Chibvumbulutso 19:11; Miyambo 2:20-22.

Armagedo sidzakhala ndi zotulukapo zowopsya, sidzadzetsa maloto kapena zipsyera zina za maganizo. Dziko latsopano la Mulungu lidzakwaniritsa chithunzi cha ulosi cholembedwa pa Yesaya 65:17-19: “Zinthu zakale sizidzakumbukirika, . . . ndipo mawu a kulira sadzamvekanso mwa iye, pena mawu akufuula.”

Minkhole yonse ya kumbuyo ya nkhondo yakupha ndi chiwawa, ngakhale akufa, adzapindula m’nkhondo imeneyi. (Salmo 72:4, 12-14; Yohane 5:28, 29) Ganizirani za zimenezo—kubwezeretsedwa kwa Paradaiso wa mtendere yemwe Mulungu poyambirirapo analingalira.

“Chiyembekezo chimenechi chimene Baibulo limapereka,” anatero Bob Honis, “chiri mfungulo ya kuchita ndi zotulukapo za nkhondo. Onse omwe avulazidwa ndi zipsyera zankhondo angapindule ku chiyembekezo choterocho. Mtundu umenewu wa chiyembekezo uli, monga mmene Baibulo limanenera, ‘nangula wa moyo.’”—Ahebri 6:19.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Zomwe zinkachitika mkati mwanga tsopano zinawonekera—kusoŵa chochita kodzetsa mantha ndi lingaliro lopanda chisungiko”

[Zithunzi patsamba 7]

Paulendo wopita ku Iwo Jima, tinaphunzira zitsanzo za chisumbucho

Honis akuwonekera pamwamba kulamanja

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Marine Corps

[Chithunzi patsamba 9]

Bob ndi Mary Honis lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena